Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 33
  • Kukwaniritsa Ulosi wa Yesaya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukwaniritsa Ulosi wa Yesaya
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Ulosi wa Yesaya Unakwaniritsidwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi Mungazime Nyali Yofuka?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Yehova Wokonda Chilungamo ndi Chiweruzo
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Yehova—Gwero la Chilungamo Chenicheni
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 33

Mutu 33

Kukwaniritsa Ulosi wa Yesaya

YESU atamva kuti Afarisi ndi otsatira chipani cha Herode akulinganiza kumupha, iye ndi ophunzira ake akuchoka kumka ku Nyanja ya Galileya. Kunoko makamu aakulu ochokera m’Palestina yense, ndipo ngakhale kunja kwa malire ake, akudza kwa iye. Iye akuchiritsa ambiri, ndi chotulukapo chakuti awo onse amene ali ndi matenda owopsa akukankhanakankhana kuti amkhudze.

Chifukwa chakuti makamuwo ngaakulu, Yesu akuuza ophunzira ake kukhala ndi bwato nthaŵi zonse lomtumikira. Mwakupalasira patali pang’ono ndi m’mphepete mwa nyanjayo, iye angachititse khamulo kusiya kumpanikiza. Iye angawaphunzitse ali m’bwato kapena kupita kudera lina m’mphepete mwa nyanja kukathandiza anthu kumeneko.

Wophunzira wina Mateyu amasonyeza kuti ntchito ya Yesu imakwaniritsa “chonenedwa ndi Yesaya mneneri uja.” Pamenepo Mateyu amagwira mawu ulosi umene Yesu anakwaniritsa:

“Tawona, mnyamata wanga, amene ndinamsankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndidzaika mzimu wanga paiye, ndipo iye adzalalikira chiŵeruzo kwa akunja. Sadzalimbana, sadzafuula; ngakhale mmodzi sadzamva mawu ake m’makwalala; bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira iye adzatumiza chiŵeruzo chikagonjetse. Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.”

Ndithudi, Yesu, ali mtumiki wokondedwa amene Mulungu akondwera naye. Ndipo Yesu akusonyeza bwino lomwe chimene chiri chilungamo chowona, chimene chikuphimbidwa ndi miyambo ya chipembedzo chonyenga. Chifukwa cha kusagwiritsira ntchito kwawo molungama lamulo la Mulungu, Afarisi sadzathandizadi munthu wodwala pa tsiku la Sabata! Kusonyeza bwino lomwe chilungamo cha Mulungu, Yesu akupeputsira anthu zothodwetsa za miyambo yosayenera, ndipo chifukwa cha ichi, atsogoleri achipembedzo akuyesa kumupha.

Kodi zikutanthauzanji kuti iye ‘sadzalimbana, kapena sadzafuula kuti amvedwe m’makwalala’? Pochiritsa anthu, Yesu ‘mwamphamvu akulamula anthu kuti asamdziŵikitse.’ Iye safuna kukhala ndi mawu opokesera omlengeza mumsewu kapena kukhala ndi mbiri yoipitsidwa yonenedwa mwa manenanena a anthu.

Ndiponso, Yesu akutengera uthenga wake wotonthoza kwa anthu amene mophiphiritsira ali ngati bango lophwanyika, lopindika ndi lopondedwa. Ali ngati chingwe cha nyali chomazima, chimene kuŵala kwake kwatsala pang’ono kuzima. Yesu samaphwanya bango lophwanyika kapena kuzimitsa chingwe cha nyali choyaka, chotuluka utsi. Koma ndi chifundo ndi chikondi, mwaluso amadzutsa ofatsa. Ndithudi, Yesu ndiye munthuyo mwa amene mitundu iyenera kuyembekezera! Mateyu 12:15-21; Marko 3:7-12; Yesaya 42:1-4.

▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akusonyezera chilungamo bwino lomwe, mopanda mkangano kapena kufuula m’makwalala?

▪ Kodi ndani ali ngati bango lophwanyika ndi chingwe cha nyali chomazima, ndipo kodi Yesu amawachitira motani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena