Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • hs mutu 2 tsamba 16-34
  • Mzimu Woyera Ukugwira Ntchito m’Malo Osaoneka a Kumwamba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mzimu Woyera Ukugwira Ntchito m’Malo Osaoneka a Kumwamba
  • Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MISONKHANO YA ANTHU AUZIMU KUMWAMBA
  • “MWANA WOBADWA YEKHA”
  • MALO OSAONEKA A NTCHITO
  • Masomphenya a Zinthu Zakumwamba
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Mulungu wa “Kalonga wa Mtendere” Akhala “Zinthu Zonse kwa Aliyense”
    Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Magwero Oposa Munthu a Mzumu Woyera
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Kumwamba
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
hs mutu 2 tsamba 16-34

Mutu 2

Mzimu Woyera Ukugwira Ntchito m’Malo Osaoneka a Kumwamba

1. Kodi n’chifukwa ninji kuli kofunika kwa ife kudziwa m’mene mzimu woyera wagwirira ntchito m’malo osaoneka akumwamba?

MUNTHU angaone kukhala wokondweretsedwa kwambiri ndi m’mene mzimu woyera wa Mulungu umagwirira ntchito m’malo ooneka ndi akuthupi kapena chilengedwe monga momwe munthu akuchidziwira. Komabe, zimene zachitika m’malo osaoneka, akumwamba zayambukira kwambiri zochitika za anthu. M’mene mzimu woyera uyenera kuyendetsedwera posachedwapa m’tsogolo muno, m’kati mwa mbadwo wathu, kukugwirizanitsidwa ndi chimene chikuchitika m’malo osaoneka ndipo chiri chofunika kwambiri kwa munthu. Chifukwa cha chimene’cho tiyenera kufuna kuzindikira m’mene mzimu woyera umagwirira ntchito m’njira yofunika kwambiri kwa ife motero’yo tsopano.

2. Kodi ndi m’njira yotani imene Salmo 104:29, 30 limasoyezera m’mene anthu akhalira odalira pa malo osaoneka akumwamba?

2 Munthu wa maganizo achimakono sangakonde kukubvomereza, koma athu ali odalira pa malo osaoneka akumwamba. Ngati Mulungu Mlengi akanatifulatira pa dziko lapansi pano, akumakhala “wakufa” kwa ife, kunena kwake titero, kodi ife tikanakhala chiani? Wamasalmo a Baibulo ananena molondola pamene iye kwa Mulungu anati: “Mukabisa nkhope yanu, ziopsyedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, nizibwerera kupfumbi kwao. Potumizira mzimu wanu, zilengedwa; ndipo mukonza’nso nkhope ya dziko lapansi.” (Salmo 104:29, 30) Chifukwa cha chimene’cho phunziro lalikulu kwa munthu sindiro munthu iye mwini, koma, m’malo mwake, Mlengi, Mulungu. Malinga ngati Mulungu ali wokondwera kutibvumbulira kanthu kena ponena za malo akumwamba osaoneka, kameneka kwakukulu-kulu kakufunikira kuphunziridwa ndi ife.

3. Kodi n’chifukwa ninji kukakhala kusaona patali ndi kusalingalira bwino kwa ife kulingalira kuti Mulungu amakhala yekha ndi wopanda nalo okhala omuyenerera kumwamba?

3 Tiyeni nthawi zonse tikumbukire kuti “Mulungu ndiye Mzimu,” kapena, “Mulugu ndi mzimu” (Yohane 4:24, NW, ndi mau a m’mphepete) Mofananamo, iye amakhala m’malo a mizimu. Yekha-yekha, ndi wopanda malo okhala omuyenerera? Ai! Kukakhala kusaona patali ndi kusalingalira kwa ife kuyerekezera kuti Mulungu angalenge kokha zinthu zakuthupi zooneka kwa ife ndipo sanalenge’nso zinthu m’malo osaoneka akumwamba. Zinthu za malo apamwamba kwambiri zotero’zo zikakhala zopangika ndi zinthu zapamwamba kwambiri koposa zija za chilengedwe chakuthupi chimene anthufe tiri mbali yake.

4. Kodi n’chifukwa ninji malo osaoneka akumwamba samadalira pa dzuwa lathu’li kaambaka kuunika?

4 Pamene tilingalira zinthu zonse zodabwitsa ndi zokongola zimene Mulungu waziika pano m’malo a zinthu zakuthupi, zimatichititsa mantha kwambiri pamene tiyesa kulingalira zinthu zones zodabwitsa ndi zaulemerero zimene iye wazilenga m’malo auzimu. Kulibe kudalira pa kuunika kwa dzuwa la mapulaneti athu kumwamba’ko. Kulibe usiku kumene’ko! Mlengi wa zounikira zopatsa kuunika iye mmwini ali Dzuwa lakumwamba, magwero a kuunika. Kwenikweni ndi mophiphiritsira ndi mwamakhalidwe, n’zoona kuti: “Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.” (1 Yohane 1:5) Kalekale asananenedwe mau onenedwa ndi wolemba Baibulo Yohane, wamasalmo analongosola Mlengi kukhala wokondweretsa mofanana ndi kuwala kwa dzuwa la pa usana, pamene iye analemba kuti: “Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.”—Salmo 84:11.

5. Kodi Mulungu ali ndi anthu a mtundu wotani m’malo osaoneka akumwamba, ndipo kodi ndi motani m’mene iwo amasiyanira ndi anthu?

5 Sikuli chabe koyenera kukhulupirira motero, koma Baibulo Loyera lenileni’lo limachitira umboni kuti Mulungu ali nawo limodzi m’malo a mizimu osaoneka anthu anzeru opangidwa ndi matupi auzimu. Iye angathe kukambitsirana ndi amene’wa mwachindunji. Iwo angathe kumuona monga momwe’di iye amawaonera. Pokhala okhala ndi mpangidwe wapamwamba kwambiri, woposa anthu, ponena za mathupi ao, iwo samasungunuka, kuphwanyika, kuonongedwa pa kumuona chabe. Iwo angathe kulankhulana naye mwachindunji, akumatumikira pamaso pake penipeni. (Luka 1:19) Osati kwa angelo, koma kwa anthu, Mulungu anati: “Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.” (Eksodo 33:20) Chotero Mulungu ananena ngakhale kwa mneneri wake Mose.

6. Malinga ndi kunena kwa Cibvumbulutso 4:11, kodi ndi motani m’mene anzake auzimu a Mulungu amene’wo anafikira kumene’ko?

6 Kodi anzake auzimu a Mulungu amene’wo anakhala kumene’ko motani? Eya, kodi ndi motani m’mene anthu awiri oyamba okwatirana anadzera pano? Tidzdatenga yankho monga momwe linaperekedwera ndi awo amene wolemba Baibulo Yohane anawaona m’masomphenya, akulambira Mulungu kumwamba. Tikugwira mau ao awa: “Inu muli woyenerera, Ambuye ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero, ulemu, ndi mphamvu, pakuti munalenga zinthu zonse; mwa chifuniro chanu izo zinakhalako ndipo zinalengedwa.”—Chibvumbulutso 4:11, An American Translation.

7, 8. Pa tsiko la chiukiriro, kodi n’chiani chimeneYesu ananena kuti mzimu ulibe, ndipo kodi iye anachita nalonji thupi limene iye anaonekera nalo?

7 Mulungu analenga anthu awiri oyamba okwatirana a thupi ndi mwazi. Kumene’ku kusanachitike, Mulungu anapanga anzake akumwaba auzumu, okhala ndi kapangidwe kapamwamba koposa kaja ka munthu. Ponena za nkhani imene’yi, Yesu Kristu ananena mau omveketsa pa tsiku la kuukitsidwa kwake kwa akufa. Iye anaonekera kwa ophunzira ake m’chipinda chotsekedwa m’Yerusalemu. Kuti achite zimene’zi, iye anaonekera atabvala thupi lofanana ndi lija limene iye anafa nalo, koma iwo analingalira kuti anali kuona mzimu. Eya, kodi ananenanji kwa iwo? Izi: “Mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, monga muona ndiri nazi Ine.”—Luka 24:36-39.

8 Pambuyo pa kukambitsirana ndi ophunzira ndi odabwa’wo, Yesu woukitsidwa’yo anazimiririka. Iye anabvula thupi kapena anasungunula thupi laumunthu lobvekedwa zobvala’lo. Iye sanamke ndi thupi limene’lo ndi zobvala zake kumka nazo ku malo a mizimu. Kukanakhala kothekera kuchita motero, kukanatanthauza kuti munthu wauzimu kumwamba ali ndi mnofu ndi mafupa, ngakhale’nso ponena za Yesu Kristu wolemekezedwa’yo.—1 Akorinto 15:50.

9. Mwchindunji kodi Mululngu analenga ndi thupi lotani anzake akumwamba’wo?

9 Polingalira zenizeni zonse’zi, Ambuye Mulungu anapanga anzake akumwamba’wo mwachindunji kukhala mizimu. Iye sanasamutse zolengedwa zaumunthu za mnofu, mwazi ndi mafupa kuchokera pa dziko lapansi kukagwirizana naye ku malo osaoneka a kumwamba. Pofotokoza mtunda wa anthu umene Mulungu analenga mwachindunji kumwamba, mtumwi Wachikristu Paulo akulemba kuti: “Ayesa angelo ake mizimu, ndi om’tumikira Iye akhale lawi lamoto.” (Ahebri 1:7) Panopo mtumwi Paulo anali kugwira mau wamasalmo Davide pamene iye akunena za Yehova Mulungu kukhala “akupanga angelo kukhala mizimu, atumiki ake moto wonyeketsa.” (Salmo 104:4, NW) Chifukwa cha chimene’cho, umboni wa Mau olembedwa a Mulungu ndiwo wakuti iye ali ndi mphamvu ya kulenga zolengedwa zauzimu kudza’nso zolengedwa zaumunthu.

10. Kodi ndi motani m’mene Genesis 1:26 amasonyezera kuti kulengedwa kwa anthu auzimu kunayambirira kuja kwa zolengedwa zaumunthu?

10 Kulengedwa kwa zolengedwa zauzimu kukuyambirira kulengedwa kwa zolengedwa zaumunthu. Mau a Mulungu monga momwe abvumbulidwira kwa ife m’chaputala choyambirira cha Baibulo amasonyeza chimene’chi. Kumene’ko timawerenga kuti: “Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa ng’ombe, ndi pa dziko lonse lapansi.” (Genesis 1:26) Tsopano, pamene Mulungu ananena kuti, “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu,” iye sanali kulankhula yekha monga ngati kuti iye anali mulungu wa awiri mwa mmodzi kapena mulungu wa atatu mwa mmodzi. Iye anali kulankhula kwenikweni ndi munthu wina wake wakumwamba wapayekha ndi wolekana ndi iye ndipo iye anali kupempha munthu wauzimu amene’yo kugwirizana naye m’kupanga zolengdwa zaumunthu, za pa dziko lapansi.

11 Kodi ndi motani m’mene Yobu 38:1-7 amasonyezera kuti panali anthu ambiri limodzi ani Mulungu pa nthawi ya kulengedwa kwa munthu?

11 Komabe, pa ntawi ya kulengedwa kwa mwamuna ndi mkazi, panali anthu auzimu ambiri ogwirizana ndi Mulungu. Panali anthu auzimu amene Mulungu anawalenga ngakhale dziko lapansi lisanalengedwe. Chenicheni chimene’chi chinauzidwa kwa Yobu wokhulupirika wa dziko la Uzi. pamene Mulungu ananena kwa iye kuti: “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira. Analemba malire ake ndani, popeza udziwa? . . . Kapena anaika ndani mwala wake wa pangondya, muja nyenyezi za m’mawa zinayimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anapfuula ndi chimwemwe?” (Yobu 38:1-7) Zimene’zo zinachitika zaka mazana ambiri mbali yotsirizira ya tsiku lakulenga lachisanu ndi chimodzi la Mulungu isanafike, pa nthawi imene Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi. (Genesis 1:27-31) Chifukwa cha chimene’cho “ana a Mulungu” osangalala amene’wo sanali zolengedwa zimene pa nthawi ina zinali pa dziko lapansi monga anthu ndipo pambuyo pake n’kusamutsiridwa pamaso pa Mulungu kumwamba. Iwo anali zolengedwa zauzimu kuyambira pa chiyambi chao cha kukhalapo.Mulungu sanadzaze konse miyamba ndi anthu ochokera pa dziko lapansi.

12. Kodi ndi motani anthu ndi angelo aliri poyerekezera ponena za mkhalidwe ndi mphamvu?

12 “Ana a Mulungu” onga mulungu amene’wo ali apamwamba kwambiri kwa munthu. Chifukwa cha chimene’cho wamasalmo Davide, atatha kuzindikira upamwamba wa Mulungu koposa miyamba, anapitirizabe kunena kuti: “Munthu ndani kuti mum’kumbukira? ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye? Pakuti munam’chepsya pang’ono ndi anthu onga Mulungu.” (Salmo 8:4, 5) Kodi ndani amene ali “anthu onga mulungu” amene’wo? Iwo ndiwo angelo, pakuti wolemba Baibulo, pofotokoza Salmo 8:5, amati, mu Ahebri 2:6-9: “Munam’chepsya pang’ono ndi angelo.” Chotero ponena za ukulu wa mkhalidwe wa kukhalako ndi mphamvu, munthu ali wotsika mosasinthika koposa “ana a Mulungu” amene’wo angelo akumwamba amene’wo.

MISONKHANO YA ANTHU AUZIMU KUMWAMBA

13. Kodi tukupeza kuti cholembedwa choyambirira chonena za misonkhano yakumwamba, ndipo pa imene’yi kodi ndani anatsogolera?

13 Misonkhano ya “ana a Mulungu” amene’wo imachitika nthawi ndi nthawi ndipo Mulungu Wam’mwambamwamba amaitsogoza. Iye wabvumbula chenicheni chimene’cho kwa ife m’Mau ake olembedwa. Zolembedwa zoyambirira zimene tikuzipeza za misonkhano yakumwamba yotero’yo zalembedwa m’machaputala awiri oyambirira a Yobu. “Ndipo” kuchiyambiyambi kwa moyo wa Yobu, “panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudzionetsera kwa Yehova, nadza’nso Satana pakati pao. Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m’ dziko ndi kuyandayenda m’mwemo.” Mavesi ena a pambuyo pake, m’chaputala chotsatirapo msonkhano wina’nso wa Yehova ndi ana ake akumwamba ukusimbidwa, ndipo kachiwiri’nso munthu wauzinu wochedwa Satana akugwiritsira ntchito mwai’iwo. (Yobu 1:6, 7; 2:1, 2) Misonkhano imene’yo, yosaonedwa ndi maso athu, iri ndi chifuno, ndipo Mulungu Wamphamvuyonse amasungitsa chilongosoko pa iyo. Onse ofikapo ayenera kuyankha kwa iye ponena za kumene iwo ali ndi ntchito zao. Ngakhale munthu wochedwa Satana anayenera kukhala waulemu, ngakhale kuli kwakuti iye ali chimene dzina lake limam’sonyezsa iye kukhala, wotsutsa Yehova Mulungu wapadera.

14. Kodi ndi msonkhano wakumwamba wotani umene ukuchulidwa mu Ahebri 12:22, 23?

14 Ponena za misonkhano ya “ana a Mulungu” auzimu yotero’yo kumvamba, tikuwerenga’nso, mu Ahebri 12:22, 23 kuti: Inu, Akristu Achibebri, “mwayandikira ku phiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo. Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo ndi kwa msonkhano wa onse.” Unyinji wonse wochuluka wa angelo’wo, umene ukukhalabe wokhulupirika kwa Atate wao wakumwamba ndi kukana kutsanzira Satana, umapanga banja limodzi lalikulu lakumwamba la Mulungu.

15. Kodi ndi motani m’mene Paul akuchulira banja lakumwamba lotero’lo mu Aefeso 3:14, 15, ndipo kodi ndi unansi wotani umene ziwalo ziri nawo kwa wina ndi mnzake?

15 Wolemba Baibulo Paulo akuchula banja lakumwamba limene’li. Polembera kalata Akristu amene amazindikira Yehova Mulungu monga atate wao wakumwamba, Paulo akunena kuti: “Chifukwa cha ichi ndipinda maondo anga kwa Atate, amene kuchokera kwa Iye pfuko lonse la m’mwamba ndi la padziko alicha dzina.” (Afeso 3:14, 15) Banja liri lonse limatenga dzina lake kwa atate wake, ndipo liyenera kumakhala mogwirizana ndi ulemu ndi kuyenera kwa dzina limene’lo. Pokhala ndi Atate mmodzi yekha, “ana a Mulungu” akumwamba ali onse abale.

16. Kodi ndi msonkhano wakumwamba wotani umene mneneri Mikaya anauona m’masomphenya m’mbali yotsirizira ya zaka za zana lakhumu B.C. E.?

16 Msonkhano wakumwamba unchitika cha kumapeto kwa zaka za zana lakhumi Nyengo yathu Ino isanakhale. Mneneri Wachiisrayeli Mikaya anaona masomphenya a uwo. Poulongosola, Mikaya kwa mafumu awiri ogwirizana, Ahabu ndi Yehosafati anati: “Tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse la Kumwamba liri chiriri m’mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere. Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Gileadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti, Pamenepo mzimu wina unatuluka, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzam’nyenga ndine.”—Mafumu 22:19-21.

17. Kodi gulu lankhondo lokhala pambali pa Mulungu pa nthawi imene’yo linapangidwa ndi anthu a mtundu wotani?

17 Tiyeni tizindikire kuti mngelo amene anatulutsa njira yopambana yopusitsira Mfunu yoipa Ahabu kuti akaonongedwe m’nkhondo akuchewa “mzimu.” Chimene’chi chikutanthauza kuti “khamu” lonse’lo ku dzanja lamanja ndi ku dzanja lamenzere la Mulungu mofananamo liri mizimu, inde, zolengedwa zauzimu za nzeru. Izo zikusiyanitsidwa ndi zolengedwa zaumunthufe.

18, 19. Kodi ndi bwalo la milandu lotani lakumwamba limene Danieli analiona m’masomphenya, lolinganizidwira zaka zathu za zana la makuni awiri?

18 Kodi anthu a lero linofe tikudziwa chenicheni chakuti bwalo la milandu linalinganizidwa kalekale kumwamba m’kati mwa zaka zathu za zana la makumi awiri zino? Masomphenya ozizwitsa anaperekedwa kwa mneneri Daniel pamene iye anali kapolo womangidwa m’Babulo zoposa zaka zikwi ziwiri kudza mazana asanu zapita’zo. M’kulongosola kwake amene’wa iye akulemba kuti:

19 “Pambuyo pake ndinaona m’masomphenya a usiku, ndi kuona chirombo chachinai, choopsya ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, . . . Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, . . . zikwi zikwe anam’tumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabukhu anatsegulidwa . . . Ndinaona m’masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumvamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anam’yandikizitsa pamaso pake. Ndipo anam’patsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse am’tumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.”—Daniel 7:7-14.

20. Kodi ndi mwana wakumwamba wa Mulungu uti amene ali wolemekezedwa kopambana monga munthu wonenedwa kukhala “mwana wa munthu” m’masomphenya a Danieli?

20 Kodi kumwamba kuli mwana wa Mulungu wauzimu ali yense amene akulemekezedwa kwambiri mofanana ndi uyu amene akuonekera m’masomphenya a Danieli monga “mwana wa munthu”? Ai! Nanga, kodi, iye ndani? Wamasalmo akum’dziwikitsa. M’Salmo 89:26, 27 iye amati: “Iye adzandichula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa. Inde ndidzamuyesa mwana wanga wayamba, womveka wa mafumu a pa dziko lapansi. Mau a Yehova amene’wa sakunena Mfumu Davide, amene Mulungu anapangana naye pangano la ufumu wosatha mu mzera wa banja lake lachifumu, kapena’so wolowa ufumu wa Davide, Solomo. Palibe ali yense wa mafumu amene’wa amene anali ana oyamba kubadwa a atate ao. (Salmo 89:27-37; 2 Samueli 7:4-17) Zenizeni za pambuyo pake zimasonyeza kuti Yehova anali kunena molosera kwa ‘mwana wake woyamba kubadwa’ kumwamba, Mwana amene anakhala naye kwa nthawi yosadziwika Yehova Mulungu asanalenge munthu.

21. Malinga ndi kunena kwa Chibvumbulutso 3:14, kodi Mulungu anali ndi mkazi wakumwamba pa nthawi imene iye anabala mwana wake “woyamba kubadwa”?

21 Mwachibadwa munthu wina angafunse kuti, Kodi ndi motani m’mene Mulungu angakhalire ndi ‘mwana woyamba kubadwa,’ pamene Iye analibe mkazi kumwamba pa nthawi imene’yo? M’kuyankha funso limene’lo, munthu amene anatsimikizira kukhala ‘woyamba kubadwa’ akudzinenera yekha. M’bukhu lotsirizira la Baibulo, m’Chibvumbulutso 3:14, iye akuti: “Izi anena Amenyo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu.” Wonena mau amene’wo anali Ambuye Yesu Kristu, woukitsidwa ndi wolemekezedwa, amene ali “mboni yokhulupirika ndi yoona” ndi amene samanama ponena za nkhani’yo. Iye mwini akunena kuti iye ndiye “woyamba wa chilengo cha Mulungu.” Chotero Mulungu sakanakhala ndi mkazi uyo amene Iye anam’lenga choyamba asanalengedwe.

22. Kodi Yesu, ngakhale kuli kwakuti anali cholengedwa, ananena za Mulungu kukhala chiani kwa iye?

22 Ngakhale kuli kwakuti iye ali “cholengedwa” ndipo osati mwana wokhala ndi amai, Yesu mosalekeza amanena za Mulungu kukhala Atate wake. (Chibvumbulutso 3:21; 14:1) Iye amanena’nso za Atate wake kukhala Mulungu wake. M’Chibvumbulutso 3:12 iye amati: “Iye wakulakika, ndidzam’yesa iye mzati wa m’Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo . . . ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga.” Zimene’ zi zikugwirizana ndi zimene iye ananena pa tsiku la chiukiriro chake kwa Mariya wa Magadala pafupi ndi manda apululu kuti: “Pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:17) Zimene’zi zinali pa Nisani 16, 33 C.E., tsiku lachitatu kuyambira pamene iye anapfuula pa mtengo wozunzirapo pa umene iye anakhomeredwa kuti afe: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?” Ndipo, potsirizira pake: “Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga.”—Mateyu 27:46; Marko 15:34; Luka 23:46; Salmo 22:1; 31:5.

“MWANA WOBADWA YEKHA”

23. M’kukhala “Mwana wobadwa yekha,” wa Mulungu, kodi Yesu Kristu akakhala pati m’ndandanda ya zolengedwa za Mulungu?

23 M’mau onenedwa kwa wolamulira Wachiyuda Nikodemo, kodi Yesu Kristu ananena za iye mwini kukhala yani? Mvetserani: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wasatha.” (Yohane 3:16) M’kunena za iye mwini monga “Mwana wobadwa yekha” wa Mulungu iye anali kudzisonyeza iye mwini kukhala “mwana woyamba kubadwa” wa Mulungu. Kulenga kwachindunji kwa Mulungu kosathandizidwa kwa zinthu zochokera m’zinthu zimene kulibe kunayamba ndi kutha ndi “mwana woyamba kubadwa” amene’yu, “Mwana wobadwa yekha.” Kuphatikiza pa kudzicha kwa Yesu “chiyambi cha chilengo cha Mulungu,” mtumwi Paulo akuonjezera dzina lofanana’lo kwa iye, kuti: “Amene ali fanizo la Mulungu wosaoneka’yo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Chotero, Mulungu atalenga “woyamba wa chilengedwe chonse,” zinthu zina zonse zimene zinakhalako pambuyo pake zinali zolengedwa zina. Polenga zinthu zina zonse’zo, Mulungu anagwiritsira ntchito “Mwana wake wobadwa yekha.”

24. Malinga ndi kunena kwa Akolose 1:15, 16 ndi Yohane 1:1-3, kodi zinthu zina zonse zinalengedwa ndi Mulungu mwa njira ya yani?

24 M’kuchitira umboni lingaliro limene’li, mtumwi Paulo choyamba akuchula “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse” ndiye kenako akupitiriza kunena kuti: “Pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaoneka’zo.” (Akolose 1:16) Tsopano tingathe kumvetsetsa mau a mtumwi Yohane mu Yohane 1:1-3, NW “Pachiyambi panali Mau, [Chigriki, Logos], ndipo Mau’yo [Logos] anali Mulungu. Amene’yu anali pachiyambi ndi Mulungu. Zinthu zonse zinakhalako kupyolera mwa iye, ndipo popanda iye palibe ngakhale chinthu chimodzi chinakhalako.” M’bukhu lotsirizira la Baibulo, lolembedwa’nso ndi Yohane, iye akutiuza kuti Yesu Kristu wolemekezedwa’yo ali ndi dzina lakuti “Mau a Mulungu,” osati Mulungu Mau: “Ndipo achedwa dzina lake, Mau [Logos] a Mulungu.” Chibvumbulutso 19:13.

25. Kodi n’chifukwa ninji ndipo ndi m’njira yotani Logos analiri ndi “kupambana”?

25 Pa uyo wochedwa “chiyambi cha chilengo cha Mulungu” panaperekedwa ulemu ndi zoyenera za “woyamba kubadwa” wa Mulungu, “Mwana wobadwa yekha.” Monga Mwana “woyamba kubadwa,” amene’yu anali wopambana pa “ana a Mulungu” onse a m’tsogolo. (Akolose 1:18) Chimene’chi chikuphatikizapo kugwirizanitsidwa kwake ndi Atate wake wakumwamba m’kuchititsa zinthu zina zonse kukhalako kumwamba ndi pa dziko lapansi.

26. Kodi ndi chifukwa ninji zolengedwa zauzimu zimene zinachititsidwa kukhalako mwa njira ya Logos sizikuchewa ana ake?

26 Pamene Mau kapena Logos anagwiritsiridwa ntchito monga njira mwa imene “ana a Mulungu” onse osawerengeka anachititsidwira kukhalako, mzimu woyera wochokera kwa Mulungu Atate wake unayenera kukhala utagwira nchito mwamphamvu kwambiri pa iye ndi kupyolera mwa iye. Uwo unali naye ndipo unali kum’gwirira ntchito. Mkhalidwe wa kugwira kwake ntchito uyenera pa nthawi imene’yo kukhala unali wofanana ndi pambuyo pake pamene iye anakhala munthu wangwiro pa dziko lapansi nachita machiritso ozizwitsa. Chotero, iye ananena kuti iye anachotsa ziwanda mwa njira ya mzimu wa Mulungu. (Luka 11:20; Mateyu 12:28) Chifukwa chakuti mzimu wa Yehova Mulungu mofananamo unagwira ntchito mwa njira ya Logos kumwamba’ko, “ana a Mulungu” amene’wo amene anachititsidwa kukhalako kupyolera mwa iye amalingalira, osati iye, koma Yehova Mulungu kukhala Mlengi ndi Atate wao. Iwo samachedwa ana a Logos. Iwo akuchewa “ana a Mulungu woona.”—Yobu 1:6; 2:1; 38:7.

27. Pa kulengedwa kwa munthu, kodi Mulungu ananena kwa yani, kuti, “Tiyeni,” ndipo kodi n’chifukwa ninji Iye anali woyenerera kunena zimene’zi?

27 Chifukwa cha chimene’cho, tsopano kuli koonekera bwino, kuti pamene Mulungu ananena pa tsiku lake la kulenga lachisanu ndi chimodzi, “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu,” iye anali kulankhula ndi “woyamba kubadwa” wake, ndi “Mwana wake wobadwa yekha.” Genessis 1:26-31) Mulungu angakhale atanena’nso kuti “Tiyeni” kwa Mwana wake pamene Mulungu analingalira kulenga angelo akumwamba, kuphatikizapo akerubi ndi aserafi. Yehova Mulungu monga Wam’mwambamwamba ndi Mlengi wa zinthu zonse anali Uyo wolingalira ponena za chimene chiyenera kupangitsidwa kukhalako. Angelo anayenera kukhala ana Ake. Monga woyembekezera kukhala Atate, iye anachita monga momwe anafunira ponena za nthawi imene iye anayenera kukhala ndi ana akumwamba auzimu. Mzimu wake unali mphamvu yokha yogwira nchito mwa imene zinthu zina zikapangitsidwa kukhalako.

28. Kodi ndi “ana a Mulungu” otani amene Adamu ndi Hava othamangitsidwa’wo anawaona pa chipata cha munda’wo, ndipo kodi n’chiani chimene chinayendetsa lupanga lozungulirazungulira’lo pamenepo?

28 M’kupita kwa nthawi “ana a Mulungu” aukerubi anaonekera pa chipata cha Munda wa Edene. Kodi n’chifukwa ninji? Eya, anthu awiri oyamba okwatirana, Adamu ndi Hava, anapandukira Mulungu ndipo anathamangitsidwa m’malo ao okhala a Paradaiso. Chotero Akerubi anaikidwa pa chipata cha munda’wo kuletsa awiri ochimwa’ wo kubwereramo kukayesa kupikisula chilango cha imfa. (Genesis 3:24) Chimene Adamu ndi Have anaona chinali akerubi obvala thupi. ‘Lupanga limene linali kumazungulirazungulira’pa chipata cha munda’wo ndithudi linali kumayendetsedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, kuingitsa anthu osalungama.

29. Kodi ndi ana a Mulungu a mtundu wotani amene Yesaya anawaona m’masomphenya, ndipo pambuyo pake, kodi Ezekieli anaona mtundu wotani?

29 M’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E. mneneri Yesaya anaona m’masomphenya “ana a Mulungu” auserafi. Aserafi amene’wa anali kutumikira Yehova Mulungu m’kachisi mwake. (Yesaya 6:1-7) Zaka za zana lotsatirapo, meneri Ezekieli m’Babulo anapatsidwa masomphenya mu amene iye anaona “ana a Mulungu” aukerubi.—Ezekieli 1:1-25; 9:3; 10:1-20; 11:22.

30, 31. Kodi n’chiani chimene chimasonyeza kuti akerubi ali aliwiro kwambiri m’kuuluka pamene Mulungu awatuma pa maulendo, ndipo kodi iwo ndi ogwirizanitsidwa ndi boma lotani?

30 Akerubi’wo, monga “zolengedwa zamoyo,” ayenera kukhala othamanga kwambiri m’kuuluka pamene Mulungu awatuma ndi mauthenga. Chotero, moyankha pempho lopempha chitandidzo kwa Mulungu, “anaberekeka pa kerubi, nauluka; nauluka msanga pa mapiko a mphepo.”

31 Mwachionekere m’malo okhala mizimu mitunda yaikulu kopambana iyenera kuyendedwa m’nthawi yaifupi. Kutalikira sikunalepheretse chithansizo chamwamsanga kudza kwa Mfumu Hezekiya ya Yerusalemu atapita ku kachisi pa nthawi ya bvuto la mtundu wonse. Iye anapemphera kuti: “Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi.” (Yesaya 37:14-37) Akerubi ali ogonjera kwa Yehova Mulungu, monga ngati kuti iye anakhala pamwamba pao; ndipo iwo adzagwirizanitsidwa ndi ufumu wake umene uyenera kudzetsa mpumulo wofululumira kwa anthu onse m’kusaukasauka kwao kwakukulu kopambana. Ogwirizana ndi chenicheni chadalitso chimene’chi ndiwo mau oyambirira a salmo lolosera akuti: “Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.” (Salmo 99:1; ndipo’nso 80:1) Malo apamwamba a Yehova mogwirizana ndi akerubi anasonyezedwa m’likasa la chipangano limene mneneri Mose analamulidwa kukhoma.—Ahebri 9:5.

32. Kodi ndi motani m’mene malo a Yehova ponena za akerubi anasonyezedwera m’chochitika cha likasa lagolidi lokhomedwa ndi Mose?

32 Likasa la golidi kapena bokosi limene’li linagwiritsiridwa nchito monga mosungira zinthu zopatulika. Linali ndi chobvundikirira choikidwa akerubi awiri agolidi pamwamba pake ofunyulula mapiko kuphimba chotetezerapo. Pamene likasa limene’li linaikidwa m’Chipinda Chopatulikitsa la chihema kapena kachisi, kuwala kozizwitsa (kuwala kwa Shekinah) kunaonekera pamwamba pa mapiko a akerubi’wo. (Eksodo 25:10-22; 2 Mafumu 19:15) Motero Yehova anasonyezedwa kukhala akukhala pampando pamwamba pa akerubi ndi kupereka zilangizo ali pamenepo. Mose akusimba za chokumana nacho cha iye mwini m’nkhani imene’yi, pamene iye akulemba kuti: “Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva Mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chiri pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiri’wo; ndipo ananena naye.”—Numeri 7:89.

MALO OSAONEKA A NTCHITO

33. Kodi ndi chifukwa ninji kumwamba kuyenera kukhala malo a ntchito yaikulu kwambiri yoposa ija imene ikuchitika pa dziko lonse lapansi lero lino?

33 Kumwamba sindiko malo ongokhala osagwira ntchito ndi kumangoyenda gwebegwebe, monga ngati kugwedezagwedeza mapazi ake m’mphepete mwa mtambo woyenda pang’onopang’ono. Munthu wokangalika kopambana m’malo onse okhalidwa, Paphata pa nyonga yonse yaikulu kwambiri, ali kumene’ko! Mzimu wake woyera monga mphamvu yogwira ntchito ikukwanira miyamba yonse yosaoneka. Ntchito ya awo okhala m’malo amene’wo ndi kutumikira Yehova iyenera kuposa kwambiri ntchito iri yonse imene ikuchitidwa pa dziko lathu lapansi’li lero lino. Mautali akulu kwambiri mosaneneka koposa awo amene ali othekera pa dziko lathu lapansi’li kapena kuchokera pano kumka ku mwezi afunikira kuyendedwa potumikira Mfumu ya chikengedwe chonse, Yehova Mulungu. Zosawerengeka ziri zinthu zoti zichitidwe, kuphatikiza pa kupereka chisamaliro ku pulaneti lathu laling’ono kwambiri’li, Dziko lapansi. Tiyenitu tisadzichititse kusaona ntchito zakumwamba chifukwa chokha chakuti maso athu ofooka’wa sangathe kuziona kwenikweni. Pali maziko ali onse kwa ife ozionera ndi maso a chikhulupiriro.—Ahebri 11:1, 27.

34, 35. Kodi ndi motani m’mene wamasalmo Davide akulongosolera kuzindikira kwake luso lapamwamba kwambiri la angelo akumwamba, ndipo kodi ndi phunziro lotani limene anthufe tingaphunzire kuchokera kwa iwo?

