Mutu 15
Kulekanitsidwa kwa Anthu pa Mkangano Waufumu
ALIYENSE wa ife wayang’anizana ndi chosankha chachikulu. Lingaliro lathu ku Ufumu Waumesiya wa Yehova wokhala m’manja mwa Yesu Kristu liri pa mkangano. Kulekanitsidwa kwa anthu amitundu yonse kulinkuchitika pa mkangano umenewu. Mwa kachitidwe ka munthu aliyense iye alinkuikidwa m’limodzi la magulu aŵiri. Limodzi lokha la magulu amenewa lidzapulumuka chiwonongeko chadziko choyandikiracho.—Mateyu 24:40, 41.
2 Yehova wakhazika kale pampando wachifumu Mwana wake wodzozedwa, Mesiya wake, kumwamba. Pamapeto a “nthaŵi zoikidwiratu za amitundu mu 1914, Mulungu anapereka kwa Yesu Kristu mitunduyo monga choloŵa chake—dziko lonse lapansi monga chuma chake. (Salmo 2:6, 8) Boma Laumesiya, lokhala ndi mfumu yodzozedwa ya Yehova pampando wachifumu, ndilo njira ya Mulungu yochitira chifuno chake chenicheni chanzeru ndi chachikondi mogwirizana ndi dziko lapansi. Chifukwa cha chimenecho, lingaliro lanu ku Ufumuwo, limasonyeza mmene mumalingalirira ulamuliro wachilengedwe chonse wa Yehova. Posakhalitsa Ufumu Waumesiya umenewo “udzaphwanya ndi kutha” dongosolo lonse landale zadziko tsopano lolamulira zochitika za anthu ndipo udzakhala boma limodzi padziko lonse lapansi. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 19:11-21) Pamene liyamba kusanduliza dziko lapansi kukhala Paradaiso, kodi mudzakhala kuti? Kodi mudzakhala pakati pa awo otsogozedwa nalo kudzasangalala ndi moyo wangwiro? Yesu analongosola maziko pa amene anthu okhala ndi moyo tsopano angakhalire ndi chiyembekezo chotero.
MFUMU NDI “ABALE AKE”
3 Pouza atumwi ake za “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” Yesu anagwiritsira ntchito miyambi ingapo, kapena mafanizo. M’lotsirizira anati: “Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.”—Mateyu 24:3; 25:31-33.
4 Wonani kuti panopa Yesu akudzitchula kukhala “Mwana wa munthu,” monga momwe iye adachitira kale mobwerezabwereza poyamba mu ulosi umenewu. (Mateyu 24:27, 30, 37, 39, 44) Kugwiritsira ntchito kwake kanenedweka kunali chokumbutsa masomphenya olosera operekedwa kwa Danieli pafupifupi zaka mazana asanu ndi limodzi papitapo, ponena za amene mneneriyo analemba: “Ndinawona m’masomphenya usiku, tawonani anadza ndi mitambo yakumwamba wina ngati mwana wa munthu [Yesu Kristu]; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake. Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu ya anthu, ndi a amanenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzawonongeka.” (Danieli 7:13, 14; Ahebri 2:5-8) Mphamvu yolamulira imeneyo yaperekedwa kale kwa Yesu Kristu. Chiyambire 1914 akulamulira ali pampando wake wachifumu wakumwamba. Kodi ndimotani mmene inuyo mwalabadirira ulamuliro wake? Kodi kakhalidwe kanu kamapereka umboni wa kulemekeza woyera Ameneyu amene Mulungu mwiniyo wampanga kukhala Wolamulira wa dziko lonse lapansi?
5 Mawu chabe ngosakwanira. Nkosavuta kwa munthu kunena kuti amakhulupirira Ufumu wa Mulungu ndi kuti amakonda Yesu Kristu. Koma m’mwambi wake wa nkhosa ndi mbuzi Yesu anasonyeza kuti, popeza iye akakhala wosawoneka kumwamba, chinthu chachikulu chimene iye akalingalira m’kutsimikizira kutsimikizirika kwa zonena za munthu chikakhala kuchita kwake ndi awo amene amaimira Kristu padziko lapansi, “abale ake.”—Mateyu 25:40, 45.
6 Kodi iwo ndani? Anthu amene Mulungu waŵasankha pakati pa anthu kukhala oloŵa nyumba limodzi ndi Kristu a Ufumu wakumwamba. Amenewa akukwanira 144 000, amene otsalira okha akali padziko lapansi. (Chivumbulutso 14:1, 4) Chifukwa chakuti iwo “abadwanso” mwa njira ya kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu, iwo ndiana a Mulungu, ndipo kaamba ka chifukwa chimenecho iwo akutchedwa m’Malemba “abale” a Yesu Kristu. (Yohane 3:3; Ahebri 2:10, 11) Yesu amaŵerengera zimene anthu amachitira “abale” amenewa, ngakhale kwa “wamg’onong’ono” wa iwo kukhala zikuchitidwa kwa iye mwini.
7 Kodi “abale” a Kristu amenewa ali kuti m’nthaŵi yathu? Kodi mudzaŵapeza pakati pa opita kutchalitchi a Dziko Lachikristu? Eya, kodi Yesu adanenanji ponena za otsatira ake owona? “Iwo saali mbali ya dziko, monga momwe ine sindiri mbali ya dziko.” (Yohane 17:16, NW) Kodi zimenezo zinganenedwedi ponena za matchalitchi a Dziko Lachikristu ndi ziŵalo zawo? Kwakukulukulu, malingaliro awo ndi khalidwe zimangosonyeza awo amene ali ofala m’mbali ya dziko kumene iwo akupezeka. Kuloŵa kwa matchalitchi m’ndale zadziko nkodziŵika kwambiri. Pamene Mpambo Wamalamulo wa Mitundu Yogwirizana unalinkulinganizidwa mu 1945, nthumwi Zachiprotesitante, Chikatolika ndi Chiyuda zinalipo monga aphungu. M’zaka zaposachedwapa, apapa a Roma atamanda Mitundu Yogwirizana monga “chiyembekezo chotsirizira cha chigwirizano ndi mtendere” ndi “bwalo lalikulu la mtendere ndi chilungamo.” Bungwe Ladziko la Matchalitchi, lokhala ndi ziŵalo za magulu achipembedzo zokwanira 300, laperekadi ndalama zogwiritsiridwa ntchito kuthandiza zipanduko zandale za dziko. Komabe, Yesu Kristu anati kwa kazembe Wachiroma Pilato: “Ufumu wanga suuli mbali ya dziko lino.”—Yohane 18:36.
8 Maumboni amasonyeza kuti gulu limodzi lokha lakhala ndi kuimira kwamphamvu Ufumuwo, likumapereka kuyesayesa kwaphamphu kuwulengeza padziko lonse lapansi, uku likupeŵa kuloŵa kwa mtundu uliwonse m’zochitika zandale zadziko za dziko lapansi. Gulu limeneli ndilo Mboni za Yehova. Pakati pawo pakupezeka otsalira a “abale” a Kristu. Motsanzira Ambuye wawo ndi atumwi ake, iwo adzipereka ku kupita kumzinda ndi mzinda ndi kunyumba ndi nyumba, akuuza anthu mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Luka 8:1; Machitidwe 8:12; 19:8; 20:20, 25) Mu 1919, pamsonkhano wa Mboni za Yehova (zodziŵika panthaŵiyo monga Ophunzira Baibulo Amitundu Yonse) mu Cedar Point Ohio, osonkhanawo anakumbutsidwa kuti “ntchito” yawo “inali ndipo ndiyo kulengeza ufumu waulemerero wa Mesiya ukudzawo.” Pamsonkhano wina wofanana mu 1922 kumeneku kunagogomezeredwanso, ndipo anafulumizidwa kuti: “Lengezani, lengezani, lengezani, Mfumu ndi ufumu wake.” Pogwiritsira ntchito njira iriyonse yopezeka kwa iwo, zapitirizabe kuchita zimenezo padziko lonse lapansi mpaka lerolino. (Mateyu 24:14) Chifukwa cha ntchito yawo, mkangano Waufumu waperekedwa pamaso panu. Kodi mukuchita nawonji?
‘MUNACHITIRA ICHI MMODZI WA ABALE ANGA’
9 “Abale” odzozedwa ndi mzimu a Kristu akumana ndi ziyeso zazikulu chifukwa cha kulalikira molimba mtima Ufumu wa Mulungu, pamene akusunga kukhala olekana ndi dziko. (Yohane 15:19, 21) Ena akumana ndi njala, ludzu ndi usiŵa. Ambiri asiya nyumba zawo kukatumikira m’madera kumene anali alendo. Pochita uminisitala wawo, iwo akumana ndi utenda ndi kuikidwa m’ndende, ngakhale imfa yochititsidwa ndi ozunza. Zokumana nazo za “abale” a Kristu zimenezi zachititsa anthu a mitundu yonse kuyang’anizana ndi chiyeso. Kodi kukonda Mulungu ndi Kristu kudzawachititsa kuthandiza oimira Ufumu wakumwamba amenewa? (Mateyu 25:35-40; yerekezerani ndi 2 Akorinto 5:20.) Osati kwenikweni chifundo chabe koma chithandizo choperekedwa chifukwa chakuti iwo ali a Kristu chimaŵerengeredwa ndi Mfumuyo kukhala chitachitiridwa iye mwiniyo.—Marko 9:41; Mateyu 10:42.
10 Awo amene amapereka chithandizo chotero Yesu amawayerekezera ndi nkhosa. Anthu amene amalephera kupereka chithandizo kwa “abale” ake amatchedwa m’mwambi wa Yesu kukhala mbuzi. “Mbuzi” zingakane kuti sizinawone Yesu Kristu. Koma iye watumiza atumiki ake kwa iwo, ndipo amenewa adzidziŵikitsa bwino lomwe. “Mbuzi” zonse zingazunze “abale” a Kristu, koma izo sizinasonkhezeredwe ndi kukonda Mfumu yakumwambayo kuthandiza oimira ake. (Mateyu 25:41-45) Iwo amamatira ku dziko limene Satana Mdyerekezi ali wolamulira wake wosawoneka. “Nkhosa” nazonso sizingawone kwenikweni Kristu. Koma, mosiyana ndi “mbuzi,” zimenezi zimasonyeza kuti izo sizikuwopa kudzigwirizanitsa ndi “abale,” a Kristu, zikumachirikiza olengeza Ufumu wa Mulungu amenewa. “Nkhosa” zimadziŵa zimene zikuchita, ndipo zimapanga chosankha chotsimikizirika moyanja Ufumu wa Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu. Ndicho chifukwa chake kachitidwe kawo kali ndi chiyanjo mmaso mwa Mfumuyo.
11 Komabe, kodi ndimotani, mmene kuliri kotheka kuti anthu a mitundu yonse aweruzidwe pamaziko amenewa? Kodi Yesu sananene kuti “abale” ake, amene Atate akaperekako Ufumu wakumwamba, akakhala kokha “kagulu ka nkhosa”? (Luka 12:32) Anthu ambiri samakumana mwachindunji ndi mmodzi wa iwo. Zowona, koma “abale” a Kristu amapanga chithime cha gulu la mitundu yonse la Mboni za Yehova. Mwanjira ya anthu olinganizidwa amenewa, mkangano wofunika Waufumu ukuperekedwa pamaso pa anthu kulikonse. Zonsezi zikutsogozedwa ndi Kristu mwiniyo ali pa mpando wake wachifumu wakumwamba ndipo mothandizidwa ndi angelo. M’maiko okwanira 200 ndi magulu a zisumbu pa dziko lonse lapansi—ngakhale kumene kulalikidwa kwa Ufumu wa Mulungu kuli koletsedwa ndi boma—ntchito yolekanitsayo ikupita patsogolo mosaletseka, ndipo khamu lalikulu la anthu likuimira kumbali ya Ufumu wa Mulungu.
12 Kodi amasonyeza motani zimenezi? Mwa kugwirira ntchito nthaŵi yonse limodzi ndi odzozedwawo, akumalengeza mwachangu kuti Ufumu ukulamulira ndi kuti posachedwapa udzathetsa dongosolo ladziko. Motero iwo amadzisonyeza poyera kukhala ataimira Ufumu Waumesiya wa Yehova ndipo mwachikondi amalimbikitsa ena kuchita mofanana. Choposa kwambiri chikhumbo cha kupulumuka chimasonkhezera anthu a mitima yolungama amenewa. Iwo amakondadi Yehova ndi njira zake. Makonzedwe a Ufumu wake ndi Kristu monga Mfumu amadzadza mitima yawo ndi chiyamikiro, ndipo amafuna kuti ena apindule nawo. Motero iwo amaloŵa kumlingo wotheratu umene iwo ali okhoza m’kupereka umboni Waufumu. Monga momwe Yesu Kristu analangizira ophunzira ake, iwo ‘amathanga kufunafuna ufumuwo,’ osalola nkhaŵa ndi zosoŵa zakuthupi kuukankhira pamalo achiŵiri. Mwanjira imeneyi amayenerera madalitso aakulu.—Mateyu 6:31-33.
KODI INU ‘MUDZALOŴA UFUMUWO’
13 Chimene chikuyembekezera awo amene akudzisonyeza kukhala “nkhosa” za m’mwambi wa Yesu chiridi chodabwitsa. Ali pampando wake wachifumu kumwamba, iye akuti kwa iwo: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pachikhazikiro chake cha dziko lapansi.” (Mateyu 25:34) Kuyambira “pachikhazikiro cha dziko lapansi,” panthaŵi imene Adamu ndi Hava choyamba anabala ana amene akanapindula ndi makonzedwe a Mulungu a kuwombola anthu, mogwirizana ndi Genesis 3:15, 16, Yehova anali kulingalira mfupo ya “nkhosa” zimenezi. (Yerekezerani ndi Luka 11:50, 51.) Wawo ndiwo mwaŵi wa kukhala ndi ungwiro waumunthu m’Paradaiso wobwezeretsedwa umene Adamu adataya. ‘Kuloŵa mu ufumu’ kwawoko sikumatanthauza kuti iwo adzapita kumwamba, chifukwa chakuti mwambiwo umasonyeza kuti “nkhosa” siziri anthu amodzimodziwo ndi “abale” a Mfumu, amene ali oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba. Chotero “nkhosa” ziyenera kukhala nzika za padziko lapansi za boma lakumwamba limenelo Greek-English Lexicon ya Liddell ndi Scott imalongosola kuti mawu Achigirikiwo basileiʹa, amene panopa atembenuzidwa kukhala “ufumu,” angazindikiridwe m’lingaliro lachete, kutanthauza “kulamulidwa ndi mfumu” kwa munthu. Ndilo lingaliro limeneli mwachiwonekere limene likugwira ntchito panopa.
14 Pamene “mbuzi” ziloŵa “m’kudulidwa kosatha,” m’chiwonongeko chotheratu monga ngati chochitidwa ndi moto, “nkhosa” zidzatetezeredwa ndi Mfumu Yaumesiya. (Mateyu 25:41, 46; yerekezerani ndi Chivumbulutso 21:8.) Popanda kufunikira kulikonse kwa kufa, iwo adzapyoletsedwa chisautso chachikulu kuloŵa mu “dziko lapansi latsopano” laulemerero limene lidzakhala lopanda chisonkhezero choipa cha Satana ndi dongosolo lake lazinthu loipa. Dalitso limenelo lidzakhala lawo chifukwa chakuti iwo akupanga chosankha chabwino pa mkangano Waufumuwo tsopano.
15 Kukakhala kolakwa kwambiri kulingalira kuti, chifukwa chakuti chiwonongeko cha “mbuzi” nchosatha, mwambiwo sungagwire ntchito kufikira mtsogolo, mwinamwake mkati mwa ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu. Mosemphana ndi zimenezo, anapereka mwambi umenewu monga mbali ya chizindikiro cha “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 24:3) Zimene akulongosola zikuchitika pambuyo pa kuikidwa kwake pampando wachifumu komanso pamene “abale” ake akali chikhalirebe m’thupi ndi kulandira mavuto amene iye akutchula. Tiri m’nthaŵi imeneyo, ndipo ikutha mofulumira kwambiri. Chifukwa cha chimenecho, nkofunika chotani nanga mmene kuliri, osati kokha kudalira kotheratu Ufumuwo koma kuthandiza ena kuwona kufunika kwa kuchita choncho tsopano.
[Mafunso]
1. Kodi nchifukwa ninji kulekanitsidwa pa mkangano Waufumu iri nkhani yaikulu kwa aliyense wa ife?
2. (a) Kodi ndimotani mmene Ufumu Waumesiya umenewu uliri wogwirizana ndi mkangano waulamuliro wa Yehova? (b) Kodi nchiyani chimene Ufumu udzakhala posachedwapa, ndipo chotero kodi nchiyani chimene tiyenera kukhala tikulingalira mwamphamvu?
3. Pa Mateyu 25:31-33, kodi Yesu analongosolanji?
4. (a) Kodi ndimotani mmene mwambiwu ukugwirizanira ndi Danieli 7:13, 14? (b) Kodi ndimafunso otani amene modzipindulitsa tingadzifunse?
5. Kodi ndimotani mmene Kristu amatsimikizirira kutsimikizirika kwa kudzinenera kwa munthu kwa kudzipereka kwa iye monga Mfumu?
6. Kodi ndani ali “abale” a Kristu amenewa?
7. Kodi nchifukwa ninji “abale” a Kristu saali ziŵalo za ma-tchalitchi a Dziko Lachikristu?
8. (a) Kodi nchiyani chimene chakuthandizani kudziŵa “abale” a Kristu? (b) Kodi ntchito yolalikira ufumu njofunika motani kwa iwo?
9. (a) Kodi ndimotani mmene mikhalidwe yolongosoledwa pa Mateyu 25:35-40 iliri yogwirizana ndi uminisitala wa Ufumu? (b) Chotero nchiyeso chiti chimene anthu kulikonse ayang’anizana nacho?
10. (a) Kodi nchifukwa ninji chitsutso choperekedwa ndi “mbuzi” chiri chosagwira ntchito? (b) Moyerekezera, kodi ndimalo otani amene “nkhosa” zatenga?
11. (a) Popeza anthu ambiri sanakumane ndi “abale” a Kristu, kodi ndimotani mmene angaweruziridwe pamaziko a zimene zalongosoledwa pano? (b) Kodi nchiyani chimene chimatsimikiziritsa chipambano cha ntchitoyi?
12. (a) Kodi ndimotani mmene “nkhosa” zimamveketsera bwino lomwe kaimidwe kamene zatenga? (b) Kodi nchifukwa ninji izo zimatero?
13. (a) Kodi nkuyambira liti pamene Yehova analingalira mphoto kwa anthu onga nkhosa amenewa? (b) Kodi kumatanthauzanji kwa iwo “kuloŵa mu ufumu”?
14. Kodi ndimotani mmene chiweruzo choperekedwa pa “mbuzi” chimasiyanira ndi choloŵa cha “nkhosa”?
15. (a) Kodi timadziŵa bwanji kuti mwambiwu umagwira ntchito tsopano? (b) Motero, kodi ndintchito yanji imene iri yofunika kwambiri?