Mutu 1
Magwero Oposa Munthu a Mzumu Woyera
1. Kodi n’chifukwa ninji mzimu woyera unali kugwira ntchito m’Munda wa Edene pamene mwanuna ndi mkazi anakumana choyamba?
PAMENE mwamuna ndi mkazi anakumana choyamba, iwo anamva mphamvu–mphamvu ya chikoka. Iwo anakondana pa nthawi yomwe’yo. Ngakhale kuli kwakuti anali amaliseche, osabvala, mwamuna woyamba ndi mkazi oyamba amene’wa anali oyera. Ndiko kuti, iwo anali opanda litsiro, audongo, opanda uchisi, angwiro m’thupi, maganizo ndi mtima. Chifukwa cha chimene’cho sanachite manyazi ndipo anakhala ndi unansi wopanda chopinga ndi Mlengi wao, Mulungu. Iwo anasangalala ndi unansi wao wonga wa mwana ndi Iye m’malo audongo ndi oyera. Iwo anali malo a chisangalalo chopanda uchisi, moyenerera ochedwa Munda wa Edene kapena Paradaiso wa Chisangalalo. Zinthu zones zimene zinawazinga zoti ziwayambukire zinali zopatsa thanzi labwino ndi zabwino. Mzimu woyera, mphamvu yoyera yogwira ntchito ya Mulungu, inali kugwira ntchito mokwanira m’menemo.
2. Kodi chifukwa ninji Magwero a mzimu woyera anatsimikizira kukhala oposa munthu?
2 Mwamuna ndi mkazi’yo, makolo anthu oyambirira a pa dziko lapansi, anali aumunthu, ndiko kuti, a pa dziko lapansi, a zinthu zimene zikupezeka pano pa dziko lapansi. Koma bwanji ponena za Mlengi wao waumulungu’yo? Amene’yu anayenera kukhala woposa munthu. Iye anali wapamwambamwamba koposa munthu mu mkhalidwe wa kukhalapo Kwake kwakumwamba. Iye anali wapamwamba’nso, kwambiri, mu mtundu wa Munthu wanzeru amene iye anali. Kunena mosabvuta, iye anali, wopangika ndi zopangira zabwino kwambiri koposa munthu. Ndicho chifukwa chake iye anali wosaoneka kwa munthu, amene mphamvu zake za kuona ziri zosa pita patali. Pamenepa, mwachibadwa, mwamuna ndi mkazi oyamba’wo sanaone Mlengi wao, Wopereka Moyo wao, Atate wao wakumwamba, ndi wosaoneka, iye anali chimene lero lino tikucha “mzimu.” Chifukwa chakuti iye ali Munthu wapayekha, monga momwe’di cholengedwa chake munthu chiliri, Mlengi’yo angachedwe “Mzimu.” Mwapadera iye ali Mzimu’yo. Iye ali Magwero osaoneka a mzimu woyera, pakuti Iye mwiniyo ndi woyera.
3. Kodi Genesis 1:1 amasonya ku ntchito za yani?
3 Dziko lathu lapansi’li ndi miyamba pamwamba pake zisanakhaleko, Munthu wauzimu amene’yu analiko ndipo kugwira ntchito. Bukhu Lopatulika linene limatipatsa cholembedwa cha mu mbiri kubwerera m’mbuyo mpaka kukafika pa nthawi imene munthu asanakhaleko limayamba ndi mau olunjika awa: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi”—Genesis, chaputula 1, vesi 1.
4, 5. Kodi n’chifukwa ninji Mulungu sayenera kulambiridwira m’nyumba iri yonse yomangidwa ndi anthu pa malo akutiakuti pa dziko lapansi?
4 Mulungu wolenga amene’yu ali wapamwamba kwambiri’di koposa miyamba imene iye anailenga ndipo chifukwa cha chimene‘cho wapamwamba kopambana koposa munthu wa pa dziko lapansi. Chotero iye ali mzimu mu mkhalidwe wake kapena m’chimene iye ali. Zaka zikwi zambiri pambuyo pa kulengedwa kwa munthu, Woyambitsa Chikristu choona anasonyeza chenecheni chimene’chocho. Pambali pa chitsime m’mbali mwa Phiri la Gerizimu mu Samariya wakale iye anati kwa mkazi Wachisamariya: “Mulungu ndiye mzimu; ndipo om’lambira Iye ayenera kum’lambira mumzimu ndi m’choonadi.” (Uthenga Wabwino wa Yohane, chaputala 4, vesi 24) Mulungu woona samafunikira kulambiridwa m’nyumba iri yonse yachipembedzo yomangidwa ndi anthu m’malo ali onse akutiakuti pa dziko lapansi, ngakhale pa Yerusalemu m’Middle East. Zaka zosakwanira makumi awiri pambuyo pa mau apita’wo, mtumwi Wachikristu anaima pamaso pa Bwalo Lalikulu la mzinda wa Atene, kumene kunali akachisi ambiri, operekedwa kwa milungu ndi milungu yachikazi ya chipembedzo chao. Iye anati:
5 “Mulugu amene analenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo, Iyeyo, ndye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m’nyumba zakachisi zomangidwa ndi manja; satumikidwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse; ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.”—Machitidwe 17:24-27.
6. Kodi ndi motani womanga kachisi woyambirira pa Yerusalemu anasonyezera kuti anazindikira chenicheni chimene’cho chonena za kulambiridwa kwa Mulungu?
6 Zaka zopsa chikwi izi zisanachitike chenicheni chimene’cho chonena za Mulungu woona, amene ali Mzimu woposa munthu, ndi woposa wadziko lapansi, chinadziwidwa ndi womanga wa kachisi woyamba wodziwika pa Yerusalemu m’Middle East. Potsegulira kachisi amene’yu amene iye anamangira dzina la Mulungu, mfumu ya pa nthawi’yo ya Yerusalemu m’pemphero kwa Iye inati: “Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo ndi m’Mambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga’yi.”—1 Mafumu 8:27.
MULUNGU MAGWERO A NYONGA YONSE
7. Kodi ndi n’jira yotani ngakhale “kumwambamwamba” sikungalandira Mulungu?
7 Wonena mau apamwambapo’wo Solomo mwana wa Mfumu Davide, anali wasanyansi wanzeru kopambana wa m’nthawi za Nyengo yathu Ino isanakhale. Pamene iye ananena kuti ngakhale m’mwamba-mwamba simungathe kulandira Mulungu amene iye anam’mangira kachisi, iye ananena choonadi cha sayansi. Dziko lathu lapansi’li liri mbali yaing’ono kwambiri ya chilengedwe chimene malire ake asayansi ali osakhoza kuwafikira kapena kuwaona ngakhale ndi makina oonera zinthu zokhala kutali amphamvu kopambana a lero lino. Komabe, chilengedwe chosadziwika ukulu wake kufikira tsopano chimene’chi sichingalandire Mulungu woona. Sichingathe kum’sunga m’kati kapena kum’bindikiritsa. Zimene ziripo kale za chilengedwe chonse, zooneka ndi zosaoneka, Mulungu woona angazipose. Iye angathe kuzipitirira ndi kulenga zinthu zina’nso kaamba ka kufutukulidwa kwa chilengedwe chonse, kupyola malire ake amene alipo, kumka m’mlengalenga mopanda malekezero. Kodi zimene’zi zikutanthauzanji?
8 Kodi Umulungu wa Mlengi uli wokhalitsa motani, ndipo kodi n’chifukwa ninji palibe kanthu kamene kali kosatheka kwa Iye?
8 Zikutanthauza kuti Mulungu samadodometsedwa kaya ndi nthawi kapena nyengo ya nthawi. Moyo wake m’mthawi zakale uli wopanda malekezero. Nthawi ya moyo wake m’tsogolo iri yopanda polekezera. Kwa Munthu wopanda malekezero wopereka malamulo wapamwamba kopambana amene’yu wa nthawi Zachikristu zisanakhale, Mose, anati: “Inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.” (Salmo 90:2) Mulungu amene’yu amakhala ndi moyo kufikira ku nthawi yosatha, kuti apitirizebe kutulutsa ndi kulenga zoposa chilengedwe chiripo’chi, kuchifutukula. Chimene’chi chimatanthauza kuti iye ali chitsime chopanda malekezero cha nyonga yonse. Zinthu zonse za chilengedwe chonse ziri mitolo ya zinthu za nyonga yochokera kwa iye. Imene’yi yaunjikidwa pamodzi kupanga miyulu yaikulu ndi yaing’ono. Wasayansi wa m’zaka za zana la makumi awiri Albert Eistein anapanga njira yake yochitira iyi: nyonga ndiyo kulemera kuchulukitsa ndi liwiro la kuunika lowirikizidwa kawiri (kapena, E=mc2). Pamenepo, n’kosadabwitsa, kuti Magwero a nyonga yonse amene’wa samaona kanthu kena kukhala kosatheka kwa iye mwini.
9, 10 Kodi ndi motani m’mene kuliri kuti Mulungu atulutsa khamu la nyenyezi “ndi kuziwerenga” ndipo palibe “isoweka”?
9 Mwa chitsanzo, onani mau pafupifupi osakhulupiririka amene Iye akunena ponena za iye mwini, pamene iye akutiuza kutukula mitu yathu kuyang’ana kumwamba usiku ndi kuchititsidwa kaso ndi nyenyezi. Iye akuti: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azicha zonse amaina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.”—Yesaya 40:26.
10 Openda nyenyezi a lero lino, ndi makina ao oonera zinthu zakutali amphamvu kopambana, angangoyerekezera chabe chiwerengero cha nyenyezi zimene iwo angathe kuziona. Siziri choncho ndi Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi. “Awerenga nyenyezi momwe ziri; azicha maina zonse’zi.” (Salmo 147:4) Iye akuyerekezera nyenyezi zonse za kumwamba ndi gulu lankhondo lalikulu kwambiri. Iye amadziwa kuchuluka kwa zimene ziri m’gulu lake la nkhondo limene’li. Iye amadziwa chiwalo chiri chonse cha gulu la nkhondo limene’li ndi dzina. Mwa chikumbukiro iye angathe kuitana maina ao. Pamene akuitana maina’wo, palibe chiwalo chiri chonse cha gulu la nkhondo la nyenyezi limene’li chimalephera kuyankha. Chiri chonse chimayankha dzina lake ndipo chimalongosola ntchito yake. Chiri chonse Iye amachipeza kukhala chikukwaniritsa chifuno chimene icho chinalengedwera. Palibe chiri chonse chikusoweka.
11. Kodi n’chifukwa ninji kuli kwakuti Mlengi samalefuka ndipo sadzalola chilengedwe chake kuguga kapena kutha mphamvu?
11 “Mphamvu zazikulu [zochuluka]” zimene Mulungu ali nazo ziri zazikulu kopambana. Ziri Zosatha. Pamene tilingalira za nyonga yokha imene iri m’dzuwa la mapulaneti athu ozungulira dzuwa, limene liri ng’anjo ya zophulika za nyuklea zofanana ndi kuphulika kwa mabomba a haidrojeni, tikudabwitsidwa kotheratu. Ndiopo pamene tilingalira za mabiliyoni osawerengeka a nyenyezi zochuluka zake zimene ziri zazikulu kwambiri koposa dzuwa lathu’li, tikupeza lingaliro lina lonena za kuyenda kwa tawatawa kwa nyonga yochokera kwa Mulungu kumene miyamba ya nyenyezi iripo’yi imaimira. Ndipo komabe Mulungu samalefuka, samatopa. Chotero, mogwirizana kotheratu ndi zinizeni kukunenedwa kuti: “Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.” (Yesaya 40:29) Iye sadzalola chilengedwe chathu chomafutukuka’chi kusakhala kapena kutha mphamvu. Pakuti chidzakhalapobe kuti chichite chifuno chimene icho chinalengedwera. Monga ndakatulo woyanga’ana nyenyezi wakale anati: “Zakumwamba zimalakikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Usana ndi usana uchulukitsa mau, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.”—Salmo 19:1, 2.
12. Kodi n’chifukwa ninji anthu ali opanda chowiringula kamba ka kunyalanyaza Mulungu ndi thayo limene iwo ali nalo kwa Iye?
12 Mokondweretsa kwa ife, Mulungu ali wosaoneka kwa anthu. Komabe, mosasamala kanthu za zimene’zi iye amatipatsa umboni wochuluka wa kukhalako kwake kwakuti dziko la mtundu wa anthu liri lopanda chowiringula chokanira kapena chonyalanyazira kukhalako kwake ndi thayo lao kwa iye. “Pakuti,” monga momwe analembera wolemba Baibulo wina, “Chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula; chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu sanam’chitira ulemu wakuyenera Mulungu.” (Aroma 1:20, 21) Pokhala ndi umboni wonsewu, iwo sangatsutse mwachipambano kuti kulibe Mulungu mofanana ndi kunena kuti “Mulungu wafa.” Iye akali moyobe ndipo ali ndi nyonga yonse yaikulu ndi chikumbukiro changwiro cha kuchita zifuno zake zolongosoledwa, zimene zalengezedwa ndi kufalitsidwa tsopano kwa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi. Ha, ndi okondwa chotani nanga m’mene tingakhalire ndi chimene’chi!
13. Kodi Mulungu ali Magwero, a china’nso chiani, kuphatikiza pa nyonga yaikulu, ndipo chifukwa ninji?
13 Sitimagwirizana ndi asayansi amakono m’kukana kwao kuti Mulugu ndiye Magwero a nyonga yonse imene tsopano ikugwira ntchito. Timadziwa kuti iye ali’nso Magwero a kanthu kena’nso kamene asayansi amakakana, osadziwa kanthu za iko. Kodi kamene’ko n’chiani? Ndiko “mzimu.” Ndipo kodi n’chifukwa ninji iye sayenera kukhala Magwero a mzimu? “Mulungu ndiye Mzimu” kapena “Mulungu ndi mzimu,”monga momwe Yesu Kristu anasonyezera zaka mazana khumi ndi anasu ndi anai zapita’zo.—Yohane 4:24, NW, ndi mau a m’mphepete.
14. Kodi n’chiani chimene chiri “mzimu woyera,” ndipo kodi ndani amene amaupereka?
14 Kwa Mulungu kumachokera mphamvu yogwira ntchito yosaoneka njira mwa imene iye amachititsira chifuniro chake kuchitidwa. Sindiyo chisonkhezero chabe chonga chimene munthu angachisonyeze pa ena mwa umunthu wake wamphamvu. Iri mphamvu imene ikugwira ntchito, ndipo imachokera kwa Mulungu amene ali woyera, ndiko kuti, wopanda uchisi kotheratu ndi wolungama. Iye amaitumiza kuti ichite chimene chiri choyera. Chotero moyenerera ikuchedwa “mzimu woyera.” Ikuchedwa choncho m’Mau olembedwa a Mulungu. Yesu Kristu iye mwini anazindikira Mulungu kukhala Magwero a mzimu woyera. M’kutsimikizira zimene’zi, iye kwa atate aumunthu a m’tsiku lake anati: “Ngati inu, okhala oipa, muziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye?”—Luka 11:13.
15. Kodi ndi mzimu wotani umene ife, mofanana ndi Mfumu Davide, tikafuna kuti ugwire nchito kwa ife?
15 Kholo Lachifumu la Kristu nalo’nso linazindikira Mulungu monga Magwero a mzimu woyera. Kuzindikira kumeneku kunakhala koonekera bwino pamene iro linabvomereza cholakwa chake pamaso pa Mulungu, nalipempha chikhululukiro ndi kuti: “Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera.” (Salmo 51:11) Kwa Mfunu Davide kuchotseredwa mzimu woyera kukatanthauza kudulidwa kwake ku Magwero ake. Zotulukapa za chimene’chi zikanangokhala zoopsya ndi zoononga. Ngati ife lero lino tiri ndi cikhulupiriro chakuti Mulungu aliko ndipo ali Magwero a mzimu woyera, pamenepo, ngati tiupempha kwa iye, iye adzapangitsa kukhala kothekera kwa ife kuulandira. Iri mphamvu imene ife tikakonda kuti ikhale ikugwira ntchito kwa ife, kodi si choncho? Ngati zimene’zi ndizo zimene tikakonda, Mulungu adzakhala wokhoza kuchita zabwino zochuluka kupyolera mwa ife ndi kutisunga kukhala oyera m’dziko loipa kwambiri.
MPHAMVU, OSATI MUNTHU
16. Kodi ndi motani m’mene kukusonyezedwera kuti liu Lachihebri’lo “mzimu” liri lolongosola kwambiri.
16 M’Mau olembedwa a Mulungu, Malemba Opatulika, liu losankhidwa kuchula mphamvu yogwira ntchito yosaoneka yochokera kwa Mulungu imene’yi liri loyenerera, iro pokhala lolongosola kwambiri. M’bukhu loyambirira la Malemba amene’wo iyo ikuchedwa ru’ahh. Katembenuzidwe koyambirira Kachigriki ka bukhu loyamba la Baibulo kanaicha pneu’ma. Chifukwa chakuti liu Lachihebri’lo ru’ahh liri ndi lingaliri la kuchita ndi kuyenda, otembenuza Achingelezi alitembenuza kukhala “mphepo yamphamvu, mpweya, mphepo ya yaziyazi, nkuntho, mphepo, mphamvu yogwira ntchito,” ndipo’nso “mzimu.” Chifukwa cha ichi m’mene liu Lachihebri’lo laumbidwira kumatithandiza kutsimikizira kaya ngati liu’lo liyenera kutembenuzidwa kukhala “mzimu” kapena mwa njira ina.
17. Kodi An American Translation imanenanji m’malo mwa “Mzimu wa Mulungu” m’Genesis 1; 2, motero kusonyezanji ponena za ru’ahh?
17 Mwa chitsanzo, m’vesi lachiwiri la Malemba Opatulika liu’lo ru’ahh likuonekera kwa nthawi yoyamba. Kodi ndi motani m’mene liyenera kutembenuziridwa m’chinenero china? Eya, katembenuzidwe Kachinyanja kofala ka Baibulo, Nyanja (Union) kamatembenuza Genesis 1:1, 2 motere: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo Mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi.” Komabe, An American Translation, losindikizidwa ndi University of Chicago mu 1939, limati: “Pamene Mulungu anayanba kulenga miyamba ndi dziko lapansi, dziko lapansi linali lopanda kanthu kali konse, lokhala ndi mdima wophimba phompho’lo ndipo mphepo yaphiphiphi” inali kukukuma pamwamba pa madzi’wo.” Muno, m’malo mwa liu’lo “Mzimu,” liu lakuti “mphepo yaphi-phi-phi likugwiritsiridwa nchito, ndipo mau’wo “mzimu wa Mulungu” akutembenuzidwa kukhala mphepo yaphiphiphi.” Motero An American Translation limasonyeza kuti liu’lo ru’ahh limatanthauza kanthu kena kosaoneka ndi kamene kakuyenda kapena kakugwira ntchito.
18. Kodi ndi motani m’mene New World Translation of the Holy Scriptures imasonyezera kuti palibe munthu wochedwa “Mzimu” amene anayendayenda pamwamba pa madzi?
18 Pochirikiza lingaliro lakuti ru’ahh amathanthauza mphamvu yosaoneka iri pa ntchito, New World Translation of the Holy Scriptures imaika m’chingelezi (chimene chikutembenuzidwa m’Chichewa) Genesis 1:1, 2 motere: “Pachiyambi Mulungu analenga miyamba ndi dziko lapansi. Tsopano dziko lapansi linakhala losakonzeka ndi lopanda kanthu ndipo panali mdima pamwamba pa madzi akuya’wo; ndipo mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu inali kuyenda-yenda cha uku ndi cha uko pamwamba pa madzi’wo.” Motero katembenuzidwe kamene’ka ndipo’nso ka An American Translation kamalongosola momvekera bwino kuti panalibe munthu wochedwa “Mzimu” amene anali kuyendayenda mosaoneka pa madzi amene anakuta dziko lonse lapansi. M’malo mwake, inali mphamvu yogwira ntchito yosakhala munthu ya Mulungu imene inali kuyendayenda cha uku ndi cha uko pamwamba pa madzi osaunikiridwa’wo.
19. Kodi tidzanenanji ponena zakuti kaya mzimu wa Mulungu kapena mphamvu yogwira ntchito unali kuyendayenda pamwamba pa madzi popanda chifukwa?
19 Kaya ndi kudzisonyeza kotani kumene mphamvu yogwira ntchito yosaoneka ya Mulungu’yo inapanga, sitikudziwa; sikukulongosoledwa m’cholembedwa choyambirira’cho. Komabe, n’zoona, kuti mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu sinali kumayendayenda cha uku ndi cha uko popanda chifukwa, popanda zotulukapo zotsimikizirika. Mwina mwake inatumikira kuchotsa mtambo uli wonse wa pfumbi wa m’mlengalenga umene dziko lapansi linali nao ndi umene unachititsa kuunika kochokera ku dzuwa lathu kusafika pamwamba pa madzi akuya’wo amene anakuta mpira wonse wa dziko lapansi.a
20. Kodi ndi motani m’mene Mulungu anapitira patsogolo ndi chifuno chake kaamba ka makolo athu a pa dziko lapansi kuti aone ndi kuunika kwa Usana?
20 Muli monse, pambuyo pa kuyenda cha uku ndi cha uko kwa mphamvu yogwira ntchito ya Mulugu pamwamba pa madzi ozama’wo, kwa utali wa nthawi wosalongosoledwa, lamulo la Mulungu linatsatirapo kuti: “Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. Ndipo anaona Mulungu kuti kuyera’ko kunali kwabwino: ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima. Ndipo Mulungu anacha kuyerako Usana, ndi mdima’wo anaucha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m’mawa, tsiku loyamba.” (Genesis 1:3-5) Motero, mogwirizana ndi chiyero cha Mulungu, mphamvu yake yogwira nchito kapena mzimu inagwira ntchito bwino lomwe, kaamba ka chifuno chabwino. Inatsimikizira kukhala “mzimu woyera.” Mwa njira ya uwo Mulungu anapitirizabe ndi chifuno chake kaamba ka makolo athu oyambirira pa dziko lapansi kuti aone ndi kuunika kwa Usana.
21. Polingalira m’mene Mulungu wayendetsera mzimu wake woyera, kodi n’chifukwa ninji tikusonkhezeredwa kumva mofanana ndi wolemba Salmo 143:10?
21 Kuyambira pa kuchulidwa koyambirira kwenikweni kwa mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, iye waigwiritsira ntchito kaamba ka phindu la munthu. Mozindikira chenicheni chimene’cho tikukoperedwa ku Magwero akumwamba a mzimu woyera. Cholembedwa cha Baibulo chonena za kugwira nchito kwake kwa zaka zikwi zambiri chimabvumbula kuti Mulungu nthawi zonse waigwiritsira ntchito m’njira yopatulika. Iyo yachita chifuno cholungama cha Mulungu. Sitiyenera konse kufuna kutsutsa mphamvu yogwira ntchito yosaoneka ya Mulungu Wamphamvuyonse. Tiyenera kulingalira mofanana ndi wolemba Baibulo amene ananena kuti: “Munditphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.”—Salmo 143:10.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Genesis 8:1 kumene liu Lachihebri’lo ru’ahh likutembenuzidwa, kukhala osati “mzimu,” koma “mphepo.”
[Chithunzi chachikulu patsamba 4]