Mutu 12
Ubatizo wa Yesu
PAFUPIFUPI miyezi isanu ndi umodzi Yohane atayamba kulalikira, Yesu, amene tsopano ali ndi zaka 30 zakubadwa, akudza kwa iye pa Yordano. Kudzachitanji? Kudzacheza? Kodi Yesu akungokondwerera kokha kuwona mmene ntchito ya Yohane ikupitira patsogolo? Ayi, Yesu akupempha Yohane kumubatiza.
Nthaŵi yomweyo Yohane akutsutsa kuti: “Ndiyenera ine kubatizidwa ndi inu, ndipo inu mudza kwa ine kodi?” Yohane akudziŵa kuti mbale wakeyo Yesu ali Mwana wapadera wa Mulungu. Eya, Yohane analumpha mokondwera m’mimba mwa amake pamene Mariya, ali ndi pakati pa Yesu, anakawachezera! Mosakayikira, amake Yohane, Elizabeti, pambuyo pake anamsimbira za zimenezi. Ndipo ayenera kukhala atamuuzanso za chilengezo cha mngelo ponena za kubadwa kwa Yesu ndi ponena za kuwonekera kwa angelo kwa abusa pausiku umene Yesu anabadwa.
Chotero Yesu sali mlendo kwa Yohane. Ndipo Yohane akudziŵa kuti ubatizo wake ngwosayenerera kwa Yesu. Uli kaamba ka awo olapa machimo awo, koma Yesu ngwopanda tchimo. Komabe, mosasamala kanthu za kukana kwa Yohane, Yesu akuumirira kuti: “Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero.”
Kodi nchifukwa ninji kuli kwabwino kuti Yesu abatizidwe? Chifukwa chakuti ubatizo wa Yesu uli chizindikiro, osati cha kulapa machimo, koma cha kudzipereka iye mwini kuchita chifuniro cha Atate wake. Yesu wakhala ali wopala matabwa, koma tsopano nthaŵi yafika yoti iye ayambe uminisitala umene Yehova Mulungu anamtumira kudziko lapansi kudzachita. Kodi muganiza kuti Yohane akuyembekezera kanthu kena kachilendo kuchitika pobatiza Yesu?
Eya, pambuyo pake Yohane akusimba kuti: “Koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzawona mzimu atsikira nakhala pa iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi mzimu woyera.” Chotero Yohane akuyembekezera mzimu wa Mulungu kudza kwa winawake amene akubatiza. Chifukwa cha chimenecho, mwinamwake iye sakudabwa kwambiri, pamene Yesu akutuluka m’madzi Yohane akupenya “mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa iye.”
Koma zoposa zimenezo zikuchitika pamene Yesu akubatizidwa. ‘Kumwamba kukumtsekugira.’ Kodi izi zikutanthauzanji? Mwachiwonekere zikutanthauza kuti pamene iye akubatizidwa, chikumbukiro cha moyo wake asanakhale munthu kumwamba chikubwereranso kwa iye. Motero, Yesu tsopano akukumbukira mokwanira moyo wake monga mwana wauzimu wa Yehova Mulungu, kuphatikizapo zinthu zonse zimene Mulungu analankhula naye kumwamba mkati mwa kukhalapo kwake asanakhale munthu.
Ndiponso, panthaŵi ya ubatizo wake, mawu ochokera kumwamba akulengeza kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” Kodi liwu limenelo nlayani? Kodi nla Yesu mwiniyo? Kutalitali! Nla Mulungu. Mwachimvekere, Yesu ali Mwana wa Mulungu, osati Mulungu mwiniyo, monga momwe anthu ena amanenera.
Komabe, Yesu ali mwana waumunthu wa Mulungu, monga momwedi munthu woyamba Adamu analiri. Wophunzira Luka, pambuyo pakufotokoza ubatizo wa Yesu, akulemba kuti: “Yesuyo, pamene anayamba ntchito yake, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye monga anthu anamuyesa mwana wa Yosefe, mwana wa Heli, . . . mwana wa Davide, . . . mwana wa Abrahamu, . . . mwana wa Nowa, . . . mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.”
Monga momwe Adamu analiri “mwana wa Mulungu,” choteronso Yesu. Yesu ali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako, zimene ziri zachiwonekere pamene tipenda moyo wa Yesu. Komabe, paubatizo wake, Yesu akuloŵa muunansi watsopano ndi Mulungu, akumakhalanso Mwana wauzimu wa Mulungu. Tsopano Mulungu akumuitaniranso kumwamba, kunena kwake titero, mwa kumuyambitsanso njira imene idzatsogolera kukutaya moyo wake waumunthu munsembe kaamba ka anthu otsutsidwa. Mateyu 3:13-17; Luka 3:21-38; 1:34-36, 44; 2:10-14; Yohane 1:32-34; Ahebri 10:5-9.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu saali mlendo kwa Yohane?
▪ Popeza kuti Yesu sanachite machimo, kodi nchifukwa ninji akubatizidwa?
▪ Polingalira zimene Yohane akudziŵa ponena za Yesu, kodi nchifukwa ninji sangakhale wodabwa pamene mzimu wa Mulungu ukudza pa Yesu?