Mutu 3
Wokonza Njira Abadwa
ELIZABETI ali pafupifupi kubala mwana wake. Kwa miyezi itatu yapitayi, Mariya wakhala akukhala naye. Koma tsopano ndinthaŵi yakuti Mariya alaŵirane naye ndi kupanga ulendo wautali wobwerera kwawo ku Nazarete. M’miyezi pafupifupi isanu ndi umodzi nayenso adzakhala ndi mwana.
Mwamsanga pamene Mariya achoka, Elizabeti akukhala ndi mwana. Nchisangalalo chotani nanga pamene kubalako kwayenda bwino ndipo Elizabeti ndi mwanayo ali ndi umoyo wabwino! Pamene Elizabeti akuwonetsa kamwana kake kwa anansi ndi achibale, onse akukondwera naye.
Tsiku lachisanu ndi chitatu pambuyo pakubadwa kwake, mogwirizana ndi Lamulo la Mulungu, khanda lalimuna mu Israyeli liyenera kudulidwa. Kaamba ka chochitika chimenechi mabwenzi ndi anansi amabwera kudzacheza. Iwo akunena kuti mwanayo ayenera kutchulidwa dzina la atate wake, Zakariya. Koma Elizabeti akulankhula mwamphamvu. “Iyayi!” iye akutero, “koma adzatchedwa Yohane.” Kumbukirani, kuti ndilo dzina limene mngelo Gabrieli ananena kuti liyenera kupatsidwa khandalo.
Komabe, mabwenzi awo, akutsutsa kuti: “Palibe wina wa abale ako amene atchedwa dzina ili.” Pamenepo, mogwiritsira ntchito chinenero cha zizindikiro, akufunsa atate wake kuti afuna kuti mnyamatayo atchedwe yani. Popempha cholembapo, Zakariya, modabwitsa onse, akulemba kuti: “Dzina lake ndi Yohane.”
Pamenepo, kulankhula kwa Zakariya kukubwezeretsedwa mozizwitsa. Mudzakumbukira kuti anatayikiridwa ndi luso lake la kulankhula pamene sanakhulupirire chilengezo cha mngelo chakuti Elizabeti adzakhala ndi mwana. Eya, pamene Zakariya alankhula, onse okhala m’malowo akuzizwa ndi kunena kwa wina ndi mnzake kuti: “Nanga mwana uyu adzakhala wotani?”
Tsopano Zakariya wadzazidwa ndi mzimu woyera, ndipo akutamanda Mulungu kuti: “Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israyeli; chifukwa iye anayang’ana, nachitira anthu ake chiwombolo, ndipo iye anatikwezera ife nyanga ya chipulumutso, mwa fuko la Davide mwana wake.” Ndithudi “nyanga ya chipulumutso” imeneyi, ndiyo Ambuye Yesu, amene ati adzabadwe. Kupyolera mwa iye, Zakariya akuti, Mulungu ‘adzatipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu, tidzamtumikira iye, opanda mantha, m’chiyero ndi chilungamo pamaso pake, masiku athu onse.’
Pamenepo Zakariya aneneratu za mwana wake wamwamuna, Yohane kuti: “Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu: pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake; kuwapatsa anthu ake adziŵitse chipulumutso, ndi makhululukidwe a machimo awo, chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu wathu. Mmenemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife; kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu munjira ya mtendere.”
Panthaŵi ino Mariya, amene mwachiwonekere akali mkazi wosakwatiŵabe, wafika kwawo ku Nazarete. Kodi chidzachitika nchiyani kwa iye pamene kukakhala kwachiwonekere kuti ali ndi pakati? Luka 1:56-80; Levitiko 12:2, 3.
▪ Kodi Yohane ngwamkulu motani kuposa Yesu?
▪ Kodi ndizinthu ziti zikuchitika pamene Yohane ali ndi masiku asanu ndi atatu akubadwa?
▪ Kodi Mulungu watembenukira kwa anthu ake motani?
▪ Kodi ndintchito yanji imene Yohane akunenedweratu kudzaichita?