Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • su mutu 9 tsamba 68-74
  • Kodi Ndani Amene Amatsogolera Njira ya Kuchipulumutso?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Amene Amatsogolera Njira ya Kuchipulumutso?
  • Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MBUSA WABWINO WENIWENI
  • M’busa Wabwino Komanso Makola Awiri a Nkhosa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Makola a Nkhosa ndi Mbusa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Makola Ankhosa ndi Mbusa
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Khamu Lalikulu la Olambira Oona—Lachokera Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
su mutu 9 tsamba 68-74

Mutu 9

Kodi Ndani Amene Amatsogolera Njira ya Kuchipulumutso?

NGATI titangovomereza utsogoleri wa Yesu Kristu ndi kupereka umboni wokhutiritsa wakuti timamumveradi ndi kuyenda m’mapazi ake tingapulumutsidwe kudziko loipali ndi kusungidwa amoyo kupyola “chisautso chachikulu” chirinkudzacho. (Machitidwe 4:12) Zimenezi zinafotokozedwa bwino mwafanizo m’zochitika zophatikizapo kuomboledwa kwa Aisrayeli akuthupi ku Igupto mu 1513 B.C.E. Mozizwitsa Yehova anatsogoza Israyeli kuchipupulumutso kupyola Nyanja Yofiira nawononga gulu lankhondo Lachiigupto lolondolalo. M’zonsezi, Mulungu anagwiritsira ntchito Mose kutsogolera anthu ake.​—⁠Yoswa 24:​5-7; Eksodo 3:⁠10.

2 Pamene Aisrayeli anatuluka mu Igupto ndi chiyembekezo cha kukaloŵa Dziko Lolonjezedwa, ena anagwirizana nawo. Monga momwe Mose pambuyo pake adalembera: “Anthu ambiri osokonezeka anabwera nawo.” (Eksodo 12:38) Kodi amenewa anali ayani? Iwo anali Aigupto kapena alendo ena amene anadziphatikiza ndi Israyeli. Anali atawona miliri yowopsa imene Yehova anali atabweretsa pamtundu wa Igupto wotsenderezawo kusonyeza kuti iye anali Mulungu wowona yekha ndi kuti milungu ya Igupto inali yonyenga ndipo sikanapulumutsa awo amene anailambira. Ndiponso, mosakaikira, zimene anamva kwa Aisrayeli za chiyembekezo cha moyo mu “dziko loyenda mkaka ndi uchi” zinamvekera kukhala zabwino kwa iwo. (Eksodo 3:​7, 8; 12:12) Koma kodi iwo anavomerezanso Mose kotheratu monga woikidwa ndi Mulungu kukhala wolamulira ndi momboli wa anthu Ake? Iwo anayesedwa mofulumira.​—⁠Machitidwe 7:​34, 35.

3 Pamene Israyeli, limodzi ndi “anthu ambiri osokonekeza,” anayandikira gombe la Nyanja Yofiira, mfumu ya Igupto ndi magulu ake ankhondo inawalondola kudzawabwezera mu ukapolo. Kuti apulumutsidwe, ayenera kukhala ndi kutsatira malangizo a Mose, chifukwa chakuti Yehova anali kugwiritsira ntchito Mose kuwatsogolera. Mwa njira ya mtambo wodabwitsa Yehova anaimika adani pamene anagaŵanitsa madzi a nyanja naumitsa pansi pa nyanja. Mosiyana kwambiri ndi zimene zinachitikira Aigupto pambuyo pake, Israyeli yense ndi “anthu ambiri osokonezeka” anapulumuka limodzi ndi Mose nawoloka pansi panyanja pouma pamenepo. (Eksodo 14:​9, 19-31) Pamene iwo analinkuwoloka, khoma la madzi kudzanja lawo lamanja ndi kudzanja lawo lamanzere ndipo mtambo wa kukhala pafupifupi kwa Mulungu uli pamwamba pawo, kanthu kena kapadera kanachitika. Baibulo limakatchula kukhala ubatizo​—⁠osati ubatizo weniweni m’madzi, koma wophiphiritsira mwa Mose monga mneneri wa Yehova, wotumidwa ndi Mulungu kukhala Momboli wawo. (1 Akorinto 10:​1, 2) Mofananamo, Aisrayeli auzimu onse amene adzapulumuka chiwonongeko cha dongosolo loipa la zinthu ayenera kuloŵa ubatizo wofanana mwa Kristu monga momboli ndi kupereka umboni wokhutiritsa wakuti akumamatira kotheratu ku utsogoleri wake. “Anthu osokonezeka” amakono ayenera kugwirizana nawo.

