Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • na tsamba 14-16
  • Akristu ndi Dzinalo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akristu ndi Dzinalo
  • Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu ndi Dzinalo
  • Akristu Oyambirira
  • Chifukwa Chake Tiyenera Kudziwa Dzina la Mulungu
    Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
  • Muzilemekeza Dzina Lalikulu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Tanthauzo la Dzina la Mulungu Ndiponso Mmene Tingaligwiritsire Ntchito
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Dzina la Mulungu
    Galamukani!—2017
Onani Zambiri
Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
na tsamba 14-16

Akristu ndi Dzinalo

PALIBE amene anganene motsimikizira kwambiri nthawi yeniyeni pamene Ayuda osunga mwambowo analeka kutchula dzina la Mulungu mofuula ndipo mmalo mwake kulowetsamo mawu Achihebri a Mulungu ndi Ambuye Mfumu. Ena amakhulupirira kuti dzina la Mulungu linazimiririka pa kugwiritsiridwa ntchito kwatsiku ndi tsiku m’nthawi ya Yesu isanafike. Koma pali umboni wamphamvu wakuti akulu a ansembe anapitirizabe kulitchula pamadzoma achipembedzo pakachisi—makamaka patsiku Lachitetezo—kufikira nthawi yeniyeni pamene kachisi anawonongedwa mu 70 C.E. Chifukwa chake, pamene Yesu anali padziko lapansi, matchulidwe a dzinalo anali odziwika, ngakhale kuti mwinamwake sanali kugwiritsiridwa ntchito mofala.

Kodi nchifukwa ninji Ayuda analeka kutchula dzina la Mulungu? Mwinamwake, mwapang’ono, chiri chifukwa cha kugwiritsira ntchito molakwa mawu a lamulo lachitatu akuti: “Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe.” (Eksodo 20:7) Ndithudi, lamuloli silinaletse kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu. Ngati zinali zotero, kodi nchifukwa ninji atumiki akale a Mulungu onga Davide analigwiritsira ntchito momasuka nasangalalabe ndi madalitso a Yehova? Ndipo kodi nchifukwa ninji kuti Mulungu analitchula kwa Mose ndi kuuza Mose kulongosolera Aisrayeli ponena za amene anali atamtuma?—Salmo 18:1-3,6,13; Eksodo 6:2-8.

Komabe, podzafika nthawi ya Yesu panali chikhotetero champhamvu cha kutenga malamulo abwino a Mulungu ndi kuwatanthauzira mwanjira yonkitsa kwambiri. Mwachitsanzo, lachinai la Malamulo Khumi linapatsa thayo Ayuda la kusunga tsiku lachisanu ndi chiwiri mlungu uliwonse monga tsiku lopuma, Sabata. (Eksodo 20:8-11) Ayuda osunga mwambo anatanthauzira lamulolo mopitiriza muyezo kwambiri, akumapanga timalamulo tambirimbiri tolamulira ngakhale chinthu chaching’ono koposa chimene chinayenera kapena sichinayenera kuchitidwa pa Sabata. Mosakaikira kunali mu mzimu umodzimodziwo kuti anatenga lamulo loyenerera, lakuti dzina la Mulungu siliyenera kuchitiridwa mwano, pamlingo wopambanitsa, akumanena kuti dzinalo silinayenera ngakhale nkutchulidwa komwe.a

Yesu ndi Dzinalo

Kodi Yesu akanatsatira mwambo wosagwirizana ndi Malemba umenewu? Kutalitali! Ndithudi iye sanaleke kuchita ntchito za kuchiritsa Pasabata, ngakhale kuti chimenechi chinatanthauza kuswa timalamulo topangidwa ndi anthu Achiyuda ndipo ngakhale kuika moyo wake pachiswe. (Mateyu 12:9-14) Ndithudi, Yesu anatsutsaAfarisi kukhala onyenga chifukwa chakuti miyambo yawo inapitirira Mawu ouziridwa a Mulungu. (Mateyu 15:1-9) Chifukwa chake, sikuli kwachiwonekere kuti iye akanaleka kutchula dzina la Mulungu, makamaka kaamba ka chenicheni chakuti dzina la iyemwini, Yesu, limatanthauza “Yehova ndiye Chipulumutso.”

Panyengo ina, Yesu anaimirira m’sunagoge nawerenga kachigawo ka mpukutu wa Yesaya. Chigawo chimene iye anawerenga chinali chimene lero timati Yesaya 61:1, 2, kumene dzina la Mulungu limawonekera nthawi yoposa imodzi. (Luka 4:16-21) Kodi iye akanakana kutchula dzina la Mulungu lolembedwa pamenepo, akumaika mawu akuti “Ambuye” kapena “Mulungu” m’malo mwake? Ndithudi iye sakanatero. Kumeneko kukanatanthauza kutsatira miyambo yosagwirizana ndi Malemba ya atsogoleri achipembedzo Achiyuda. M’malo mwake, timawerenga kuti: “Anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, ndipo osati monga alembi awo.”—Mateyu 7:29.

Kunena zowona, monga momwe tamverakale, iye anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kwa Mulungu kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Ndipo m’pemphero la usiku wa imfa yake isanachitike, iye anati kwa atate wake: “Ndaliwonetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa ine padziko lapansi . . . Atate woyera, sungani awa m’dzina lanu amene mwandipatsa ine.”—Yohane 17:6, 11.

Ponena za malongosoledwe awa ochitidwa ndi Yesu kudzina la Mulungu, bukhu lotchedwa Der Name Gottes (Dzina la Mulungu) limalongosola, patsamba 76 kuti: “Tiyenera kuzindikira chenicheni chozizwitsa chakuti kuzindikiridwa kwa vumbulutso la Mulungu m’Chipangano Chakale nkwakuti ndilo vumbulutso la dzina lake ndi kuti limeneli likulembedwa monsemo kufikira mbali zotsiriza za Chipangano Chakale, inde, limapitirizabe mpaka mbali zotsirizira za Chipangano Chatsopano, kumene, mwachitsanzo, pa Yohane 17:6, timawerenga kuti: “Ndaliwonetsera dzina lanu.’”

Inde, kukanakhala kosalingalirika koposa kuganiza kuti Yesu analephera kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu, makamaka pamene iye anagwira mawu kuchokera m’zigawozo za Malemba Achihebri mu zimene linalembedwamo.

Akristu Oyambirira

Kodi otsatira a Yesu a m’zaka za zana loyamba anagwiritsira nchito dzina la Mulungu? Iwo analamuliridwa ndi Yesu kupanga ophunzira a anthu amitundu yonse. (Mateyu 28:19, 20) Unyinji wa anthu kwa amene akalalikirako sanazindikire Mulungu amene anadzivumbula kwa Ayuda ndi dzina lakuti Yehova. Kodi ndimotani mmene Akristu akakhozera kudziwikitsa Mulungu wowona kwa iwo? Kodi kukakhala kokwanira kungomutcha kuti Mulungu kapena Ambuye? Ayi. Mitundu inali ndi milungu ya iwo eni ndi azimbuye. (1 Akorinto 8:5) Kodi ndimotani mmene Akristu apangira kusiyana kuwoneka bwino pakati pa Mulungu wowona ndi milungu yonama? Kokha mwakugwiritsira ntchito dzina la Mulungu wowona.

Chotero, wophunzira Yakobo analankhula pamsonkhano wa akulu m’Yerusalemu kuti: “Simiyoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake. Ndipo mawu a aneneri avomereza pamenepo.” (Machitidwe 15:14, 15) Mtumwi Petro, m’nkhani yake yodziwika bwino pa Pentekoste, anasonyeza mfundo yofunika ya uthenga Wachikristu pamene anagwira mawu a mneneri Yoweli kuti: “Yense amene akaitana padzina la Ambuye adzapulumutsidwa.”—Yoeli 2:32; Machitidwe 2:21.

Mtumwi Paulo sakusiya chikaikiro ponena za kufunika kwa dzina la Mulungu kwa iye. M’kalata yake kwa Aroma, iye anagwira mawu amodzimodziwo a mneneri Yoeli ndipo akupitirizabe kulimbikitsa Akristu anzake kusonyeza chikhulupiriro chawo m’mawu amenewo mwa kutuluka kukalalikira ponena za dzina la Mulungu kwa ena kotero kuti nawonso, apulumutsidwe. (Aroma 10:13-15) Pambuyo pake iye analemba m’kalata yake kwa Timoteo kuti: “Yense wakutchula dzina la Ambuye adzipatule pa chosalungama.” (2 Timoteo 2:19) Chakumapeto kwazaka zazana loyamba, mtumwi Yohane anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu m’malemba ake. Mawu akuti “Aleluya,” kutanthauza “Tamandani Ya,” amawoneka mobwerezabwereza m’bukhu la Chivumbulutso.—Chivumbulutso 19:1, 3, 4, 6.

Komabe, Yesu ndi otsatira ake anali atalosera kuti mpatuko ukachitika mumpingo Wachikristu. Mtumwi Petro anali atalemba kuti: “Pakakhalanso aphunzitsi onama pakati panu.” (2 Petro 2:1; wonaninso Mateyu 13:36-43; Machitidwe 20:29, 30; 2 Atesalonika 2:3; 1 Yohane 2:18, 19.) Machenjezo amenewa anakwaniritsidwa. Chotulukapo chimodzi chinali chakuti dzina la Mulungu linakankhidwira kumbuyo. Iro linafikira ngakhale pochotsedwa m’makope ndi m’matembenuzidwe Abaibulo! Tiyeni tiwone mmene zimenezo zinachitikira.

[Mawu a M’munsi]

a Ena akutchula chifukwa china chakuti: Ayuda angakhale atasonkhezeredwa ndi nthanthi Yachigiriki. Mwachitsanzo, Philo, wanthanthi Wachiyuda wa ku Alexandria amene anali kukhala ndi moyo pafupifupi m’nthawi ya Yesu, anasonkhezeredwa kwakukulu ndi wanthanthi Wachigiriki Plato, amene anamlingalira kuti anauziridwa ndi Mulungu. Lexikon des Judentums (Dikshonale ya Chiyuda), pamutu wakuti “Philo,” imalongosola kuti Philo “anagwirizanitsa chinenero ndi ziganizo zanthanthi Yachigiriki (Plato) limodzi ndi chikhulupiriro chovumbulutsidwa cha Ayuda” ndi kuti poyambirira “anali ndi chiyambukiro chowoneka pa abambo atchalitchi Chachikristu.” Philo anaphunzitsa kuti Mulungu anali wosakhoza kulongosoledwa ndipo, chifukwa cha chimenecho, anali wopanda dzina.

[Chithunzi patsamba 14]

Chithunzithunzi ichi cha mkulu wansembe Wachiyuda, chokhala ndi chizindikiro panduwira yake m’mawu Achihebri akuti “Chiyero ncha Yehova,” chikupezeka mu Vatican

[Chithunzi patsamba 15]

Monga momwe matembenuzidwe Abaibulo Achijeremani a 1805 amasonyezera, pamene Yesu anawerenga m’mpukutu wa Yesaya m’sunagoge, iye anatchula dzina la Mulungu mofuula.—Luka 4:18, 19

[Zithunzi patsamba 16]

Petro ndi Paulo, anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu pamene anagwira mawu mu ulosi wa Yoweli.—Machitidwe 2:21; Aroma 10:13

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena