Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • su mutu 10 tsamba 75-81
  • “Sadzamvanso Njala”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Sadzamvanso Njala”
  • Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “PITANI KWA YOSEFE”
  • KUKHUTIRITSA NJALA YATHU NDI LUDZU TSOPANO
  • Njala Yopatsa Imfa mu Nthawi ya Mwana Alilenji
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kupulumutsa Moyo mu Nthawi ya Njala
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Yehova Sanamuiwale Yosefe
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • ‘Kodi Mulungu Sindiye Amamasulira Maloto?’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
su mutu 10 tsamba 75-81

Mutu 10

“Sadzamvanso Njala”

LIMODZI lamavuto aakulu oyang’anizana ndi dziko lerolino limakhudza chakudya. Mitengo yokwera imachititsa mavuto kwa ambiri. Njala yeniyeni imayang’anizana ndi ena. Kunasimbidwa posachedwapa kuti chaka chirichonse anthu 40 miliyoni​—⁠m’zaka zina okwanira 50 miliyoni​—⁠amafa chifukwa chakuti samakhala ndi chakudya chimene akufunikira. Pafupifupi nthaŵi khumi chiŵerengero chimenecho chimasoŵa kwambiri zakudya zokwanira. Angakhale maiko ena amatulutsa chakudya chochulukirapo kuposa chimene iwo angadye, kaŵirikaŵiri mkangano wandale zadziko ndi umbombo wamalonda umalepheretsa zoyesayesa za kupangitsa makombowo kupezeka kwa awo owafuna koposa.​—⁠Yerekezerani ndi Chivumbulutso 6:​5, 6.

2 Ngakhale m’maiko amene amawonekera kukhala ndi zochuluka akuyang’anizana ndi mtsogolo mosakondweretsa. Chifukwa ninji? Njira zamakono zamalimidwe kaŵirikaŵiri zimadalira pa petulo, ndipo kupezeka kwake kwa padziko lonse nkochepa. Kudalira kwambiri pa mafeteleza amalonda kukuipitsa madzi awo. Kugwiritsiridwa ntchito mopambanitsa kwa makhwala ophera tizirombo, kolinganizidwira kutetezera mbewu, kumawononganso tizirombo timene kukhala chonde kwa nthaka mtsogolo kumadalirapo. Pafupifupi m’mbali iriyonse zochita za anthu, mavuto owopsa amapitirizabe kuchuluka. Aurelio Peccei, prezidenti wa bungwe la mitundu yonse la anthu anzeru anayerekezera dzikoli ndi “mpholopolo yonjanja pamene ikuchoka patsoka kumka patsoka.” Kodi nkwanzeru kuika ziyembekezo zanu zamtsogolo padziko lokhala ndi mbiri yotero?​—⁠Yeremiya 10:23; Miyambo 14:⁠12.

3 Mwanzeru, anthu mamiliyoni ambiri avomereza kufunikira kwawo chithandizo chimene Mulungu yekha angapereke. Pokhala atapenda ulosi wa Baibulo, amadziŵa kuti Yehova Mulungu wakhazika kale pampando wachifumu Mwana wake wakumwamba Yesu Kristu ndipo wampatsa dziko lonse lapansi monga chuma chake. (Salmo 2:​7, 8) Iye ali ndi nzeru ndi mphamvu yotsimikiziritsa kuti anthu onse adzagaŵiridwa mowoloŵa manja dzinthu dzadziko lapansi. (Salmo 72:​7, 8, 16; Akolose 1:​15-17) Pamene dongosolo lamakono ladyera lichotsedwa, Kristu adzatsogolera zoyesayesa za anthu opulumuka kotero kuti dziko lonse lapansi lidzakhala Paradaiso wobalitsa.

4 Komabe, anthu amene adzapindula kosatha ndi ulamuliro wake, ndiwo amene amazindikira kuti munthu samakhala ndi moyo ndi mkate wokha, anthu amene amazindikira mapindu auzimu ndi chofunika chachikulu cha kupeza nyonga kuchokera m’kuphunzira ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. Mobwerezabwereza Baibulo limagogomezera kufunika kwa zimenezi. (Yohane 4:34; 6:27; Yeremiya 15:16) Yesu anakugogomezera pamene anati: “Kwalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.’ ” (Mateyu 4:⁠4) Tifunikira chakudya chauzimu choterocho tsopano, ngati titi tipulumuke mapeto a dziko lamakono. Ponena za mmene tingachipezere kwalongosoledwa mwafanizo kaamba ka ife m’cholembedwa Chabaibulo chonena za Yosefe ndi abale ake.

“PITANI KWA YOSEFE”

5 Mulungu anapereka kwa Yosefe, mdzukulutuvi wa Abrahamu maloto osonyeza kuti Yosefe akakhala ndi mbali yaikulu m’moyo. Chifukwa cha ichi, ndiponso kaamba ka chenicheni chakuti anakondedwa kwambiri ndi atate wake, abale khumi a amayi ena a Yosefe anamuda. Anapangana kumupha koma potsirizira pake anamgulitsa monga kapolo, ndipo anatengeredwa ku Igupto. Kodi chifuno cha Mulungu kwa Yosefe chinali kudzachitidwa motani tsopano?​—⁠Genesis 37:​3-11, 28.

6 Pamene Yosefe anali ndi zaka 30 za kubadwa, Yehova anachitisa Farao, wolamulira wa Igupto, kukhala ndi maloto aŵiri amene anamvutitsa. M’loyamba anawona ng’ombe zisanu ndi ziŵiri “zamawonekedwe okongola ndi zonenepa,” ndiponso ng’ombe zina zisanu ndi ziŵiri “zamawonekedwe oipa ndi zowonda.” Zowondazo zinayamba kudya zonenepa. M’loto lina Farao anawona ngala zisanu ndi ziŵiri paphesi limodzi, “zodzala ndi zabwino,” ndi ngala zina zisanu ndi ziŵiri zimene zinali “zofota, zowonda, zopserera ndi mphepo yakummaŵa.” Kachiŵirinso, zowondazo zinadya zonenepazo. Kodi zonsezi zinatanthauzanji? Palibe aliyense wa anzeru a Igupto anakhoza kumasulira malotowo. Koma wonyamula chikho wa Farao anakumbukira kuti, pamene anali m’ndende, Yosefe, wandende mnzake, anali atamasulira maloto molondola. Mwamsanga Farao anaitana Yosefe.​—⁠Genesis 41:​1-15.

7 Mosadzitengera thamo, Yosefe anauza Farao kuti: “Loto la Farao liri limodzi: chimene Mulungu ati achite wamasulira Farao.” (Genesis 41:​16, 25) Yosefe analongosola kuti loto lachiŵiri linatanthauza zofanana ndi loyamba ndipo linagogomezera kutsimikizirika kwake. Zaka zisanu ndi ziŵiri za dzinthu mu Igupto zinayenera kutsatiridwa ndi zaka zisanu ndi ziŵiri za njala. Iye analangiza Farao kuika munthu wokhoza kuyang’anira kukundika zakudya mkati mwa zaka za dzinthu mokonzekera njala. Pozindikira kuti Mulungu mwiniyo mwachiwonekere anaululira zonsezi kwa Yosefe, Farao anaika Yosefe kukhala woyang’anira zakudya, akumampatsa ulamuliro mu Igupto kukhala wachiŵiri kwa Farao mwiniyo. Monga momwe kunanenedweratu, zaka zisanu ndi ziŵiri za dzinthu dzodabwitsa zinafika, ndipo Yosefe anachititsa chakudya chambirimbiri kukundikidwa. Ndiyeno njala yonenedweratuyo inakantha dzikolo. Pamene anthu anapempha Farao chakudya, iye anayankha: “Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani.” Chotero Yosefe anawagulitsira tirigu​—⁠choyamba analipirira ndi ndalama, kenako ndi zoŵeta zawo, ndipo potsirizira pake anasinthanitsa ndi iwo eni ndi munda wawo. Kuti apitirizebe kukhala ndi moyo, anafunikira kudzipereka kotheratu ku kugwirira ntchito Farao.​—⁠Genesis 41:​26-49, 53-56; 47:​13-26.

8 Njala inakanthanso maiko ozungulira Igupto. Potsirizira pake abale enieni mwa amayi ena a Yosefe anadza kuchokera ku Kanani. Zoposa zaka 20 zinali zitapita kuyambira pamene iwo anamgulitsa mu ukapolo, ndipo sanamzindikire. Anamuŵeramira, monga momwe maloto a Yosefe kalekale anali ataneneratu, nafuna kugula zakudya. (Genesis 37:​6, 7; 42:​5-7) Mwanzeru Yosefe anawayesa nawona umboni wokhutiritsa wakuti maganizo awo kwa iye ndi atate wawo anasinthadi. Potsirizira pake anadziulula nalongosola kuti kunali kwenikweni “kaamba ka kusungidwa kwa moyo” kuti Mulungu adamtumiza ku Igupto patsogolo pawo. Atauzidwa ndi iye, iwo anasamutsira atate wawo ndi mabanja awo ku Igupto. (Genesis 45:​1-11) Zonsezi zinalembedwera phindu lathu, ndipo tanthauzo lake lolosera limakhudza zochitika m’nthaŵi yathu.​—⁠Aroma 15:⁠4.

KUKHUTIRITSA NJALA YATHU NDI LUDZU TSOPANO

9 Mmodzi wa anakatande aakulu a mavuto a anthu ndiyo njala yauzimu. Chifukwa chakuti asiya Yehova, iye sakuwapatsa kuzindikira Mawu ake, ndipo, chifukwa cha chimenecho, akukanthidwa ndi njala “sinjala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova.” (Amosi 8:11) Anthu omva njala yauzimu amapwaira mayankho a mafunso ofunika onga ngati: “Kodi tanthauzo la moyo nchiyani? Kodi nchifukwa ninji anthu amafa? Kodi pali chiyembekezo chenicheni chirichonse chamtsogolo? Popengetsedwa ndi njala yauzimu, kaŵirikaŵiri anthu otero amadzivulaza ndi ena pamene aloŵa m’khalidwe loipa ndi laupandu kukhutiritsa zilakolako zawo.

10 Mosiyana, Yehova wapereka chakudya chauzimu chochuluka kwa atumiki ake okhulupirika, ndipo chikondi chowona chikupezeka pakati pawo. Iye wawatsegulira kuzindikira kwawo chowonadi chauzimu chokhutiritsa m’Mawu ake ouziridwa ndipo wawapatsa ntchito yochita monga mboni zake. Iwo mokondwa amauza ena chowonadi chimenechi amene ali anjala mwauzimu afunafuna moyo mogwirizana ndi Mulungu. (Yesaya 65:​13, 14; Luka 6:21) Kalero mu Igupto wakale zaka zisanu ndi ziŵiri zanjala zinadza pambuyo pa zisanu ndi ziŵiri za dzinthu. Koma m’nthaŵi yathu nyengo ya njala yauzimu ndi zakudya zochuluka zauzimu ikuyendera pamodzi.

11 Lerolino amene ali wolamulira sindiye Farao. Yehova Mulungu, Farao Wamkuluyo, ndiye Wolamulira Wachilengedwe chonse. Wapereka kwa Yesu Kristu ulamuliro wachiŵiri kokha kwa wake. Monga Yosefe Wamkuluyo, Yesu ndiye Munthu kwa amene Yehova waikizira thayo lakugaŵira chakudya chauzimu chochirikiza moyo. Nthanthi zachipembedzo ndi zadziko za dzikoli zasiya anthu ali ndi njala yauzimu yoluma. Kokha mwa kutembenukira kwa Yesu Kristu ndi kulandira chakudya chauzimu m’njira imene akulangiza kuti iwo angachirikizidwe. Anthu mamiliyoni ambiri, ophiphiritsiridwa ndi Aigupto okanthidwa ndi njala, akuchita zimenezo. Kupyolera mwa Yesu Kristu akudzipatulira kotheratu kwa Yehova kunthaŵi yonse, ndipo motero akuphatikizidwa m’khamu lalikulu la opulumuka oyembekezeredwa a Tsiku lirinkudza la mkwiyo la Mulungu.

12 Koma Yesu ali kumwamba. Kodi amapereka motani chakudya chauzimu kutipindulitsa padziko lapansi pano? Iye adaneneratu kuti akatero kupyolera mwa ‘kapolo wake wokhulupirika ndi wanzeru.’ (Mateyu 24:​45-47) Ameneyo ali “kapolo” wachiungwe, wopangika ndi mpingo wake wa odzozedwa ndi mzimu amene ali chikhalirebe pa dziko lapansi. (Yerekezerani ndi Yesaya 43:10.) Otsalira a amenewa ali chikhalirebe padziko lapansi. Mpingo Wachikristu wowona umenewu ngwokhoza kudziŵika mosavuta mwa kuyerekezeredwa kwa ziphunzitso zake ndi zochita ndi Baibulo. Umaphunzitsa mowonadi zimene Yesu analamula. Chifukwa cha chimenecho sunaloŵe m’nkhani zandale zadziko za dzikoli, koma ziŵalo zake zonse ziri olengeza poyera Ufumu wa Mulungu. Iwo sanagaŵanikire pakati pa mipatuko ya Dziko Lachikristu. Ngogwirizana, monga Yesu ananenera kuti akatero​—⁠iwo onse ali Mboni za Yehova motsanzira Ambuye wawo. (Wonani Yohane 17:​16, 20, 21; Mateyu 24:14; 28:​19, 20; Chivumbulutso 1:⁠5.) Iwo amadya chakudya chauzimu chochuluka ndipo ali ofunitsitsa kwambiri kuchigaŵana ndi ena.

13 Anthu ambiri aseka Akristu odzozedwa amenewa, kuti: ‘Kodi muganiza kuti muli bwinopo koposa ife? Kodi muganiza kuti ndinu nokha amene muli olondola?’ Koma m’kupita kwa nthaŵi anthu ena amavomereza modzichepetsa kuti Yehova mowonadi alidi ndi mboni padziko lapansi ndi kuti izo zimalengezadi mawu Ake. Iwo amafika pa kuzindikira kuti Baibulo limasonyeza kuti kudzakhala mpingo Wachikristu wowona umodzi wokha ndi kuti ziŵalo zake zikakhala zogwirizana. (Aefeso 4:5; Aroma 12:⁠5) Kupendedwa kowona mtima ndi kodzichepetsa kwa maumboni kwawatsogoza ku gulu limenelo. Abale khumi a mwa amayi ena a Yosefe anaphiphiritsira anthu otero, amene papitapo anazunza atsatiri odzozedwa a Yesu kapena amene anachirikiza ozunza otero koma amene tsopano akusonyeza kusintha kowona mtima. (Yohane 13:20) Moyamikira amalandira chakudya chauzimu choperekedwa ndi Yesu Kristu kudzera mwa kagulu ka ‘kapolo wake wokhulupirika.’ Iwo amapeza nyonga yauzimu pamene akudya chowonadi Chabaibulo cholongosoledwa m’mabukhu a Watch Tower, nthaŵi zonse amafika pamisonkhano ya Mboni za Yehova ndipo amakangalika m’kuchita chifuniro cha Mulungu. Kodi ndinu mmodzi wa odzichepetsa amenewa?​—⁠Ahebri 10:​23-25; yerekezerani ndi Yohane 4:⁠34.

14 Chakudya chosangalatsa chimadyedwa ndi onse amene mwachikondi amapereka miyoyo yawo motero kuti igwiritsiridwe ntchito ndi Mlengi wawo kupyolera mwa Yesu Kristu. Mwauzimu, “sadzamvanso njala ngakhale ludzu. . . . chifukwa Mwana wankhosa [Yesu Kristu], wa kukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe amadzi amoyo.”​—⁠Chivumbulutso 7:​16, 17; Yesaya 25:​6-9.

[Mafunso]

1. Kodi nkhaŵa ya dziko ponena za chakudya ndiyaikulu motani?

2. Ngakhale m’maiko mmene muli chakudya chambiri, kodi nchifukwa ninji anthu amakhala ndi chifukwa cha kudera nkhaŵa?

3. Kodi ndani amene ali wokhoza kutsimikiziritsa anthu onse chakudya chochuluka, ndipo kodi nchiyani chimene chimakupatsani chidaliro chimenecho?

4. Kuti tipindule ndi zakudya zakuthupi zimenezo, kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita tsopano?

5. Kodi ndimotani mmene Yosefe anafikira kukhala kapolo mu Igupto?

6. (a) Kodi ndimotani mmene maganizo a Farao analunjikitsidwira kwa Yosefe? (b) Kodi nchiyani chimene chinali maloto amene anavutitsa maganizo a Farao?

7. (a) Kodi ndimotani mmene Yosefe anafikira kukhala woyang’anira chakudya wa Igupto? (b) Pamene njala inakula kodi nchiyani chimene Aigupto anachita kuti akhalebe ndi moyo?

8. (a) Kuti apeze zakudya zofunika, kodi nchiyani chimene chinafunika kwa abale a Yosefe mwa amayi ena? (b) Kodi nchifukwa ninji cholembedwa cha zimenezi chasungidwa?

9. (a) Kodi nchiyani chimene chimachititsa njala yauzimu m’dziko lerolino? (b) Kodi nchifukwa ninji imeneyi iri umodzi wa anakatande aakulu amavuto a anthu?

10. (a) M’kukwaniritsidwa kwa Yesaya 65:​13, 14, kodi ndimkhalidwe wotani umene uli pakati pa atumiki a Yehova? (b) Kodi nyengo ya njala yauzimu ndi ya zakudya zochuluka zauzimu iri liti?

11. (a) Kodi ndani amene akuphiphiritsiridwa ndi Farao ndi Yosefe, ndipo kodi nchifukwa ninji motero? (b) Kodi ndimotani mmene njira yotengedwa ndi “khamu lalikulu” yafananira ndi ija ya Aigupto okanthidwa ndi njala?

12. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu kumwamba amachititsira chakudya chauzimu kupezeka kwa ife padziko lapansi pano? (b) Kodi nchiyani chimene chimakukhutiritsani maganizo ponena za kudziŵika kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?

13. (a) Kodi ndim’njira zotani zimene anthu ambiri adzisonyeza kukhala ofanana ndi abale a kwa amayi ena khumi a Yosefe? (b) Kodi ndimotani mmene tonsefe tingapindulire ndi chakudya chauzimu choperekedwa ndi Kristu kudzera mwa kagulu ka “kapolo”?

14. Kodi ndimikhalidwe yauzimu yotani imene ikulandiridwa ndi awo amene akugwirizana ndi ziphunzitso zophunziridwa m’chochitika Chabaibulo chimenechi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena