Mutu 34
Kusankha Atumwi Ake
KWAKHALA pafupifupi chaka ndi theka chiyambire pamene Yohane Mbatizi anadziŵikitsa Yesu monga Mwanawankhosa wa Mulungu ndipo Yesu anayamba uminisitala wake wapoyera. Panthaŵi imeneyo, Andreya, Simoni Petro, Yohane, ndipo mwinamwake Yakobo (mbale wake wa Yohane), ndiponso Filipo ndi Natanayeli (wotchedwanso Bartolomeyo), anali atakhala ophunzira ake oyamba. M’nthaŵi yokwanira, ambiri anagwirizana nawo m’kutsatira Kristu.
Tsopano Yesu ali wokonzekera kusankha atumwi ake. Ameneŵa adzakhala atsamwali ake apafupi amene adzapatsidwa maphunziro apadera. Koma asanawasankhe, Yesu akupita kuphiri nathera usiku wonse akupemphera, mwachiwonekere akumapempha nzeru ndi dalitso la Mulungu. Pamene kucha, iye akuitana ophunzira ake ndipo kuchokera pakati pawo akusankha 12. Komabe, popeza kuti iwo akupitirizabe kukhala ophunzira a Yesu, nawonso akutchedwabe ophunzira.
Asanu ndi mmodzi amene Yesu akusankha, otchulidwa pamwambapa, ali awo amene anakhala ophunzira ake oyamba. Mateyu, amene Yesu anamuitana kuchokera pantchito yake yokhometsa msonkho, akusankhidwanso. Asanu ena osankhidwa ndiwo Yudasi (wotchedwanso Tadeyo), Yudasi Iskariote, Simon Mkanani, Tomasi ndi Yakobo mwana wa Alifeyo. Yakobo ameneyu amatchedwanso Yakobo Wamng’ono, mwinamwake chifukwa chakuti ngwochepa thupi kapena wazaka zakubadwa zochepa koposa mtumwi Yakobo winayo.
Pakali pano 12 ameneŵa akhala ndi Yesu kwanthaŵi yotalikirapo, ndipo akuŵadziwa bwino lomwe. Kunena zowona, ambiri a iwo ndiwo achibale ake. Yakobo ndi mbale wake Yohane mwachiwonekere ali abale a Yesu. Ndiponso mwinamwake Alifeyo anali mbale wake wa Yosefe, atate wa Yesu womlera. Chotero mwana wa Alifeyo, mtumwi Yakobo akakhalanso mbale wa Yesu.
Ndithudi, Yesu, analibe vuto m’kukumbukira maina a atumwi ake. Koma kodi inu mungawakumbukire? Eya, ingokumbukirani kuti pali aŵiri otchedwa Simoni, aŵiri otchedwa Yakobo, ndipo aŵiri otchedwa Yudasi, ndi kuti Simoni ali ndi mbale wake Andreya, ndipo Yakobo ali ndi mbale wake Yohane. Ndiyo mfungulo ya kukumbukira atumwi asanu ndi atatu. Ena anayiwo amaphatikizapo wamsonkho (Mateyu), munthu amene pambuyo pake anakayikira (Tomasi), ndi wina amene anaitanidwa ali pansi pa mtengo (Natanayeli), ndi tsamwali wake Filipo.
Khumi ndi mmodzi a atumwiwo ngochokera ku Galileya dera la kwawo kwa Yesu. Natanayeli ngwochokera ku Kana. Filipo, Petro, ndi Andreya ngochokera ku Betsaida, Petro ndi Andreya pambuyo pake anasamukira ku Kapernao, kumene kukuwonekera kukhala kumene Mateyu anali kukhala. Yakobo ndi Yohane anali m’bizinesi la nsomba ndipo mwachiwonekere anali kukhala ku kapena pafupi ndi Kapernao. Kukuwonekera kuti Yudase Iskariote, amene pambuyo pake anapereka Yesu, ndiye mtumwi yekha wochokera ku Yudeya. Marko 3:13-19; Luka 6:12-16.
▪ Kodi ndiatumwi ati amene angakhale anali abale a Yesu?
▪ Kodi ndiati amene ali atumwi a Yesu, ndipo kodi mungakumbukire motani maina awo?
▪ Kodi atumwiwo anachokera kumadera ati?