Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 11/15 tsamba 3-4
  • Kodi Kusala Kudya Nkwachikale?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kusala Kudya Nkwachikale?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiŵiya Ndiponso Mwambo
  • Kodi Kusala Kudya Kumathandiza Munthu Kuyandikira kwa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kusala Kudya?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Mulungu Amafuna Kusala Kudya?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Afunsidwa za Kusala Chakudya
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 11/15 tsamba 3-4

Kodi Kusala Kudya Nkwachikale?

“NDAKHALA ndikusala kudya Lolemba lililonse kuyambira pamene ndinali wachichepere,” akutero Mrudulaben, mkazi wachuma wachimwenye wazaka 78. Imeneyi yakhala mbali ya kulambira kwake, njira yotsimikizirira kuti akhale ndi ukwati wabwino ndi ana athanzi, ndiponso chitetezero cha mwamuna wake. Tsopano pokhala mkazi wamasiye, iye akupitiriza kusala kudya pamasiku a Lolemba kaamba ka thanzi labwino ndiponso kaamba ka kulemerera kwa ana ake. Mofanana naye, akazi achihindu ochuluka amapanga kusala kudya kwa nthaŵi zonse kukhala mbali ya moyo wawo.

Prakash, mwamuna wabizinesi wazaka zake zapakati wokhala mu mlaga wa Mumbai (Bombay), ku India, akunena kuti amasala kudya chaka chilichonse pamasiku a Lolemba a Sawan (Shravan). Umenewu ndi mwezi wokhala ndi tanthauzo lapadera lachipembedzo pa kalendala yachihindu. Prakash akulongosola kuti: “Ndinayamba zimenezi kaamba ka zifukwa zachipembedzo, koma tsopano ndimapeza chisonkhezero chowonjezereka cha kupitiriza zimenezi kaamba ka zifuno za thanzi. Popeza kuti Sawan imafika pa kutha kwa nyengo ya monsoon, imapatsa mpata thupi langa kuti lidziyeretse lokha pa matenda a m’nyengo zamvula.”

Ena amalingalira kuti kusala kudya kumathandiza munthu mwakuthupi, mwamaganizo ndi mwauzimu. Mwachitsanzo Grolier International Encyclopedia inati: “Kufufuza kwasayansi kwaposachedwapa kukusonyeza kuti kusala kudya kungakhale kokomera thanzi ndipo, ngati kuchitidwa mosamala, kungachititse munthu kuzindikira zinthu bwino kwambiri.” Kukunenedwa kuti Wafilosofi wachigiriki Plato anali kusala kudya kwa masiku khumi kapena kuposa pamenepo ndi kuti katswiri wamasamu Pythagoras anachititsa ophunzira ake kusala kudya asanayambe kuwaphunzitsa.

Kwa ena, kusala kudya kumatanthauza kulekeratu chakudya chilichonse ndi madzi kwa nyengo ina yoikika, pamene kuli kwakuti ena amamwa zakumwa pa kusala kudya kwawo. Kuleka kudya zakudya zina kapena kupeŵa mtundu wina wa chakudya kumalingaliridwa kukhala kusala kudya ndi ambiri. Koma kusala kudya kwa nyengo yaitali kopanda chisamaliro kungakhale kwangozi. Mtolankhani Parul Sheth akunena kuti thupi litagwiritsira ntchito makabohaidireti ake, kenako limasintha maproteni a m’minyeŵa kukhala shuga ndiyeno limatembenukira pa mafuta a m’thupi. Kusintha mafuta kukhala shuga kumatulutsa zinthu za poizoni zotchedwa ketone body. Pamene zimenezi ziyamba kuchuluka, zimamka ku ubongo, zikumawononga ubongo ndi fupa lamsana. “Apa mpamene kusala kudya kungakhale kwangozi,” akutero Sheth. “Ungasokonezeke maganizo, ndipo zoipa kwambiri. . . . [Kungachititse munthu] kukomoka kwa nthaŵi yaitali ndipo potsirizira pake kufa.”

Chiŵiya Ndiponso Mwambo

Kusala kudya kwagwiritsiridwa ntchito monga chiŵiya champhamvu pa zolinga za ndale kapena za chitaganya cha anthu. Katswiri wa chiŵiya chimenechi wotchuka anali Mohandas K. Gandhi wa ku India. Pokhala wolemekezedwa kwambiri ndi anthu mamiliyoni mazana ambiri, iyeyo anagwiritsira ntchito kusala kudya kuti apereke chisonkhezero champhamvu pa makamu achihindu a ku India. Polongosola za chotulukapo cha kusala kudya kwake kuti athetse mkangano pakati pa antchito a m’mafakitale ndi eni mafakitale, Gandhi anati: “Chotulukapo chake chachikulu chinali chakuti panakhala mkhalidwe wabwino. Mtima wa eni mafakitale unakhudzidwa . . . Kunyanyala ntchito kunalekedwa nditasala kudya kwa masiku atatu okha.” Pulezidenti wa ku South Africa, Nelson Mandela, anakhala ndi phande pa kusala kudya kwa masiku asanu m’zaka zake za ukaidi womangidwira chifukwa cha ndale.

Komabe, unyinji wa awo amene asalapo kudya, achita zimenezo kaamba ka zifukwa za chipembedzo. Kusala kudya kuli mwambo wotchuka m’Chihindu. Pamasiku oikika, likutero buku lakuti Fast and Festivals of India [Kusala Kudya ndi Mapwando a ku India], “kusala kudya kotheratu kumachitidwa . . . samamwa konse ngakhale madzi. Amuna ndi akazi omwe amatsatira mosamalitsa kusala kudya . . . kuti apeze chimwemwe, kulemerera ndi chikhululukiro pa zophophonya ndi machimo.”

Kusala kudya kumachitidwa ndi onse m’chipembedzo cha Ajaini. The Sunday Times of India Review ikusimba kuti: “Mmuni [munthu wanzeru] wachijaini ku Bombay [Mumbai] anangomwa matambula aŵiri okha a madzi oŵiritsidwa patsiku​—kwa masiku 201. Anataya makilogalamu 33.” Ena amasala kudya kufikiradi pa kudzipha ndi njala, ali okhulupirira kuti zimenezi zidzawabweretsera chipulumutso.

Kwa anthu ambiri aakulu msinkhu otsatira Chisilamu, kusala kudya ndi thayo m’mwezi wa Ramadan. Sayenera kudya chakudya kapena kumwa madzi kuyambira pa kutuluka kwa dzuŵa kukafika pa kuloŵa kwa dzuŵa kwa mwezi wonse. Aliyense wodwala kapena amene ali paulendo m’nthaŵiyi ayenera kukwaniritsa masikuwo mwa kusala kudya panthaŵi ina. Lent, nyengo ya masiku 40 Isitala isanafike, ndiyo nthaŵi ya kusala kudya kwa ena a m’Dziko Lachikristu, ndipo magulu ena achipembedzo amasala kudya pamasiku ena apadera.

Kusala kudya sikunathedi konse. Ndipo popeza kuti kuli mbali ya zipembedzo zochuluka, tingafunse kuti, Kodi Mulungu amafuna kusala kudya? Kodi pali nthaŵi zimene Akristu angasankhe kusala kudya? Kodi kumeneku kungakhale kopindulitsa? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.

[Chithunzi patsamba 3]

Chipembedzo cha Jaini chimaona kusala kudya monga njira yopezera chipulumutso cha sou

[Chithunzi patsamba 4]

Mohandas K. Gandhi anagwiritsira ntchito kusala kudya monga chiŵiya champhamvu pa zolinga za ndale kapena za chitaganya cha anthu

[Chithunzi patsamba 4]

M’Chisilamu, kusala kudya ndi thayo m’mwezi wa Ramadan

[Mawu a Chithunzi]

Garo Nalbandian

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena