Mutu 16
Kodi Inu Mwininu Mudzachitanji?
CHOSANKHA cha kutumikira Yehova sichinthu chimene munthu wina aliyense angakupangireni. Ngati mnzanu wa mu ukwati ali mtumiki wokhulupirika wa Yehova, limenelo lingakhale dalitso lamtengo wapatali. Mofananamo, ngati makolo anu amakonda Yehova, muli mu mkhalidwe wachiyanjo. Mikhalidwe yapanyumba yoteroyo ingapereke chisonkhezero chachikulu kulinga ku kugwirizana ndi awo amene amalambira Yehova “mu mzimu ndi chowonadi.” (Yohane 4:23, 24) Koma m’kupita kwa nthaŵi inu muyenera kupanga chosankha chanu. Kodi mumakondadi Yehova ndipo mumafuna kukhala mmodzi wa atumiki ake? Kodi mumafunadi kukhala m’dziko limene mudzakhala chilungamo?
2 Ngati ndinu kholo, ndithudi mukufuna ana anu kuti alandire madalitso a moyo wamuyaya mu Ufumu wa Mulungu. Simungalamulire zimene adzachita pamene asinkhuka mokwanira kusonyeza njira yawo m’moyo. Koma zimene inumwini mukuchita ndi kulambira kowona zingachititse chisonkhezero champhamvu—kaya chabwino kapena choipa. Ngati inu mukanati muleke kutumikira Yehova, kumeneko kukanamanitsa ana anu chimene chikanakhala mwaŵi wawo wabwino koposa wa kuyamba kuyenda panjira ya kumoyo wamuyaya. Kapena ngati mukanapanga kudzipatulira kwa Mulungu ndiyeno nkugwa mphwayi ponena za kukukwaniritsa, kumeneku kungachititse tsoka lauzimu kwa banja lonse, limodzi ndi kutayika kwa chirichonse m’chisautso chachikulu. Koma ngati munapereka chitsanzo cha kukhulupirika, ngati inumwininu muthandiza ana anu kuphunzira Mawu a Mulungu, ngati mukulitsa mwa inumwini ndi mwa iwo kukonda Yehova ndikulemekeza gulu lake lowoneka, ngati muwathandiza kuzindikira mmene aliri otetezereka mwa kuchita chifuniro cha Mulungu, ngati muwasonyeza mmene agapezere chisangalalo mu utumiki wopatulika, pamenepo mukuwapatsa chiyambi chabwino kwambiri pamsewu wakumoyo. Zimenezi nzotheka kokha ndi dalitso la Yehova. (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 1:5.) Lipempheni mosalekeza. Kuyesayesa kwambiri kukufunikanso kwa inu. Koma chotulukapo chidzakhala choyenerera chotani nanga!
3 Mwinamwake mkhalidwe umene umayang’anizana nanu ngwakuti ziŵalo zina za banja lanu ziribe chikondi cha pa Yehova chimene inu muli nacho. Kodi izo zimayesa kukulefulani kuti “musadzigwirizanitse”? Kapena kodi pali chitsutso chotsimikizirika? Kodi mukanachitanji kuti muwathandize kukhala ndi chisangalalo chanu m’kuzindikira chifuno cha Mulungu? Kaŵirikaŵiri zopinga zingagonjetsedwe mwa kuitanira ziŵalo za banja kutsagana nanu ku Nyumba Yaufumu kuti akadziwonere okha zimene zimachitika kumeneko. Muli kumeneko, iwo angalankhule ndi mmodzi wa akulu kuti athetse mafunso amene ali nawo ponena za zikhulupiriro ndi ntchito za Mboni za Yehova. Koma bwanji ngati chitsutsocho chipitirira? Pamenepo mufunikira kudzifunsa: ‘Kodi ndimakondadi Yehova ndi Mwana wake Yesu Kristu ndipo kodi ndiri woyamikira mokwanira kaamba ka zinthu zonse zimene iwo atichitira kotero kuti ndikufunitsitsa kupirira mavutowo kuti ndisonyeze chikondi changa ndi chiyamikiro? Kodi ndimakonda banja langa lenileni kwambiri kuti ndipereke chitsanzo choyenera kotero kuti, ngati nkotheka, nawonso angathandizidwe kugwiritsitsa makonzedwe a Mulungu a moyo wamuyaya?’—Mateyu 10:36-38; 1 Akorinto 7:12, 13, 16.
CHIZINDIKIRO CHIMENE MITUNDU IKUTEMBENUKIRAKO
4 Tsopano mwaŵi ukuperekedwa kwa anthu kulikonse kuti asonyeza kukonda kwawo Yehova mwa kudzigwirizanitsa ndi Ufumu wake Waumesiya. Boma limenelo ndilo njira mwa imene dzina la Yehova lidzayeretsedwa. Lingaliro lathu ku Ufumu limapereka umboni wa mmene timalingalirira ponena za Yehova mwiniyo.
5 Yehova anauzira mneneri Yesaya kulemba kuti: “Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Jese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu: ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.” (Yesaya 11:10) “Muzu wa Jese” umenewo ndiye Ambuye Yesu Kristu wolemekezedwayo. Pamene anayamba kugwiritsira ntchito ulamuliro waufumu, monga “muzu” wopereka moyo anapereka nyonga yatsopano ku mzera wa mafumu Aumesiya amene anachokera mwa Jese kudzera mwa mwana wake Mfumu Davide. (Chivumbulutso 5:5; 22:16) Kuyambira 1914 iye wakhala ‘akuimira monga chizindikiro cha anthu,’ posonkhanira anthu amene akufuna boma lolungama. Yehova mwiniyo wamdzutsa monga Chizindikiro chimenecho, Mfumu Yaumesiya yeniyeni.—Yesaya 11:12.
6 Koma kodi ndimotani mmene anthu padziko lapansi pano angasonkhanire mozungulira Mfumu yakumwamba? Iwo afunikira kupatsidwa chidziŵitso kuchokera m’Baibulo kotero kuti amuwone ndi maso a kuzindikira. Motsogozedwa ndi mzimu woyera, otsalira a Israyeli wauzimu akhala akuchita ntchitoyi mwamphamvu, kulengeza mbiri yabwino ya Ufumu Waumesiya wokhazikitsidwa wa Mulungu padziko lonse lapansi. Anthu osiyanasiyana a m’mitundu yonse amvetsera moyamikira. Iwo afunsira ponena za zofuna za Mulungu kwa iwo kuti akhale nzika za Ufumuwo. Akumakhala ndi umuyaya wa moyo padziko lapansi Laparadaiso. Mokhutira ndi mayankho operekedwa kuchokera m’Baibulo, iwo achita mogwirizana ndi amenewa ndipo aimira ku mbali ya Ufumu Waumesiya wa Yehova. Kodi inu mwachita zimenezo?
‘ADZAMVA KOMA OSACHITA’
7 Chifukwa cha ntchito yachangu ya Mboni za Yehova, izo zimakhala nkhani yokambiritsirana ya kaŵirikaŵiri pakati pa anthu. Koma kodi anthu amenewa amalingalira motani ponena za uthenga umene Mboni za Yehova zimalengeza? Kachitidwe ka ambiri nkonga kaja ka andende anzake a mneneri Ezekieli m’Baibulo. Ponena za iwo, Yehova anati: “Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, ana a anthu amtundu wako anena kuti, Tiyeni tikamve mawu ofuma kwa Yehova. Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mawu ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pawo anena mwachikondi, koma mtima wawo utsata phindu lawo. Ndipo tawona, akuyesa iwe ngati nyimbo yachikondi ya woimba bwino, woimba limba bwino; pakuti akumva mawu ako, koma osachita. Ndipo pakuchitika ichi, pakuti chifikadi, pamenepo adzadziŵa kuti panali mneneri pakati pawo.”—Ezekieli 33:30-33.
8 Pali anthu ambiri amene amakhumbira Mboni za Yehova ndi amene amakonda mabukhu awo ofotokoza Baibulo. Iwo angavomerezedi lingaliro la phunziro Labaibulo lapanyumba laulere. Ena amafika ndi mabwenzi awo kumisonkhano yapadera yochitidwa ndi Mboni. Mwachitsanzo, pa Chikumbutso cha chaka ndi chaka cha imfa ya Yesu Kristu, sikwachilendo kuti chiŵerengero cha ofikapo chikhale choŵirikiza chiŵerengero cha mboni za Yehova zokangalika. M’maiko ena, chiŵerengero chimakwera kuŵirikiza kasanu chiŵerengero cha Mboni. Koma kodi iwo adzachitanji ndi chowonadi cha Baibulo chimene amamva. Oposa mamiliyoni atatu achilabadira mwachindunji ndipo agwirizanitsa nacho miyoyo yawo. Koma ena amachiwona monga ngati kuti chinali ngati nyimbo yokondweretsa, kanthu kena kowasangalatsa. Iwo amakhala pambali, mwinamwake akumapereka mawu olimbikitsa koma osapatulira miyoyo yawo kwa Mulungu ndi kusaloŵa mu utumuki wake wopatulika.
9 Kodi nchiyani chimene chingapindulidwe mwa kukaikira ndi kuyembekezera? Ndithudi osati chiyanjo cha Yehova ndi chitetezero mkati mwa tsiku lolipsira lirinkudza. Kuti mukhale pakati pa opulumuka, muyenera kupereka umboni wokhutiritsa tsopano wakuti ‘mwadzigwirizanitsa kwa Yehova’ ndi kuti muli wake.—Zekariya 2:11; Mateyu 7:21.
ANAPANGA CHOSANKHA CHABWINO
10 Onse amene akhala olambira Yehova monga otsatira Yesu Kristu apanga chosankha chawochawo kutero. Izi ziri choncho ndi onse amene ali oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba. Tsopano mwaŵi wamtengo wapatali ngwotsegukira ena kuti apange chosankha chawo, ndi chiyembekezo cha kupulumuka chisautso chachikulu ndi kukhala mu ungwiro padziko lapansi. Hobabu anapereka chitsanzo chimene iwo ayenera kutsanzira.
11 Hobabu anali mlamu wa Mose. Iye sanali Mwisrayeli koma anali chiŵalo cha fuko la Akeni okhala m’dera la Amidyani. Aisrayeli atatha kulandira Chilamulo kudzera mwa Mose ndipo atatha kumanga chihema chopatulika cholambirira Yehova, nthaŵi inafika yosinthira kumpoto cha ku Dziko Lolonjezedwa. Mtambo njo woimira kukhalapo kwa Yehova unayenera kupita patsogolo pawo, ukumasonyeza njira yooti atsatire ndi malo omangapo msasa. Koma kukakhala kothandiza kukhala ndi munthu amene anadziŵa dzikolo ndi kopeza zinthu zofunidwa ndi omanga misasa. Mose anaitana Hobabu kuti agwirizane nawo, koma poyamba Hobabu anakana, akumalingalira kuti kukanakhala bwinopo kutsala ndi abale ake m’malo obadwira. Komabe, Mose anamlimbikitsa kulingaliranso ndi kutsagana nawo kuti ‘atumikire monga maso’ a Israyeli ndipo motero kukhala woyenerera kulandira madalitso amene Yehova akapereka pa anthu ake. Mwanzeru Hobabu anatero, monga momwe kwasonyezedwera pa Oweruza 1:16.—Numeri 10:29-32.
12 Lerolino pali anthu amene anaphiphiritsiridwa ndi Hobabu. Ngakhale saali Aisrayeli auzimu, amadzigwirizanitsa ndi amenewa pamene akupita ku Dongosolo Latsopano la Mulungu. Kuti achite zimenezi, ayenera kudula zigwirizano ndi achibale audziko ndi maboma a anthu. Motsogozedwa ndi Mose Wamkulu, Yesu Kristu, iwo mokondwera akutumikira limodzi ndi otsalira a “abale” a Kristu, kaŵirikaŵiri akumafunafuna magawo atsopano kaamba ka kulalikidwa kwa mbiri yabwino. Ambiri a iwo asamukira m’madera amene kufunika kwa olengeza ufumu kunali kwakukulu kwenikweni, kaŵirikaŵiri monga apainiya kapena amishonale, akumagwiritsira ntchito nthaŵi yawo mokwanira kulengeza Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chenicheni chokha cha anthu. Pali chikhalirebe mipata yambiri ya kuloŵa m’ntchito yopatulika yotero. Anthu oyeneretsedwa akuitanidwa kuti adzipereke ndipo motero kulandira madalitso amene amatsagana ndi utumiki wotukulidwa woterowo. Kodi mungatero?
13 Zaka zokwanira 180 Hobabu atasankha kutsagana ndi Israyeli, mmodzi wa mbadwa zake, mwamuna wotchedwa Heberi, ankakhala ndi mkazi wake, Yaeli, pafupi ndi Megido. Heberi adadzilekanitsa ndi Akeni onse ndipo adaloŵa mu unansi wamtendere ndi Yabini, mfumu Yachikanani amene mwankhalwe anatsendereza Israyeli. Pamene Yehova anadzutsa Baraki monga wolanditsa Israyeli, kazembe wankhondo wa Yabini, Sisera, anasonkhanitsa gulu lake lankhondo ndi magaleta ankhondo mazana asanu ndi anayi okhala ndi zikwakwa zomangiriridwa ku magudumu. Koma Yehova anamenyera anthu ake nkhondo, Akumachititsa chisokonezo mu msasa wa adani, ndi chigumula cha mwadzidzidzi kutitimiritsa magaletawo. Sisera mwiniyo anasiya galeta lake nathaŵa ndi miyendo kumka cha ku hema wa Yaeli mkazi wa Heberi. Monga momwe Sisera anali atayembekezera, anamuitanira mu hema.—Oweruza 4:4-17; 5:20, 21.
14 Tsopano chiyeso chinayamba. Kodi akachitanji kwa mdani wa anthu a Yehova ameneyu? Anafunda Sisera ndi bulangete, nathetsa ludzu lake ndi mkaka wosasa nayembekezera kufikira atagona tulo. Pamenepo mkaziyo “anatenga chichiri cha hema, natenga nyundo m’dzanja lake nam’dzera monyang’ama, nakhomera chichiri chiloŵe m’litsipa mwake; nichinapyoza kuloŵa m’nthaka; popeza anali m’tulo tofa nato ndi kulema; nafa.” Zimene mkaziyo anachita zinafunikira kulimba mtima, ndi kukonda Yehova ndi anthu ake. Zinaphatikizaponso kachitidwe kotsimikiza ndi kuyesayesa kwake.—Oweruza 4:18-22; 5:24-27, 31.
15 Monga momwe kuliri ndi olambira Yehova osakhala Aisrayeli, Yaeli amaphiphiritsira “nkhosa zina” zimene zimachitira zabwino abale auzimu a Kristu. Mosasamala kanthu za zigwirizano zimene achibale awo enieni angakhale nazo ndi dziko ndi kagulu kake kolamulira, “nkhosa” sizimavomereza kutsenderezedwa kwa anthu a Yehova ndi olamulira a dziko. Kukhulupirika kwawo kwaperekedwa kwa Baraki Wamkulu, Ambuye Yesu Kristu, ndi kwa otsatira ake owona. A kagulu ka Yaeli amenewa samasamulira dzanja mwachindunji olamulira a dziko, koma amagwiritsira ntchito chirichonse chimene chiri chopezeka kwa iwo kulepheretsa zoyesayesa za kutsendereza atumiki a Yehova. Iwo samaleka kulengeza kuti akugwirizana kotheratu ndi chifuno cha Yehova cha kuwononga adani ake onse.
16 Palibe kutaya nthaŵi. Ngati mumakhulupiriradi Yehova ndi Ufumu wake Waumesiya ndipo ngati mwagwirizanitsa moyo wanu ndi zofunika za Baibulo, pamenepo, mosazengereza, sonyezani zimenezo poyera. Sonyezani mzimu wa mfule Yachiitiyopiya yosimbidwa m’Machitidwe mutu 8. Mwamsanga atazindikira chimene chinafunidwa kwa iye, anafunsa Filipo, amene adamlongosolera mbiri yabwino yonena za Yesu kuti: “Chindiletsa ine nchiyani ndisabatizidwe?” Ndipo mwamsanga anabatizidwa m’madzi.
17 Pokhala mutapanga chiyambi chabwino motero, limbikitsani unansi wanu ndi Yehova tsiku ndi tsiku, funafunani njira zogwiritsira ntchito Mawu ake mokwanira kwambiri m’moyo wanu, ndipo loŵani mokwanira monga momwe kungathekere m’ntchito yofunika yolengeza Ufumu yochitidwa mkati mwa masiku otsiriza a dongosolo la zinthu lino.
[Mafunso]
1. Kodi nchosankha chotani chimene chiyenera kupangidwa pamaziko aumwini?
2. (a) Kodi nchifukwa ninji lingaliro la kholo kukutumikira Yehova liri lofunika kwenikweni? (b) Kodi nzinthu zisanu zotani zimene makolo angachite kuti apatse ana awo chiyambi chabwino kwambiri?
3. (a) Ngati mukumana ndi chitsutso chochokera ku ziŵalo za banja, kodi nchiyani chimene chingachitidwe? (b) Koma kodi bwanji ngati chitsutsocho chipitiriza?
4. Kodi tingasonyeze motani kuti timakondadi Yehova?
5. (a) Pa Yesaya 11:10, kodi nchiyani chimene chidanenedweratu kaamba ka nthaŵi yathu? (b) Kodi chimatanthauzanji?
6. (a) Kodi nchiyani chimene chatheketsa anthu kusonkhanira Mfumu yakumwamba? (b) Chifukwa cha ‘kutembenukira mofunsira’ ku “chizindikiro,” kodi nchiyani chimene anthu aphunzira?
7. Kodi nkachitidwe kotani ku uthenga wa Baibulo kamene kadanenedweratu pa Ezekieli 33:30-33?
8. Kodi ndimotani mmene anthu ena amaperekera umboni za lingaliro limenelo?
9. Mmalo mwa kukaikira ndi kuyembekezera, kodi anthu anzeru adzachitanji?
10, 11. (a) Kodi Hobabu anali yani, ndipo kodi ndichiitano chotani chimene chinaperekedwa kwa iye? (b) Kodi tikudziŵa motani chosankha chimene anapanga?
12. (a) Kodi ndani lerolino amene ali ngati Hobabu, ndipo m’njira zotani? (b) Kodi nchiitano chotani lerolino chimene chiri ngati chija cha Mose kwa Hobabu?
13. (a) Kodi Yaeli anali yani, ndipo kodi nchiyani chimene chinali malo a mwamuna wake ponena za atumiki a Yehova? (b) Kodi ndimotani mmene Yaeli anakumanira ndi chiyeso?
14. Kodi Yaeli anapanga chosankha chotani, ndipo kodi chimenechi chinapereka umboni wanji?
15. Kodi ndimotani mmene anthu lerolino amasonyezera kuti ali ngati Yaeli?
16, 17. (a) Kodi nchitsanzo chotani chimene chiri choyenerera kutsanziridwa ndi ife chimene chalembedwa pa Machitidwe mutu 8? (b) Pambuyo pake kodi nchiyani chimene tiyenera kupitirizabe kuchita?