Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/1 tsamba 15-20
  • Kupulumutsa Moyo mu Nthawi ya Njala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupulumutsa Moyo mu Nthawi ya Njala
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoperekedwa Kaamba ka Kudyetsa Kwauzimu
  • Kubwezera, Chilango, kapena Chifundo
  • Chakudya Chauzimu cha Mwana Alilenji
  • “Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Yehova Sanamuiwale Yosefe
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Njala Yopatsa Imfa mu Nthawi ya Mwana Alilenji
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kukhululukira Ena Kutsegula Njira ya Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/1 tsamba 15-20

Kupulumutsa Moyo mu Nthawi ya Njala

1. Kodi ndi kachitidwe kanzeru kotani kamene Yosefe anakachita mkati mwa zaka za zochuluka, ndipo ndi chotulukapo chotani?

MWAMSANGA pambuyo pa kukhazikitsidwa kwake monga woyang’anira chakudya, Yosefe anayendera dziko la Igupto. Iye anapangitsa zinthu kukonzekeretsedwa pofika nthawi imene zaka za zochuluka zinayamba. Tsopano nthaka inabala zinthu zake zambirimbiri! Yosefe anapitiriza kusonkhanitsa zakudya kuchokera m’minda yozungulira mzinda ulionse, akumazisunga izo mu mzinda. Iye anapitiriza “kusonkhanitsa tirigu ngati mchenga wa mnyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; chifukwa anali wosawerengeka.”​—Genesis 41:46-49.

2. Ndi pa kudzipereka kwaumwini kotani kumene anthu anali okhoza kupeza chakudya?

2 Zaka zisanu ndi ziwiri za zochuluka zinatha, ndipo njala inayamba monga mmene Yehova anali ataneneratu​—njala osati kokha mu Igupto koma “padziko lonse lapansi.” Pamene anthu anjala mu Igupto anayamba kulira kwa Farao kaamba ka mkate, Farao anauuza iwo: “Pitani kwa Yosefe. Chimene iye anena kwa inu, chitani.” Yosefe anagulitsa tirigu kwa Aigupto kufikira ndalama zawo zinatha. Kenaka iye anayamba kulandira zoweta zawo monga malipiro. Pomalizira, anthuwo anabwera kwa Yosefe, ndi kunena: “Tiguleni ife ndi dziko lathu kaamba ka mkate, ndipo ife limodzi ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao.”Chotero Yosefe anagula dziko lonse la Aigupto kaamba ka Farao.​—Genesis 41:53-57; 47: 13-20.

Zoperekedwa Kaamba ka Kudyetsa Kwauzimu

3. Kodi ndi kufulumiza kotani kumene Yesu ananeneratu kwa kupereka chakudya panthawi yake?

3 Monga mmene tirigu amene anagawiridwa ndi Yosefe anatanthauza moyo kwa Aigupto, choteronso chakudya chauzimu chowona chiri chofunikira kaamba ka kudyetsa Akristu omwe amakhala akapolo a Yehova mwa kudzipereka kwawo kwa iye kupyolera mwa Yosefe Wamkulu, Yesu Kristu. Mkati mwa uminisitala wake wa padziko lapansi, Yesu ananeneratu kuti otsatira mapazi ake odzozedwa adzakhala ndi thayo la kugawira zoperekedwa zimenezi. Iye anafunsa: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake? Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero.”​—Mateyu 24:45, 46.

4. Kodi ndimotani mmene chakudya chomaperekedwa ndi gulu la “kapolo” lerolino chimafananira ndi zimene Yosefe anakonza mu tsiku lake?

4 Otsalira okhulupirika a gulu la “kapolo wanzeru” ameneyu lerolino amapita kuutali ulionse wa Malemba kuwona kuti mboni zodzipereka za Yehova, limodzinso ndi anthu okondwerera mu dziko lonse lapansi, amalandira chakudya chauzimu chopatsa moyo. Chidaliro chimenechi chimazindikiridwa monga thayo lopatulika ndipo limachitidwa monga utumiki wopatulika kwa Yehova. Kuwonjezerapo, “kapolo” wakonzekeretsa mipingo ndi kuipatsa iyi mabukhu a Baibulo mu unyinji wotero kotero kuti ali ndi “mbewu” yokwanira ya Ufumu kaamba ka kufalitsa mwapoyera m’minda yawo yogawiridwa. Ichi chimagwirizana ndi mtsiku la Yosefe, pamene iye anasonkhanitsa anthu mu mizinda ndi kuwapatsa iwo tirigu osati kokha kaamba ka chakudya komanso kaamba ka kudzala ndi chiyang’aniro cha kututa mtsogolo.​—Genesis 47:21-25; Marko 4: 14, 20; Mateyu 28:19, 20.

5. (a) Kodi ndi chisamaliro chapadera chotani chimene “kapolo” amapereka ku zosowa za nyumba mu nthawi_ za ngozi? (b) Kodi ndimotani mmene “kusefukira” kwa chakudya chauzimu mu 1986 kumafananira ndi zoperekedwa za mu nthawi ya Yosefe?

5 Ngakhale pamene ntchito yolalikira poyera iri pansi pa chiletso ndipo Mboni za Yehova zikuzunzidwa, ‘kapolo wokhulupirika’ amawona kugawira kwa chakudya chauzimu kumeneku monga chidaliro chopatulika. (Machitidwe 5:29, 41, 42; 14:19-22)Pamene ngozi zichitika, monga ngati namondwe, kusefukira kwa madzi, ndi zivomezi, “kapolo” amawona ku icho kuti ponse pawiri zosowa zakuthupi ndi zauzimu za nyumba ya Mulungu zaperekedwa. Ngakhale awo amene ali mundende za chibalo afikiridwa mokhazikika ndi mawu osindikizidwa. Malire autundu samaloledwa kuletsa kuyenda kwa chakudya chauzimu kwa awo amene akuchifuna icho. Kuti alinganizane ndi kugawira kofunikira kumafunikira kulimba mtima, chikhulupiriro mwa Yehova, ndipo kawirikawiri, kuchenjera koyenerera ndi luso. Kuzungulira dziko lonse lapansi mkati mwa 1986 mokha, “kapolo” anatulutsa kusefukira kwa Mabaibulo ndi mabukhu a zikuto zolimba 43, 958, 303, limodzinso ndi magazini 550,216,455​—zowonadi “chiwerengero chachikulu kwambiri, chonga mchenga wa mnyanja.”

Kubwezera, Chilango, kapena Chifundo

6, 7. (a) Kodi ndimotani mmene njala inatulukiramo mkugwadira pamaso pa Yosefe kwa abale ake opeza khumi? (b) Ndi mnjira ziti mmene Yosefe iye mwini anali pachiyeso tsopano?

6 Kenaka njala inafika kudziko la Kanani. Yakobo anatumiza abale opeza khumi a Yosefe kupita ku Igupto kukagula tirigu. Koma iye sanatumize Benjamini, mbale yekha weniweni wa Yosefe, chifukwa chamantha, monga mmene ananenera, kuti “choipa chingamgwere iye.” Popeza Yosefe anali amene amagulitsa, abale ake anabwera kwa iye ndi kugwada pamaso pake. Ngakhale kuti iwo sanamuzindikire iye monga mbale wawo, Yosefe anawadziwa iwo.​—Genesis 42:1-7.

7 Yosefe tsopano anakumbukira maloto ake oyambirira ponena za iwo. Koma nchiyani chimene akanachita? Kodi iye abwezere? Mu nthawi yawo ya kufuna kokulira, kodi iye awakhululukire kachitidwe kamene iye analandira pamanja awo? Bwanji ponena za chisoni choipa cha bambo wake? Kodi icho chiyenera kuiwalidwa? Kodi ndimotani mmene abale ake amamverera tsopano pa choipa chachikulu chimene iwo anachita? Yosefe, nayenso anali pachiyeso mu nkhaniyi. Kodi kachitidwe kake kadzakhala kogwirizana ndi kachitidwe kamene Yosefe Wamkulu, Yesu Kristu, adzasonyeza mtsogolo, monga kwalongosoledwera pa 1 Petro 2:22, 23: “Amene sanachita chimo, ndipo m’kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo; amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsya, koma anapereka mlandu kwa iye woweruza kolungama.”

8. Kodi Yosefe adzatsogozedwa ndi chiyani, kuchitira chitsanzo chiyani mchigwirizano ndi Yesu ndi ophunzira ake?

8 Popeza Yosefe anatha kuwona dzanja la Yehova mkuyendetsa zinthu, iye akanakhala wosamalira kusunga malamulo a Mulungu ndi maprinsipulo. Mu njira yofananayo, Yesu nthawi zonse anali wofunitsitsa ‘kuchita chifuniro cha atate wake’ pamene iye anagawira moyo wosatha kwa ‘aliyense wokhulupirira iye.’ (Yohane 6:37-40) Monga “atumiki m’malo mwa Kristu,”ophunzira ake odzozedwa nawonso adzakwaniritsa chidaliro chawo chopatulika mu “kulankhula kwa anthu onse mawu a moyo umene.”​—2 Akorinto 5:20; Machitidwe 5:20.

9, 10. (a) Kodi ndi njira yotani imene Yosefe tsopano anatenga, ndipo nchifukwa ninji? (b) Kodi ndimotani mmene Yosefe anasonyezerera chifundo chofanana ndi chimene Yesu adzasonyeza?

9 Yosefe sanadzivumbulutse iye mwini kwa abale ake panthawi imeneyo. M’malo mwake, iye analankhula kwa iwo mwaukali kudzera mwa wotanthauzira, akumanena: “Inu ndinu azondi!” Popeza iwo anatchula za mbale wochepera, Yosefe analamula iwo kutsimikizira kukhulupirika kwawo mwa kubweretsa ameneyo ku Igupto. Yosefe anamva iwo akunena molapa kwa wina ndi mnzake kuti kutembenuka kwa zinthu kumeneku kungakhale chilango kaamba ka kumugulitsa kwawo iye, Yosefe mu ukapolo. Akutembenukira kumbali, Yosefe analira. Mosasamala kanthu za chimenechi, iye anamupangitsa Simeoni kumangidwa kufikira iwo atabwerera ndi Benjamini.​—Genesis 42:9-24.

10 Yosefe sanali kubwezera kaamba ka cholakwa chomwe anachita kwa iye. Iye anafuna kutsimikizira kaya kulapa kwawo kunali kwenikweni, kochokera pansi pa mtima, kotero kuti iwo ayenera kusonyezedwa chifundo. (Malaki 3:7; Yakobo 4:8) Ndi khalidwe lachikondi, lofanana ndi limene Yesu adzasonyeza, Yosefe sanadzaze kokha matumba awo ndi tirigu komanso anabwezera ndalama zawo kwa iwo pakamwa pa thumba la aliyense. Kuwonjezerapo, iye anawapatsa kamba wa paulendo.​—Genesis 42:25-35; yerekezani ndi Mateyu 11:28-30.

11. (a) Mkupita kwanthawi, kodi nchiyani chimene Yakobo anakakamizidwa kuchita, ndipo kodi nchifukwa ninji iye pomalizira anavomereza? (b) Kodi ndimotani mmene Aroma 8:32 ndi 1 Yohane 4:10 mofananamo amatsimikizira ife za chikondi cha Mulungu?

11 Mkupita kwanthawi, iwo anamaliza chakudya chimene anabweretsa kuchokera mu Igupto. Yakobo anafunsa ana ake amuna asanu ndi anayi kubwerera ndi kugula chowonjezereka. Poyambirirapo, iye anachonderera mchigwirizano ndi Benjamini, akumati: “Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m’njira mmene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.” Komabe, pambuyo pa kukakamizidwa kwakukulu ndi kudzipereka kwa Yuda kukhala mwaumwini ndi thayo pa Benjamini, Yakobo mosafunitsitsa anavomereza kuwalola iwo kumtenga mnyamatayo limodzi nawo.​—Genesis 42:36-43:14.

12, 13. (a) Kodi ndimotani mmene Yosefe anaperekera chiyeso kuvumbulutsa khalidwe lamtima la abale ake? (b) Kodi ndimotani mmene chotulukapo chake chinapatsira Yosefe maziko kaamba ka kusonyeza chifundo?

12 Pamene Yosefe anawona kuti Benjamini anabwera ndi abale ake, iye anawaitana iwo kulowa mnyumba yake, kumene iye anapanga phwando. Kwa Benjamini iye anamupatsa mbali kuwirikiza nthawi zisanu kuposa mbali ya aliyense wa enawo. Kenaka Yosefe anapanga chiyeso chomalizira pa abale ake. Kachiwirinso, iye anabwezera ndalama zawo m’thumba la aliyense, koma chikho chake chapadera cha siliva chinaikidwa kukamwa kwa thumba la Benjamini. Pambuyo pa kunyamuka kwawo, Yosefe anatumiza woyang’anira nyumba yake kuwazenga iwo mlandu wa kuba ndi kufufuza m’matumba awo kaamba ka chikho chake. Pamene icho chinapezeka m’thumba la Benjamini, abalewo anang’amba zovala zawo. Iwo anatsogoleredwa kukawonana ndi Yosefe. Yuda anapanga kuchonderera kwamphamvu kaamba ka chifundo, akumadzipereka kukhala kapolo m’malo mwa Benjamini kotero kuti mnyamatayo abwerere kwa atate wake.​—Genesis 43:15-44:34.

13 Wokhutiritsidwa tsopano kaamba ka kusintha mtima kwa abale ake, Yosefe sakanathanso kuletsa malingaliro ake. Pambuyo pa kulamulira aliyense kutuluka kuchoka pa iye, Yosefe ananena: “Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe m’Aigupto. Tsopano musaphwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha kuti munandiguli-

tsa ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo. . .ndikhazikitse inu mutsale m’dziko lapansi, ndi kusunga inu amoyo ndi chipulumutso chachikuru.”Iye kenaka anati kwa abale ake:“Fulumirani kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, ‘. . . Tsikirani kwa ine. Musachedwe. Ndipo mudzakhala m’dziko laGoseni, ndipo. . . ndidzachereza inu komweko, pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi inu ndi banja ndi onse muli nawo.’ ”​—Genesis 45:4-15.

14. Kodi ndi mbiri yachimwemwe yotani imene inaperekedwa kwa Yakobo?

14 Pamene Farao anamva mbiri ponena za abale a Yosefe, iye anauza Yosefe kutenga magaleta kuchokera mdziko la Igupto kupita kubweretsa atate ake ndi onse a m’banja lake ku Igupto chifukwa zabwino koposa za dziko zinali zawo. Pakumva zomwe zinachitika, Yakobo anatsitsimulidwa mzimu ndi kupfuula: “Chakwana! Yosefe mwana wanga akali ndi moyo! Ndidzamuka ndikamuwone iye ndisanafe!”​—Genesis 45:16-28.

Chakudya Chauzimu cha Mwana Alilenji

15. Kodi ndi kwandani kumene ife tsopano timayang’ana kaamba ka chakudya chauzimu, ndipo kodi ndimotani mmene tingatsimikizidwireza kuchuluka kwake?

15 Kodi nchiyani chimene izi zonse zimatanthauza kwa ife lerolino? Nthawi zonse odera nkhawa kaamba ka zosowa zathu zauzimu, timafunikira kuyang’ana kwa Wina amene ali wamkulu koposa Farao wachifundo wa m’nthawi ya Yosefe. Iye ali Mbuye Wadziko Lonse Yehova, yemwe amapereka chakudya ndi chitsogozo kupyolera mu masiku ano akuda adziko lanjala kaamba ka chowonadi cha Baibulo. Tadzikangalitsa ife eni ndi zikondwerero za Ufumu wake, kubweretsa chachikhumi chathu, monga mmene kunaliri mu nkhokwe yake. Ndi moolowa manja chotani nanga mmene iye watsegulira kwa ife “mazenera a kumwamba,” kukutsanulira dalitso, “kufikira adzasoweka malo akuulandira !​—Malaki 3:10.

16. (a) Ndi kuti kokha kumene “chakudya” chopulumutsa moyo chingapezeke lerolino? (b) Kodi ndimotani mmene kufesedwa kwa “mbewu” m’malo mwa anthu anjala kwafutukulidwira?

16 Kudzanja lamanja la Yehova kuli Woyang’anira Wachakudya wake, tsopano Mfumu yokhazikitsidwa, Yesu wolemekezedwa. (Machitidwe 2:34-36) Monga momwe anthu anayenera kudzigulitsa iwo eni monga akapolo ndi kukhalabe ndi moyo, chotero onse lerolino omwe afuna kukhalabe ndi moyo ayenera kubwera kwa Yesu, kukhala otsatira ake odzipereka kwa Mulungu. (Luka 9:23, 24) Monga mmene Yakobo anatsogolera ana ake kupita kwa Yosefe kaamba ka chakudya, chotero Yehova amatsogolera anthu olapa kwa Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu. (Yohane 6:44, 48-51) Yesu akusonkhanitsa otsatira ake mu mipihgo yonga mizinda​—yoposa 52, 000 yamphamvu kuzungulira padziko lonse lapansi lerolino​—kumene iwo akudyetsedwa kuchokera ku gome la chakudya chauzimu ndipo akugawiridwa ndi “tirigu” wosefukira, monga “mbewu” kaamba ka kufesa m’munda. (Genesis 47:23, 24; Mateyu 13:4-9, 18-23) Mboni zimenezi za Yehova ziri ogwira ntchito odzipereka! Owonjezereka a iwo ali kudzipereka kaamba ka utumiki waupainiya wanthawi zonse, ndi ambiri a iwo chiŵirengero cha 595, 896 akugawana, monga chiŵerengero chapamwamba, mu mwaŵi wantchito imeneyi mu mwezi umodzi chaka chapita. Chimenecho chimapanga avereji ya apainiya oposa 11 mu mpingo ulionse!

17. Kodi ndi mbiri ina ya ulosi yotani imene iridi ndi kufananako mu kugwirizana kwa abale khumi opeza ndi Yosefe?

17 Chiri chodziwikiratu kuti abale opeza khumi a Yosefe, tsopano olapa kaamba kamachitidwe awo ndi kawonedwe kawo kakale anali ogwirizana ndi iye mu Igupto, amene, limodzi ndi Sodomo, amaimira dziko mu limene Yesu anapachikidwa. (Chivumbulutso 11:8) Ichi chimatikumbutsa ife za Zekariya 8: 20-23, yemwe amafika pachimake ndi kulongosola kwa “amuna khumi” omwe adzanena, “Ndimuka nanu,” kunena kuti, ndi anthu odzozedwa a Yehova, a amene otsalira akutumikirabe pano padziko lapansi.

18. Chiyanjo chapadera chosonyezedwa kwa Benjamini chimafanana ndi chiyani mu nthawi yamakono?

18 Komabe, bwanji ponena za mbale weniweni wa Yosefe, Benjamini, amene kubadwa kwake kovutikira kunagulitsa moyo wamkazi wokondedwa wa Yakobo Rakele? Benjamini anali mwapadera woyanjidwa ndi Yosefe, amene mosakaikira anali ndi chiyanjo chathithithi ndi mwana wa mayi wake. Ichi moyenerera chimawerengera pa kulandira kwa Benjamini gawo lowirikiza nthawi zisanu pamene abale 12 onse poyamba anagwirizanitsidwa pa phwando mnyumba ya Yosefe. Kodi Benjamini moyenerera samaimira otsalira odzozedwa a Mboni lerolino, ambiri a amenewo kukhala atapulumuka anasonkhanitsidwa kumbali ya Ambuye kuyambira mu 1919? Gulu la “Benjamini limeneli lalandiradi gawo lapadera kuchokera kwa Yehova, pamene ‘mzimu wake uchitira umboni ndi mzimu wawo.’ (Aroma 8:16) Awa, nawonso, ayesedwa ponena za umphumphu wawo pamene “nkhosa” za Ambuye zatumikira iwo.​—Mateyu 25:34-40.

19. Kodi ndi kufanana kwa mtundu wanji kumene kuyenera kuwonedwa pakati pa kusamuka kwa mabanja a Israyeli kupita ku Goseni ndi kusonkhamtsidwa kwa anthu a Mulungu lerolino?

19 Chiri chosangalatsa kuti, pamene Farao anakonzekeretsa kumubweretsa Yakobo ndi mbumba yake ku , Igupto, “miyoyo” yomwe inakhala kumeneko inafika chiwerengero cha 70, kuchulukitsa kwa 7 ndi 10. (Genesis 46:26, 27) Ziŵerengero ziŵiri zimenezi zimagwiritsidwa ntchito mowonekera mu Malemba onse,“7” kaŵirikaŵiri kusonyeza chiŵerengero chakumwamba ndi “10” chiŵerengero chotheratu cha padziko lapansi. (Chivumbulutso 1:4, 12, 16; 2:10; 17:12) Ichi chimafanana ndi mkhalidwe lerolino, pamene tingayembekezere kuti Yehova adzasonkhanitsa mu “dziko lake,” paradaiso wauzimu mu amene tikusangalala nave tsopano, aliyense womalizira wa banja lake la Mboni. (Yerekezani ndi Aefeso1:10. ) “Yehova azindikira iwo amene ali ake,”ndipo ngakhale: tsopano iye akuwakhazikitsa iwo “padera lokometsetsa la dziko,” monga mmene analiri Goseni mu ulamuliro wa Farao.​—Genesis 47:5, 6; 2 Timoteo 2:19.

20. Mosasamala kanthu zanjala yauzimu lerolino, kodi nchifukwa ninji tiyenera kukondwera?

20 M’tsiku la Yosefe, zaka zanjala zinatsatizana ndi zaka za zochuluka. Lerolino, izo zimayendera limodzi. Mkusiyanitsa ndi njala yauzimu mu dziko la kunja kwa chiyanjo cha Yehova, pali chakudya chauzimu chochuluka m’malo olambirira a Yehova. (Yesava 25:6-9; Chivumbulutso 7:16, 17) Inde, ngakhale pali njala ya kumva mawu a Yehova mu Chipembedzo cha Dziko, monga mmene Amosi ananeneratu, mawu a Yehova amatuluka kuchokera ku Yerusalemu wa kumwamba. Ndimotani mmene icho chimatipangira ife kusangalala!​—Amosi 8:ll; Yesaya 2:2, 3; 65:17, 18.

21. (a) Kodi ndi mwawi waukulu wapadera wotani umene ife timasangalala nawo lerolino? (b) Kodi tiyenera kukhala oyamikira kaamba ka chiyani, ndipo ndimotani mmene tingasonyezere chiyamikiro chathu?

21 Lerolino pansi pa chitsogozo cha Yosefe Wamkulu, Yesu Kristu, tiri ndi mwaŵi waukulu wa kusonkhanitsidwa mu mipingo yonga mizinda. Kumeneko timakhala ndi phwando lachakudya cholemerera chauzimu chochuluka ndiponso kufesa mbewu za chowonadi ndi kubukitsa mbiri yabwino kuti chakudya chauzimu chiripo. Ichi timachita kaamba ka phindu la onse amene amavomereza ziyeneretso ndi zoperekedwa za chikondi zokonzedwa ndi Wolamulira Wadziko Lonse Yehova. Tingakhale oyamikira chotani nanga kWa Mulungu wathu kaamba ka mphatso ya Mwana wake, Yosefe Wamkulu, yemwe amatumikira monga Woyang’anira wanzeru wachakudya chauzimu! Ali iye amene watumizidwa ndi Yehova kugwira ntchito monga Mpulumutsi wamoyo mnthawi ino yanjala yauzimu. Lolani aliyense wa ife asonyeze kufunitsitsa mu kupereka utumiki wopatulika kutsanzira chitsanzo chake ndipo pansi pa utsogoleri wake!

Kodi Mukuwona Kufanana Kwake?

◻ Kodi ndimotani mmene Yosefe anafananira ndi Yesu monga Woyang’anira Wachakudya?

◻ Kodi nchiyani mu chitsanzo cha Yosefe chimene chimafanana ndi kukhala kapolo kwa Mulungu kupyoiera mwa kudzipereka?

◻ Kodi ndi mtundu wanji umene wasonyezedwa ndi Yosefe ndi Yesu monga chitsanzo kaamba ka ife lerolino?

◻ Mofanana ndi mu nthawi ya Yosefe, kodi ndi makonzedwe otheratu akugawira chakudya otani amene alipo lerolino?

◻ Kodi kulingalira kwathu kwa chitsanzo chimenechi kuyenera kutifulumiza ife kuchita chiyani?

[Chithunzi patsamba 16, 17]

M’dziko lomizidwa ndi njala yauzimu, Yosefe Wamkulu amapereka zochuluka kaamba ka onse amene amabwera kwa iye mu chikhuluplriro

Monga mmene abale khumi opeza anasonyezera chigonjero kwa Yosefe, khamu lallkulu tsopano llmazlndiklra Kristu

Mofanana ndi miyoyo 70 ya banja la Yakobo, chiwerengero chotheratu cha “nkhosa” za Yehova chifika mu “dziko“ lokometsetsa—paradalso wauzimu amene tikusangalala naye tsopano

[Chithunzi patsamba 18]

Gulu lamakono la Benjamini layanjidwa mwapadera ndi Kristu, kulandira “panthawi yake chakudya” chochuluka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena