Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • go mutu 10 tsamba 160-175
  • “Khamu Lalikulu” Litamanda Boma la Dziko Likudza’lo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Khamu Lalikulu” Litamanda Boma la Dziko Likudza’lo
  • Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KULEKANITSA OCHIRIKIZA UFUMU NDI OSACHIRIKIZA
  • OSACHIRIKIZA BOMA LA DZIKO LIKUDZA’LO
  • “OPULUMUKA CHISAUTSO CHACHIKULU”
  • Kulekanitsidwa kwa Anthu pa Mkangano Waufumu
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Kodi Nkhosazo ndi Mbuzizo Zili ndi Mtsogolo Motani?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Pamene Kristu Adza Mumphamvu ya Ufumu
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
go mutu 10 tsamba 160-175

Mutu 10

“Khamu Lalikulu” Litamanda Boma la Dziko Likudza’lo

1, 2. Kodi mitundu yonse ya pa dziko lapansi tsopano ikusonkhanitsidwa pamaso pa yani?

MITUNDU yonse ya dziko lapansi, ija ya m’kati mwa Mitundu Yogwirizana ndi ija imene idakali kunja kwa gulu la dziko limene’lo, tsopano yasonkhanitsidwa pamaso pa Mfumu ya Mulungu yolongedwa pa mpando wachifumu, Mwana wake Yesu Kristu. Zimene’zi ziri monga momwe’di Mwana wa Mulungu ananeneratu pamene anali pa dziko lapansi zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo. M’fanizo lotsirizira loperekedwa mu ulosi wake umene umalongosola mwatsatane-tsatane “chizindikiro cha kukhala pafupi [kwake] [parousia] ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu,” Yesu Kristu anati:

2 “Pamene Mwana wa munthu adza mu ulemerero wake, ndi angelo onse limodzi naye, pamenepo iye adzakhala pansi pa mpando wake wachifumu waulemerero. Ndipo mitundu yonse idzasonkhanitsidwa pamaso pake.”—Mateyu 25:31,32, NW.

3. Kodi ndi motani m’mene ena anganenere motsutsa mau apita’wo?

3 Ambiri adzatsutsa kukwaniritsidwa kwa ulosi wouziridwa umene’wo lero lino, akumawiringula kuti sakuona anthu oposa mabiliyoni anai’wo a m’mitundu yonse, mafuko ndi maonekedwe a khungu akusonkhanitsidwa pa malo ena akulu pamaso pa mpando wachifumu wooneka wakumwamba wokhala ndi Mwana wa munthu, Yesu Kristu, wokhalapo, wozingidwa ndi “angelo onse” a kumwamba. Tikubvomerezana ndi otsutsa amene’wa kuti iwo sakuona kusonkhanitsidwa kwa m’mitundu yonse kotero’ko. Choyamba, kodi ndi motani m’mene okhala pa dziko lapansi onse mabiliyoni anai akanafikira pa malo osonkhanira amene’wo, ngakhale ngati njira zonse zoyendera zimene ziripo lero lino zikanaperekedwa kuti azigwiritsire ntchito? Ndithudi chinthu chotero’cho n’chosatheka.

4. Kodi n’chifukwa ninji kusonkhanitsa kotero’ko sikukupanga bvuto kaamba ka Yesu tsopano?

4 Komabe, opita kutali m’lengalenga aumunthu amene anapanga kutera kusanu ndi kumodzi pa mwezi m’zaka zaposachedwapa anali okhoza kuona kutuluka kwa dziko ndi kulowa kwa dziko ali pa mwezi ndipo’nso kuona mpira wonse wa dziko lapansi womazungulira’wo pamene iwo anali kuyenda m’chombo chao chopita kutali m’mlengalenga pakati pa mwezi ndi dziko lapansi. Ha, ndi koposa chotani nanga m’mene Kristu Yesu wauzimu wolemekezedwa’yo angatengerere nkhope ya dziko lonse lapansi ali pa mpando wake wachifumu wokhala pamwamba kwambiri koposa mwezi! Chiyambire pa kukwezedwera kwake ku dzanja lamanja la Atate wake mu 33 C.E., iye nthawi zonse wakhala wokhoza kuchita zimene’zi. Chotero, pamenepa, kodi ndi m’lingaliro lotani m’mene kuliri kuti mitundu yonse ikusonkhanitsidwa pamaso pake chiyambire pa kukhazikitsidwa kwake pa mpando wachifumu kumwamba pa kutha kwa Nthawi za Akunja mu 1914?

5. Kodi ndi motani m’mene mitundu yasonkhanitsidwira pamaso pa Kristu wokhazikitsidwa pa mpando wachifumu’yo?

5 Eya, mkhalidwe wasinthira mitundu’yo chiyambire pamene kubwereka kwao ulamuliro wa dziko popanda chidodometso copangidwa ndi ulamuliro wa Mulungu wa m’chilengedwe chaponseponse kunatha mu 1914. (Luka 21:24; Salmo 110: 1,2) Pamene Yesu Kristu anatembenuzira chisamaliro chake kwa mitundu kuyambira pa nthawi imene’yo kumkabe m’tsogolo, iye anatero monga Mfumu Yaumesiya yomalamulira. (Chibvumbulutso 11:15; 12:10) Iye tsopano akuyang’anizana nayo ndipo akuipenda ponena za mkhalidwe wao ponena za kugonjera ku ulamuliro woyenera Waumesiya. Iyo yonse ikuchitiridwa monga gulu limodzi la ndale za dziko la dziko lonse, monga gulu logwirizana, ndipo yonse pamodzi, iyo ikuyang’anizana naye ndi kuchita naye pa mkangano waukulu kwambiri wa ulamuliro wa dziko. Iyo tsopano iyenera kupanga chosankha pakati pa ulamuliro wa mtundu wa anthu ndi ulamuliro wa m’chilengedwe chonse wa Mulungu wokhala m’manja mwa ufumu wake Waumesiya. Chifukwa cha “ulamuliro wa Kristu wake,” Mwana wa Mulungu wokhazikitsidwa pa mpando wachifumu’yo tsopano wapatsidwa chilolezo cha “kuweta mitundu ndi ndodo yachitsulo” ndi kuiphwanya m’nthawi yake yokwanira. (Chibvumbulutso 12:5; NW; 19:15; Salmo 2:8, 9) Mitundu yoyembekezera kuonongedwa’yo tsopano yasonkhana pamodzi pansi pa gulu la Mitundu Yogwirizana, koma osati kuti igonjere ku ulamuliro wa Kristu.

6. Kodi ndi motani m’mene mitundu yonse yauzidwira ponena za mkhalidwe wao wosinthidwa?

6 Mitundu yonse yauzidwa za kusintha mkhalidwe wao pamaso pa Yehova Mulungu, Woika Nthawi za Akunja kapena “nthawi zoikidwiratu za mitundu.” (Danieli 4:16, 23,25,32; Luka 21: 24) Kodi ziri choncho motani? Mwa kutumiza kwa Yehova “oimira” ake Aufumu ku mitundu, kukalalikira ‘mbiri yabwino imene’yi ya ufumu m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse,’ monga momwe’di Yesu Kristu ananeneratu m’Mateyu 24:14, NW. “Oimira” Aufumu amene’wa ali “osankhidwa” a Mulungu, “abale” auzimu a Yesu Kristu. (2 Akorinto 5:20; Aefeso 6:20; Yohane 20:17; Ahebri 2:11,12) Mwa Mautumiki a woimira amene’wo ndi kulengeza Ufumu ku mitundu yonse, iwo akusonkhanitsidwa pamaso pa Mfumu yodzozedwa ya Mulungu, Yesu Kristu, amene ali ndi ndodo yachifumu yachitsulo. Mboni Zachikristu za Yehova zalowetsa kale uthenga wa Ufumu umene’wo m’maiko okwanira mazana awiri kudza, khumi, ndipo chotulukapo cha chimene’chi, ophunzira a Mfumu Yesu Kristu akupezeka kukhala okangalika m’maiko onse’wo. (Mateyu 28:19, 20) M’njira imene’yi mitundu yonse yasonkhanitsidwa pamodzi pamaso pa mpando wachifumu wa Mfumu yokhazikitsidwa pa mpando wachifumu monga odziwitsidwa, pa malo amodzi, pansi pa thayo lofanana.—Yerekezerani ndi Mateyu 24:31; Yesaya 43:9.

KULEKANITSA OCHIRIKIZA UFUMU NDI OSACHIRIKIZA

7, 8. (a) Kodi Mfumu’yo likugawanitsa mitundu’yo motero molingana ndi kusiyana kwa ndale za dziko? (b) Kodi kulekanitsa’ko kukuchitidwa pa maziko otani?

7 Kodi ndi motani m’mene “Mwana wa munthu” wokhala pa mpando wake wachifumu wakumwamba waulemerero akuchitira ndi mitundu yosonkhanitsidwa motero’yo pamaso pake? M’fanizo lake Yesu Kristu akupitirizabe kuti: “Ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.”—Mateyu 25:31-33.

8 Tiyenera kuona kuti Mfumu Yesu Kristu sakulekanitsa mitundu kukhala magulu awiri, gulu limodzi lolimbana ndi gulu lina m’kusagwirizana kwa ndale za dziko. M’malo mwake, iye akulekanitsa anthu amene amakhala m’mitundu imene’yo, motero kulola munthu ali yense kupanga chosankha chake cha iye mwini mosasamala kanthu za zimene boma la mtundu lom’lamulira limachita. Ntchito ya kulekanitsa imene’yi ikuchitika m’kati mwa “kukhala pafupi” kosaoneka kwa Kristu mu mphamvu Yaufumu ndi ulemerero waukulu. (Mateyu 24:3, 37, 39, 40) Kodi ntchito ya kulekanitsa imene’yi imachitika pa maziko otani? Pa maziko a chichirikizo chao cha ufumu wa Kristu kapena kuukana kwao. Chotero, tsopano, kodi ndi mtundu wotani wa chifuyo umene ukuphiphiritsira ochirikiza Ufumu, ndipo ndi mtundu uti osachirikiza? Tiyeni tione:

9, 10. Kodi onga nkhosa amene akulekanitsidwira ku dzanja lamanja la Mfumu’yo anachita chiani?

9 “Pomwepo Mfumu’yo idzanena kwa iwo a ku dzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi: pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu; ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine; wamariseche Ine, ndipo munandibveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m’nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.”—Mateyu 25:34-36.

10 Motero “nkhosa” zimaphiphiritsira ochirikiza ufumu Waumesiya umene unalinganizidwira anthu onga nkhosa amene’wo kuyambira pa kukhazikitsidwa kwa mtundu wa anthu. Koma popeza kuti Mfumu Yesu Kristu sanakhale wooneka m’thupi m’kati mwa “kukhala pafupi” kwake kwa tsopano’ku m’mphamvu ya Ufumu ndi ulemerero, kodi ndi motani m’mene anthu onga nkhosa amene’wa achitira zinthu zotero’zo kwa iye? Fanizo lake likupitirizabe kuti:

11. Kodi ndi motani m’mene Mfumu’yo ikuyankhira mafunso a “nkhosa”?

11 “Pomwepo olungama adzam’yankha Iye kuti, Ambuye tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani? Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukubvekani? Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m’nyumba yandende, ndipo tinadza kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang’ono-ng’ono awa, munandichitira ichi Ine.”—Mateyu 25:37-40.

12. Kodi “nkhosa” zolungama’zo zachita zinthu zimene’zi motani, ndipo chifukwa ninji?

12 Mwa kunena’ko “abale anga,” Mfumu Yesu Kristu akutanthauza “osankhidwa ake,” awo amene ali “olowa nyumba a Mulungu, koma olowa nyumba limodzi ndi Kristu.” (Mateyu 24:31; Aroma 8:17, NW) Mwa abale auzimu amene’wa, pali chikhalirebe otsalira apang’ono otsala pa dziko lapansi. Onse’wa mwakhama akhala ndi phande m’kukwaniritsa ulosi wa Yesu, wakuti, “Mbiri yabwino imene’yi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse,” pakuti iwo akudziwa “chizindikiro” cha “kukhala pafupi” kosaoneka kwa Kristu kapena parousia chakuti ufumu wa Mulungu uli pafupi pa khomo. Kaamba ka kuchita zimene’zi chiyambire pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914, iwo akhala anthu okhala ndi njala, ludzu, umariseche, kudwala, kusakhala pa nyumba kapena kukhala opanda nyumba, ndipo ngakhale kuikidwa m’ndende chifukwa cha kulalikira chabe “mbiri yabwino imeni’yi ya ufumu.” (Mateyu 24:14, 32, 33, NW; Marko 13:9, 10; Luka 21:29-31) Anthu “olungama” onga nkhosa’wo amathandiza “abale” auzimu a Kristu chifukwa chakuti iwo amayanja Ufumu umene “oimira” Achikristu amene’wa akuulalikira kwa iwo. Iwo amatamanda ufumu umene’wo monga ulamuliro woyenera kaamba ka mtundu wonse wa anthu.

13, 14. (a) Kodi “nkhosa” zimene’zi zakhala ngati osakhala Ayuda ati m’nthawi ya Mkazi wa Mfumu Estere? (b) Kodi iwo akukhala ophunzira a Mfumu, motani?

13 Iwo modziwa amapereka chithandizo kaamba ka kupititsidwa patsogolo kwa kulengezedwa kwa ufumu, chifukwa chakuti iwo amapempherera boma la dziko limene’lo ndipo amalibvomereza. Ndicho chifukwa chake chithandizo chao kwa “abale” ake auzimu chiri chowerengeredwa kwambiri ndi Mfumu Yesu Kristu. Iwo kale-kale anaphiphiritsiridwa ndi osakhala Ayuda amene anathandiza Ayuda okhala pa upandu’wo m’nthawi ya mkazi wa Mfumu Estere ndi Nduna Yaikulu Moredekai m’kati mwa kulamulira kwa Ahasuwero, mfumu ya Perisiya.—Estere 8:17; 9:3.

14 Chifukwa cha chimene’cho, kwa amene’wa lonjezo la Mfumu likugwira ntchito: “Munthu ali yense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m’dzina langa chifukwa muli ake a Kristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake.” (Marko 9:41) Chotero tsopano opereka chitonthozo olungama onga nkhosa’wo akupatsidwa mfupo ya kukhala ndi mwai wa kugwirizana ndi otsalira a “abale” a Kristu m’kulalikira “mbiri yabwino imene’yi ya ufumu” pa dziko lonse ndi kugwirizana ndi otsalira m’mabvuto ao kaamba ka njira imene’yi. Kweni-kweni iwo akukhala “ophunzira” a Kristu Mfumu, akumadzipereka kwa Atate wakumwamba wa Mfumu’yo, Yehova Mulungu, ndi kubatizidwa m’madzi mochitira chzindikiro kudzipereka kotero’ko.—Mateyu 28:19, 20.

15. Kodi “nkhosa” zikudalitsidwa ndi gawo lotani la utumiki?

15 Chifukwa cha kachitidwe ka kudzipereka kamene’ka, anthu olungama onga nkhosa’wo akupangidwa kukhala amithenga a ufumu wa Mulungu Waumesiya, opatsidwa mokwanira ntchito ya kulalikira boma la dziko lateokratiki limene’li kwa anthu a mafuko onse, mitundu, maonekedwe a khungu ndi zinenero. Ndithudi iwo amakhala awo “odalitsika a Atate [wa Kristu].”

16. Kodi ndi motani m’mene “nkhosa” zikulowera Ufumu wolinganizidwa kale-kale?

16 Kaamba ka kukhulupirika kwao ku ulamuliro wa m’chilengedwe chonse wa Atate wa Mfumu’yo iwo adzafupidwa—osati ndi cholowa mu ufumu wakumwamba limodzi ndi Yesu Kristu ndi “abale” ake auzimu—koma ndi cholowa m’malo a pa dziko lapansi olamulidwa ndi ufumu Waumesiya. Liu’lo “ufumu” kawiri-kawiri limagwiritsiridwa ntchito kutanthauza chigawo pa chimene ufumu umalamulirapo. Chigawo cha Ufumu chimene’chi chidzakhala Paradaiso wa pa dziko lapansi za amene Yesu Kristu ananena zoposa zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo, atangotsala pang’ono kufera pa mtengo wozunzirapo, pamene iye anati kwa womvera chisoni womafa, “Zoondai ndinena ndi iwe lero lino [Tsiku la Paskha, 33 C.E.], Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43, NW) Koma pamene Mulungu anathamangitsa Adamu ndi Hava m’paradaiso wa Edene, iye anali kulingalira Paradaiso wobwezeretsedwa amene’yu, malinga ndi zimene iye ananena m’Genesis 3:15, ndipo pamenepo panali pa “kukhazikitsidwa kwa dziko.”—Mateyu 25:34.

OSACHIRIKIZA BOMA LA DZIKO LIKUDZA’LO

17, 18. Kodi ndi chiweruzo chotani chimene chikuperekedwa pa “mbuzi,” ndipo chifukwa ninji?

17 Mosemphana ndi chiitano cha Mfumu cha “kulowa ufumu [chigawo cholamulidwa] wokonzedwera kwa [nkhosa zolungama] kuyambira pa chikhazikiro chake cha dziko,” pali chiweruzo choperekedwa pa “mbuzi” zophiphiritsira za fanizo’lo. Ponena za amene’wa fanizo’lo likupitirizabe kunena kuti:

18 Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a ku dzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, ku moto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi amithenga ake: pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa Ine: ndinali mlendo, ndipo simunandilandira Ine; wamaliseche ndipo simunandibveka Ine; wodwala, ndi m’nyumba yandende, ndipo simunadza kundiona Ine. Pomwepo iwo’nso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamariseche, kapena m’nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu? Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang’ono-ng’ono, munalibe kundichitira ichi Ine.”—Mateyu 25:41-45.

19. Kodi Mfumu ikulingalira mkhalidwe wao kukhala kunyalanyaza kosadziwa?

19 Panopo tingafunse kuti, Kodi Mfumu’yo imalingalira nkhani’yi kukhala cholakwa chadala chabe cha kagulu ka “mbuzi”? Kodi iye amaona mkhalidwe wao kukhala ukusonyeza kunyalanyaza kwao kosadziwa chabe? Ndithudi ai, pamene tiona kuti iye akucha onyalanyaza amene’wa kukhala “otembereredwa” ndipo akuwalamula kumka ku “moto wosatha wokolezedwera Mdierekezi ndi angelo ake.” Mfumu’yo iyenera kuwawerengera kapena kuwaweruza kukhala oipa, malinga ndi kunena kwa lamulo Lamalemba: “Temberero la Yehova liri pa nyumba ya woipa, koma malo okhala a anthu olungama iye amawadalitsa.” (Miyambo 3:33, NW) Koma kodi n’chifukwa ninji kagulu ka “mbuzi” kayenera kutembereredwa chifukwa cha kulephera chabe kuthandiza ndi kutonthoza “abale” a Kristu?

20, 21. Ngati sanadziwe lamulo lochitira zinthu liri lonse, kodi n’chiani chimene “nkhosa” ndi “mbuzi” zinadziwa?

20 Ngati tinena kuti “mbuzi” zophiphiritsira’zo zinali “zotembereredwa” ndi zoweruzidwira ku chionongeko limodzi ndi Mdierekezi ndi angelo ake kaamba ka kunyalanyaza kosadziwa chabe “abale” a Kristu, pamenepo, moyenerera, tiyenera kunena kuti “nkhosa” zophiphiritsira’zo zinadalitsidwa ndi kufupidwa ndi malo m’chigawo cholamulidwa ndi Ufumu’wo kaamba ka kuchitira zabwino mosadziwa chabe “abale” a Kristu. Pamenepo, kodi ndi kuyenera kotani kumene kukakhalapo m’zabwino zimene “nkhosa” zinachitira “abale” a Kristu? Kapena kodi ndi kusayenera kotani kumene m’kunyalanyaza kumene “mbuzi” sizinazindikire kuti zinali kuchita? Nangano, chilungamo chiri kuti, m’kufupa kagulu kamodzi kosazindikira ndi kulanga kagulu kena kosazindikira? Chilungamo mwachionekere palibe kuli konse m’kachitidwe kotero’ko.

21 Tiyeni tibvomereze kuti magulu onse’wo anali osadziwa lamulo lakuti zimene iwo anachitira kapena sanachitire “abale” auzimu a Kristu iwo anazichitira kapena sanazichitire Kristu iye mwini. Ngakhale ziri choncho, iwo sanali osazindikira cheni-cheni chakuti iwo anali kuchita ndi “abale” ake! Kulekeranji kutero?

22. Kodi “abale” a Kristu anayenera kulalikira kwa yani? Limodzi ndi kulabadira kotani?

22 Tiyenera kugwirizanitsa fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi ndi zimene iye ananena poyambirira mu ulosi wake wonena za “chizindikiro cha kukhala pafupi [kwake] ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu.” (Mateyu 24:3, NW) Iye ananena za ntchito zobvomerezeka kaamba ka “abale” ake auzimu pamene, pa Mateyu 24:14, NW, anawauza kuti: “Mbiri yabwino imene’yi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse.” Osati ku mitundu yochedwa Yachikristu yokha kapena ku Chikristu cha Dziko, koma ku “mitundu yonse” “m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.” Komabe Yesu anauza’nso “abale” ake auzimu kuti: “Pamenepo anthu adzakuperekani ku chisautso ndipo adzakuphani, ndipo mudzakhala anthu odedwa ndi mitundu yonse chifukwa cha dzina langa.”—Mateyu 24:9, NW

23. Kodi kusazindikiridwa kumatsimikizira “abale” a Kristu kusakhala otero?

23 Kudedwa chifukwa cha dzina lake kumatanthauza kuti “abale” a Kristu akadzisonyeza ndi kulalikira kwao “mbiri yabwino ya ufumu” pa dziko lonse ndi mwa kumapanga kwao ophunzira, ake akumawabatiza. (Mateyu 28:19,20) Anthu onse, kapena maboma autundu amene anthu amene’wa amachirikiza amakana kubvomereza kuti olalikira “mbiri yabwino” amene’wa ali “abale” auzimu a Kristu. Koma kodi zimene’zi zimasonyeza kweni-kweni kuti iwo sali kweni-kweni “abale” auzimu a Kristu? Ai!

24. Kodi ndi liti pamene kunyalanyazidwa kwa “abale” a Kristu kumakhala kosowetsa chowiringula?

24 Kukana kwa anthu onse kuzindikira “abale” auzimu a Kristu kuti sali otero, ndi kudedwa kumene’ku kwa m’mitundu yonse chifukwa cha zimene iwo akulalikira ponena za Ufumu kwasonkhezera anthu m’kuwachitira kwao. Kumene mtundu uli ndi Lamulo la Zoyenera lomatetezera ufulu wa kulambira, anthu sangagwirizane nawo m’kuzunza mwachiwawa “abale” a Kristu. Koma chifukwa cha kuopa lingaliro la anthu kapena chifukwa cha kugwirizana nacho, osakhala ndi phande otero’wo ku chizunzo’cho mwadala amakana kuthandiza, kutonthoza kapena kuchirikiza “abale” a Kristu. Chotero mkhalidwe wao wamphwayi, kunyalanyaza kwao, n’kopanda chifukwa chowiringulira.—Miyambo 29:18.

25. Kodi n’chifukwa ninji sipangakhale mphwayi pa nkhani’yo popanda chilango?

25 Fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi limalowetsamo zinthu zonse’zi pamodzi. Kulephera kuthandiza ndi kutonthoza “abale” a Kristu kumayendera limodzi ndi kulephera kuthandiza ndi kuchirikiza ufumu wa Kristu, boma la dziko likudza’lo. Imene’yi ndi nkhani yofunika kwambiri, palibe malo a pakati ndi pakati, palibe kulolera molakwa, palibe kutenga mbali zonse ziwiri, ponena za nkhani ya boma la dziko. Yesu Kristu Mfumu’yo amada kukhala wofunda. (Chibvumbulutso 3:16) Yesu anati’nso: “Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza-mwaza.” (Mateyu 12:30; Luka 11:23) Ponena za zimene’zi palibe chisalungamo kwa Yesu m’kulengeza kuti osachirikiza onga mbuzi’wo a “mpando wake wachifumu” kapena ufumu ali “otembereredwa” ndi oyenera kulangidwa limodzi ndi Mdierekezi ndi angelo ake. Dzina’lo “Mdierekezi” limatanthauza “Woneneza,” ndipo “mbuzi” zimene’zi zikuikidwa m’gulu limodzi ndi Mdierekezi Wamkulu chifukwa chakuti izo zimamvetsera zoneneza za Mdierekezi ndi angelo ake ndipo ali oipidwa ndi “abale” a Kristu. (Chibvumbulutso 12:10) Izo ziyenera kugawana naye tsoka lake.

26. Kodi ndi liti pamene Mfumu’yo idzauza “mbuzi” kumka ku “moto”?

26 Pamenepo, tiyeni, tisakhale ndi liwongo la kupanga zowiringula kaamba ka “mbuzi” ndipo motero kukaikira chiweruzo cholungama cha Kristu Mfumu’yo. Mosasamala kanthu zakuti kaya ali yense akukonda lingaliro lake kapena ai, fanizo la Yesu likumaliza ponena za chiweruzo choperekedwa pa “mbuzi” zokhala ndi liwongo’zo ndi “nkhosa’ zolungama’zo, kuti: “Ndipo amene’wa adzachoka kumka [mbuzi zophiphiritsira] ku chilango cha nthawi zonse, koma olungama ku moyo wa nthawi zonse.” (Mateyu 25:46) Kodi ndi liti pamene Kristu Mfumu’yo adzauza “mbuzi” zotembereredwa’zo kumka ku “moto” wophiphiritsira, “kudulidwa” (Chigriki: ko’la-sis)? Kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu kutachitidwa pa dziko lonse lapansi ndi “abale” ake auzimu ndipo “mapeto” akudza pa dongosolo iri la zinthu limene tsopano liri ‘m’mapeto’ ake. (Mateyu 24:3, 14, NW) Pamenepo “chisautso chachikulu” chidzaulika pa dziko lonse, koma “mbuzi” sizidzapulumuka konse.—Mateyu 24:21,22.

27. Kodi “mbuzi” zikudulidwa” ku chiani, kwa utali wotani?

27 “Kudulidwa” kosatha (ko’la-sis) kwa “mbuzi” kuli kosemphana ndi “moyo wosatha” umene “nkhosa” zikufupidwa nawo. Chiri chilango chosatha, chifukwa chakuti mpangidwe umene’wu wa chilango sudzachotsedwa pa “mbuzi” zimene’zi zimene zikuphedwa mu “chisautso chachikulu.” Izo sizidzakhala ndi chiukiriro kuchokera kwa akufa. Izo zikukumana ndi imfa ina’yo imene Baibulo limainena, “imfa yachiwiri,” imene ikuphiphiritsiridwa ndi “nyanja ya moto.” Izo sizidzamasulidwa’nso ku “nyanja ya moto” yophiphiritsira imene’yi monga momwe Satana Mdierekezi ndi ziwanda zake sadzamasulidwira. (Chibvumbulutso 20:10-15; Genesis 3:15) Izo zidzaonongeka mu “chisautso chachikulu” chimene chidzafika pa kuwirima mu “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Harmagedo.—Chibvumbulutso 16:14, 16, NW; 19:11-21.

“OPULUMUKA CHISAUTSO CHACHIKULU”

28, 29. Kodi “nkhosa” zikupulumuka chiani, monga momwe kwasonyezedwera m’Chibvumbulutso 7:13-15?

28 Sitikudera nako nkhawa ‘kudulidwa kosatha’ limodzi ndi “mbuzi” mu “chisautso chachikulu” chikudza’cho, eti? Ai ngati tikufuna kusangalala ndi boma la dziko likudza’lo la Yehova Mulungu lokhala m’manja mwa Mwana wake Yesu Kristu. Chosankha chathu chanzeru ndi cholemekeza Mulungu chikakhala cha kudzitsimikizira tsopano kukhala ngati “nkhosa” zodalitsidwa. Kagulu kopangidwa ndi “nkhosa” zophiphiritsira kadzapyola kamoyo “chisautso chachikulu.” Kupulumuka kumene’ku kudzachititsa kumka kwao ku “moyo wosatha” pansi pa boma la dziko likudza’lo. Padzakhala “khamu lalikulu” losawerengeka la opulumuka onga nkhosa a “chisautso chachikulu” otero’wo. Tiri ndi chitsimikiziritso cha chimene’chi monga momwe kukulongosoledwera m’kukambitsirana kwa pakati pa “mkulu” wapadera ndi mmodzi wa “abale” a Kristu, mtumwi Yohane. Ponena za kukambitsirana kumene’ku timawerenga kuti:

29 Ndipo mmodzi wa akulu anayankha, nanena ndi ine, Iwo obvala zobvala zoyera ndiwo ayani, ndipo achokera kuti? Ndipo ndinati kwa iye Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zobvala zao, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa. Chifukwa chake ali ku mpando wachifumu wa Mulungu; ndipo am’tumikira Iye usana ndi usiku m’Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi.”—Chibvumbulutso 7:13-15.

30. Kodi iwo akupulumuka pansi pa chitetezo chotani, kuti akaimirire pamaso pa yani?

30 Mulungu akufutukula “chihema” chake cha chitetezo pa anthu obvala miinjiro yoyera amene’wa. Zimene’zi zikusonyeza m’mene kuliri kuti, kuphatikiza pa otsalira a “abale” auzimu a Kristu kwa amene iwo akhala akuchitira zabwino, iwo ndiwo okha ochokera pakati pa chiwerengero cha anthu cha dziko lapansi pa nthawi’yo amene “akutuluka m’chisautso chachikulu.” M’kati mwa “chisautso chachikulu” chimene’cho mipando yachifumu yonse ya olamulira a mitundu idzakhala itagubuduzidwa ndi kuonongedwa. (Hagai 2:22) Ndicho chifukwa chake palibe mpando wachifumu wina uli wonse umene ukunenedwa m’masomphenya amene’wa a mtumwi Yohane koma “mpando wachifumu wa Mulungu.” (Chibvumbulutso 7:10-15) Palibe wina ali yense amene akuonedwa atakhala pa mpando wachifumu koma Mulungu. Malo ake a ntchito monga Wolamulira wa chilengedwe chonse, kuphatikizapo dziko lathu lapansi’li, akuchirikizidwa!

31. Kodi ndi kachitidwe kotani, kosasonyezedwa m’fanizo la Yesu, kamene iwo akalandira?

31 Masomphenya amene’wa akusonyeza kuti opulumuka obvala miinjiro yoyera a “chisautso chachikulu” amene’wa achita zochuluka zoposa zimene zikusonyezedwa m’fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi. Iwo “anatsuka zobvala zao, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” Cheni-cheni chofotokozedwa chimene’chi chikugogomezera kuti iwo ali okhulupirira mwanawankhosa wa Mulungu, Yesu Kristu, ndipo alandira nsembe yake yotetezera machimo, mwazi wake wokhetsedwa. Chimene’chi ndi chimodzi cha zinthu zimene zimawasonkhezera kuthandiza, kutonthoza, ndi kugwira ntchito limodzi ndi “abale” auzimu a Mwanawankhosa. Koposa zonse, iwo ayang’ana kwa Atate wakumwamba wa Mwanawankhosa, Wolamulira wa Chilengedwe Chonse kaamba ka chipulumutso kutuluka “m’chisautso chachikulu.”

32. Kodi ndi motani m’mene iwo amakwaniritsira chofunika chachikulu cha chipulumutso chotero’cho?

32 “Khamu lalikulu” limasonyeza kuti iro limakwaniritsa zofunika zazikulu kaamba ka chipulumutso chimene’cho mwa lingaliro limene iwo amakhala nalo kulinga ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi zimene iwo amabvomereza poyera pamaso pake. Cheni-cheni chimene’chi chikukhala choonekera bwino kwa ife pamene tikuwerenga kuti: “Zitatha izi [kutatha kusindikizidwa chizindikiro kwa Aisrayeli auzimu 144,000, abale auzimu a Mwanawankhosa] ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uli wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atabvala zobvala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwao; ndipo apfuula ndi mau akulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.”—Chibvumbulutso 7:9,10.

33. Kodi ndi kubvomereza kotani kumene iwo amapanga kwa Mulungu ndi Mwana wake? Motani?

33 Litabvala zobvala zoyenera, “khamu lalikulu” limene’li, limene liribe Aisrayeli auzimu ali onse, likuima mwaulemu pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu, likumam’zindikira kukhala Wolamulira wa Dziko. (Chibvumbulutso 11:15) Monga ngati ndi makhwatha a kanjedza, iwo mogwirizana akum’tamanda monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, Uyo woyenerera kukhala pa mpando wachifumu wokhala ndi ulamuliro wa chilengedwe chonse. (Yerekezerani ndi Yohane 12:12, 13.) Iwo amazindikira’nso “Mkulu wa moyo” amene Yehova Mulungu wam’gwiritsira ntchito “Mwanawankhosa,” Yesu Kristu Mwana wake. (Machitidwe 3:15; Yohane 1:29, 36) Chotero iwo mosangalala akubvomereza pamaso pa kumwamba ndi dziko lapansi Magwero a chipulumutso chao kutuluka mu “chisautso chachikulu” ndipo’nso Woimira wake Wamkulu kaamba ka chimene’cho.

34. Kodi ndi kuyambira liti, kweni-kweni, pamene pakhala kusonkhanitsidwa kwao?

34 M’kati wa “mapeto a dongosolo la zinthu” ano, maka-maka chiyambire 1935 C.E., “khamu lalikulu” limene’li lasonkhanitsidwa ndi kugwirizanitsidwa mosasamala kanthu za mtundu, pfuko ndi anthu m’mene atengedwamo. Iwo amva kulalikidwa kwa pa dziko lonse kwa “mbiri yabwino imene’yi ya ufumu.” Polabadira chidziwitso cha pa nthawi yake chofalitsidwa pa tsamba 250 (ndime 34) la Nsanja ya Olonda (Yachingelezi) ya August 15, 1934, iwo anapiritizabe kudzipereka kwa Yehova Mulungu kupyolera mwa Mwanawankhosa wake Yesu Kristu. Kudzipereka kwao anakuchitira chizindikiro ndi ubatizo wa m’madzi. Iwo agwirizana ndi otsalira a “abale” auzimu a Kristu m’kulalikira “mbiri yabwino” kufikira ku malekezero a dziko lapansi. Ha, ndi kokondweretsa chotani nanga m’makutu athu kumva iwo akutamanda boma la dziko la Yehova likudza’lo!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena