Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 15 tsamba 42-tsamba 43 ndime 3
  • Yehova Sanamuiwale Yosefe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Sanamuiwale Yosefe
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • “Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Njala Yopatsa Imfa mu Nthawi ya Mwana Alilenji
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kupulumutsa Moyo mu Nthawi ya Njala
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Abale a Yosefe Amuda
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 15 tsamba 42-tsamba 43 ndime 3
Yosefe akufotokoza tanthauzo la maloto a Farao

MUTU 15

Yehova Sanaiwale Yosefe

Yosefe ali m’ndende, Farao yemwe anali mfumu ya ku Iguputo, analota maloto. Palibe amene ankadziwa tanthauzo la malotowo. Wantchito wina wa Farao ananena kuti Yosefe akhoza kufotokoza tanthauzo lake. Nthawi yomweyo, Farao anatuma anthu kuti akatenge Yosefe.

Atafika, Farao anamufunsa kuti: ‘Kodi ungandiuze tanthauzo la maloto anga?’ Yosefe anayankha kuti: ‘Pa zaka 7 zikubwerazi, mu Iguputo muno mukhala chakudya chambirimbiri koma kenako kudzabwera zaka zina 7 za njala. Musankhe munthu wanzeru kuti asonkhanitse chakudya kuti anthu anu asadzafe ndi njala.’ Farao anayankha kuti: ‘Ndakusankha iweyo. Ukhala woyangʼanira dziko lonse la Iguputo. Ine ndekha ndikhala wamkulu kwa iwe.’ Kodi Yosefe anadziwa bwanji tanthauzo la maloto a Farao? Yehova ndi amene anamuthandiza.

Yosefe akulangiza anthu kuti asunge chakudya

Ndiyeno Yosefe anasonkhanitsa chakudya kwa zaka 7. Kenako padziko lonse panali njala mogwirizana ndi zimene Yosefe ananena. Anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana ankabwera kudzagula chakudya kwa Yosefe. Ndiyeno bambo ake atamva kuti ku Iguputo kuli chakudya, anatuma ana awo 10 kuti apite kukagula chakudyacho.

Ana a Yakobo anapita kwa Yosefe ndipo iye atangowaona anawazindikira. Koma azichimwene akewo sanamuzindikire. Iwo anamugwadira ndipo izi zinali zogwirizana ndi maloto amene Yosefe analota ali wamng’ono. Koma iye ankafuna kudziwa ngati abale akewo anali adakali ndi chidani. Choncho anawauza kuti: ‘Inu ndinu akazitape! Mwabwera kuno kudzafufuza malo amene dziko lathu lili lofooka.’ Iwo anayankha kuti: ‘Ayi si choncho. Tachokera ku Kanani ndipo m’banja lathu tinalimo amuna 12. M’bale wathu wina anamwalira ndipo wamng’ono watsala ndi bambo athu.’ Kenako Yosefe anati: ‘Mukabwere ndi mng’ono wanuyo kuti ndikukhulupirireni.’ Zitatero azichimwene ake a Yosefewo anabwerera kwawo.

Ndiyeno chakudya chija chitatha, Yakobo anauza ana akewo kuti apitenso ku Iguputo. Pa ulendowu anatenga mng’ono wawo uja ndipo dzina lake linali Benjamini. Pofuna kuwayesa abale akewo, Yosefe anabisa kapu yake m’thumba la Benjamini n’kuwauza kuti aba kapuyo. Antchito a Yosefe anapeza kapuyo m’thumba la Benjamini ndipo izi zinadabwitsa kwambiri abale akewo. Iwo anapempha Yosefe kuti awalange iwowo m’malo mwa Benjamini.

Apa Yosefe anadziwa kuti abale akewo anasintha kwambiri. Iye analephera kudzigwira moti anayamba kulira n’kunena kuti: ‘Ndine Yosefe, m’bale wanu uja. Kodi bambo anga adakali ndi moyo?’ Abale akewo anadabwa kwambiri. Koma iye anawauza kuti: ‘Musadandaule ndi zimene munandichitira zija. Mulungu ndi amene ananditumiza kuno kuti akupulumutseni. Bwererani kwa bambo anga msanga ndipo mukawatenge n’kubwera nawo kuno.’

Abale akewo anapita kukauza bambo awo nkhani yabwinoyi ndipo anawatenga n’kupita nawo ku Iguputo. Yosefe ndi bambo akewo atakumananso anasangalala kwambiri chifukwa panali patadutsa zaka zambiri asanaonane.

Yosefe wakumana ndi bambo ake, a Yakobo ndipo akupatsana moni

“Ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukiraninso machimo anu.”​—Mateyu 6:15

Mafunso: Kodi Yehova anathandiza bwanji Yosefe? Kodi Yosefe anasonyeza bwanji kuti anakhululukira abale ake?

Genesis chaputala 40 mpaka 45; 46:1-7, 26-34; Salimo 105:17-19; Machitidwe 7:9-15

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena