Mutu 6
Dziko Limene Linawonongedwa
KALEKALE, chiwonongeko cha dziko chinali kuyandikira. Anthu a mitundu yonse angakhale okondwera kuti pakati pa makolo awo akale panali munthu amene sanaseke chenjezo la Mulungu la chigumula chapadziko lonse. Chifukwa chakuti Nowa anamvetsera namvera, iye ndi mkazi wake, ana ake aamuna atatu ndi akazi awo anapulumuka. Tonsefe, tabadwa kuchokera kwa iwo.—Genesis 10:1, 32.
2 Mulungu anawononga dziko limenelo chifukwa chakuti anawona kuti dziko lapansi linadzaza chiwawa. “Dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo.” (Genesis 6:3, 5, 13) Mikhalidwe inali yofanana kwambiri ndi imene iri m’zaka zathu za zana la 20.
3 Kodi nchiyani chimene chidachititsa mkhalidwe m’nthaŵi ya Nowa kukhala wowopsa motero? Chochititsa chachikulu chikuululidwa pa Genesis 6:2, pamene pamasimba kuti: “Ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.” Koma kodi nchiyani chimene chinali cholakwa ndi zimenezo? Eya, amenewa sanali chabe amuna aumunthu amene anasankha kukwatira. “Ana a Mulungu” amenewa anali angelo, mizimu, amene anawona akazi okongola padziko lapansi ndi zikondwerero za ukwati ndi amene anadziveka mpangidwe waumunthu. (Yerekezerani ndi Yobu 1:6.) Kuvala kwawo matupi aumunthu ndi kukwatira zinali machitidwe osamvera Mulungu. Malemba amalongosola kuti iwo “anasiya malo awo okhala oyenera” ndi kuti kugona kwawo ndi akazi kunali “kosati kwachibadwa” kuipitsa. (Yuda 6, 7, NW; 1 Petro 3:19, 20) Ana awo anali aakulu mopambanitsa. Amenewa anatchedwa Anefili, kapena “ogwetsa,” chifukwa chakuti anali amphamvu.—Genesis 6:4.
4 Ngakhale analinkukhala pakati pa dziko loipa limenelo, Nowa anapeza chiyanjo m’maso mwa Yehova. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “Nowa anali munthu wolungama.” Anadziŵa nkhani zodzutsidwa mu Edene, ndipo anadzisonyeza kukhala wopanda liwongo, “mwamuna wokhulupirika.” (Genesis 6:8, 9; The Jerusalem Bible) Ncholinga cha kusunga Nowa ndi banja lake, kudzanso mbewu ya mtundu uliwonse wa nyama zapamtunda ndi mbalame, Yehova anamlangiza kukhoma chingalaŵa, chinyumba chachikulu chonga bokosi. Monga momwe Mulungu analongosolera kuti: “Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiwononge zamoyo zonse, mmene muli mpweya wamoyo pansi pa thambo; zinthu zonse m’dziko lapansi zidzafa.” (Genesis 6:13-17) Mwanzeru, Nowa anamvetsera Mulungu namvera.
5 Chigumula chinadza m’chaka cha 2370 B.C.E., monga momwe kwasonyezedwera ndi kuŵerengera zaka kwa tsatanetsatane kwa Baibulo. Chinali chigumula chachikulu koposa m’mbiri ya anthu, ngakhale kufikira nthaŵi yamakono. Chinali chachikulu koposa chakuti “anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pa thambo lonse.” (Genesis 7:19) Mwa njira ya Chigumula “dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka.” (2 Petro 3:6) Koma wina angafunse, ‘Ngati ngakhale mapiri aatali koposa anamizidwa ndi madzi, kodi madzi onsewo tsopano alikuti?’ Mwachiwonekere ali padziko lapansi pompano.
6 Kuyenera kuzindikiridwa kuti Baibulo silimanena kuti mapiri alionse m’nthaŵi ya Nowa anali aatali monga Phiri la Everest. Asayansi anena kuti kalelo ambiri a mapiri anali otsikirapo koposa nthaŵi ino ndi kuti ena akankhidwira pamwamba kuchokera pansi pa nyanja. Ndiponso, kukukhulupiriridwa kuti panali nthaŵi pamene nyanja zamchere zenizenizo zinali zocheperapo ndipo maiko anali okulirapo koposa mmene aliri tsopano, monga momwe kukuchitiridwa umboni ndi magwero amtsinje ochokera kutali pansi pa nyanja zamchere. Koma ponena za mkhalidwe wamakono, magazine a National Geographic, m’kope lake la January 1945, anasimba kuti: “Pali madzi owirikiza nthaŵi khumi m’kuchuluka kwawo m’nyanja zamchere kuposa mtunda umene uli pamwamba pa nyanja. Kankhirani mtunda wonsewo molingana m’nyanja, ndipo madzi akamiza dziko lonse lapansi, kuzama mailo imodzi ndi theka.” Chotero, madzi achigumula adagwa, kutukuka kwa mapiri kusanachitike ndipo kutsika kwa makwaŵa kunachititsa madzi kuchoka pamtunda ndipo kupangika kwa malo achisanu kumalekezero a kumpoto ndi kummwera kusanachitike, panali madzi okwanira kumiza “mapiri aatali onse,” monga momwe Baibulo limalongosolera.—Genesis 7:17-20; 8:1-3; yerekezerani ndi Salmo 104:8, 9.
7 Ndithudi chigumula chadziko lonse chachikulu choterocho chiyenera kukhala chitapereka lingaliro losadzaiŵalika pa awo amene anachipyola. Mibadwo yamtsogolo ikauzidwa za icho. Popeza cholembedwa Chabaibulo chimanena kuti mitundu yonse yachokera ku kagulu ka opulumuka Chigumula kamodzimodziko nkoyenera kuyembekezera kuti m’mbali zonse za dziko lapansi mukakhala umboni wa chikumbukiro chakalekale cha chigumula chachikulu chimenecho. Kodi ziri choncho? Inde, ndithudi!
8 Pamene mbadwa za opulumuka Chigumula zinasamukira kumalo akutali ndipo pamene nthaŵi inapita, zenizenizo zinayamba kuipitsidwa ndipo nkhaniyo inasinthidwira ku malingaliro achipembedzo amomwemo. Koma sikungakhale malunji kuti m’nthano zachikale padziko lonse muli zikumbukiro za chigumula chachikulu chimene chinawononga anthu kusiyapo oŵerengeka amene anasungidwa pamodzi. Chikumbukiro cha ichi chikupezedwa m’Mesopotamia ndi Asia, mu Australia ndi zilumba za Pacific, pakati pa mafuko ambiri Aamwenye mu North ndi South America, m’nthano zosimbidwa pakati pa Agiriki akale ndi Aroma, m’Scandinavia, ndi pakati pa mafuko a mu Afrika. Unyinji wa zosimbidwa zimenezi umatchula kusungidwa kwa nyama m’bwato limodzi ndi anthu. Ndendende ndi cholembedwa cha Baibulo, ena amasimba kuti mbalame zinatumizidwa kuti atsimikizire pamene madzi anaphwa. (Yerekezerani ndi Genesis 7:7-10; 8:6-12.) Kulibe chochitika china chakale chimene chikukumbukiridwa kwambiri motero.
9 Zochitika za m’mbiri zogwirizanitsidwa ndi Chigumula zayambukira miyambo ngakhale kufikira m’tsiku lathu. Motani? Eya, Baibulo limasimba kuti Chigumula chinayamba mu “mwezi wachiŵiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi aŵiri la mwezi.” “Mwezi wachiŵiri” umenewo umagwirizana ndi mbali yotsirizira ya October ndi mbali yoyambirira ya November pa makalendala athu. (Genesis 7:11) Chifukwa cha chimenecho nkoyenerera kuzindikiridwa kuti anthu ambiri padziko lonse amasunga Tsiku la Akufa kapena Phwando la Makolo panthaŵi imeneyo ya chaka. Chifukwa ninji panthaŵiyo? Chifukwa chakuti miyambo imeneyi imasonyeza kukumbukiridwa kwachiwonongeko chochititsidwa ndi Chigumula.”a
10 Komabe, ndilo Baibulo lenilenilo, limene liri ndi umboni wosaipitsidwa wa chimene chinachitika. Chimene Nowa anawona ndi kukumana nacho pambuyo pake chinaphatikizidwa m’Baibulo. Zaka mazana ambiri pambuyo pake, Mulungu mwiniyo, polankhula mwa mneneri Yesaya, anatchula “madzi a Nowa.” (Yesaya 54:9) Mwana wachisamba wa Mulungu anawona zochitika za tsiku la Nowa. Pambuyo pake, ali padziko lapansi, Ameneyu, Yesu Kristu, anatchula Chigumula monga chenicheni cha mumbiri ndiponso iye analongosola chifukwa chake anthu ambirimbiri anafa panthaŵi imeneyo.
“SANAMVETSERE”
11 Yesu sananene kuti munthu aliyense kusiyapo banja la Nowa anali wachiwawa kwambiri. Mmalo mwake, iye analongosola kuti: “Monga momwe iwo analiri m’masiku amenewo chisanafike chigumula, kudya ndi kumwa, amuna kukwatira ndi akazi kukwatitsidwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalaŵa; ndipo iwo sanamvetsere kufikira chigumula chinadza chinakokolola onse, motero kudzakhala kufika kwa Mwana wa munthu [Yesu Kristu].”—Mateyu 24:37-39, NW.
12 Sikunali kolakwa kwa iwo kudya ndi kumwa mosapambanitsa kapena kukwatira mwaulemu. Koma pamene anachenjezedwa za chiwonongeko cha dziko lonse, kupitirizabe kwawo kulunjikitsa miyoyo yawo pa zolondola zawo zoterozo kunasonyeza kuti iwo sanakhulupiriredi ngakhale Nowa kapena Yehova Mulungu, amene uthenga wake wa chenjezo Nowa analengeza. Ngati iwo anakhulupirira, akanafunsa mwaphamphu mmene kupulumuka kunaliri kotheka ndiyeno kuchitapo kanthu mofulumira kufitsa zofunika. Mwinamwake ena a anthuwo anavomereza kuti kanthu kena kanayenera kuchitidwa kuthetsa chiwawa chowanda cha masiku amenewo, koma mosakaikira chigumula chadziko lonse chinawonekera kukhala chosayembekezereka kwambiri kwa iwo. Chotero, monga momwe Yesu anenera, iwo “sanamvetsere [uthenga wa Mulungu mwa Nowa], kufikira chigumula chinadza, chinakokolola onse.” Zimenezo zinalembedwa monga chitsanzo chochenjeza kwa ife.
13 Mofananamo mtumwi Petro wouziridwayo anapereka chenjezo pamene analemba kuti: “Masiku otsiriza [mmene ife tsopano tiri] adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Liri kuti lonjezo la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.” Anthu otero samafuna kuwona kukhala ndi thayo kwa aliyense. Motero amachotsa m’maganizo mwawo lingaliro la kufika kwa Kristu ndi chimene kudzatanthauza kwa iwo amene akulondola njira ya moyo yopanda umulungu. Koma Petro akupitiriza kuti: “Pakuti ichi aiŵala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pamawu a Mulungu; mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka; koma miyamba ndi dziko lapansi la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.”—2 Petro 3:3-7.
14 Iwo amene akunyoza akanyalanyaza chenicheni chakuti “mawu a Mulungu” samakhala osakwaniritsidwa. Kuti atsutse lingaliro lawo, mtumwi Petro akutibwezera mmbuyo kunthaŵi ya chilengedwe. Panthaŵi imeneyo Mulungu anati: “Pakhale thambo pakati pa madzi, lilekanitse madzi ndi madzi.” Pokhala atanena mawu amenewo, “Mulungu anapanga thambo, analekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi anali pamwamba pa thambolo.” Chotero “mawu a Mulungu,” maneno ake a chifuno, anakwaniritsidwa. (Genesis 1:6, 7) Mawu ake anakwaniritsidwanso pamene analamula chigumula chadziko lonse m’nthaŵi ya Nowa ndipo anagwiritsira ntchito madzi amenewo kuwonongera “dziko lapansi la masiku aja.” Ndipo kudzakhala mwa mawu osaletseka a Mulungu amodzimodziwo kuti chiwonongeko chidzadza padongosolo la zinthu lamakono lopanda umulungu.
15 Chimene chinachitika panthaŵi ya Chigumula chinali chitsanzo cha zinthu zirinkudza. Dziko lapansi silinawonongedwe kalero, koma anthu opanda umulungu anatero. Pamenepa, kodi nchiyani, chimene chikutanthauzidwa ndi mawu akuti “miyamba ndi dziko la masiku ano zaikika kumoto”? (2 Petro 3:7; 2:5) Eya, kodi moto weniweni ukanakhala nchiyambukiro chotani padzuŵa ndi nyenyezi zotentha kwambiri kale m’miyamba yeniyeniyo? Ndipo kodi ndimotani mmene kupsereza dziko lapansi lenileni kukayeneranira ndi chifuno cha Mulungu cha kulipanga kukhala Paradaiso? Mwachiwonekere, “miyamba ndi dziko la masiku ano,” monga momwe zatchulidwira panopa, ziyenera kukhala zophiphiritsira. (Yerekezerani ndi Genesis 11:1; 1 Mafumu 2:1, 2; 1 Mbiri 16:31.) “Miyamba” ikuimira maulamuliro aboma otukulidwa pamwamba pa anthu onse, ndipo “dziko lapansi” ndilo chitaganya cha anthu opanda umulungu. M’tsiku lalikulu la Yehova iwo adzawonongedwa kotheratu monga ngati apserezedwa ndi moto. Iwo amene akupitirizabe kunyoza chenjezo laumulungu la zimenezi akuika miyoyo yawo paupandu waukulu.
KUPULUMUTSIDWA KWA ANTHU ODZIPEREKA KWAUMULUNGU
16 Cholembedwa cha chigumula chimafotokoza mokondweretsa mwafanizo mfundo imene ife lerolino tikufunikira kulabadira. Kodi imeneyo nchiyani? Atatchula zimene Mulungu anachita m’nthaŵi ya Nowa, mtumwi Petro akutsiriza kuti: “Yehova adziŵa kupulumutsa anthu odzipereka kwaumulungu m’chiyeso, koma kusunga osalungama kaamba ka tsiku la chiweruzo kuti achotsedwe.” (2 Petro 2:9, NW) Pamenepa, mfungulo ya kupulumutsidwa, ndiyo kukhala munthu wodzipereka kwaumulungu.
17 Kodi zimenezo zimatanthauzanji? Mwachiwonekere Nowa anali munthu wodzipereka kwaumulungu. “Nowa anayenda ndi Mulungu wowona.” (Genesis 6:9) Analondola njira ya moyo imene imagwirizana ndi chifuniro cha Yehova chovumbulutsidwa. Anali ndi unansi weniweni ndi Mulungu. Kukhoma chingalaŵa ndi kusonkhanitsa mbewu za mbalame ndi nyama zonse inali ntchito yaikulu. Nowa sanali ndi mkhalidwe wa kuyembekezera ndi kuwona. Anali ndi chikhulupiriro. Nowa “anachita monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.” (Genesis 6:22; Ahebri 11:7) Anthu anafunikira kukumbutsidwa za njira zolungama za Yehova ndi kuchenjezedwa za kudza kwa chiwonongeko cha opanda umulungu. Nowa anachitanso zimenezo monga “mlaliki wa chilungamo.”—2 Petro 2:5.
18 Bwanji za mkazi wa Nowa, ana ake aamuna ndi akazi awo—kodi nchiyani chimene chinafunidwa kwa iwo? Cholembedwa cha Baibulo chimalunjikitsa chisamaliro chapadera pa Nowa chifukwa chakuti anali mutu wa banja, koma enawo anayeneranso kukhala anali anthu odzipereka kwaumulungu. Kodi nchifukwa ninji ziri choncho? Mkhalidwe wa ana a Nowa unatchulidwa pambuyo pake ndi Yehova kwa mneneri wake Ezekieli kusonyeza kuti, ngati Nowa akanakhala anali mu Israyeli panthaŵi imeneyo, ana ake sakanayembekezera chipulumutso chifukwa cha chilungamo cha atate wawo. Iwo anali aakulu mokwanira kumvera kapena kusamvera, motero iwo eni anafunikira kupereka umboni wa kudzipereka kwawo kwa Yehova ndi njira zake zolungama.—Ezekieli 14:19, 20.
19 Polingalira kutsimikizirika kwa chiwonongeko cha dziko choyandikira, Baibulo limatilimbikitsa kuchikumbukira ndi kudzitsimikizira kuti ife, nafenso, ndife anthu odzipereka kwaumulungu. (2 Petro 3:11-13) Pakati pa mbadwa za Nowa, pali anthu lerolino m’mbali zonse zadziko lapansi amene akulabadira uphungu wanzeru umenewo ndi amene adzakhala opulumuka kuloŵa mu “dziko lapansi latsopano.”
[Mawu a M’munsi]
a The Worship of the Dead (London; 1904), lolembedwa ndi Colonel J. Garnier, tsamba 3-8; Life and Work at the Great Pyramid (Edinburgh; 1867), Vol. II, lolembedwa ndi Profesala C. Piazzi Smyth, tsamba 371-424.
[Mafunso]
1. (a) Kodi chiwonongeko chadziko ndi kale lonse chinayang’anizanapo ndi anthu? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyamikira kuti Nowa sananyoze chenjezo lake?
2. Kodi nchifukwa ninji Mulungu anawononga dziko limenelo?
3. Kodi nchiyani chidachititsa mkhalidwewo kukhala wowopsa kwambiri?
4. (a) Kodi nchifukwa ninji Nowa anasonyezedwa chiyanjo ndi Mulungu? (b) Kodi ndikukonzekera kotani kumene kunapangidwa kaamba ka kusungidwa kwa moyo?
5. Kodi Chigumula chinali chachikulu motani?
6. Pambuyo pa Chigumula, kodi madzi onsewo anapita kuti?
7, 8. Kodi ncholembedwa cha Chigumula chotani chimene chiripo kuwonjezera pa Baibulo?
9. Kodi ndimachitidwe otani amene amasonyeza zikumbukiro za zochitika za “mwezi wachiŵiri” pakalendala ya Nowa?
10. Kodi nchifukwa ninji cholembedwa Chabaibulo cha Chigumula chiri chodalirika koposa ndi chopindulitsa koposa?
11. Kodi nchifukwa ninji anthu ochuluka motero anawonongedwa m’Chigumula?
12. Kodi nchifukwa ninji ‘kusamvetsera’ kwawo kunali kowopsa kwambiri?
13. (a) Monga momwe kunanenedweratu, kodi ndimotani mmene anthu ambiri lerolino amachitira pamene auzidwa kuti Kristu wafika mosawoneka, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi nchiyani chimene Petro akunena kuti iwo akunyalanyaza?
14. Kodi nchifukwa ninji kukwaniritsidwa kwa “mawu a Mulungu” panthaŵi ya chilengedwe ndi m’nthaŵi ya Nowa kumatipangitsa kulingalira mwamphamvu lerolino?
15. (a) Kodi nchifukwa ninji 2 Petro 3:7 sakuneneratu kupserezedwa kwa planetili Dziko Lapansi? (b) Pamenepa kodi nchiyani chimene chiri “miyamba” ndi “dziko lapansi” zimene “zaikika kumoto”?
16. Monga momwe kwasonyezedwera pa 2 Petro 2:9, kodi nchiyani chimene chiri mfungulo ya chipulumutso?
17. Kodi ndimotani mmene Nowa anaperekera umboni wa kudzipereka kwaumulungu?
18. Kodi nchifukwa ninji aliyense amene anapulumuka Chigumula ayenera kukhala anali ndi kudzipereka kotero?
19. Motero, kodi nchiyani chimene tiyenera kukhala tikuchita, ndipo motani?