Mutu 21
M’Sunagoge wa Tauni ya Kwawo kwa Yesu
MOSAKAYIKIRA muli kuchita chidwi kwakukulu m’Nazarete pamene Yesu abwerera kwawo. Asanapite kukabatizidwa ndi Yohane kuposa pang’ono chaka chimodzi chapitacho, Yesu anadziŵika monga mmisiri wamatabwa. Koma tsopano akudziŵika kulikonse monga wochita zozizwitsa. Anthu okhala momwemo ali ofunitsitsa kumuwona akuchita zozizwitsa zimenezi pakati pawo.
Chiyembekezo chawo chikubuka pamene Yesu, malinga ndi chizolowezi chake, apita kusunagoge. Mkati mwa ulaliki wake, iye akuimirira kuti aŵerenge, ndipo mpukutu wa mneneri Yesaya ukuperekedwa kwa iye. Akupeza pamene pakunena za Wodzozedwa ndi mzimu wa Yehova, pamalo amene m’Baibulo lathu lerolino ali pa chaputala 61.
Ataŵerenga mmene Ameneyu adzalalikira za kumasulidwa kwa a mnsinga, kuchiritsidwa kwa akhungu, ndi za chaka chokomera Yehova, Yesu akubwezera mpukutuwo kwa kalinde nakhala pansi. Maso onse akumyang’ana dwii. Pamenepo akulankhula, mwinamwake kwa nthaŵi yotalikirapo, akumafotokoza kuti: “Lero lembo ili lakwaniritsidwa m’makutu mwanu.”
Anthu akudabwa pa ‘mawu ake achisomo’ nanena kwa wina ndi mnzake kuti: “Kodi uyu simwana wa Yosefe?” Koma podziŵa kuti iwo akufuna kumuwona iye akuchita zozizwitsa, Yesu akupitiriza kuti: “Kwenikweni mudzati kwa ine nkhani iyi, Sing’anga iwe, tadzichiritsa wekha zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kuno.” Mwachiwonekere, amene kale anali anansi a Yesu akulingalira kuti kuchiritsa kuyenera kuyamba kwawo, kupindulitsa anthu ake choyamba. Chotero akulingalira kukhala ataluluzidwa ndi Yesu.
Pozindikira kuganiza kwawo, Yesu akusimba za nkhani ina yowayenerera. Munali akazi amasiye ambiri mu Israyeli mkati mwa masiku a Eliya, iye akutero, koma Eliya sanatumizidwe kwa aliyense wa ameneŵa. Mmalomwake, anapita kwa mkazi wina wamasiye amene sanali Mwisrayeli ku Sidoniya, kumene anachitako chozizwitsa chopulumutsa moyo. Ndipo m’masiku a Elisa, kunali akhate ambiri, koma Eliya anachiritsa Naamani yekha wa ku Suriya.
Atakwiyitsidwa ndi zoyerekezera za m’mbiri zosakondweretsa zimenezi zovumbula dyera lawo ndi kupanda chikhulupiriro, a m’sunagogewo akunyamuka natulutsira Yesu kunja kwa mzinda. Ali kumeneko, pamwamba pa phiri limene Nazarete wamangidwapo, iwo akuyesa kumponyera pansi. Koma Yesu akupokonyoleka m’manja mwawo nazemba ali wotetezereka. Luka 4:16-30; 1 Mafumu 17:8-16; 2 Mafumu 5:8-14.
▪ Kodi nchifukwa ninji muli kuchita chidwi kwakukulu m’Nazarete?
▪ Kodi anthu akuganiza motani za kulankhula kwa Yesu, komano nchiyani chimene chikuwakwiyitsa kwambiri?
▪ Kodi anthu akuyesa kuchitanji kwa Yesu?