Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 21 tsamba 56-tsamba 57 ndime 6
  • Zimene Zinachitika Yesu Ali ku Sunagoge wa ku Nazareti

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Zinachitika Yesu Ali ku Sunagoge wa ku Nazareti
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • M’Sunagoge wa Tauni ya Kwawo kwa Yesu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nazarete—Kwawo kwa Mneneri
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Yesu Anachita Zozizwitsa Koma Anakanidwa Ngakhale Kwawo ku Nazareti
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kuchoka ku Nyumba ya Yairo ndi Kuchezeranso ku Nazarete
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 21 tsamba 56-tsamba 57 ndime 6
Yesu ali musunagoge ndipo akuwerenga mpukutu wa Yesaya

MUTU 21

Zimene Zinachitika Yesu Ali ku Sunagoge wa ku Nazareti

LUKA 4:16-31

  • YESU ANAWERENGA MPUKUTU WA YESAYA

  • ANTHU A KU NAZARETI ANAFUNA KUPHA YESU

Mosakayikira anthu anasangalala kwambiri Yesu atabwereranso ku Nazareti. Yesu ankagwira ntchito ya ukalipentala ali m’derali koma pa nthawiyi n’kuti patapita chaka chimodzi kuchokera pamene anabatizidwa ndi Yohane. Koma tsopano anthu ambiri ankamudziwa ngati munthu amene amachita zinthu zamphamvu ndi zozizwitsa. Anthu a ku Nazareti ankafunitsitsa kuona Yesu akuchita zinthu zozizwitsa.

Yesu atapita ku sunagoge, monga mwa chizolowezi chake, anthu ambiri ankayembekezera kuona zinthu zodabwitsa. Mwambowu unayamba ndi pemphero ndipo kenako anawerenga mabuku a Mose monga mmene zinkakhalira “m’masunagoge sabata lililonse.” (Machitidwe 15:21) Pa mwambowu, ankawerenganso mbali zina za mabuku a aneneri. Mosakayikira, Yesu ataimirira kuti ayambe kuwerenga, anazindikira anthu ambiri omwe ankakumana nawo pa nthawi imene ankasonkhana nawo m’sunagogeyu. Kenako anamupatsa mpukutu wa mneneri Yesaya ndipo anapeza pamene pamanena za Wodzozedwa ndi mzimu wa Yehova. M’Baibulo mawu amenewa amapezeka pa Yesaya 61:1, 2.

Yesu anawerenga za mmene Wodzozedwayo adzalengezere za ufulu kwa anthu ogwidwa ukapolo, kutsegula maso a akhungu komanso za kubwera kwa chaka chokomera Yehova. Atatero, Yesu anapereka mpukutuwo kwa wotumikira m’sunagogemo n’kukhala pansi. Anthu onse anamuyang’anitsitsa. Kenako analankhula kwa kanthawi ndithu ndipo ananenanso kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”—Luka 4:21.

Anthu anadabwa kwambiri ndi “mawu ogwira mtima otuluka pakamwa pake,” ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi iyeyu si mwana wa Yosefe?” Koma Yesu atazindikira kuti anthuwo akufuna kuti awachitire zozizwitsa ngati zimene anamva akuchita m’madera ena, ananena kuti: “Mosakayikira mawu akuti, ‘Wochiritsa iwe, dzichiritse wekha,’ mudzawagwiritsa ntchito pa ine. Mudzanena kuti: ‘Tinamva kuti unachita zinthu zambiri ku Kaperenao. Zinthu zimenezo uzichitenso kwanu kuno.’” (Luka 4:22, 23) N’kutheka kuti anthuwa ankaona kuti zikanakhala bwino Yesu akanayamba kuchiritsa anthu akwawo. Koma chifukwa chakuti sanachite zimenezo, ankaona kuti Yesu waachita chipongwe.

Yesu atadziwa zimene anthuwa ankaganiza, anawauza zinthu zimene zinachitika m’nthawi ya ana a Isiraeli. Anawauza kuti m’nthawi ya Eliya kunali akazi amasiye ambiri ku Isiraeli komabe Eliya sanatumidwe kwa akaziwo. M’malomwake anapita kwa mkazi wamasiye amene sanali Mwisiraeli. Mkaziyu ankakhala ku Zarefati, tauni yomwe inali kufupi ndi Sidoni. Kumeneko Eliya anaukitsa mwana wa mayiyo. (1 Mafumu 17:8-16) Yesu anawauzanso kuti m’nthawi ya Elisa, ku Isiraeli kunali akhate ambiri, koma mneneriyo anachiritsa Namani wa ku Siriya yemwe ankadwala khate.—2 Mafumu 5:1, 8-14.

Anthu amene anali musunagoge akududuluza Yesu kuti akamuponyere kuphedi

Kodi anthuwo anatani atazindikira kuti zimene Yesu ananenazo zinasonyeza kuti iwowo anali anthu odzikonda komanso opanda chikhulupiriro? Anthuwo anakwiya kwambiri moti anaimirira n’kumutulutsira kunja kwa mzinda. Anapita naye pamwamba pa phiri lomwe anamangapo mzinda wa Nazareti kuti akamuponye kuphedi. Koma Yesu anawapulumuka n’kuthawa. Zitatero, Yesu anapita ku Kaperenao kumpoto chakumadzulo kwa nyanja ya Galileya.

  • N’chifukwa chiyani anthu a ku Nazareti, komwe kunali kwawo kwa Yesu, anasangalala kwambiri?

  • Kodi anthuwo anatani atamva zimene Yesu ananena, koma n’chiyani chinawakwiyitsa?

  • Kodi anthu a ku Nazareti ankafuna kumuchita chiyani Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena