Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ws mutu 22 tsamba 180-189
  • Mulungu wa “Kalonga wa Mtendere” Akhala “Zinthu Zonse kwa Aliyense”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mulungu wa “Kalonga wa Mtendere” Akhala “Zinthu Zonse kwa Aliyense”
  • Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyeso Chomaliza pa Anthu Onse
  • Aserafi, Akerubi, Angelo
  • Cholinga cha Yehova Chikwaniritsidwa ndi Ulemerero
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Mzimu Woyera Ukugwira Ntchito m’Malo Osaoneka a Kumwamba
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Chifuno cha Yehova Chipeza Chipambano Chaulemerero
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
    “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
Onani Zambiri
Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
ws mutu 22 tsamba 180-189

Chaputala 22

Mulungu wa “Kalonga wa Mtendere” Akhala “Zinthu Zonse kwa Aliyense”

1. Kodi Yesu Kristu akupereka chitsanzo ku zolengedwa zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi m’chiyani?

MWAMSANGA pambuyo pa chiukiriro chake, “Kalonga wa Mtendere” analankhula kwa mmodzi wa ophunzira ake kuti: “Ndikwera kumka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:17) Ndi mawu amenewo iye anavomereza kuti Atate wake wakumwamba analinso Mulungu wake, Iye yekha amene anamlambira. M’kulambira kotero iye anapereka chitsanzo kwa zolengedwa zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi.

2, 3. (a) Kodi ndimotani mmene 1 Akorinto 15:24-26, 28 amalongosolera chochita chapadera cha Yesu cha kudzigonjetsera kwa Atate ŵake? (b) Kodi chotulukapo chake chaulemerero chidzakhala chotani?

2 Ndichitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga chimene “Kalonga wa Mtendere” adzakhala kwa anthu onse angwiro pamene mokhulupirika adzigonjetsa mwa njira yapadera kwa Iye amene ali Mfumu yoyenerera ya chilengedwe chaponseponse! Zimenezi zidzasonyezedwa mosayerekezeka pamapeto a Kulamulira kwake kwa Zaka Chikwi pa anthu, pamene adzakhala atabwezeretsa mtendere, chisungiko, ndi chigwirizano padziko lonse lapansi. Muulosi wosalakwa, tikutsimikiziridwa za zimenezi:

3 “Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe. Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira atayika adani onse pansi pa mapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa. Ndipo pamene zonsezo zagonjetsedwa kwa iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.” (1 Akorinto 15:24-26, 28) Kapena monga momwe The Amplified Bible imamasulira mbali yomalizira ya vesi 28 kuti: “Kotero kuti Mulungu akhale zonse m’zonse—ndiko kuti, akhale chirichonse kwa aliyense, akhale wapamwamba, munthu wosonkhezera ndi wolamulira.”

4. (a) Kodi ndimotani mmene nzika za padziko lapansi zidzalabadirira ku chitsanzo cha atate wawo watsopano? (b) Kodi ndimbali yatsopano yotani ya chigonjero imene idzakhalapo panthaŵiyo?

4 Pamene “Kalonga wa Mtendere” apereka Ufumu kwa Mulungu wake pamapeto a Kulamulira kwa Zaka Chikwi, nzika za padziko lapansi zidzazindikira za chochitika chimenechi cha Atate wawo watsopanoyo. Ali naye monga Mfumu yopereka Chitsanzo, iwo mofananamo adzadzigonjetsera mwanjira yatsopano kwa Mulungu Wam’mwambamwamba. Tsopano kwanthaŵi yoyamba adzapereka chigonjero chachikondi mwachindunji kwa Yehova, inde, kulambira, kowona mtima konse ndi chowonadi, osafunikiranso utumiki wa wansembe Yesu, osati ngakhale popemphera.

5. Kodi mkhalidwe wa mafumu anzake a Yesu Kristu 144 000 udzakhala wotani?

5 Mwanjira imeneyi Mulungu Wam’mwabamwamba kachiŵirinso akhala Mfumu ya chilengedwe chaponseponse popanda woimira wake waufumu kumwamba kapena padziko lapansi. Mwachiwonekere mafumu anzake a Yesu Kristu okwanira 144 000 amene iye anawawombola padziko lapansi adzagwada pamaso pa Wolamulira Wachifumu wamkulu ndipo mwa lingaliro lowonjezereka limeneli adzamvomereza kukhala Mfumu ya Chilengedwe Chonse.

Chiyeso Chomaliza pa Anthu Onse

6. (a) Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa anthu osamvera mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu? (b) Kodi mkhalidwe wa amene Yesu awatembenuzira kwa Atate wake wakumwamba udzakhala wotani?

6 Kuti avomereze Yehova monga Woweruza wamkulu, Yesu Kristu ali ndi chikhumbo cha kufuna kuti chivomerezo cha Mulungu chofunika koposacho chisonyezedwe pantchito imene Yesu wakwaniritsa mkati mwa Kulamulira kwake kwa Zaka Chikwi. Mkati mwa kulamulira kumeneko, anthuwo amene anakana kuchita mogwirizana ndi malamulo achilungamo ndi amene anasonyeza kusamvera chifuniro cha Mfumuyo adzakhala atawonongedwa. Motero, awo amene Yesu Kristu akuwatembenuzira kwa Yehova Mulungu, Woweruza womalizira, adzakhala omvera amene afikira ungwiro waumunthu.

7. (a) Kodi nchiyani chimene chidzaikidwa pa chiyeso chofufuza Yesu atabwezera Ufumuwo? (b) Kodi anthu otukulidwira ku ungwiro adzayesedwa motani?

7 Panopa idzakhala nthaŵi ya kuyesedwa kwa mkhalidwe wachipiriro wa kudzipereka kwa anthu kwa Mfumu ya Chilengedwe Chonse, Yehova Mulungu. Monga momwe zinaliri m’nkhani ya Yobu, funsolo nlakuti: Kodi iwo amakonda ndi kulambira Mulungu kokha kaamba ka zinthu zonse zabwino zimene wawachitira, kapena kodi amamkonda chifukwa cha zimene iye ali mwa iye yekha—Mfumu Yoyenerera yachilengedwe chonse? (Yobu 1:8-11) Koma kodi ndimotani mmene anthu angwirowo adzayesedwera kukhulupirika kwa mtima? Baibulo limayankha: Satana Mdyerekezi ndi ziŵanda zake adzamasulidwa “kwakanthaŵi” kuchokera kuphompho limene akhala obindikiritsidwako kwa zaka chikwi. (Chivumbulutso 20:3) Mwa kulola Mdyerekezi kuyesa anthu obwezeretsedwa, mamembala a anthu otukulidwira ku ungwiro ngati angatsimikiziridwe ponena za umphumphu aliyense payekha kwa Mulungu m’lingaliro langwiro.—Yerekezerani ndi Yobu 1:12.

8. (a) Atamasulidwa kuphompho, kodi nchiyani chimene Satana ndi ziŵanda zake adzayesa kuchita? (b) Amene adzalola kuti asochezedwe ndi ziŵanda zake adzakhala atatenga mkhalidwe uti?

8 Zaka zikwi zisanu ndi ziŵiri zidzakhala zitapita, Satana Mdyerekezi anali wokhoza kunyenga Adamu ndi Hava angwirowo kuchimwa mwa kutenga njira yadyera. Malemba samanena kuti ndi njira zopereka ziyeso zotani zimene Yehova adzalola Satana ndi ziŵanda kugwiritsira ntchito pambuyo pa kumasulidwa kwawo kuchokera kuphompho. Koma mosakaikira padzakhala kusonkhezera dyera ndi chikhumbo cha kudzilamulira popanda Mulungu. Popeza kuti iye adzakhala wopandukirabe ufumu wa Yehova, Mdyerekezi adzakhala ndi chikhoterero cha kuchititsanso anthu kukhala opanduka. Mlingo weniweni wachipambano umene magulu auchiŵanda omasulidwa ameneŵa adzakhala nawo sukudziŵikanso, koma padzakhala anthu opanduka okwanira kuti awoneke kukhala khamu lalikulu. Kuchimwa kwa cholengedwa chirichonse chaumunthu, chimene tsopano chidzakhala changwiro, panthaŵiyo kudzachitidwa mwaluntha, ndipo chifukwa chake, kudzakhala kwadala, kolinganizidwa. Kudzatanthauza kupandukira kulambira kumodzi kokha kwa Mulungu wowona ndi wamoyo ndi kuima kumbali ya Satana Mdyerekezi. (Chivumbulutso 20:7, 8) Motero, m’chochitika cha opanduka amenewo, Yehova samakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”

9. (a) Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa awo amene sasunga umphumphu kwa Yehova Mulungu? (b) Kodi ndimotani mmene malo osawoneka adzachotseredwera opanduka onse? (c) Kodi ndimkhalidwe waulemerero wotani umene panthaŵiyo udzafunga kumwamba ndi padziko lapansi?

9 Komabe, okhulupirika, amakana kugonjera ku zigomeko ndi zitsenderezo za osochezedwa, autundu. Mosakaikira, okhulupirika amasankha kulola Yehova kukhala “zinthu zonse kwa aliyense” wa iwo. Kuti pakhale chilungamo, ufumu wa Yehova uyenera kugogomezeredwa mwamphamvu. Motero, opanduka onse a padziko lapansi osonkhezeredwa ndi Satana adzasesedwa kosatha. Adzawonongedwa kotheratu! Malo osawoneka achilengedwe nawonso ayenera kuchotseredwa opanduka onse. Motero, kuti kuyeretsedwa kwa chilengedwe chonse kumalizidwe, Satana Mdyerekezi ndi makamu ake onse a ziŵanda adzafafanizidwa kotheratu. Motero miyamba ndi dziko lapansi zidzachotseredwa kuipitsa kulikonse kwauchimo. (Chivumbulutso 20:9, 10) Chiyero cha Yehova chidzafunga kulikonse. (Yerekezerani ndi Zekariya 14:20.) Dzina lopatulika la Mulungu Wam’mwambamwamba lidzalemekezedwa kumwamba ndi padziko lapansi. Onse okhala kumwamba ndi padziko lapansi adzachita chifuniro chake chachikulu mwachisangalalo.

10. Kodi ndim’njira ziti m’zimene dziko lapansi lidzakhalira losiyana ndi mkhalidwe wa planeti lina lirilonse umene lidzakhala nawo ku umuyaya wonse?

10 Ku umuyaya wonse dziko lathu lapansi lidzakhala ndi kusiyana kumene palibe planeti lina m’mlengalenga mosatha monse lidzakhala, ngakhale kuli kwakuti dziko lapansi silingakhale planeti lokha limene lidzakhalidwapo ndi anthu. Mwapadera, iro lidzakhala kumene Yehova walemekezera ufumu wake wachilengedwe chonse motsimikizirika, akumakhazikitsa chitsanzo cha lamulo chosatha ndi cha chilengedwe chaponseponse. Lidzakhala planeti lokha limene Yehova Wamakamu adzakhala atamenyerapo ‘nkhondo yatsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ Lidzakhala planeti lokha ku limene Mulungu anatumizako Mwana wake wokondedwa koposa kukhala munthu ndi kufa kuti awonjole nzika za planetili ku uchimo ndi imfa. Lidzakhala planeti lokha limene Yehova adzakhala atatengako nzika zake 144 000 kukhala “oloŵa nyumba ake a Mulungu, ndi oloŵa nyumba anzake a Kristu.”—Aroma 8:17.

Aserafi, Akerubi, Angelo

11, 12. (a) Kodi ndizolengedwa zauzimu zotani zimene Yesaya anawona m’masomphenya? (b) Kodi nchikondwerero chotani chimene zimenezi ziri nacho mwa anthufe?

11 Mulungu, Magwero aulemerero a chilengedwe chonse, chakumwamba ndi cha padziko lapansi, adzafikira kukhala “zinthu zonse” osati kokha kwa oloŵa nyumba limodzi ndi Kristu okwanira 144 000 komanso kwa ena m’malo akumwamba. M’chaputala 6 cha bukhu la Yesaya, tikupatsidwa masomphenya ochepa amabwalo akumwamba. Mmenemo timaŵerenga kuti: “Ndinawona Ambuye atakhala pampando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala m’kachisi. Pamwamba pa iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; aŵiri anaphimba nawo nkhope yake, aŵiri nauluka nawo. Ndipo wina anafuula kwa mnzake nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wamakamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.”—Yesaya 6:1-3.

12 Ha Yesaya anayanjidwa kwakukulukulu chotani nanga kuti anawona Woyera koposa onse m’chilengedwe chonse atakhala pampando wake wachifumu wakumwamba akumatumikiridwa ndi aserafi aulemerero! Ndimasomphenya ochititsa mantha chotani nanga amenewo, osonyeza malo antchito oyanjidwa kwambiri amene aserafi amenewo ali nawo, chifukwa chakuti iye ali Woyera Koposayo amene kupatulika kwake anakutamanda pamene anachitira umboni chiyero chake mwa kugogomezera katatu! Aserafi ali okondwerera m’kuthandiza olambira a Yehova kukhala oyera monga momwe Mulungu aliri woyera.—Yesaya 6:5-7.

13. (a) Kodi ndizolengedwa zauzimu za mtundu wina ziti zimene Baibulo limativumbulira? (b) Kodi Yehova akulongosoledwa motani mogwirizana nazo?

13 Monga momwedi kuliri kuti pali zolengedwa zosiyanasiyana pano padziko lapansi, zimene zimasonyeza mphamvu ya Yehova Mulungu, mofananamo m’malo auzimu muli zolengedwa za mitundu ina. Baibulo limavumbula kuti zimenezi ndizo akerubi aulemerero, amene ayenera kukhala akumauluka liŵiro lofulumira kwambiri. (Salmo 18:10; yerekezerani ndi Ahebri 9:4, 5.) Genesis 3:24 amasonyeza kuti pambuyo pooti Adamu ndi Hava achimwira Mulungu wakumwamba woyerayo mwa kudya zipatso zoletsedwa, Mlengi anaimika akerubi chakummaŵa kwa njira yobwerera m’Paradaiso wachikondwerero amene anali ndi “lupanga lamoto la kuzungulira ponsepo.” Yehova akunenedwa kukhala ‘wokhala pakati pa akerubi.’ (Salmo 99:1; Yesaya 37:16) Motero iye amasonyezedwa kukhala akulamulira pamwamba pa akerubi.

14. (a) Kodi ndizolengedwa zauzimu za mtundu wina ziti zimene siziyenera kunyalanyazidwa? (b) Kodi ndizochuluka motani?

14 Amene sayenera kunyalanyazidwa pakati pamiyandamiyanda ya zolengedwa zauzimu ndiwo angelo. Pali mamiliyoni ambiri a iwo. (Danieli 7:9, 10) Pakati pawo pali angelo ogaŵiridwa kutumikira olambira a Yehova padziko lapansi. Yesu anachenjeza kuti palibe munthu amene ayenera kukhumudwitsa aliyense wa olambira a Yehova chifukwa chakuti “angelo awo apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wakumwamba.” (Mateyu 18:10; Ahebri 1:14) Pamapeto pamasiku okwanira 40 a Yesu osala kudya m’chipululu ndi pambuyo pa kugonjetsa kwake mwachipambano mayeso atatu ovuta obweretsedwa ndi Mdyerekezi, unali mwaŵi wotani nanga kuti angelo anatumikira zosoŵa zakuthupi za Yesu wofookayo ndi wanjala!—Mateyu 4:11.

15, 16. (a) Fotokozani chigwirizano chonga banja chimene chidzakhalapo kumwamba ndi padziko lapansi. (b) Kodi ndimphotho yochokera kwa Yehova yotani imene idzapatsidwa kwa anthu otukulidwira ku ungwiro amene apyola chiyesocho mwachipambano? (c) Kodi Yehova adzawona motani kufikiridwa kwa chifuno chake choyambirira?

15 M’malo akumwamba komweko, nzika zaulemerero zauzimu zidzakhala abale kwa wina ndi mnzake, pamene kuli kwakuti pano padziko lapansi banja laumunthu lotukulidwira kuungwiro lidzapangidwa kukhala abale ndi alongo kwa wina ndi mnzake. Iwo adzakhala m’chifanizo ndi chifanefane cha Mulungu kumlingo waukulu umene Adamu ndi Hava, anali nawo, pamene anali kungotuluka kumene m’manja olenga a Yehova Mulungu, ‘m’chifanizo ndi chifanefane,’ cha Mlengi wawo. (Genesis 1:26, 27) Pambuyo pa kupambana chiyeso chotsiriza, anthu otukulidwira kuungwiro adzapatsidwa kuyenera kwa kukhala ndi moyo kosatha ndipo mwachikondi adzalandiridwa monga “ana a Mulungu,” akumakondwera mu ufulu waulemerero, ndi kukhala mbali ya gulu la Yehova logwirizana kumwamba ndi padziko lapansi.—Aroma 8:21.

16 Ha ndichisangalalo ndi chimwemwe za anthu ake onse zotani nanga zimene Yehova Mulungu adzayang’ana nazo kufikiridwa kwa chifuno chake choyambirira—ntchito yake yosayerekezereka yakuti zinthu zonse zichitike mogwirizana ndi chifuno chake choyamba—zolengedwa zonse ziri muumodzi wosagaŵanika ndi iye!

17. Polingalira zonse zimenezi, kodi ndani amene sangakhoze kukana kuchita chiyani, mogwirizana ndi mawu a wamasalmo?

17 Polingalira zonse zimenezi, kodi ndani amene adzakhoza kukana kulemekeza Wolinganiza waumulungu wodabwitsayo? Akumalunjikitsa mawu ake moyenerera ku zolengedwa zapamwamba koposa munthu, wamasalmoyo amati: “Lemekezani Yehova, inu angelo ake; amphamvu zolimba, akuchita mawu ake, akumvera liwu la mawu ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa iye.”—Salmo 103:20, 21.

18. Kodi wamasalmo amatsiriza motani bukhu la Masalmo?

18 Wamasalmo wosangalala, wouziridwa akumaliza bukhu la Masalmo mwa mawu aŵa achilimbikitso: “Haleluya. Lemekezani Mulungu m’malo ake oyera; mlemekezeni m’thambo lamphamvu yake. Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunyinji. Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze. Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang’ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira zazingwe ndi chitoliro. Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa. Zonse zakupuma zilemeke Yehova. Haleluya.”—Salmo 150:1-6.

19. (a) Kodi ndim’chomangira chotani chimene pamenepo chilengedwe chonse chidzagwirizanitsidwiramo? (b) Kodi, kwenikweni, zolengedwa zonse zaluntha, zidzanenanji?

19 Potsirizira chilengedwe chonse chidzakhala chogwirizana m’chomangira changwiro chimene chidzakhala kuumuyaya wonse, chomangira cha kulambiridwa kumodzi kwa Atate wakumwamba chifukwa chakuti ana ake amamkonda ndi kumlemekeza koposa zinthu zonse. Inde, pamenepo kudzachitika kuti zolengedwa zonse zanzeru zidzati, kwenikweni, monga momwe aserafi ananenera: “Woyera, woyera, woyera, Yehova wamakamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.” Ndithudi, pamenepo, Mulungu wa “Kalonga wa Mtendere” adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense”—kunthaŵi zanthaŵi.

[Chithunzi pamasamba 188, 189]

Chilengedwe chonse chidzakhala chogwirizana m’kulambiridwa kwamtendere kwa Mfumu ya Chilengedwe Chonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena