Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • tp mutu 3 tsamba 22-33
  • Kodi Zipembedzo za Dziko Zikupereka Chitsogozo Choyenera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zipembedzo za Dziko Zikupereka Chitsogozo Choyenera?
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zipembedzo za Dziko Zimapititsa Patsogolo Makhalidwe Abwino?
  • Zotulukapo za Kukana Mawu a Mulungu
  • Kutha kwa Zipembedzo za Dziko Kukuyandikira
  • Chifukwa Chake Chipembedzo cha Dziko Chidzatha
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Zipembedzo Zabodza Zimaphunzitsa Zinthu Zonama Zokhudza Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Zipembedzo Zonse Zimakondweretsa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
tp mutu 3 tsamba 22-33

Mutu 3

Kodi Zipembedzo za Dziko Zikupereka Chitsogozo Choyenera?

1. Kodi ndimafunso ofunika otani ponena za zipembedzo zadziko amene akudzutsidwa panopa?

“CHIPEMBEDZO chakhala chimodzi cha zisonkhezero zamphamvu kopambana m’mbiri,”28 inatero The World Book Encyclopedia. Koma kodi zipembedzo za dziko zakhala chisonkhezero chowona kaamba ka mtendere ndi chisungiko? Kodi izo zaphunzitsa otsatira awo kuti chikondi chaubale chiyenera kupambana malire autundu ndi kusiyana kwaufuko? Ndiponso, Kodi matchalitchi a Dziko Lachikristu, Chikatolika, Chiprotesitanti, ndi Orthodox, atsimikizira kukhala owona ku zonena zawo za kutsatira Yesu Kristu monga “Kalonga wa Mtendere”? Kapena kodi iwo awonjezeradi maudani amene akuwopseza mtsogolo mwa anthu? Kupenda cholembedwacho kudzapereka yankho lodabwitsa.

2. Kodi nchiyani chimene magwero osiyansiyana akutiuza ponena za cholembedwa cha mbiri yakale?

2 Pa mfundoyi, Parade Magazine inati: “Mbiri imapereka maphunziro kwa awo amene ali ofunitsitsa kuphunzira. Limodzi la maphunziro oyambirira koposa ndiro nkhondo zochititsidwa ndi kusiyana kwa chipembedzo ndi mpatuko ziri nthawi zonse zankhalwe koposa, zosatha koposa ndi zovuta koposa kuzithetsa.”29 Ndipo monga momwe Chicago Tribune inafotokozera: “Chipembedzo chachikulu chirichonse chimalalikira mtendere ndi ubale ndi chifundo, chikhalirechobe zina zankhalwe zoipa kopambana ndi zopanda chifundo koposa m’mbiri zachitidwa m’dzina la Mulungu.”30 Ali ndi maumboni a m’mbiri otere m’maganizo, mkonzi wanyuzipepala C. L. Sulzberger moyenerera anafunsa kuti: “Mulimonse mmene nkhaniyi ingakhalire yosavomerezeka, kodi sikuyenera kuzindikiridwa kuti kuwonjezera pa zochititsa zina—ulamuliro wolanda chuma, wa kusankhana mafuko, ulamuliro wa asilikali ankhondo—chipembedzo chakula mosalekeza kukhala chiwopsezo chachikulu ku moyo wamunthu?”31

3. Kodi ndimachitachita omvetsa chisoni otani achipembedzo amene mbiri ya zaka za zana la20 lathuli ikuvumbula?

3 Inde, mbiri yaipitsidwa ndi mwazi wankhondo zochirikizidwa ndi chipembedzo. M’zaka za zana lathu zokha zino, mkati mwa nkhondo zadziko ziŵiri ndi pambuyo pake, tawona chochitika chomvetsa chisoni cha azipembedzo okhaokha akuphana wina ndi mnzake—Akatolika kupha Akatolika, Aprotesitanti akupha Aprotesitanti, Asilamu akupha Asilamu, ndi ena. Ndipo atsogoleri achipembedzo a mbali zolimbanazo, ngakhale ziri zachipembedzo chimodzimodzi, anadalitsa magulu ankhondo amene mwamsanga akakhala akupha abale awo achipembedzo.

4. (a) Kodi nchifukwa ninji matchalitchi a Dziko Lachikristu ali ndi liwongo lalikulu koposa? (b) Kodi nchiyani chimene ndemanga imodzi yankhani ya mkonzi idanena ponena za nkhondo?

4 Pakati pa aliwongo koposa m’nkhaniyi ndiwo matchalitchi a Dziko Lachikristu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti amadzinenera kuti amaimira Mulungu wa Baibulo ndi Mwana wake Yesu Kristu, amene anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Chikhalirechobe kuphana koipitsitsa koposa konse kwachitikira mkati mwenimweni mwa Dziko Lachikristu. Monga momwe nkhani ya mkonzi mu Waterloo Courier ya ku Iowa inanenera kuti: “Ndiponso Akristu anali osanyansidwa konse ndi kumenyana nkhondo ndi Akristu ena. Ngati iwo akananyansidwa, zochuluka za nkhondo zankhanza kopambana mu Ulaya sizikanachitika konse. . . . Nkhondo Yadziko I ndi II, imene inali ndi ziwerengero zapamwamba koposa za nthawi zonse za Akristu akupha Akristu anzawo, sizikanachitika konse.”32

5. (a) Kodi nchiyani chimene Baibulo limauza momvekera bwino awo amene amatumikiradi Mulungu? (b) Kodi ndifunso lotani limene ziwalo zatchalitchi ziyenera kufunsa ponena za tchalitchi chawo?

5 Pankhaniyi, Baibulo liri lomvekera bwino: Awo amene amatumikiradi Mulungu amalangizidwa ‘kufunafuna mtendere ndi kuulondola,’ ‘kusula malupanga awo kukhala zolimira,’ ndi ‘kusaphunziranso nkhondo.’ (1 Petro 3:11; Yesaya 2:2-4) “Tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera kwa woipayo [Satana Mdyerekezi], namupha mbale wake.” (1 Yohane 3:10-12) Koma otsatira azipembedzo za dziko lino amapitirizabe kupha abale awo, monga momwe anachitira Kaini, ndipo atsogoleri awo achipembedzo achirikiza awo amene amalondola njirayo. Chotero, ngati inu muli m’chipembedzo, dzifunseni kuti: ‘Ngati anthu onse padziko lapansi akanakhala achipembedzo changa, kodi nkhondo zikanalekeka ndipo kodi dziko lapansili tsopano likanakhala malo amtendere weniweni?’

6. Kodi nchiyani chimene mkhalidwe wogawanika ndi wankhondo wa zipembedzo za dziko umatsimikizira?

6 Mkhalidwe wogawanika ndi wankhondo wa zipembedzo zadziko umatsimikizira kuti Mulungu sakuzichirikiza. Izi zingakhale zodabwitsa kwa awo amene amalingalira kuti chipembedzo chonse chiyenera kukhala chabwino popeza kuti chimadzinenera kukhala choimira Mulungu. Chikhalirechobe Baibulo limasonyeza bwino kuti “Mulungu sali Mulungu wachisokonezo koma wamtendere.” (1 Akorinto 14:33) Limasonyezanso kuti pali zonse ziwiri chipembedzo chowona ndi chipembedzo chonyenga. Ndipo limafotokoza kuti kulambira kokha kozikidwa pa chowonadi, kopanda chinyengo, kumachirikizidwa ndi Mulungu.—Mateyu 15:7-9; Yohane 4:23, 24; Tito 1:16.

7. (a) Kodi ndimawu otani amene Baibulo limagwiritsira ntchito kufotokoza zipembedzo za dziko? (b) Kodi ndiliwongo lotani limene lanenedwa motsutsana nawo?

7 Kwenikweni, chifukwa chakuti zipembedzo zadziko, zadzipereka ku uhule kuti zipeze phindu la ndale zadziko, lazamalonda, ndi makhalidwe a anthu, Baibulo limaziphiphiritsira kukhala zofanana ndi mkazi wachigololo. Polongosola “mkazi wachigololo,” ameneyu ilo limati: “Momwemo munapezedwa mwazi wa . . . onse amene anaphedwa padziko.” (Chivumbulutso 17:1-6; 18:24) Inde, zipembedzo za dziko lino ziri ndi liwongo lalikulu la mwazi poyerekezera ndi kupha konse kochitidwa m’mbiri yadziko! Pa ichi izo zidzaimbidwa mlandu.

8. Kodi ndimotani mmene mawu a Yesu onena za “atsogoleri akhungu” amagwirira ntchito lerolino?

8 Mwachiwonekere, chipembedzo chirichonse chimene zochita zake ziri zosiyana ndi Baibulo sichingapeze konse chipambano m’kutsogolera anthu ku mtendere weniweni ndi chisungiko. Ndicho chifukwa chake Yesu ananena za atsogoleri a chipembedzo chonyenga m’tsiku lake kuti: “Iwo ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse aŵiri adzagwa m’mbuna.” (Mateyu 15:14) Mofananamo, zipembedzo za dziko lerolino, ziri “atsogoleri akhungu” m’nkhani ya nkhondo ndiponso m’mbali zina zofunika za moyo.

Kodi Zipembedzo za Dziko Zimapititsa Patsogolo Makhalidwe Abwino?

9, 10. (a) Kodi nchifukwa ninji kugwiritsitsa miyezo yowona ya makhalidwe abwino kuli kofunika ku mtendere ndi chisungiko? (b) Monga momwe kwaphunzitsidwira m’Baibulo, kodi nchiyani chimene chimapititsa patsogolo makhalidwe abwino otero?

9 Kodi aliyense angathe kusangalala ndi mtendere weniweni ndi anansi ake kapena chisungiko chenicheni ngati miyezo yowona ya makhalidwe abwino sikusungidwa? Ngati palibe miyezo yotero, kunama, kuba, chigololo, ndi zizolowezi zofanana nazo zimakhala zofala. Kumbali ina, kukonda mnansi kowona kuyenera kupititsa patsogolo makhalidwe abwino.

10 Baibulo limasonyeza lingaliro la Mulungu ponena za makhalidwe abwino motere: “Iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo. Pakuti iri, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina lirilonse, limangika pamodzi m’mawu amenewa, kuti, Udzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha. Chikondano sichichitira mnzake choipa.”—Aroma 13:8-10.

11, 12. (a) Kodi munthu amene samachirikiza miyezo ya makhalidwe abwino angayembekezere kukhala pamtendere ndi Mulungu? (b) Kodi ndani amene moyenerera amakhazikitsa miyezoyo?

11 Komabe, chofunika kwambiri koposa chimenechi, kodi mukhulupirira kuti munthu aliyense angathe kukhala pamtendere ndi Mulungu, akumakhala ndi chitsimikiziro cha chiyanjo Chake ndi tchinjirizo, ngati sagwiritsira ntchito miyezo ya Mulungu ya makhalidwe abwino? Kodi inu mukanalemekezadi Mulungu amene sanafunikire makhalidwe abwino otere kwa awo amene amadzinenera kuti akumtumikira?

12 Kuti Mulungu afune kukhulupirika kumiyezo yake, akafunikira kumveketsa chimene miyezoyo iri. Chimenecho iye wachichita m’Mawu ake, Baibulo. (2 Timoteo 3:16, 17) Kunena kuti munthu aliyense ayenera kudzipangira miyezo yake ya makhalidwe abwino ndi kuitsatira sikwanzeru mofanana ndi kuuza munthu aliyense kuti ayenera kudzipangira malamulo akeake a pamsewu ndi kuwatsatira. Mudziŵa chimene chikanakhala chotulukapo chake. Moyenerera Baibulo limasonyeza kuti pali njira imodzi yokha yobweretsa chivomerezo cha Mulungu. Monga momwe Yesu adanenera, njira zina zonse zimatsogolera kokha ku chiwonongeko.—Mateyu 7:13, 14; Luka 13:24.

13-15. (a) Kodi ndimafunso otani onena za makhalidwe abwino amene afunikira kufunsidwa ponena za ziwalo za tchalitchi cha munthuwe? (b) Kodi nchiyani chimene Baibulo limati chiyenera kuchitidwa ndi chiwalo cha mpingo chimene chipitirizabe kuswa malamulo a Mulungu? (c)  Kodi izi zimachitidwa m’matchalitchi?

13 Kodi matchalitchi, makamaka a Dziko Lachikristu, amachirikiza miyezo ya Mulungu ya makhalidwe abwino ndipo chotero kupereka chitsogozo kaamba ka mbali ina yonse yadziko? Kodi nchiyani chimene miyoyo ya ambiri amene ali a m’matchalitchi amenewo imavumbula? Kodi muli ndi tchalitchi chanu? Pamenepo dzifunseni kuti: ‘Ngati anthu onse padziko lapansi akanakhala monga momwe ziwalo za chipembedzo changa zimakhalira, kodi kukanathetsa upandu, machitidwe a bizinesi osawona mtima, nkhondo ndi chisembwere?’

14 Baibulo limachenjeza kuti: “Chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse” ndi kuti “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (Agalatiya 5:9; 1 Akorinto 15:33) Chifukwa chake iro limalangizanso Akristu kuti “musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere iyai. . . . Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.”—1 Akorinto 5:11-13.

15 Ndithudi, munthu angapange cholakwa ndiyeno nkuwongokera. Koma bwanji za awo amene ali ndi chizolowezi cha kuchita zinthu zotero? Ngati anthu amenewa amadzinenera kukhala akutumikira Mulungu, iwo ali onyenga. Ndithudi inu mumanyansidwa ndi chinyengo, ndipo Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amadana nacho ndi iwo amene amachichita. (Mateyu 23:27, 28; Aroma 12:9) Pamenepa, bwanji, za chipembedzo chanu? Kodi chimatsatira lamulo la Baibulo la “kuchotsa” awo amene amapitirizabe kuswa malamulo a Mulungu ndi amene samasonyeza kulapa kowona mtima? Kapena kodi chimaloleza anthu otero kupitirizabe kukhala m’mkhalidwe wabwino, ndipo chotero kuika paupandu enawo? Kodi icho chimapereka kokha utumiki wa pakamwa ku makhalidwe abwino pamene kwenikweni chikunyalanyaza cholakwa, kapena ngakhale kuchilekerera?—Mateyu 15:7, 8.

16. (a) Kodi nchiyani chimene atsogoleri achipembedzo ambiri tsopano akunena ponena za khalidwe la zakugonana? (b) Kodi nchiyani chimene Baibulo limanena ponena za khalidwe lotero?

16 Atsogoleri achipembedzo owonjezerekawonjezereka akunena kuti dama, chigololo, kugonana kwa anthu a ziŵalo zofanana siziri zolakwa kwenikweni. Koma iwo sali ogwirizana ndi malingaliro a Mulungu. Mawu ake amafotokoza momvekera bwino kuti: “Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena mbala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10.

Zotulukapo za Kukana Mawu a Mulungu

17-19. (a) Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo anawonera Baibulo? (b) Kodi ndimotani mmene atsogoleri achipembedzo ambiri lerolino amawonera Baibulo?

17 Chifukwa chachikulu chimene zipembedzo za dziko lino ziliri mu mkhalidwe wogawanika, ndi wachipolowe woterowo nchakuti zimanyalanyaza malamulo a Mulungu monga momwe akupezekera m’Mawu ake, Baibulo. Ndithudi, atsogoleri achipembedzo ochuluka amakana Baibulo kukhala Mawu ouziridwa a Mulungu. Chikhalirechobe, mtumwi Paulo wouziridwayo adanena kuti: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu.” (2 Timoteo 3:16) Paulo anatilimbikitsanso kuvomereza Baibulo ‘osati monga mawu a anthu, komatu monga momwe ali ndithu mawu a Mulungu.’ (1 Atesalonika 2:13) Ndithudi Yehova Mulungu, Mlengi Wamphamvuyonse wa chilengedwe chonse chochititsa mantha ichi, akanalemba bukhu ndi kutsimikizira kuti linali langwiro mkati mwa zaka mazana ambiri!

18 Komabe, New Catholic Encyclopedia imati: “Mawu ambiri a Baibulo saali owona pamene apendedwa mogwirizana ndi chidziŵitso chamakono cha sayansi ndi mbiri yakale.”39 Polemba mu U.S. Catholic wansembe wina anafotokoza kuti chilengedwe cha dziko lapansi sichikanachitika mwanjira imene chafotokozedwera mu Genesis. Ndipo ponena za cholembedwa chake cha kulengedwa kwa anthu, iye anati: “Fuko laumunthu silinayambe mwanjirayo.”40 Bishopo wa Episikopolo anati: “Baibulo liri ndi zolakwa, zosalungama ndi mawu otsutsana. Chifukwa chake kuli komvekera bwino chifukwa chake matchalitchi aakulu Achikristu samawona Baibulo kukhala losalakwa.”41 M’Mangalande, bishopo wa Angilikani ananena kuti chiukiriro cha Kristu chinali “tsenga lenileni.”42

19 Chotero, unyinji wa atsogoleri achipembedzo umaluluza Baibulo kapena samaphunzitsa otsatira awo kulilemekeza ndi kutsatira malamulo a Mulungu olembedwamo. Ndicho chifukwa chachikulu cha umbuli wochititsa mantha wa kusadziwa Mawu a Mulungu m’Dziko Lachikristu monse. Wochitira ndemanga wachipembedzo M. J. McManus analemba izi ponena za ofika kutchalitchi kuti: “Pali zikhoterero zochepa m’chipembedzo zimene zimawopseza kwambiri kufooketsa chipembedzo cholinganizidwa m’ma-1980 mofanana ndi mkhalidwe womvetsa chisoni wa chidziŵitso cha Baibulo.” Iye ananena kuti “Baibulo likali chikhalirebe bukhu losaŵerengedwa, lachilendo” kwa unyinji wa opita ku tchalitchi.43

20, 21. Kodi zotulukapo za kukana ziphunzitso Zabaibulo zakhala zotani?

20 Kodi nchiyani chimene chakhala chotulukapo cha zonsezi? Kodi zipembedzo za dziko zakhala zokhoza kusonyeza kuti zingathe kululuza ziphunzitso Zabaibulo ndi kutulutsabe mtendere kapena makhalidwe abwino pakati pa ziwalo zawo? M’malo mwake, mikhalidwe ikuipiraipira padziko lonse lapansi. Mitundu yokhala ndi zipembedzo zosakhala Zachikristu yakhalanso kochitikira kupanda mpumulo, kugawanika, chisalungamo chandale zadziko, ndi kuipaipa kwa makhalidwe mowonjezerakawonjezereka. Koma kwa nthawi yaitali Dziko Lachikristu lakhala kwakukulukulu pakati pa okanthidwa kopambana ndi upandu, chisembwere, kumwerekera ndi mankhwala oledzeretsa, nkhondo yamafuko ndi nkhondo. Kwachitika monga momwedi Mawu odalirika a Mulungu adaneneratu kuti: “Akana mawu a Yehova, ali nayo nzeru yotani?”—Yeremiya 8:9.

21 Umboniwu ngosakanika. Umasonyeza kuti zipembedzo za dziko siziri chisonkhezero chowona cha mtendere ndi chisungiko. Ndipo zasiya otsatira awo ali osadziŵa za chiyembekezo chowona—Ufumu wa Mulungu. Pamenepa, kodi zonsezi, zikutanthauzanji?

Kutha kwa Zipembedzo za Dziko Kukuyandikira

22, 23. Kodi nchiyani chimene Baibulo limati chidzadza pa zipembedzo zonyenga za dzikoli?

22 Yesu Kristu analongosola kuti: “Mmera, wonse umene Atate wanga wakumwamba sanaubzala, udzazulidwa.” (Mateyu 15:13) Zipatso zoipa zotulutsidwa ndi zipembedzo za dziko lino zimatsimikizira kuti sizinabzalidwe ndi Mulungu. Chotero, Baibulo limaneneratu kudza kwa chiwonongeko cha madongosolo onse onyenga a kulambira.

23 Polankhula za madongosolo a zipembedzo amenewa mwadzina lophiphiritsira lakuti “Babulo Wamkulu,” wonga mkazi wachigololo Mulungu akunena zotsatirazi ponena za ulamuliro wa dziko lonse wachipembedzo chonyenga: “Machimo ake anaunjikizana kufikira m’mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake. . . . Miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo adzapserera ndi moto; chifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.”—Chivumbulutso 18:2, 5-8.

24. Kodi ndimotani mmene chiwonongeko chotero chidzafikira, ndipo kuchokera ku magwero ati?

24 Wonani kuti chiwonongeko ichi chidzadza mwadzidzidzi kwambiri, monga “m’tsiku limodzi.” Modabwitsa ndi kuchititsa mantha anthu ambiri, chipembedzo chonyenga chidzathetsedwa, kuwonongedwa, ndi mitundu yandale za dziko yeniyeniyo imene kwanthawi yaitali yachita nayo uhulewo.—Chivumbulutso 18:10-17, 21 17:12, 16.

25. (a) Pa Chivumbulutso 18:4, kodi nchiyani chimene anthu okhumba chivomerezo cha Mulungu amalimbikitsidwa kuchita? (b) Kodi nchiyani chimene chiyenera kusonkhezera munthu kuchita motero?

25 Chifukwa cha chimenecho chiitano chaumulungu ndicho chakuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga, kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.” (Chivumbulutso 18:4) Kuchita kachitidwe kameneko kumatanthauza kuti munthuyo awone chipembedzo chonyenga monga momwe Mulungu amachiwonera. Kumatanthauza kuti amaipidwa nacho chifukwa cha zipatso zake zovunda, chinyengo chake, ndi kukhulupirira malaulo kwake. Kuipidwa kuyenera kumvedwa chifukwa cha njira mu imene chipembedzo chonyenga chaimirira Mulungu molakwa pamaso pa anthu ndi njira mu imene chawonjezerera kuvutika ndi kupsinjika kwa anthu. (Aroma 2:24; Yeremiya 23:21, 22) Ngati mudziwa izi, mudzachotsa chichirikizo chonse m’zipembedzo zotero, motero kusonyeza chichirikizo chanu chotheratu cha chiweruzo cha Mulungu pa izo.

26. (a) M’kuwonjezera, kodi nchiyani chimene munthu ayenera kupeza ngati ati akhale ndi mtendere wa Mulungu ndi tchinjirizo? (b) Kodi ndianthu a mtundu wotani amene munthu ayenera kuyang’ana pofunafuna kupeza awo amene amagwiritsira ntchito kulambira kowona?

26 Komabe, kungosiya sikuli kokwanira. Muyenera kufunafuna ndi kupeza kulambira kwowona, ndi kopanda chinyengo kumene kudzakubweretserani mtendere wa Mulungu ndi tchinjirizo pamene chiwonongeko chonenedweratucho chifika. Awo olowa m’kulambira kowona kumeneko ayenera kukhala anthu amene ‘asula kale malupanga awo kukhala zolimira ndi kusaphunziranso nkhondo.’ (Yesaya 2:4) Ayenera kukhala anthu amene amakhulupirira Mawu a Mulungu ndi kuwatsatira, akumawalola kukhala mphamvu yotsogoza m’miyoyo yawo. (Salmo 119:105) Ayenera kusonyeza chikondi chenicheni, ndi chopanda mpeni kumphasa kwa anthu anzawo. (Yohane 13:35; Aroma 13:8) Kodi pali kulambira kotere padziko lapansi lerolino? Mamiliyoni ambiri amakupeza pakati pa Mboni za Yehova. Zimadziwika padziko lonse lapansi kaamba ka kumamatira kwawo kumalamulo a Mulungu monga momwe akupezekera m’Baibulo. Ndipo mtendere ndi chisungiko zimene iwo ali nazo zimasonyeza kutsimikizirika ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu.

27. Kodi nchiyani chimene mudzakhoza kudziwonera nokha mwa kufika pamisonkhano ya Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yawo?

27 Mboni za Yehova ziri zodera nkhawa kwambiri ndi mkhalidwe waupandu mu umene chipembedzo chonyenga chalowetsamo anthu. Izo zikuyesayesa mowona kupatsa Mawu a Mulungu malo oyamba m’miyoyo yawo. Inu mukuitainidwa kufika pamisonkhano yawo pa Nyumba Yaufumu kwanuko ndi kudzifufuzira ukulu wa m’mene zimasonyezera mzimu wa Mulungu ndi kusangalala ndi mtendere ndi chisungiko zimene umadzetsa. Mudzawonanso m’mene izo zimaphunzirira ndi kugwiritsira ntchito zimene Mulungu amafuna kwa anthu amene adzapulumuka chiwonongeko chirinkudza ndi kukhala ndi moyo m’Dongosolo lake Lolungama mu ulamuliro wa Ufumu wake wakumwamba.

[Bokosi patsamba 29]

Atsogoleri achipembedzo owonjezerekawonjezereka akuvomereza zimene Baibulo limatsutsa kukhala chisembwere, monga momwe zitsanzo izi za mitu yankhani ndi nkhani zanyuzi zimasonyezera:

“Pamene Zoipa Zisanduka Zabwino Atsogoleri Achipembedzo Adzatiuza.” “[Tchalitchi cha Ingalande] tsopano chikusiya mkhalidwe wake wachikale wolamulira motsendereza ufulu. Kugonana popanda ukwati, ndi munthu mmodzi kapena oposa, . . . kudzalingaliridwa kukhala kovomerezedwa mwamakhalidwe kuyambira tsopano kumka mtsogolo.”—Alberta Report.33

“Apasitala Akhala Chete ponena za Kugonana Popanda Ukwati.” “Apasitala a ku Amereka akhala chete moluluza m’kulalikira za kugonana ukwati usanachitike . . . Iwo akuwopa kuti adzatayikiridwa ndi ena a m’mipingo yawo. Yesaya anadziwa za ansembe otere. M’Mutu 1 wa bukhu lake iye anagwira mawu Ambuye kukhala akulankhula za iwo kuti, ‘Ndidzabisa maso anga kwa inu; ngakhale mukupereka mapemphero ochuluka, sindidzamvetsera; manja anu ngodzala magazi.’”—Telegraph, North Platte, Nebraska.34

“Chigololo m’Lingaliro Lolekerera.” “Mtsogoleri wachipembedzo Wachingelezi . . . anakwiya pamene analankhula lingaliro lolekerera la Tchalitchi kulinga ku Lamulo Lachisanu ndi Chiwiri. . . . ‘Mkhalidwe wathu ndiwo kusamalira osati kuweruza,’ iye anatero.”—The Sunday Times, Perth, Australia.35

“Okhulupirira m’Chigwirizano Akuvomereza Maukwati a Aziwalo Zofanana.”—The New York Times.36

“Gulu la akatswiri la United Church of Canada lachirikiza kuikidwa kwa ogonana aziwalo zofanana okangalika kukhala aminisitala.”—The Toronto Star.37

“Kuvomereza Uhule Mwalamulo—Ndiwo Chothetsera Mavuto Chopatulika Mtima.”—Nkhani ya Mkonzi yolembedwa ndi bishopo Wamkulu Wakatolika mu Philadelphia Daily News.38

[Zithunzi patsamba 25]

Atsogoleri achipembedzo adetsa ndi mwazi manja awo mwa kuchirikiza otsendereza ufulu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena