Mutu 52
Yesu Adyetsa Zikwi Zambiri Mozizwitsa
ATUMWI 12 asangalala ndi ulendo wochititsa nthumanzi wolalikira m’Galileya monse. Tsopano, mwamsanga pambuyo pa kuphedwa kwa Yohane, akubwerera kwa Yesu ndipo akusimba zokumana nazo zawo zokondweretsazo. Powona kuti iwo atopa ndi kuti anthu ochuluka motero akudza napita kotero kuti iwo alibe ngakhale nthaŵi ya kudya, Yesu akuti: ‘Tiyeni timuke kumalo atokha kumene mungapumule.’
Ataloŵa m’bwato lawo, mwinamwake pafupi ndi Kapernao, iwo akuyamba kupita kumalo akutali a iwo okha, mwachiwonekere chakummaŵa kwa Yordano kupitirira Betsaida. Komabe, anthu ambiri, akuwawona akuchoka, ndipo ena adziŵa za kuchoka kumeneko. Onsewo akuthamangira kutsogolo m’mphepete mwagombelo, ndipo pamene bwato lifika, anthuwo ali konko kuwachingamira.
Potuluka m’bwato ndi kuwona khamu lalikulu, Yesu akugwidwa chisoni chifukwa anthuwo ali ngati nkhosa zopanda mbusa. Chotero iye akuchiritsira odwala awo nayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.
Nthaŵi ikupita mofulumira, ndipo ophunzira a Yesu akudza kwa iye nanena: “Malo ano ngakuchipululu, ndipo nthaŵi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite kumidzi kukadzigulira okha kamba.”
Komabe, poyankha Yesu akuti: “Apatseni ndinu adye.” Pamenepo, popeza kuti Yesu akudziŵa kale chimene akachita, akuyesa Filipo mwakumfunsa kuti: “Tidzagula kuti mikate yoti adye awa?”
Malinga ndi lingaliro la Filipo mkhalidwewo ngwosatheka. Eya, pali pafupifupi amuna 5,000, ndipo mwinamwake anthu oposa bwino lomwe 10,000 poŵerenganso akazi ndi ana! Filipo akuyankha kuti “mikate ya lupiya matheka mazana aŵiri [panthaŵiyo lupiya la theka linali malipiro a tsiku limodzi] sikwanira iwo, kuti yense atenge pang’ono.”
Mwinamwake kuti asonyeze kusatheka kwa kudyetsa ochuluka chotero, Andreya akudzipereka kuti: “Pali mnyamata amene ali nayo mikate pano isanu ya barele ndi tinsomba tiŵiri,” akumawonjezera kuti, “koma nanga izi zifikira bwanji otere?”
Popeza iri nthaŵi ya ngululu, mwamsanga Paskha wa 32 C.E. asanachitike, pali maudzu obiriŵira ambiri. Chotero Yesu akuuza ophunzira ake kuti auze anthuwo kuseyama pamaudzu m’magulu a 50 ndi 100. Iye akutenga mitanda isanu ndi nsomba ziŵirizo, nayang’ana kumwamba, nadalitsa. Pamenepo akuyamba kunyema mitandayo ndi kugaŵa nsomba. Iye akupereka zimenezi kwa ophunzira ake, amenenso, akugaŵira anthu. Mozizwitsa, anthu onse akudya kufikira atakhuta!
Pambuyo pake Yesu akuuza ophunzira ake kuti: “Sonkhanitsani kuti kasatayike kanthu.” Pamene akutero, akuzadza mitanga 12 ndi makombo ochokera ku zimene iwo adya! Mateyu 14:13-21; Marko 6:30-44; Luka 9:10-17; Yohane 6:1-13.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akufunafuna malo achete kaamba ka atumwi ake?
▪ Kodi Yesu akupita nawo kuti ophunzira ake, ndipo kodi nchifukwa ninji kufunikira kwawo kwa mpumulo sikukukwaniritsidwa?
▪ Pamene kulinkuda, kodi ophunzirawo akulimbikitsa chiyani, koma kodi ndimotani mmene Yesu akusamalirira anthuwo?