Malo Kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa
Nazarete—Kwawo kwa Mneneri
“NDIPO makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.” Inde, ngakhale m’nthaŵi ya uminisitala wa Yesu, kungomtchula iye kunakumbutsa mzinda umene tsopano ngotchuka wa Nazarete. Chotero, awo odza kudzamgwira sananene kuti anali kufunafuna Yesu koma “Yesu Mnazarayo.”—Mateyu 21:11; 26:71; Yohane 18:3-5; Machitidwe 26:9.
Chithunzi chiri pamwambachi chikusonyeza zimene mungapeze ngati muchezera Nazarete lerolino. Tsopano ngwokulirapo kwambiri kuposa pamene mngelo anabwera “ku mudzi wa ku Galileya dzina lake Nazarete” kudzawuza Mariya kuti akabala Mwana wa Mulungu. (Luka 1:26-33) Kalelo, Nazarete anali wofanana kwenikweni ndi mudzi wosonyezedwa pa tsamba lotsatirali, nyumba za ngondya zinayi zounjikana kumbali kwa chitunda. Yosefe ndi Mariya mwinamwake anakhala m’nyumba yofanana ndi zimenezi. Koma pamene Mariya anatsala pang’ono kukhala ndi mwana, iwo anapita kum’mwera ku Betelehemu, ndipo kumeneko Yesu anabadwa. Pambuyo pake iwo anathaŵira ku Igupto kutetezera kamwanako ku machenjera a Herode ofuna kukapha. Pambuyo pake, “anabwera ku Galileya, ku mudzi kwawo, ku Nazarete.”—Luka 2:4, 39; Mateyu 2:13-23.
Motero Yesu anakulira, osati mu mzinda wotchuka monga Yerusalemu kapena Tiberiya, koma m’malo abata. Nazarete anali m’dambo lozingidwa ndi zitunda za Kunsi kwa Galileya, kumene mbewu, mpesa, azitona, ndi nkhuyu zinachuluka. Anali malo a nyengo ya chirimwe yozizilira bwino, chikhalirechobe nyengo zake zachisanu sizinali zozizira mopambanitsa monga Kumtunda kwa Galileya.
Yosefe anasunga mkazi wake, ana ake aamuna, ndi aakazi mwakugwira ntchito monga mmisiri wa mitengo, mwinamwake wokhala ndi shopu monga iyi pano mu Nazarete wamakono. Iye ayenera kuti anakonza mitanda ya denga ndi zitseko zamatabwa za nyumba za mu mzinda, kapena matebulo, mipando, kapena zopanga zina zamatabwa. Tidziŵa kuti Yesu anapenyerera ndi kuphunzira, popeza kuti nayenso anadzatchedwa “mmisiri wa mitengo.” (Marko 6:3; Mateyu 13:55) Ntchito yaulimi mu Nazarete mwachiwonekere inatsogolera ku ntchito zina. Mwinamwake Yesu anasema goli longa lowoneka pa nyama ziri pano. Panthaŵiyo, mwinamwake Yosefe ankagwiritsira ntchito ziŵiya zake kupanga zolimira kapena zopunthira mbewu zokokedwa kumbuyo kwa goli.—2 Samueli 24:22; Yesaya 44:13.
Monga mnyamata, Yesu mothekera anayendayenda m’malo ozungulira Nazarete, onga ngati “Kana wa m’Galileya,” makilomita khumi ndi atatu kumpoto, kumene pambuyo pake anakachitira chozizwitsa chake choyamba. (Yohane 2:1-12) Akumayendayenda kwa chifupifupi makilomita khumi kum’mwera koma chakum’mawa kulinga ku Chigwa cha Yezreeli ndi Phiri la More, Yesu anakhoza kufika ku mzinda wa Nayini, wowoneka pa tsamba 17.a (Oweruza 6:33; 7:1) Kumbukirani kuti mkati mwa ulendo wake woyamba waulaliki, Yesu anafika pa maliro chapafupi ndi Nayini. Mosonkhezeredwa ndi chifundo, iye anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye.—Luka 7:11-16.
Nazarete sanakhazikitsidwe pa iriyonse ya misewu yaikulu yopyola m’dzikolo, komabe anali ndi njira zosavuta zofikira ku misewu yoteroyo. Mungawone zimenezi pa mapu ya pachikuto cha 1990 Kalenda ya Mboni za Yehova, imene irinso ndi chithunzi chokulirapo cha Nazarete lerolino. Njira yochokera kum’mawa kupita kumadzulo kupyola m’Chigwa cha Yezreeli inagwirizanitsa doko la Acre, kapena Ptolemayi, ndi Nyanja ya Galileya ndi Chigwa cha Yordano. Njira yochokera kum’mwera ku Damasiko inadutsa njirayi ikumatsikira kunsi kupyola m’Samariya mpaka ku Yerusalemu.
Nazarete anali ndi sunagoge wake, ndipo kuchiyambiyambi kwa uminisitala wake, Yesu anapita kumeneko “monga anazoloŵera.” Iye anaŵerenga Yesaya 61:1, 2, akumailozeretsa kwa iyemwini. Kodi ndimotani mmene anthu amzindawo akachitira, ena a iwo amene anamuwona akukula ndipo mwina kumlipira kaamba ka ntchito yake ya umisiri wamitengo? Iwo anakwiitsidwa ndikuyesa kumponya kuchokera pa chikweza, koma Yesu anathaŵa. (Luka 4:16-30) Mwachiwonekere, zimene anachita pambuyo pake mu Nayini ndi kwinakwake zinamvedwa ku Nazarete, popeza kuti pamene anabwerako ndikuphunzitsa m’sunagoge, palibe aliyense analankhula za kumupha. Chikhalirechobe, “sanachita kumeneko zamphamvu zambiri,” popeza kuti omzoloŵera mu Nazarete sanaike chikhulupiriro mwa iye monga mneneri.—Mateyu 13:53-58.
Marko akulemba mawu a Yesu kuti: “Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m’dziko la kwawo ndimo, ndi pakati pa abale ake, ndi m’nyumba yake.” Nzachisoni chotani nanga kuti zinalidi tero kwa ambiri mu Nazarete. Chikhalirechobe, tingalingalire mzinda umenewo kukhala kwawo kwa Mneneri amene tasankha kumlemekeza.—Marko 6:4.
[Mawu a M’munsi]
a Nazarete ndi #2 pa mapu yapachikuto pa 1990 Kalenda ya Mboni za Yehova. Phiri la More likuwonekera pansi pa #3.
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 17]
[Chithunzi patsamba 17]
[Chithunzi patsamba 17]