Ubatizo
Tanthauzo: Liwu lakuti “batiza” likuchokera ku liwu Lachigiriki lakuti ba·ptiʹzein, lotanthauza “kuviika, kunyika.” (A Greek-English Lexicon, la Liddell ndi Scott) Ubatizo wammadzi Wachikristu ndiwo chizindikiro chapoyera chakuti munthu wobatizidwayo anapanga kudzipatulira kwathunthu, popanda chotsala, ndi kotheratu kupyolera mwa Yesu Kristu kuchita chifuniro cha Yehova Mulungu. Pakati pa zinthu zina, Malemba amasonyanso ku ubatizo wa Yohane, kubatizidwa ndi mzimu woyera, ndi kubatizidwa ndi moto.
Kodi anthu okhulupiriradi Mawu a Mulungu amaleka kubatizidwa?
Mat. 28:19, 20, NW: “Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira mwa anthu amitundu yonse, mukumawabatiza m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera, mukuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndakulamulirani.”
Mac. 2:41: “Amene analandira mawu ake anabatizidwa.”
Mac. 8:12: “Pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Kristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.”
Mac. 8:36-38: “Ndipo monga anapita panjira pawo, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo [Mwitiyopiya] anati, Tawonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe? Ndipo anamuuza kuti aimitse galeta; . . . ndipo [Filipo] anambatiza iye.”
Ubatizo wammadzi Wachikristu—kodi ndiwo mwa kuwaza kapena mwa kumizidwa kotheratu?
Marko 1:9, 10: “Yesu . . . anabatizidwa [“kumizidwa,” ED, Ro] ndi Yohane [mu Mtsinje wa] Yordano. Ndipo pomwepo, alimkukwera potuluka m’madzi, anawona iye thambo litang’ambika.”
Mac. 8:38: “Ndipo anatsikira onse aŵiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipo anambatiza [“kummiza,” ED, Ro] iye.”
Kodi ubatizo wamakanda unachitidwa ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba?
Mat. 28:19, NW: “Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira . . . mukumawabatiza.”
Mac. 8:12: “Pamene anakhulupirira Filipo . . . anabatizidwa, amuna ndi akazi.”
Komabe, pambuyo pake, Origen (185-254 C.E.) analemba kuti: “Uli mwambo wa tchalitchi kuti ubatizo uchitidwe ngakhale kwa makanda.” (Selections From the Commentaries and Homilies of Origen, Madras, India; 1929, p. 211) Mwambowu unatsimikiziridwa ndi Msonkhano wa ku Carthage (cha mu 252 C.E.).
Wolemba mbiri wachipembedzo Augustus Neander analemba kuti: “Nthaŵi zonse chikhulupiriro ndi ubatizo zinali zogwirizana china ndi chinzake, ndipo motero pali kuthekera kwakukulu . . . kwakuti mwambo wa ubatizo wamakanda unali wosadziŵika panyengo ino [m’zaka za zana loyamba]. . . . Chenicheni chakuti unazindikirika kwa nthaŵi yoyamba kukhala mwambo wa atumwi mkati mwa zaka za zana lachitatu, uli umboni wotsutsa mmalo mwa kuvomereza kuti unayambidwa ndi atumwi.”—History of the Planting and Training of the Christian Church by the Apostles (New York, 1864), p. 162.
Kodi ubatizo wammadzi Wachikristu umachititsa
kukhululukidwa kwa machimo?
1 Yoh. 1:7: “Ngati tiyenda m’kuunika, monga iye ali m’kuunika, . . . mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.” (Chotero, simadzi a ubatizo koma mwazi wa Yesu umatichotsera uchimo.)
Mat. 3:11: “Inetu [Yohane Mbatizi] ndikubatizani inu ndi madzi kuloza kukutembenuka mtima; koma iye wakudza pambuyo panga [Yesu Kristu], ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake.” (Vesi 5, 6, ndiponso Machitidwe 13:24, amasonyeza kuti zimene Yohane anachita zinalunjikitsidwa, osati kwa anthu onse, koma kwa Ayuda. Chifukwa ninji? Chifukwa cha machimo a Ayuda ochimwira pangano Lachilamulo ndi kuwakonzekeretsa kaamba ka Kristu.)
Mac. 2:38: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu.” (Kodi ubatizo weniweniwo unabweretsa chikhululukiro kwa iwo? Talingalirani: Zimenezi zinanenedwa kwa Ayuda amene anali ndi thayo la kupha Kristu. [Wonani vesi 22, 23.] Ubatizo wawo ukapereka umboni wa kanthu kena. Wa chiyani? Wakuti tsopano akukhulupirira Yesu monga Mesiya, Kristuyo. Kuli kokha mwa kuchita kwawo zimenezi kuti machimo awo akakhululukidwa. [Mac. 4:12; 5:30, 31])
Mac. 22:16: “Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane padzina lake.” (Ndiponso Machitidwe 10:43)
Kodi ndani amene amabatizidwa ndi mzimu woyera?
1 Akor. 1:2; 12:13, 27: “Kwa . . . oyeretsedwa mwa Kristu Yesu . . . pakutinso mwa mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kuloŵa m’thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Ahelene, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa mzimu mmodzi. Inu ndinu thupi la Kristu.” (Monga momwe Daniel 7:13, 14, 27 amasonyezera, “oyera mtima” otere amakhala ndi mbali mu Ufumu limodzi ndi Mwana wa munthu, Yesu Kristu.)
Yoh. 3:5: “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi mzimu, sakhoza kuloŵa ufumu wa Mulungu.” (Munthuyo ‘amabadwa mwa mzimu’ panthaŵi ya ubatizo wake ndi mzimu umenewo. Luka 12:32 amasonyeza kuti ali kokha a “kagulu kochepa” amene ali ndi mwaŵi umenewo. Wonaninso Chivumbulutso 14:1-3.)
Kodi onse obatizidwa ndi mzimu woyera amalankhula m’malirime kapena ali ndi mphatso ya kuchiritsa?
1 Akor. 12:13, 29, 30: “Pakutinso mwa mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kuloŵa m’thupi limodzi . . . Kodi ali onse atumwi? . . . Ali onse ochita zozizwa? Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malirime?”
Wonaninso “Kuchiritsa” ndi “M’Malirime, Kulankhula.”
‘Ubatizo wa akufa’—kodi umatanthauzanji?
1 Akor. 15:29: “Adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo?”
Mkhala pakati Wachigriki hy·perʹ, wotembenuzidwa panopa “chifukwa,” amatanthauzanso “mwa,” “mmalo mwa,” “kaamba ka,” “kaamba ka chifuno cha,” ndi zina zotero. (A Greek-English Lexicon, la Liddell ndi Scott) Kodi amatanthauzanji m’lembali? Kodi Paulo anali kuvomereza kubatiza anthu amoyo mmalo mwa awo amene anafa ali osabatizidwa?
Malemba ena okha amene amatchula imfa mwachindunji mogwirizanitsa ndi ubatizo amasonya ku ubatizo umene munthu aliyense payekha iye mwiniyo amaloŵamo, osati ubatizo mmalo mwa munthu wina, amene wafa
Aroma 6:3: “Kodi simudziŵa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake?” (Ndiponso Marko 10:38, 39)
Akol. 2:12: “Popeza [mamembala amoyo ampingo m’Kolose] munaikidwa m’manda pamodzi ndi iye mu ubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi iye m’chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu amene anamuukitsa iye kwa akufa.”
Matembenuzidwe mu “Revised Union Nyanja Version” ngolondola mwa garamala ndipo ngogwirizana ndi malemba ena a Baibulo
1 Akor. 15:29: “Ngati sikutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa chaiwo?” (Chotero iwo amabatizidwa, kapena kumizidwa, kuloŵa m’njira ya moyo imene idzatsogolera ku imfa yaumphumphu mofanana ndi ija ya Kristu ndiyeno kuukitsidwira kumoyo wauzimu monga momwe anachitira iye.)
Kodi nchiyani chimene chiri chotulukapo cha mu ubatizo wa moto?
Luka 3:16, 17: “Iyeyu [Yesu Kristu] adzakubatizani inu ndi . . . moto. Amene chouluzira chake chiri m’dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake . . . mankhusu adzatentha m’moto wosazima.” (Chiwonongeko chake chikakhala chosatha.)
Mat. 13:49, 50: “Adzatero pachimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino, nadzawataya m’ng’anjo ya moto.”
Luka 17:29, 30: “Tsiku limene Loti anatuluka m’Sodomu unavumba moto ndi sulfure zochokera kumwamba, ndipo zinawawononga onsewo; momwemo kudzakhala tsiku lakuvumbuluka Mwana wa munthu.”
Suli wofanana ndi ubatizo wa mzimu woyera, umene unali wa ophunzirawo
Mac. 1:5, NW: “Yohane, ndithudi, anabatiza ndi madzi, koma inu [atumwi okhulupirika a Yesu] mudzabatizidwa mu mzimu woyera pasanapite masiku ambiri kuchokera panthaŵi ino.”
Mac. 2:2-4, NW: “Mwadzidzidzi panachitika kuchokera kumwamba phokoso longa ngati lija lamphepo yolimba yothamanga, ndipo linadzadza nyumba yonseyo mmene iwo anali kukhala. Ndipo malirime onga ngati a moto anakhala owonekera kwa aliyense wa iwo ndipo anagawidwa, ndipo linakhala pa aliyense [koma silinaphimbe kapena kumiza] aliyense wa iwo, ndipo iwo onse anakhala odzadzidwa ndi mzimu woyera nayamba kulankhula ndi malirime osiyanasiyana, monga momwe mzimu unali kuwalolera iwo kulankhula.”