34 Mogwirizana ndi zifuno za Ambuye Mulungu, ana ake akumwamba anakhala ndi miyoyo yokangalika kopambana. Iwo ali okhoza kuchita zochuluka kwambiri koposa zimene anthufe tingachite. Iwo ali oposa anthu. Mphamvu yao ife sitingathe kuiyerekezera. Malinga ndi kunena kwa mbiri ya Baibulo, iwo, mwa mzimu woyera, atheketsedwa kuchita zinthu zimene sayansi singathe kuzichititsa.

35 Davide anazindikira luso lao loposa la anthu pamene iye anatembenuzira maganizo ake kwa iwo nati: “Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake. Lemekezani Yehova, inu, makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chokoma.” (Salmo 103:20, 21) M’kuchita chifuniro cha Yehova, makama a angelo akumwamba amene’wo amapereka chitsanzo chabwino kwambiri choti munthu wapadziko lapansi achitsanzire. Ngati zolengedwa zoposa anthu zamphamvu kwambiri zotero’zo sizimadzilingalira kukhala zoyeneretsedwa mwa izo zokha kutumikira Mlengi wao, pamenepo ife ofooka, okhala kanthawi kochepa pansi pano sitiyenera kukhala odzilingalira ndi odzikhutira kwakuti n’kupandukira Yehova Mulungu, tikomaona kukhala opanda thayo kotheratu kwa iye. Kuli bwino kwambiri kwa ife kumlemekeza.

36. Kodi ndi motani, m’mene mzimu woyera umadzisonyezera m’miyamba yonse, ndipo n’chifukwa ninji umodzi kumene’ko sudzaponderezedwa?

36 Mzimu woyera wochokera kwa Mulungu umadzisonyeza m’miyamba yonse monga Mwana wake wobadwa yekha, akerubi ake, aserafi ake ndi angelo ake onse mwachikondi amam’tumikira iye, Mulungu mmodzi yekha wamoyo ndi woona. Mzimu wake, woperekedwa kwa okhulupirika onse’wa, umatulutsa pakati pawo “umodzi wa mzimu m’chomangira chogwirizanitsa cha mtendere”, tikabwereka mau ku Aefeso 4:3. Iwo onse amagwirizana pamodzi pansi pa Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova. Mwa utumiki wao wogwirizana m’ntchito zao zonse zosiyanasiyana, iwo akum’lambira kwenikweni. Umodzi wa kutumikira wotero’wo ndi kulambira sudzaponderezedwa ngakhale ndi ziwanda.

37. Kodi ndani amatsogolera kumwamba m’kulambira ndi kutumikira Mulungu, ndipo kodi ndi motani m’mene kuzindikira cheni cheni chimene’cho kunasonyezedwera m’masomphenya a Yohane m’Chibvumbulutso 5:11-14?

37 Wotsogolera m’kupereka utumiki wosagwedera ndi kulambira kwa Mulungu ndiye “woyamba kubadwa,” “Mwana wobadwa yekha” wa Yehova. Amene’yu pa nthawi ina anali wofunitsitsa kutumikira monga Mwanawankhosa wa nsembe pano pa dziko lapansi. Mosasiyana kwambiri ndi Akristufe, makamu akumwamba amayamikira kudzipereka nsembe kotero’ko. Motsimikizira zimene’zi, mtumwi Yohane akupatsidwa masompheya a chochitika cha kumwamba amene tsopano akukhala ndi kukwaniritsidwa kwake m’zaka zathu za zana la makumi awiri, motere:

“Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva mau a angelo ambiri pozinga mpando wachifumu, ndi zamoyo ndi akulu; ndipo mawerengedwe ao anali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi; akunena ndi mau akulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwa’yo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko. Ndipo cholengedwa chiri chonse chiri m’mwamba, ndi padziko, ndi pansi pa dziko ndi m’nyanja, ndi zonse ziri momwemo, ndinazimva zirikunena, kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi ufumu, kufikira nthawi za nthawi, Ndipo zamoyo zinai zinati, Amen. Ndipo akulu’wo anagwa pansi nalambira.”—Chibvumbulutso 5:11-14.

38. Polingalira masomphenya amene’wo, kodi pali chosankha chotani choti ife tipange, ndipo kodi ife tidzapatsidwa mzimu woyera m’chochitika chotani?

38 Bwanji ife amene tsopano tiri pa dziko lapansi, inde, pa nkhope ya dziko lapansi ndipo mpaka tsopano sitiri “pansi pa nthaka” m’manda? Pali chosankha choti ife tipange. Kodi tiyenera kukhala ndi phande m’kukwaniritsa masomphenya olosera amene’wo mwa kugwirizana ndi zikwi zikwi za angelo oyera ndi kupereka ulemu woyenera kwa Mwana wonga Mwanawankhosa wa Mulungu ndi kupereka kudzipereka kwathu kwa mtima wonse kwa Uyo wokhala pa mpando wachifumu, Yehova Mulungu? Ngati tisankha kuchita zimene’zi mwa kufuna kwathu kwa ife eni, pamenepo, mofanana ndi makamu aulemerero akumwamba, tidzapatsidwa mzimu woyera wochokera kwa Wopereka mphatso iri yonse yangwiro, Yehova Mulungu—Yakobo 1:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena