Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 80 tsamba 188-tsamba 189 ndime 1
  • Yesu Anasankha Atumwi 12

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anasankha Atumwi 12
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Anasankha Atumwi 12
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kusankha Atumwi Ake
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kusankha Atumwi Ake
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yesu Aphunzitsa pa Phiri
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 80 tsamba 188-tsamba 189 ndime 1
Yesu ali ndi atumwi ake 12

MUTU 80

Yesu Anasankha Atumwi 12

Yesu atalalikira pafupifupi kwa chaka ndi hafu, ankafunika kusankha zinthu zina zofunika kwambiri. Anafunika kusankha anthu apadera oti azigwira nawo ntchito yolalikira. Anthuwa anafunikanso kuwaphunzitsa kuti adzathe kutsogolera mpingo wa Chikhristu iye akadzapita kumwamba. Yesu anaona kuti m’pofunika kuti Yehova amutsogolere posankha anthuwo. Choncho anapita kuphiri kwayekhayekha ndipo anapemphera usiku wonse. Kutacha, anaitana ophunzira ake ena ndipo anasankhapo anthu 12 oti akhale atumwi. Kodi ukukumbukira mayina awo? Anali Petulo, Andireya, Yakobo, Yohane, Filipo, Batolomeyo, Tomasi, Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni ndi Yudasi Isikariyoti.

Andireya, Petulo, Filipo, Yakobo

Andireya, Petulo, Filipo, Yakobo

Atumwi 12 amenewa ankayenda ndi Yesu. Kenako atawaphunzitsa, anayamba kumapita okha. Yehova anawapatsa mphamvu kuti azitha kutulutsa ziwanda komanso kuchiritsa odwala.

Yohane, Mateyu, Batolomeyo, Tomasi

Yohane, Mateyu, Batolomeyo, Tomasi

Yesu ankaona kuti atumwi 12 amenewa ndi anzake ndipo ankawakhulupirira. Koma Afarisi ankaganiza kuti atumwiwo anali osaphunzira komanso anthu wamba. Komatu Yesu anawaphunzitsa kuti azigwira bwino ntchito yawo. Atumwiwo anakhalabe ndi Yesu pa nthawi yofunika kwambiri pa moyo wake. Mwachitsanzo, analipo Yesu atatsala pang’ono kuphedwa komanso ataukitsidwa. Mofanana ndi Yesu ambiri mwa atumwiwa anali ochokera ku Galileya. Ndipo ena anali okwatira.

Yakobo mwana wa Alifeyo, Yudasi Isikariyoti, Tadeyo, Simoni

Yakobo mwana wa Alifeyo, Yudasi Isikariyoti, Tadeyo, Simoni

Koma atumwiwa sanali angwiro ngati ife tomwe ndipo ankalakwitsa zinthu zina. Pena ankalankhula asanaganize ndiponso ankasankha molakwika. Nthawi zinanso sankaleza mtima komanso ankakangana kuti wamkulu ndi ndani. Komabe atumwiwa anali anthu abwino ndipo ankakonda Yehova. Iwo ndi amene anali anthu oyamba kukhala mumpingo wa Chikhristu Yesu atapita kumwamba.

“Ndakutchulani kuti anzanga, chifukwa ndakudziwitsani zinthu zonse zimene ndamva kwa Atate wanga.”​—Yohane 15:15

Mafunso: Kodi Yesu anasankha anthu 12 ati kuti akhale atumwi ake? Kodi Yesu anatumiza atumwi ake kuti akagwire ntchito iti?

Mateyu 10:1-10; Maliko 3:13-19; 10:35-40; Luka 6:12-16; Yohane 15:15; 20:24, 25; Machitidwe 2:7; 4:13; 1 Akorinto 9:5; Aefeso 2:20-22

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena