Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 83 tsamba 194-tsamba 195 ndime 1
  • Yesu anadyetsa anthu ambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu anadyetsa anthu ambiri
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Anadyetsa Anthu Masauzande Ambiri ndi Mikate Komanso Nsomba Zochepa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Mozizwitsa Adyetsa Zikwi
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Yesu Adyetsa Zikwi Zambiri Mozizwitsa
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yesu Anapereka Chakudya Modabwitsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 83 tsamba 194-tsamba 195 ndime 1
Atumwi akupereka chakudya kwa anthu

MUTU 83

Yesu Anadyetsa Anthu Ambiri

Tsiku lina atumwi anabwera kuchokera kumene ankalalikira. Apa n’kuti Pasika wa mu 32 C.E. atangotsala pang’ono kufika. Atumwiwo anali atatopa kwambiri ndipo Yesu ananyamuka nawo pa boti kupita ku Betsaida kuti akapume. Koma atayandikira kumtunda anaona kuti anthu ambirimbiri afika kale ndipo akuwadikira. Ngakhale kuti inali nthawi yoti apume ndi ophunzira ake, Yesu anawalandira bwino. Anachiritsa odwala onse ndipo kenako anayamba kuwaphunzitsa. Yesu anawaphunzitsa zokhudza Ufumu wa Mulungu tsiku lonse. Ndiyeno madzulo, atumwi anamuuza kuti: ‘Anthuwatu ali ndi njala. Auzeni azipita kuti akapeze chakudya.’

Mnyamata akupatsa Yesu mkate ndi nsomba

Yesu anayankha kuti: ‘Asapite. Inuyo muwapatse chakudya.’ Atumwiwo anafunsa kuti: ‘Mukutanthauza kuti tipite kukawagulira chakudya?’ Ndiyeno mtumwi wina dzina lake Filipo anati: ‘Ngakhale tikanakhala ndi ndalama zambiri sitingakwanitse kugula chakudya cha anthu onsewa.’

Yesu anawafunsa kuti: ‘Chakudya chomwe tili nacho n’chochuluka bwanji?’ Andireya anati: ‘N’chochepa kwambiri. Tili ndi mikate 5 ndi nsomba ziwiri basi.’ Kenako Yesu anati: ‘Bweretsani.’ Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pa udzu m’magulu a anthu 50 komanso 100. Yesu anatenga mikate ndi nsombazo n’kuyang’ana kumwamba ndipo anapemphera. Kenako anapereka chakudyacho kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo ankapereka kwa anthu. Panali amuna 5,000 ndiponso akazi ndi ana koma onse anadya n’kukhuta. Atumwiwo anatolera zotsalira n’cholinga choti pasatayidwe kalikonse. Zotsalazo zinadzadza mabasiketi 12. Izitu zinali zodabwitsa kwambiri.

Anthu ataona zimenezi anadabwa kwambiri moti ankafuna kuti Yesu akhale mfumu yawo. Koma Yesu anadziwa kuti imeneyo sinali nthawi imene Yehova ankafuna kuti iye akhale mfumu. Kenako anauza anthu onse kuti azipita ndipo iye ndi atumwi ake anapita tsidya lina la nyanja ya Galileya. Atumwiwo anakwera boti koma Yesu anapita yekha kuphiri kuti akapemphere kwa Atate ake. Yesu ankayesetsa kupeza mpata wopemphera ngakhale kuti ankatanganidwa kwambiri.

“Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chimabweretsa moyo wosatha. Mwana wa munthu adzakupatsani chakudya chimenechi.”​—Yohane 6:27

Mafunso: Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda kwambiri anthu? Kodi zimene anachitazi zikusonyeza kuti Yehova ndi wotani?

Mateyu 14:14-22; Luka 9:10-17; Yohane 6:1-15

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena