Mutu 28
Afunsidwa za Kusala Chakudya
PAFUPIFUPI chaka chimodzi chapita chiyambire pamene Yesu anafika pa Paskha wa 30 C.E. Pofika tsopano, Yohane Mbatizi wakhala ali m’ndende kwa miyezi ingapo. Ngakhale kuti iye anafuna kuti ophunzira ake akhale otsatira a Kristu, sionse amene atero.
Tsopano ena a ophunzira a Yohane womangidwawo akudza kwa Yesu namfunsa kuti: “Chifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kaŵirikaŵiri, koma ophunzira anu sasala?” Afarisi amasala kudya kaŵiri pamlungu monga mwa mwambo wachipembedzo chawo. Ndipo mwinamwake ophunzira a Yohane amatsatira mwambo wofananawo. Kungakhalenso kuti iwo akusala kudya kulira kuikidwa kwa Yohane m’ndende ndi kudabwa chifukwa chake ophunzira a Yesu sakugwirizana nawo m’kusonyeza chisoni kumeneku.
M’kuyankha Yesu akufotokoza kuti: “Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthaŵi imene mkwati akhala nawo? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.”
Ophunzira a Yohane ayenera kukumbukira kuti Yohane iye mwiniyo ananena za Yesu monga Mkwati. Chotero pamene Yesu adakalipo, Yohane sakalingalira kusala chakudya kukhala koyenera, ndipo ngakhalenso ophunzira a Yesu. Pambuyo pake, pamene Yesu afa, ophunzira ake akulira ndi kusala kudya. Koma pamene aukitsidwa ndi kupita kumwamba, alibe chifukwa china cholirira ndi kusala kudya.
Kenako, Yesu akupereka mafanizo awa: “Kulibe munthu aphathika chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pakuti chigamba chake chizomoka ku chofundacho, ndipo chichita chiboo chachikulu. Kapena samathira vinyo watsopano m’matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba awonongeka: koma athira vinyo watsopano m’matumba atsopamo.” Kodi mafanizo ameneŵa agwirizana pati ndi kusala kudya?
Yesu anali kuthandiza ophunzira a Yohane Mbatizi kuzindikira kuti palibe amene ayenera kuyembekezera kuti otsatira ake agwirizane ndi machitachita Achiyuda akale, monga ngati mwambo wakusala kudya. Iye sanadzere kudzaika dzigamba ndi kupitirizabe madongosolo akale a kulambira kumene kunali kwakuthaitha. Chikristu sichikanachititsidwa kuti chigwirizane ndi Chiyuda cha m’tsikulo ndi miyambo yake ya anthu. Ayi, sichikanakhala monga chigamba chatsopano pamalaya akale kapena vinyo watsopano m’matumba akale. Mateyu 9:14-17; Marko 2:18-22; Luka 5:33-39; Yohane 3:27-29.
▪ Kodi ndani amene akusala kudya, ndipo ncholinga chotani?
▪ Kodi nchifukwa ninji ophunzira a Yesu sasala kudya pamene ali nawo, ndipo pambuyo pake kodi ndimotani mmene chochititsa kusala kudya chidzachotsedwera msanga?
▪ Kodi ndimafanizo otani amene Yesu akusimba, ndipo akutanthauzanji?