Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • su mutu 7 tsamba 54-60
  • Chitani Mwanzeru Poyang’anizana ndi Tsoka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitani Mwanzeru Poyang’anizana ndi Tsoka
  • Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “DZIKO LAPANSI LIPITA”
  • “IWO ANALAPA CHIFUKWA CHA ZIMENE YONA ANALALIKIRA”
  • PEMPHANI MTENDERE MOFULUMIRA
  • Agibeoni Anzeru
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yoswa ndi anthu a ku Gibiyoni
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
su mutu 7 tsamba 54-60

Mutu 7

Chitani Mwanzeru Poyang’anizana ndi Tsoka

PAMENE achenjezedwa ndi magwero odalirika kuti ngozi iri pafupi, anthu anzeru amachitapo kanthu kutetezera miyoyo yawo. (Miyambo 22:⁠3) Koma zikwi zosaŵerengeka zawonongeka mosafunika chifukwa chakuti chidaliro chawo chinaikidwa polakwika. Mosasamala kanthu za machenjezo akuloŵa m’mabwato opulumukira, apaulendo mazana ambiri anamira ndi sitima yapanyanja yotchedwa Titanic mu 1912 chifukwa chakuti anakhulupirira mawu akuti iyo inali yosakhoza kumira. Pamene Phiri la Pelée m’Martinique linayamba kutulutsa phulusa la volokano ndi miyala mu 1902, anthu a ku Saint-Pierre woyandikirayo anachita mantha, koma popeza kuti zikondwerero zadyera za ziŵalo zotchuka za chitaganyacho zinali pangozi, atsogoleri andale zadziko amomwemo ndi mkonzi wa nyuzipepala yamomwemo anafunafuna kuziziritsa mantha a anthu, akumawalimbikitsa kusachoka. Mwadzidzidzi phirilo linaphulika, ndipo anthu 30 000 anawonongeka.

2 M’nthaŵi yathu chenjezo lofulumiradi kwambiri likuperekedwa​—⁠osati lonena za ngozi ina yapamalopo koma lonena za kuyandikira kwa nkhondo ya Mulungu yapadziko lonse ya Harmagedo. (Yesaya 34:​1, 2; Yeremiya 25:​32, 33) Mboni za Yehova mobwerezabwereza zafika m’nyumba za anthu padziko lonse lapansi, zikumawafulumiza kuchita mwanzeru, ndi cholinga cha kupulumutsidwa kwa miyoyo yawo. Kodi inu mumakonda moyo mokwanira kuti mutsatire kachitidwe kofunika, ndi kutero mofulumira, mosazengereza?

“DZIKO LAPANSI LIPITA”

3 Chinthu chachikulu m’kuyembekezera kwanu kupulumuka ndicho mkhalidwe wanu ku dziko. Malinga ngati muli moyo monga munthu muli m’dziko. Koma simufunikira kukhala ndi zikhumbo zake zoipa ndi kutsanzira ntchito zake zoipa. Simufunikira kudzigwirizanitsa nalo mwa kuika chidaliro chanu mwa anthu ndi zolinganiza zawo mmalo mwa Mulungu ndi chifuno chake. Koma muyenera kupanga chosankha; simungakhale kumbali zonse ziŵiri. “Yense wa kufuna kukhala bwenzi la dziko, akudziika mdani wa Mulungu.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti, monga momwe Mawu a Mulungu akutiuzira, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”​—⁠Yakobo 4:​4, NW; 1 Yohane 5:19; Salmo 146:​3-5.

4 Mwachiwonekere, Yehova sadzaloŵetsa m’Dongosolo lake Latsopano lolungama anthu amene kakhalidwe kawo kamapereka umboni wakuti amamamatira ku zimene Mulungu amatsutsa. Kodi nchiyani chimene chiri zina za zinthuzi? Zambiri ndizo machitachita ndi malingaliro zimene dziko limalandira mosavuta. Koma ngati ife tifuna kupulumuka mapeto a dziko loipa lino, pamenepo, mosasamala kanthu za chimene ena amachita ndi kulingalira, tidzalabadira chenjezo la Baibulo lakuti adama, achigololo, ogonana aziŵalo zofanana ndi iwo amene anachita utchisi wachisembwere ndi kusadziletsa sadzakhala pakati pa opulumuka. Mosasamala kanthu kuti ndimwakaŵirikaŵiri chotani mmene ena akutembenukira kukunama ndi kuba, ife tidzakana kakhalidwe koteroko. Mosasamala kanthu za kufala kwa machitachita amatsenga, ife tidzawapeŵa. Ngakhale kuli kwakuti ena angakhale ansanje, kuyamba ndewu, kupsa mtima, kapena kuyesa kuzemba kugwiritsidwa mwala ndi anamgoneka kapena kumwa mopambanitsa zakumwa zoledzeretsa, sitidzawatsanzira. Ndipo ngati tinachita zinthu zimenezi, tidzayang’anizana ndi kufunika kwa kusintha. Ngakhale ngati zina za zimenezi zinawonekera kukhala “zabwino” kwa ife kale, tidzazileka. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tikukondadi Mulungu, tikukonda moyo, ndipo Mawu a Mulungu amachenjeza kuti “iwo akuchitachita zotere sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.”​—⁠Agalatiya 5:​19-21; Aefeso 5:​3-7; 1 Akorinto 6:​9, 10; 2 Akorinto 7:1; Chivumbulutso 22:⁠15.

5 Ngati mpata wa kukhala ndi moyo kosatha m’chimwemwe uli wamtengo wapatali kwa ife, tifunikira kuphunzira mmene tingakondweretsere Wopereka moyoyo, Yehova Mulungu. (Machitidwe 17:​24-28; Chivumbulutso 4:11) Mopita patsogolo tiyenera kugwiritsira ntchito Mawu ake kumbali iriyonse ya miyoyo yathu. Pamene tikutero, mwamsanga tidzapenda mwamphamvu lingaliro lathu kulinga kwa ife eni ndi anthu ena, kulinga ku chuma chathu ndi zofikiridwa, ndi kulingalira mmene zimenezi zimayambukirira kaimidwe kathu pamaso pa Mulungu. Anthu otikweteza angakhale ndi lingaliro lodzikweza la iwo eni, la fuko lawo kapena khungu kapena mtundu, koma tidzalingalira mwamphamvu lemba limene limati: “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.”​—⁠Yakobo 4:6; Zefaniya 2:​2, 3; Salmo 149:⁠4.

6 Ngakhale kuli kwakuti ena amadzilola kumangidwa ukapolo ndi zilakolako zodzutsidwa ndi anthu okondetsa zinthu zakuthupi kapena zosonkhezeredwa ndi chilakolako cha kutchuka, tidzapenda moyo wathu weniweni mothandizidwa ndi 1 Yohane 2:​15-17, amene amati: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye. Pakuti chirichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako chathupi ndi chilakolako chamaso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita ndi chilakolako chake, koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthaŵi yonse.” Ngati tifunikira kupanga masinthidwe, ino ndiyo nthaŵi ya kuwachita.

7 Dziko lino ndi kakhalidwe kake sizidzapitirizabe kosatha. Siliri “losakhoza kumira.” Anthu audziko angayeseyese kugwira owatsatira, akumawachititsa kulingalira kuti zoyesayesa zawo zingakonze dziko. Koma njira yokha yopulumutsidwira kutsoka loyandikira ndiyo kulabadira uthenga wa chenjezo wa Mulungu. Mu imeneyi Anineve m’nthaŵi ya mneneri Yona amapereka chitsanzo chimene timachita bwino kulabadira.

“IWO ANALAPA CHIFUKWA CHA ZIMENE YONA ANALALIKIRA”

8 M’zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E., Yehova anatuma Yona kupita kwa anthu a Nineve, likulu la Asuri, kukalengeza kuti, chifukwa cha kuipa kwawo, Nineve anali kudzagwetsedwa. Pamene Yona anachenjeza kuti m’masiku 40 okha iwo akawonongedwa, kodi iwo anachita motani? Mmalo mwa kuseka, iwo “anayamba kukhulupirira Mulungu, ndipo iwo anapitiriza kulalikira kusala kudya ndi kuvala ziguduli.” Mfumu yeniyeniyo inagwirizana nawo nifulumiza anthu onse kufuulira mwaphamphu kwa Mulungu ndi kuleka njira zawo zoipa ndi chiwawa chawo. Iyo inati: “Kodi pali yani amene akudziŵa kaya Mulungu wowona . . . angabweze mkwiyo wake waukulu, kotero kuti tisawonongeke?” Chifukwa chakuti iwo anasiya njira yawo yoipa, Yehova anawachitira chifundo. Miyoyo yawo inapulumutsidwa.​—⁠Yona 3:​2-10, NW.

9 Monga chidzudzulo kwa Ayuda osakhulupirira m’zaka za zana loyamba C.E., Yesu anasonyeza chochitika cha m’mbiri chimenecho, akumati: “Anthu a ku Nineve adzauka pa mlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwake kwa Yona; ndipo wonani, wa kuposa Yona ali pano.”​—⁠Mateyu 12:⁠41.

10 Bwanji ponena za nthaŵi yathu? Kodi aliyense akusonyeza kulapa kotero? Inde, pali zikwi zambiri padziko lonse zimene, mofanana ndi Anineve, zingakhale zisanadzitche kukhala zolambira Mulungu wa Baibulo. Koma zimene tsopano zikulabadira uthenga wa chenjezo wa Yehova. Pamene amva chifukwa chake chiwonongeko chikubwera padziko lino, amafunafuna chifundo cha Mulungu. Ali ndi kusintha maganizo ndi mtima kowona ponena za kakhalidwe kawo kakale ndipo tsopano akudzipereka kuchita “ntchito zoyenera kutembenuka mtima.” (Machitidwe 26:20; wonaninso Aroma 2:⁠4.) Kodi chiri chikhumbo chanu kukhala mmodzi wa iwo? Ngati ziri choncho, musazengereze.

PEMPHANI MTENDERE MOFULUMIRA

11 Agibeoni m’nthaŵi ya Yoswa anachitanso mwanzeru kotero kuti miyoyo yawo ikapulumutsidwe. Iwo anali Akanani amene kakhalidwe kawo kanali koipa ndi kokondetsa zinthu zakuthupi, kolambira mafano ndi kauchiŵanda. Yehova adaali atalamulira chiwonongeko chawo. Iwo anadziŵa mmene Yehova adapulumutsira Israyeli ku Igupto zaka 40 zapitazo ndi kuti mafumu amphamvu Aamori kummaŵa kwa Mtsinje wa Yordano analiri osakhoza kuima pamaso pawo. Aliyense anazindikira kuti, popanda kugwiritsiridwa ntchito kwa zida zankhondo zogumulira malinga, malinga aakulu a Yeriko adagwa phwata pamaso pawo ndi kuti mzinda wa Ai unasandutsidwa mulu wabwinja. (Yoswa 9:​3, 9, 10) Nzika za mzinda wa Gibeoni zinafuna kukhala ndi moyo, koma zinazindikira kuti sizikanakhoza kupambana m’nkhondo yomenyana ndi Mulungu wa Israyeli. Kanthu kena kanafunikira kuchitidwa mofulumira. Kotani? Iwo sakaumiriza pangano ndi Aisrayeli, koma iwo analingalira kuti ayenera pafupifupi kuyesa kulipeza. Motani?

12 Anachita mwanzeru, akumatumiza kwa Yoswa amuna amene kawonekedwe kawo kanasonyeza ngati kuti adaayenda ulendo wautali kwambiri. Pofika kwa Yoswa, ananena kuti anachokera kudziko lakutali, kuti adamva zinthu zazikulu zimene Yehova adachita ndipo, monga oimira a anthu a mtundu wawo, adafika kudzadzipereka kukhala atumiki ndi kudzapempha kuti pangano lichitidwe nawo. Yoswa ndi akalonga a Israyeli anavomereza. Pambuyo pake, pamene chinyengocho chinadziŵika, Agibeoniwo anavomereza modzichepetsa kuti anali kuwopera miyoyo yawo ndipo anasonyeza kufunitsitsa kuchita chirichonse chofunidwa kwa iwo. (Yoswa 9:​4-25) Yehova adawona nkhani yonseyo. Sananyengedwe. Iye adawona kuti iwo sanali kuyesa kuipitsa anthu ake, monga momwe Amoabu adachitira papitapo, ndipo anazindikira chikhumbo chawo chowona mtima cha kukhala ndi moyo. Motero iye anaŵalola kuikidwa pa kugwira ntchito pansi pa Alevi pa chihema chopatulika, kutema nkhuni ndi kutunga madzi, motero kuchirikiza kulambiridwa kwa Yehova. Ndithudi, kuti akhale ovomerezeka kaamba ka utumiki wotero, iwo anafunikira kusiya machitachita awo akale onyasa.​—⁠Yoswa 9:27; Levitiko 18:​26-30.

13 Polingalira chenicheni chakuti tikukhala ndi moyo pafupifupi ndi mapeto a “masiku otsiriza,” nkofunika kwambiri kwa anthu onse amene akufuna kupulumuka kuchita mosazengereza, ndipo ndi kuwona mtima konse. Yesu Kristu, amene ali wolipsira wa Yehova lerolino, sanganyengedwe monga momwe Yoswa anachitira. Njira yokha imene anthu oterowo angaloŵere m’kakonzedwe ndi iye kuti awapulumutse ku kuphedwa njakuti iwo alengeze poyera kukhulupirira kwawo Yehova kukhala Mulungu wowona. (Yerekezerani ndi Machitidwe 2:​17-21.) Ayeneranso kulandira Yesu Kristu m’ntchito zimene Mulungu wapereka kwa iye ndi kukhala ndi moyo pambuyo pake monga anthu amene saali okonda kakhalidwe kadziko lotsutsidwa lino. Pamenepo ayenera kukhala atumiki odzichepetsa a Mulungu, akumapereka utumiki wopatulika kwa iye mogwirizana ndi mpingo wa anthu ake.​—⁠Yohane 17:16; Chivumbulutso 7:​14, 15.

14 Mwamsanga Agibeoni atagwirizana ndi anthu a Yehova, anatsenderezedwa kwambiri. Mafumu asanu Aamori anazinga Gibeoni kuti akakamize nzikazo kubwereranso kumbali yawo, motsutsana ndi Israyeli. Agibeoni anatumiza pempho lofulumira kwa Yoswa la chithandizo, ndipo chipulumutso chimene analandira chinali chimodzi cha zodabwitsa koposa m’mbiri yonse. Yehova analoŵetsa adaniwo m’chisokonezo, anawagwetsera matalala kuchokera kumwamba, nachititsa kuunika kwa dzuŵa kutanimphitsidwa mwapadera kufikira Aisrayeli atagonjetsa kotheratu adaniwo. (Yoswa 10:​1-14) Kupulumutsidwa kwa Agibeoni kunali kulosera kupulumutsidwa kodabwitsa kwambiridi kwa khamu lalikulu la olambira Mulungu wowona pankhondo yachilengedwe chonse ya Harmagedo. Mpata wa kupeza chipulumutso chimenecho ngwotsegukira anthu a mtundu uliwonse ngati achita mwanzeru tsopano. Kodi mukudzipezera mpata umenewo?​—⁠Chivumbulutso 7:​9, 10.

[Mafunso]

1. Kodi nchifukwa ninji anthu anawonongeka mosafunikira (a) pamene Titanic inamira? (b) pamene phiri la Pelée linaphulika?

2. (a) Kodi ndichenjezo lofulumira lotani limene lirinkuperekedwa m’nthaŵi yathu? (b) Kodi nchifukwa ninji mkhalidwewo uli wowopsa?

3. Kodi nchifukwa ninji lingaliro lathu kulinga ku dziko limayambukira chiyembekezo chathu cha kupulumuka?

4. (a) Mogwiritsira ntchito Baibulo, longosolani machitachita ndi lingaliro zimene zidzalepheretsa anthu kupeza moyo pansi pa Ufumu wa Mulungu. (b) Kodi nchifukwa ninji alionse amene achita zinthu zimenezi ayenera kuzisiya mofulumira?

5. (a) Ngati moyo uli wamtengo wapatali kwa ife, kodi tiyenera kuphunzira kuchitanji? (b) Kodi ndimikhalidwe yabwino kwambiri yotani imene ikutchulidwa m’malemba pamapeto a ndime ino? Kodi iyo njofunika motani? Kodi tingaikulitse motani?

6, 7. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupenda miyoyo yathu mothandizidwa ndi 1 Yohane 2:​15-17?

8. Kodi ndimotani mmene Anineve anasonyezera nzeru pamene Yona anapereka chenjezo la Mulungu kwa iwo, ndipo limodzi ndi zotulukapo zotani?

9, 10. (a) Kodi ndimbali yotani imene Yesu ananena kuti Anineve anali chitsanzo cha kutsatira? (b) Kodi ndani lerolino amene ali ofanana ndi Anineve amenewo?

11. (a) Kodi nchiyani chimene chinali magwero a Agibeoni? (b) Kodi nchifukwa ninji anapempha mtendere ndi Israyeli?

12. (a) Mosasamala kanthu za njira imene anagwiritsira ntchito, kodi nchifukwa ninji Agibeoni anapulumutsidwa? (b) Kodi ndimasinthidwe otani amene iwo anafunikira kupanga, ndipo ndintchito yanji imene anapatsidwa?

13. (a) Kodi tingapindule motani ndi chochitika cholosera chimenecho chokhudza Agibeoni? (b) Kuti apulumutsidwe ndi Yoswa Wamkuluyo, kodi nchiyani chimene chikufunika kwa anthu lerolino?

14. Kodi nchifukwa ninji kupulumutsa kwa Yehova Agibeoni kumagulu ankhondo a adani kuli kwatanthauzo kwa ife?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena