Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 114 tsamba 264-tsamba 265 ndime 4
  • Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Pamene Kristu Adza Mumphamvu ya Ufumu
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Nkhosazo ndi Mbuzizo Zili ndi Mtsogolo Motani?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Tizithandiza Abale a Khristu Mokhulupirika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • “Khamu Lalikulu” Litamanda Boma la Dziko Likudza’lo
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 114 tsamba 264-tsamba 265 ndime 4
Anthu amitundu yonse akuyang’ana kumwamba kudikira kuti Yesu awaweruze

MUTU 114

Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi

MATEYU 25:31-46

  • YESU ANANENA FANIZO LA NKHOSA NDI MBUZI

Yesu ali paphiri la Maolivi ananena fanizo la anamwali 10 komanso la ndalama za matalente. Pomaliza kuyankha funso la atumwi ake lokhudza chizindikiro cha kukhalapo kwake komanso chizindikiro chakuti dziko la Satanali latsala pang’ono kutha, Yesu ananenanso fanizo lina. Fanizoli limanena za nkhosa ndi mbuzi.

Yesu anayamba kufotokoza zimene zinachitika m’fanizoli kuti: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero.” (Mateyu 25:31) Pamene ankanena fanizoli, Yesu anasonyezeratu kuti ankanena za iyeyo chifukwa nthawi zambiri ankadzitchula kuti “Mwana wa munthu.”—Mateyu 8:20; 9:6; 20:18, 28.

Yesu wakhala pampando wake wa ulemelero ndipo akuweruza anthu okhulupirika omwe ali ngati nkhosa

Kodi fanizo limeneli lidzakwaniritsidwa liti? Lidzakwaniritsidwa Yesu “akadzafika mu ulemerero wake” limodzi ndi angelo n’kukhala “pampando wake wachifumu waulemerero.” M’mbuyomo Yesu anali atanenapo kale kuti “Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu” pamodzi ndi angelo ake. Kodi zimenezi zidzachitika liti? Zidzachitika “chisautso chikadzangotha.” (Mateyu 24:29-31; Maliko 13:26, 27; Luka 21:27) Choncho fanizoli lidzakwaniritsidwa Yesu akadzabwera mu ulemerero wake m’tsogolo. Kodi adzachita chiyani pa nthawi imeneyo?

Yesu ananena kuti: “Mwana wa munthu akadzafika. . . , mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye ndipo adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Adzaika nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi adzaziika kumanzere kwake.”—Mateyu 25:31-33.

Ponena za nkhosa zomwe zidzakhale kudzanja lake lamanja Yesu ananena kuti: “Pamenepo mfumu idzauza a kudzanja lake lamanja kuti, ‘Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Lowani mu ufumu umene anakonzera inu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.” (Mateyu 25:34) N’chifukwa chiyani Mfumuyi inakonda nkhosa?

Mfumuyo inanena kuti: “Ine ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya. Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino. Ndinali wamaliseche koma inu munandiveka. Ndinadwala koma inu munandisamalira. Ndinali m’ndende koma inu munabwera kudzandiona.” Ndiyeno anthu ‘olungama’ omwe ndi nkhosazo anafunsa mmene anachitira zinthu zimenezo. Mfumu inayankha kuti: “Pa mlingo umene munachitira zimenezo mmodzi wa abale anga aang’ono awa, munachitira ine amene.” (Mateyu 25:35, 36, 40, 46) Mosakayikira anthuwa sanachite zinthu zabwino zimenezi ali kumwamba chifukwa kumwamba kulibe anthu odwala kapena anjala. Choncho zimenezi ziyenera kukhala zinthu zimene anachitira abale ake a Khristu padziko lapansi.

Gulu la anthu osakhulupirika likuweruzidwa kuti ndi mbuzi

Nanga n’chiyani chimene chinachitikira mbuzi zomwe zinaikidwa ku dzanja lake la manzere? Yesu anafotokoza kuti: “Kenako [Mfumu] adzauza a kumanzere kwake kuti, ‘Chokani pamaso panga inu otembereredwa. Pitani kumoto wosatha wokolezedwera Mdyerekezi ndi angelo ake. Pakuti ndinamva njala koma inu simunandipatse chakudya. Ndinamva ludzu koma inu simunandipatse chakumwa. Ndinali mlendo koma inu simunandilandire bwino. Ndinali wamaliseche koma inu simunandiveke. Ndinadwala komanso ndinali m’ndende, koma inu simunandisamalire.’” (Mateyu 25:41-43) Mpake kuti mbuzi zidzalandira chiweruzo chimenechi chifukwa cholephera kusonyeza chifundo kwa abale ake a Khristu pa nthawi imene anali padziko lapansi.

Atumwi anazindikira kuti chiweruzo chimene chidzaperekedwe m’tsogolo sichidzasintha mpaka kalekale. Yesu anawauza kuti: “Pamenepo [Mfumu] adzawayankha kuti, ‘Ndithu ndikukuuzani, Popeza simunachitire zimenezo mmodzi wa aang’ono awa, simunachitirenso ine.’ Ndipo iwowa adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu, koma olungama ku moyo wosatha.”—Mateyu 25:45, 46.

Zimene Yesu ananena poyankha funso la atumwi, zimathandiza kwambiri otsatira ake kuganizira za khalidwe lawo komanso zochita zawo.

  • Kodi m’fanizo la Yesu lonena za nkhosa ndi mbuzi, ndani amene akuimira “Mfumu,” ndipo fanizoli lidzakwaniritsidwa liti?

  • N’chifukwa chiyani Yesu adzaweruze kuti nkhosa zidzapeze moyo wosatha?

  • N’chifukwa chiyani anthu ena adzaweruzidwe kuti ndi mbuzi? Ndipo kodi nkhosa ndi mbuzi zidzakhala ndi tsogolo lotani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena