Chifukwa Chake Chipembedzo cha Dziko Chidzatha
“Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.”—CHIVUMBULUTSO 18:4.
1. (a) Kodi Babulo Wamkulu wagwa motani? (b) Kodi chochitika chimenechi chakhudza motani Mboni za Yehova?
“WAGWA, Babulo Wamkulu”! Inde, kwa Yehova ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga wagwa. Zimenezi zakhala choncho chiyambire 1919, pamene otsalira a abale a Kristu anamasuka ku mphamvu ya Dziko Lachikristu, mbali yaikulu ya Babulo wachinsinsiyo. Chotero, iwo akhala aufulu kutsutsa chipembedzo chonyenga ndi kulengeza ulamuliro wolungama wa Mulungu mwa Ufumu Waumesiya. M’zaka zonse za zana lino, Mboni zokhulupirika za Yehova zavumbula chigwirizano cha zipembedzo zimene Satana amalamulira chimene wagwiritsira ntchito kunyenga nacho “dziko lonse.”—Chivumbulutso 12:9; 14:8; 18:2.
Kodi Babulo Wamkulu Wagwa Motani?
2. Kodi mkhalidwe wamakono wa zipembedzo za dziko ngwotani?
2 Komabe, wina akhoza kufunsa kuti, ‘Kodi munena bwanji kuti Babulo wagwa, pamene chipembedzo chikuoneka kuti chikukula m’maiko ambiri?’ Monga Chikatolika, Chisilamunso chili ndi okhulupirira oposa mamiliyoni chikwi. Chiprotesitanti chikukulirakulira ku America, kumene matchalitchi atsopano ndi akachisi akumangidwa nthaŵi zonse. Anthu miyandamiyanda amatsatira miyambo ya Chibuda ndi Chihindu. Komabe, kodi ndi kufikira pati pamene chipembedzo chonsechi chimayambukira m’njira yabwino khalidwe la anthu miyandamiyanda ameneŵa? Kodi chaletsa Akatolika ndi Aprotesitanti kuphana ku Northern Ireland? Kodi chadzetsa mtendere weniweni kwa Ayuda ndi Asilamu ku Middle East? Kodi chagwirizanitsa Ahindu ndi Asilamu ku India? Ndipo, posachedwapa, kodi chaletsa a Orthodox a ku Serbia, Akatolika a ku Croatia, ndi Asilamu a ku Bosnia kuchita “kuyeretsa fuko,” kufunkha, kugwirira chigololo, ndi kuphana wina ndi mnzake? Nthaŵi zambiri chipembedzo changokhala dzina wamba, chikumaoneka ngati nsalu yopyapyala yokongola zedi koma yosamuka kung’ambika mutaikoka pang’ono.—Agalatiya 5:19-21; yerekezerani ndi Yakobo 2:10, 11.
3. Kodi nchifukwa ninji chipembedzo chikuweruzidwa ndi Mulungu?
3 Malinga ndi kaonedwe ka Mulungu, kuchirikiza chipembedzo kwa makamu sikumasintha choonadi chosakanika—chipembedzo chonse chikuweruzidwa ndi Mulungu. Babulo Wamkulu, malinga ndi mbiri yake, ayenera kuweruzidwa moipa chifukwa “machimo ake anaunjikizana kufikira m’mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.” (Chivumbulutso 18:5) M’mawu aulosi, Hoseya analemba kuti: “Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kavumvulu.” Zipembedzo zonse zonyenga za Satana padziko lonse zidzalandira chilango chokwana chifukwa cha kunyalanyaza kwawo Mulungu, chikondi chake, dzina lake, ndi Mwana wake.—Hoseya 8:7; Agalatiya 6:7; 1 Yohane 2:22, 23.
Musankhepo
4, 5. (a) Kodi tikukhala m’mikhalidwe yotani lerolino? (b) Kodi ndi mafunso ati amene tiyenera kuyankha?
4 Tili chakumapeto kwa “masiku otsiriza,” ndipo monga Akristu oona tikuyesayesa kuti tipyole “nthaŵi zoŵaŵitsa” zimenezi. (2 Timoteo 3:1-5) Akristu oona ali ogonera m’dziko la Satana, limene limasonyezadi umunthu wake woipa monga wambanda, wabodza, ndi woneneza. (Yohane 8:44; 1 Petro 2:11, 12; Chivumbulutso 12:10) Tazingidwa ndi chiwawa, chinyengo, ukatangale, kusaona mtima, ndi chisembwere chonyansa. Mapulinsipulo anyalanyazidwa. Kukonda zokondweretsa ndi dyera nzofala. Ndipo nthaŵi zambiri atsogoleri achipembedzo amalekerera makhalidwe oipa mwa kululuza chiletso chomveka cha Baibulo ponena za mathanyula, dama, ndi chigololo. Chotero funso nlakuti, Kodi mukuchirikiza ndi kulekerera kulambira konyenga, kapena kodi mukuchita mokangalika kulambira koona?—Levitiko 18:22; 20:13; Aroma 1:26, 27; 1 Akorinto 6:9-11.
5 Ino ndi nthaŵi ya kusefa. Chotero, pali chifukwa chachikulu kwambiri chosiyanitsira kulambira konyenga ndi koona. Kodi zipembedzo za Dziko Lachikristu zachitanso chiyani chimene chikuzichititsa kukhala ndi mlandu waukulu?—Malaki 3:18; Yohane 4:23, 24.
Chipembedzo Chonyenga Chazengedwa Mlandu
6. Kodi Dziko Lachikristu lakhala motani losakhulupirika ku Ufumu wa Mulungu?
6 Ngakhale kuti anthu miyandamiyanda m’Dziko Lachikristu amagwiritsira ntchito Pemphero la Ambuye nthaŵi zonse, mmene amapempherera Ufumu wa Mulungu kudza, iwo achirikiza zolimba ulamuliro uliwonse wandale, nanyalanyaza ulamuliro wateokrase. Zaka mazana angapo zapita “akalonga” a Tchalitchi cha Katolika, monga Kadinala Richelieu, Mazarin, ndi Wolsey, analinso akulu adziko, nduna za boma.
7. Kodi Mboni za Yehova zinawavumbula motani atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu zaka zoposa 50 zapitazo?
7 Zaka zoposa 50 zapitazo, m’kabuku kamutu wakuti Religion Reaps the Whirlwind, Mboni za Yehova zinavumbula kuloŵa m’ndale kwa Dziko Lachikristu.a Zimene zinanenedwa nthaŵiyo zikugwirabe ntchito mwamphamvu yofanana lerolino: “Kupenda moona mtima khalidwe la atsogoleri achipembedzo a matchalitchi onse kumavumbula kuti atsogoleri achipembedzo a ‘Dziko Lachikristu’ lonse akutengamo mbali mwachangu m’ndale za ‘dziko loipa lilipoli’ ndipo akuloŵa m’zochitika zake zadziko.” Panthaŵiyo Mboni zinadzudzula Papa Pius XII chifukwa chochita mapangano ndi Hitler wa Nazi (1933) ndi Franco Mfasisti (1941), ndiponso chifukwa chakuti papa anasinthana akazembe m’March 1942 ndi dziko la Japan loukira anzake, patangopita miyezi ingapo kuchokera pamene anaukira Pearl Harbor moipa. Papayo analephera kulabadira chenjezo la Yakobo lakuti: “Akazi achigololo inu, kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.”—Yakobo 4:4.
8. Kodi Tchalitchi cha Roma Katolika chaloŵa motani m’ndale lerolino?
8 Kodi mkhalidwe uli wotani lero? Apapa amaloŵabe m’ndale, kupyolera mwa atsogoleri ake achipembedzo ndi anthu wamba owaimira. Apapa aposachedwapa avomereza United Nations mwa kupita kukalankhula kwa bungwe lopangidwa ndi anthu kaamba ka kunamizira kudzetsa mtendere wa dziko. Kope laposachedwapa la L’Osservatore Romano, nyuzipepala yalamulo ya Vatican, inalengeza kuti nduna zatsopano zisanu ndi ziŵiri, “akazembe oimira maiko ku Holy See,” zinapereka zikalata zawo kwa “Atate Woyera.” Kodi tingaganize za Yesu ndi Petro akusinthana nduna ndi ena? Yesu anakana kulongedwa ufumu ndi Ayuda ndipo anati Ufumu wake sunali wa dziko lino.—Yohane 6:15; 18:36.
9. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti zipembedzo zachiprotesitanti sizili bwino kuposa zinzawo zachikatolika?
9 Kodi atsogoleri achiprotesitanti ali bwino kuposa anzawo achikatolika? Ku United States, zipembedzo zambiri zamwambo zachiprotesitanti, ndiponso Amormoni, zimadziŵika kukhala kumbali ya timagulu tina ta ndale. Bungwe la Christian Coalition (Chigwirizano Chachikristu) laloŵa kwambiri m’ndale za United States. Atsogoleri ena achipembedzo achiprotesitanti amachirikiza moonekera malingaliro osiyana a ndale. Zimaiŵalika nthaŵi zina kuti ku United States, olankhulira anthu zandale monga Pat Robertson ndi Jesse Jackson, ali kapena analinso “Alevulendi,” monganso alili phungu wa Nyumba ya Malamulo ya Britain Ian Paisley wa ku Northern Ireland. Kodi iwo amalungamitsa motani kaimidwe kawo?—Machitidwe 10:34, 35; Agalatiya 2:6.
10. Kodi ndi mawu otani omveka amene anakambidwa mu 1944?
10 Ifenso tikufunsa monga momwe Religion Reaps the Whirlwind inafunsira mu 1944 kuti: “Kodi gulu lililonse limene limachita mapangano ndi maulamuliro a dziko ndi kudziloŵetsa mokangalika m’zochitika zandale za dzikoli, likumafuna kupeza phindu m’dzikoli ndi kutetezedwa nalo . . . lingakhale tchalitchi cha Mulungu kapena kuimira Kristu Yesu padziko lapansi? . . . Mwachionekere, atsogoleri onse amene amagwirizana ndi maufumu a dzikoli sangaimire ufumu wa Mulungu mwa Kristu Yesu.”
Mzimu wa Kaini wa Chipembedzo Chonyenga
11. Kodi chipembedzo chonyenga chinatsanzira motani chitsanzo cha Kaini?
11 M’mbiri yonse, chipembedzo chonyenga chasonyeza mzimu wakupha achibale wa Kaini, amene anapha mbale wake Abele. “Mmenemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: yense wosachita chilungamo saali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera kwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.” Pokhala wosalolera kulambira kwa mbale wake koyera ndi kolandirika kwa Mulungu, Kaini anasankhapo chiwawa—njira yomaliza imene aja osoŵa yankho lanzeru amatsatira.—1 Yohane 3:10-12.
12. Kodi pali umboni wotani wakuti chipembedzo chaloŵa m’nkhondo ndi m’mikangano?
12 Kodi maumboni akuchirikiza kuzenga mlandu chipembedzo chonyenga kumeneku? M’buku lakuti Preachers Present Arms, mlembi wake anati: “M’mbiri ya kutsungula, . . . mphamvu ziŵiri zakhala zogwirizana pamodzi kupanga chigwirizano cha zinthu ziŵiri. Ndizo nkhondo ndi chipembedzo. Ndipo, pa zipembedzo zonse zazikulu za dziko, . . . palibe chimene chadzipereka kwambiri [pankhondo] monga [Dziko Lachikristu].” Zaka zingapo zapitazo, nyuzipepala ya The Sun ya ku Vancouver, Canada, inati: “Mwinamwake lili vuto la zipembedzo zonse zolinganizika kuti tchalitchi chimatsatira mbendera . . . Kodi ndi nkhondo iti imene inamenyedwapo popanda mbali zomenyanazo kunena kuti Mulungu anali kumbali yawo?” Mungakhale mutaona umboni wa zimenezi m’tchalitchi china kwanuko. Nthaŵi zambiri, mbendera ya dzikolo imakhala kuguwa. Kodi muganiza kuti Yesu akanachita perete pansi pa mbendera iti? Mawu ake amveka bwino kwazaka mazana ambiri: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi”!—Yohane 18:36.
13. (a) Kodi chipembedzo chonyenga chalephera motani mu Afirika? (b) Kodi ndi chizindikiro chotani chodziŵira Chikristu chimene Yesu anapereka?
13 Zipembedzo za Dziko Lachikristu sizinaphunzitse nkhosa zawo choonadi ponena za chikondi chenicheni cha pa abale. M’malo mwake, mikangano ya mitundu, malilime, ndi mafuko imaloledwa kugaŵanitsa anthu awo. Malipoti akusonyeza kuti atsogoleri achipembedzo achikatolika ndi achiangilikani anathandizira kwambiri magaŵano amene anachititsa mafuko kupululutsana ku Rwanda. The New York Times inati: “Kupulula anthu ku Rwanda kwachititsa Aroma Katolika ambiri kumeneko kuganiza kuti atsogoleri a tchalitchi anawagulitsa iwo. Nthaŵi zambiri tchalitchi chinagaŵanika mokondera mafuko, Ahutu ndi Atutsi.” Nyuzipepala imodzimodziyo inagwira mawu wansembe wa Maryknoll amene anati: “Tchalitchi chinalephereratu ku Rwanda mu 1994. Arwanda ambiri m’lingaliro lina aiŵalako za tchalitchi. Sichilinso chodalirika.” Zili zosiyana chotani nanga ndi mawu a Yesu akuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yohane 13:35.
14. Kodi ndi mbiri yotani ya khalidwe imene zipembedzo zazikulu zosakhala zachikristu zikupereka?
14 Zipembedzo zina zazikulu za Babulo Wamkulu sizinaperekenso chitsanzo chabwino. Kupulula anthu kowopsa kwa mu 1947, pamene India anagaŵidwa, kumasonyeza kuti zipembedzo zazikulu kumeneko sizinabale mzimu wololera. Chiwawa chopitiriza cha mafuko ku India chimasonyeza kuti anthu ochuluka sanasinthe. Nchifukwa chake magazini a India Today anafika pakunena kuti: “Upandu woipitsitsa wakhala ukuchitidwa m’dzina la chipembedzo. . . . Chimadzetsa chiwawa chowopsa ndipo chili mphamvu yowononga kwambiri.”
“Zodabwitsa Kwambiri”
15. Kodi mkhalidwe wa chipembedzo kumaiko akumadzulo ngwotani?
15 Ngakhale othirira ndemanga akudziko aona kulephera kwa chipembedzo kukhutiritsa anthu, kuwaphunzitsa makhalidwe abwino enieni, ndi kukaniza mzimu wa dziko kuti usawaloŵere. M’buku lake lakuti Out of Control, amene kale anali phungu pa zachitetezo cha dziko la United States Zbigniew Brzezinski analemba kuti: “Nzodabwitsa kwambiri kuti chipambano chachikulu koposa cha lingaliro lakuti ‘Mulungu ali wakufa’ sichinachitikire m’maiko olamuliridwa ndi ziphunzitso za Marx . . . koma m’maiko ademokrase Akumadzulo aufulu, amene mwamwambo akulitsa mphwayi pa makhalidwe. Kumeneko, umboni umasonyeza kuti chipembedzo chasiya kukhala mphamvu yaikulu yokhudza kakhalidwe ka anthu.” Anapitiriza kuti: “Mphamvu ya chipembedzo pa mwambo wa ku Ulaya yachepa kwambiri, ndipo Ulaya lero—kuposa ndi America—ali kwenikweni chitaganya chosapembedza.”
16, 17. (a) Kodi ndi uphungu wotani umene Yesu anapereka ponena za atsogoleri achipembedzo m’tsiku lake? (b) Kodi ndi muyezo wotani wabwino umene Yesu anatchula ponena za zipatso?
16 Kodi Yesu ananenanji za atsogoleri achipembedzo achiyuda m’tsiku lake? “Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose [kuphunzitsa Torah, Chilamulo]; chifukwa chake zinthu zilizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zawo; pakuti iwo amalankhula, koma samachita.” Inde, chinyengo chachipembedzo sichachilendo ayi.—Mateyu 23:2, 3.
17 Zipatso za chipembedzo chonyenga zimachitsutsa. Muyeso umene Yesu anapereka umachiyenerera kwambiri: “Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Inde chomwecho pa zipatso zawo mudzawazindikira iwo.”—Mateyu 7:17-20.
18. Kodi Dziko Lachikristu likanayeretsa motani magulu ake?
18 Ngati zipembedzo za Dziko Lachikristu zingatsatire mosamalitsa chilango chachikristu cha kuchotsa, kapena kutulutsa, pa kusayeruzika konse kochitidwa ndi aja omwe amati ndi anthu ake, kodi nchiyani chimene chingachitike? Kodi chingachitike nchiyani kwa abodza onse osalapa, adama, achigololo, amathanyula, akatangale, apandu, ogulitsa anamgoneka ndi omwerekera nawo, ndi a m’timabungwe ta upandu? Mosakayikira, zipatso zamphuchi za Dziko Lachikristu zimaliyeneretsa kulandira chiwonongeko chochokera kwa Mulungu basi.—1 Akorinto 5:9-13; 2 Yohane 10, 11.
19. Kodi ndi kuvomereza kotani kumene kwachitika ponena za atsogoleri achipembedzo?
19 Pamsonkhano wa onse wa Tchalitchi cha Presbyterian ku United States, opezekapo anavomereza kuti: “Tikuyang’anizana ndi tsoka limene ukulu wake ndi zotulukapo zake nzowopsa. . . . Pakati pa 10 ndi 23 peresenti ya atsogoleri achipembedzo m’dziko lonse lino achita modzutsa chilakolako choipa kwa obwera kutchalitchi, anthu amene iwo amatumikira, antchito awo, ndi ena ambiri, ngakhale kugona nawo.” Wamalonda wina wa ku United States anafotokoza mfundoyo bwino mwachidule kuti: “Magulu achipembedzo alephera kuphunzitsa miyezo yawo ya makhalidwe yofunika kwambiri, ndipo nthaŵi zambiri, ayambitsa vutolo.”
20, 21. (a) Kodi Yesu ndi Paulo anatsutsa motani chinyengo? (b) Kodi ndi mafunso ati amene ayembekeza kuyankhidwa?
20 Kutsutsa kwa Yesu chinyengo chachipembedzo kudakali kugwira ntchito lero monga momwe zinalili m’nthaŵi yake: “Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza ine ndi milomo yawo; koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Koma andilambira ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.” (Mateyu 15:7-9) Mawu a Paulo kwa Tito amafotokozanso za mkhalidwe wamakono: “Avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pantchito zonse zabwino osatsimikizidwa.”—Tito 1:16.
21 Yesu anati ngati munthu wakhungu atsogolera wakhungu mnzake, onse aŵiri amagwa m’mbuna. (Mateyu 15:14) Kodi mukufuna kudzawonongedwa pamodzi ndi Babulo Wamkulu? Kapena kodi mukufuna kuyenda m’mabande owongoka maso anu ali otseguka ndi kusangalala ndi dalitso la Yehova? Mafunso amene tikuyang’anizana nawo tsopano ngakuti: Kodi ndi chipembedzo chiti, ngati chilipo, chimene chimapatsa zipatso zaumulungu? Kodi tingakuzindikire motani kulambira koona kovomerezeka kwa Mulungu?—Salmo 119:105.
[Mawu a M’munsi]
a Kofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., mu 1944; tsopano analeka kukasindikiza.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Babulo Wamkulu ali ndi kaimidwe kotani pamaso pa Mulungu lerolino?
◻ Kodi chipembedzo chonyenga chazengedwa mlandu pachifukwa chiti?
◻ Kodi chipembedzo chonyenga chasonyeza motani mzimu wa Kaini?
◻ Kodi ndi muyezo wotani umene Yesu anatchula wopimira chipembedzo chilichonse?
[Chithunzi patsamba 13]
M’mbiri yonse atsogoleri achipembedzo aloŵa m’ndale
[Zithunzi patsamba 15]
Atsogoleri achipembedzo ameneŵa analinso akulu adziko amphamvu
Kadinala Mazarin
Kadinala Richelieu
Kadinala Wolsey
[Mawu a Chithunzi]
Kadinala Mazarin ndi Kadinala Richelieu: Kuchokera m’buku lakuti Ridpath’s History of the World (Vol. VI ndi Vol. V motsatizana). Kadinala Wolsey: Kuchokera m’buku lakuti The History of Protestantism (Vol. I).