4 Yehova wapereka ulamuliro waukulu kwa Mwana wake, Yesu Kristu. Kupyolera mwa iye Mulungu wapangitsa kukhala kotheka kwa ife kuti ‘tipulumutsidwe kudongosolo loipa lazinthu liripoli,’ kotero kuti sitifunikira kulandira nalo choikidwiratu chake chosasangalatsa. (Agalatiya 1:​3-5; 1 Atesalonika 1:​9, 10) Kupyolera mwa Mose, Yehova anapereka malamulo kwa Israyeli amene anakhudza ziyembekezo zamoyo zapanthaŵiyo za anthuwo. Pamene anamvera malamulo amenewo anapindula kwambiri. Koma malamulo ena analinso ndi chilango cha imfa chifukwa cha kusamvera. Pambuyo pake, Yesu anakhala mneneri wamkulu koposa Mose. Zimene anaphunzitsa zinali “mawu a moyo wosatha,” ndipo kulephera dala kumvera mawu amenewo kumatsogolera kuimfa imene kulibe chipulumutso. Chifukwa cha chimenecho, nkofunika chotani nanga, kuti tilabadire zimene akunena!​—⁠Yohane 6:​66-69; 3:36; Machitidwe 3:​19-23.

5 Kwa anthu ena, lingaliro la kugonjera kwa mtsogoleri silimawonekera kukhala labwino. Iwo awona kugwiritsiridwa ntchito kolakwa mopambanitsa kwa ulamuliro. Koma mawu a Yesu enieni amasonyeza mzimu umene uli wotsimikiziritsa. Mosangalala akutiitana kuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupulumutsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima; ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:​28-30) Ndichiyembekezo chokondweretsa chotani nanga! Awo amene alabadira chiitano chachikondi chimenecho, akumaika chidaliro chawo chonse mwa iye, sadzagwiritsidwa mwala. (Aroma 10:11) Iwo adzapeza chisungiko chonga chija cha nkhosa m’gulu la mbusa wachikondi.

MBUSA WABWINO WENIWENI

6 Mtundu wa Israyeli unali ngati gulu lankhosa limene linali la Yehova. Iye anapereka pangano Lachilamulo, limene linatumikira monga makoma otetezera a kholalo, likumawatsekereza ku kakhalidwe ka mitundu Yachikunja yosapembedza. Linatsogoleranso olabadirawo kwa Mesiya. (Aefeso 2:​14-16; Agalatiya 3:24) Ponena za Mbusa Mfumu waumesiya ameneyo, Yehova adaneneratu kuti: “Ndidzadziutsira mbusa mmodzi [nkhosa zanga]; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide.” (Ezekieli 34:​23, 31) Izi sizinatanthauze kuti Davide, amene panthaŵiyo anali wakufa, adzalamuliranso iye mwini monga mfumu pa anthu a Mulungu. Mmalo mwake, kuchokera m’mzera wachifumu wa Davide Yehova akadzutsa mbusa mfumu mwa amene Mulungu akapereka chisungiko. (Yeremiya 23:​5, 6) Panthaŵi zosiyanasiyana amuna anadzitcha monama kukhala mpulumutsi Waumesiya, koma m’chaka cha 29 C.E., Yehova anagwiritsira ntchito Yohane Mbatizi kudziŵikitsa Yesu Kristu kwa “nkhosa” za Israyeli kukhala iye wotumidwadi ndi Mulungu, Mesiya wokhala ndi maumboni owona. Ameneyu anali Mwana wa Mulungu wakumwamba, amene moyo wake weniweni unasamutsidwira ku mimba ya namwali Wachiyuda kotero kuti akabadwire mu mzera wachifumu wa Davide. Dzinalo Davide limatanthauza “wokondedwa,” chotero, moyenerera, pambuyo pa ubatizo wa Yesu m’madzi, Yehova analengeza momveka ali kumwamba kuti: “Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa iwe ndikondwera bwino.”​—⁠Marko 1:⁠11.

7 Yosakwanira miyezi inayi imfa yake isanachitike, Yesu anati: “Ndine mbusa wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.” (Yohane 10:11) Iye anasiyanitsa ntchito yake ndi ija ya amesiya onyenga amene anali atadza poyambirira, akumati: “Iye wosaloŵa m’khola lankhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyo ndiye wakuba ndi wolanda. Koma iye wakuloŵera pakhomo, ndiye mbusa wankhosa. Iyeyu wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mawu ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina awo, nazitsogolera kunja. Pamene atatulutsa zonse za iye yekha, azitsogolera; ndi nkhosa zimtsata iye; chifukwa zidziŵa mawu ake. Koma mlendo sizidzamtsata, chifukwa sizidziŵa mawu a alendo.”​—⁠Yohane 10:​1-5, 8.

8 Awo okhala m’khola Lachiyuda amene analabadira chitsogozo cha pangano Lachilamulo analandira Yesu monga Mesiya pamene Yohane Mbatizi monga “wapakhomo” anamsonyeza. Iwo anadzakhala “nkhosa zake” za Yesu, ndipo anazitsogolera ku khola lophiphiritsira latsopano la Yehova. Kholali linaimira unansi wachiyanjo ndi Yehova pamaziko a pangano latsopano, limene linapangidwa ndi Israyeli wauzimu ndipo linalimbikitsidwa ndi mwazi weniweni wa Yesu. Kupyolera mwa pangano limeneli kunakhala kowathekera kupeza moyo wakumwamba limodzi ndi Kristu monga “mbewu” ya Abrahamu mwa imene madalitso akadzera kwa anthu amitundu yonse. (Ahebri 8:6; 9:24; 10:​19-22; Genesis 22:18) Yesu Kristu, amene Mulungu anaukitsa kwa akufa ndi kumbwezeretsa ku moyo wakumwamba, ndiye “khomo” lakhola lapangano latsopano limeneli. Mogwirizana ndi chifuno cha Atate wake, waloŵetsa m’khola limeneli chiŵerengero chochepa chokha​—⁠144 000 chabe​—⁠choyamba chochokera pakati pa Ayuda, ndipo pambuyo pake pakati pa Asamariya ndi Akunja. Monga Mbusa wabwino, Yesu amadziŵa iriyonse yankhosa zake ndi dzina ndipo amazipatsa chisamaliro chake chachikondi ndi uyang’aniro.​—⁠Yohane 10:​7, 9; Chivumbulutso 14:​1-3.

9 Komabe, Yesu sakulekezeretsa ubusa wake ku “kagulu ka nkhosa” aka kamene kamapeza Ufumu wakumwamba. (Luka 12:32) Iye anatinso: “Nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola iri; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (Yohane 10:16) Kodi amenewa ndani? Ndiwo anthu amene sali m’pangano latsopano; sali Aisrayeli auzimu. Ndiwo anthu amene akusonkhanitsidwa m’kakonzedwe ka Yehova ka moyo wamuyaya padziko lapansi pamaziko a chikhulupiriro chawo mumtengo wa nsembe ya mwazi wa Yesu. Unyinji wa iwo wagwirizana mwathithithi ndi mamembala a Israyeli wauzimu tsopano pamene amenewa akali chikhalirebe padziko lapansi, ndipo limodzi nawo, amayang’ana kwa Kristu monga Mbusa Wabwino. Awo a “nkhosa zina” amene akali chikhalirebe amoyo padziko lapansi ndi amene tsopano akuwonekera ndiwo amene amapanga “khamu lalikulu” la Chivumbulutso 7:​9, 10, 14, limene liri ndi chiyembekezo cha kupulumuka chisautso chachikulu chirinkudzacho.

10 Kuti ayenerere kulongosola kwa Baibulo kwa “nkhosa zina” zoterozo zimene zikutetezeredwa ndi kusungidwa ndi Mbusa Wabwino, munthu ayenera “kumvetsera” mawu Ake ndi kupereka umboni wa kukhaladi mbali ya “gulu limodzi” limene limaphatikizapo oloŵa nyumba enieni a Ufumu wakumwamba. Kodi inu mukuchita zimenezo? Kodi mukumvetsera mawu ake mosamalitsa chotani?

11 Mosakaikira inu mudziŵa kuti Yesu anati: “Lamulo langa ndi iri, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu.” (Yohane 15:12) Kodi ndimotani mmene lamulo limenelo likuyambukirira moyo wanu? Kodi chikondi chimene mumasonyeza ndicho chimene Yesu anasonyeza? Kodi nchopandadi mpeni kumphasa? Kodi zochita ndi malingaliro anu zimapereka umboni wa chikondi choterocho kwa onse mu mpingo Wachikristu ndi kwa ziŵalo za banja lanu?

12 Mtumwi Paulo akulongosola kuti ngati ife kwenikweni ‘timva’ Yesu ndipo ‘tikuphunzitsidwa naye,’ umunthu wathu wonse udzasintha. Tidzavula umunthu umene umagwirizana ndi kakhalidwe kathu kakale ndipo tidzavala “umunthu watsopano,” umene umasonyeza mikhalidwe yabwino kwambiri ya Yehova. (Aefeso 4:​17-24; Akolose 3:​8-14) Pamene muphunzira Baibulo, kodi mukulingalira mwamphamvu mbali zimene inuyo mufunikira kupangamo masinthidwe kuti mukondweretse Mulungu? Kodi mukupanga masinthidwe otero mosamalitsa? Kodi mukulabadira ntchito yofunika imene Yesu analamula kaamba ka nthaŵi yathu​—⁠kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu​—⁠ndipo kodi mukufunafuna njira za kuichita? Kodi kuyamikira kukoma mtima kwapadera kwa Yehova kulinga kwa inu kukusonkhezera mwa inu chikhumbo chenicheni cha kutero?​—⁠Mateyu 24:⁠14.

13 Tifunikira kukhala osamala kusalola mitima yathu kutisokeretsa. Anthu mamiliyoni ambiri amati amakhulupirira Yesu Kristu, ndipo mwinamwake iwo angagwire mawu zina za zinthu zimene iye anaphunzitsa, koma amagwiritsira ntchito kokha zimene iwo amaziwona kukhala zosavuta. Ena angapeŵe kuloŵa m’khalidwe limene angalilingalire kukhala loipitsitsa. Chiyembekezo cha moyo padziko lapansi Laparadaiso mu Ufumu wa Mulungu chingamvekere kukhala chabwino kwa iwo, ndipo iwo tsopano angasangalale kugwirizana ndi awo amene akuyesayesa mowona mtima kugwiritsira ntchito ziphunzitso Zachikristu m’miyoyo yawo. Koma ngati tifuna kukhala pakati pa awo amene akupulumuka kuloŵa “dziko lapansi latsopano,” tiyenera kumvetsera mwatcheru chinthu chirichonse chimene Yesu ananena. Nkofunika kuzindikira kuti sitingakhoze kutsogolera mapazi athu bwino lomwe. Tiyenera kumvetsera Mwana wa Mulungu, woikidwa ndi Yehova kukhala Mpulumutsi wa anthu ake, ndi kuyenda m’mapazi ake mosamalitsa.​—⁠Yeremiya 10:23; Mateyu 7:​21-27; 1 Petro 2:⁠21.

[Mafunso]

1. (a) Kodi nkuchiyani kumene tiyenera kugonjera kuti tipulumuke “chisautso chachikulu”? (b) Kodi ndimotani mmene zimenezi zinasonyezedwera mwafanizo ndi njira imene Mulungu anagwiritsirira ntchito Mose?

2. (a) Kodi ndani amene anali “anthu ambiri osokonezeka” amene anachoka ku Igupto ndi Aisrayeli? (b) Kodi mosakaikira nchiyani chimene chinawakopa? (c) Kodi ndipankhani iti pa imene mwamsanga anayesedwa?

3. (a) Kodi nchifukwa ninji kunali kofunika kutsatira malangizo a Mose? (b) Kodi nchiyani chimene chinali tanthauzo la ‘kubatizidwa mwa Mose’? (c) Kodi nchifukwa ninji umenewo uli wofunika kwa Aisrayeli auzimu?

4. Kodi ulamuliro umene Yehova wapatsa Kristu ngawukulu motani?

5. Kodi nchiyani chimene chimapangitsa kugonjera Yesu kukhala kokondweretsa kwambiri?

6. (a) Kodi ndimotani mmene mtundu wa Israyeli unaliri ngati nkhosa m’khola? (b) Kodi nlonjezo lotani limene Yehova anapereka ponena za mbusa wa “nkhosa” zimenezi, ndipo kodi linakwaniritsidwa motani?

7. (a) Monga “mbusa wabwino,” kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuzama kwa nkhaŵa yake yachikondi kaamba ka “nkhosa”? (b) Kodi ndimotani mmene zimenezo zinasiyanira ndi khalidwe la amesiya oyambirira, onyenga?

8. (a) Kodi ndi mu “khola” latsopano liti m’limene Yesu analoŵetsa Ayuda amene anamtsatira? (b) Kodi ndiangati amene wawaloŵetsa m’khola limeneli?

9. Kodi ndani amene ali “nkhosa zina” zimene Yesu akutchula, ndipo ndiliti pamene izo zikusonkhanitsidwa?

10. Kuti mukhale mmodzi wa “nkhosa zina” zimenezo, kodi nchiyani chimene chifunika?

11. Kodi nchiyani chimene chidzapereka umboni wakuti tikumvetseradi zimene Yesu ananena pa Yohane 15:⁠12?

12. (a) Ngati ‘tiphunzitsidwa ndi Yesu,’ kodi ndimasinthidwe otani amene kumeneku kudzapanga mwa ife? (b) Chotero, kodi nchiyani chimene tiyenera kukhala tikuchita ndi zinthu zimene tiphunzira m’Baibulo?

13. (a) Ngati sitisamala, kodi ndimotani mmene mitima yathu ingatisokeretsere? (b) Pamenepa, kodi ndikufikira pati, pamene tiyenera kutsatira mapazi Akristu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena