Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 107
  • Fanizo la Phwando Laukwati

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Fanizo la Phwando Laukwati
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Fanizo la Phwando la Ukwati
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mfumu Inaitanira Anthu ku Phwando la Ukwati
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Asangalatsidwa ndi Mfarisi Wotchuka
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kucherezedwa ndi Mfarisi
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 107

Mutu 107

Fanizo la Phwando Laukwati

MWANJIRA ya mafanizo aŵiri, Yesu wavumbula alembi ndi akulu ansembe, ndipo afuna kumupha. Koma Yesu sanatherane nawobe. Iye akupitiriza kuwauza za fanizo linabe, akumati:

“Ufumu wakumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wake phwando laukwati, natumiza akapolo ake kukaitana oitanidwa ku ukwati umene; ndipo iwo sanafuna kudza.”

Yehova Mulungu ndiye Mfumu imene ikulinganiza phwando laukwati kaamba ka Mwana wake wamwamuna, Yesu Kristu. Potsirizira pake, mkwatibwi wa otsatira odzozedwa 144,000 adzagwirizanitsidwa ndi Yesu kumwamba. Nzika za Mfumuyo ndiwo anthu a Israyeli, amene, poloŵetsedwa m’pangano Lachilamulo mu 1513 B.C.E., analandira mwaŵi wa kukhala “ufumu wa ansembe.” Motero, pachochititika chimenecho, iwo choyamba anaitaniridwa kuphwando laukwati.

Komabe, chiitano choyambacho kwa oitanidwawo sichinatuluke kufikira m’mphakasa ya 29 C.E., pamene Yesu ndi ophunzira ake (akapolo a mfumu) anayamba ntchito yawo ya kulalikira Ufumu. Koma Aisrayeli akuthupi amene analandira chiitano choperekedwa ndi akapolocho kuyambira 29 C.E. kufikira 33 C.E. anali osafunitsitsa kudza. Chotero Mulungu anapereka mpata wina kwa mtundu woitanidwawo, monga momwe Yesu akusimbira kuti:

“Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Wonani, ndakonza phwando langa; ng’ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsa: idzani ku ukwati.” Chiitano chachiŵiri chimenechi ndi chomaliza cha oitanidwawo chinayamba pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene mzimu woyera unatsanuliridwa pa otsatira a Yesu. Chiitano chimenechi chinapitirizabe kufikira 36 C.E.

Komabe, unyinji wa Aisrayeliwo, unakananso chiitano chimenechi. “Iwo ananyalanyaza, nachoka,” Yesu akutero, “wina ku munda wake, wina ku malonda ake; ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha.” “Koma,” Yesu akupitirizabe, “mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wawo.” Zimenezi zinachitika mu 70 C.E., pamene Yerusalemu anatenthedwa psiti ndi Aroma, ndipo ambandawo anaphedwa.

Pamenepo Yesu akufotokoza chimene chinachitika panthaŵiyo: “Pomwepo [mfumuyo] inanena kwa akapolo ake, Zaukwati tsopano zapsa, koma oitanidwawo sanayenera. Chifukwa chake pitani inu kumphambano za njira, ndipo amene aliyense mukampeze, itanani kuukwatiku.” Akopolowo anachita zimenezi, ndipo ‘chipinda cha madzoma aukwati chinadzaza ndi oseyama pagome.’

Ntchito iyi ya kusonkhanitsa alendo ochokera kumakwalala a kunja kwa mzinda wa oitanidwawo inayamba mu 36 C.E. Ofisala wa gulu lankhondo Lachiroma Korneliyo ndi banja lake anali oyamba mwa anthu osadulidwa osakhala Ayuda osonkhanitsidwa. Kusonkhanitsidwa kwa osakhala Ayuda ameneŵa, onse amene anali kubwezeretsedwa kwa awo amene poyambilira anakana chiitanocho, kwapitirizabe kudzafika m’zaka za zana la 20.

Muli mkati mwa zaka za zana la 20 limeneli pamene chipinda cha madzoma aukwati chikufikira pakudzaza. Pamenepo Yesu akusimba chimene chikuchitika, akumati: “Koma mfumuyo mmene inadza kuwawona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosavala chovala chaukwati; nanena kwa iye, Mnzangawe, unawaloŵa muno bwanji wosakhala nacho chovala chaukwati? Ndipo iye analibe mawu. Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.”

Munthu wopanda chovala chaukwatiyo amaphiphiritsira Akristu m’dzina lokha a Chikristu Chadziko. Mulungu sanavomereze konse ameneŵa monga okhala nacho chizindikiro choyenera cha kukhala Aisrayeli auzimu. Mulungu sanawadzoze konse ndi mzimu woyera monga oloŵa nyumba a Ufumu. Chotero iwo akuponyeredwa kunja kumdima kumene adzalandira chiwongeko.

Yesu akumaliza fanizo lake mwakunena kuti: “Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo oŵerengeka.” Inde, panali ambiri amene anaitanidwa kuchokera mumtundu wa Israyeli kuti adzakhale ziŵalo za mkwatibwi wa Kristu, koma ochepekera chabe a Israyeli wakuthupi anasankhidwa. Ochuluka a alendo a 144,000 amene amalandira mphotho yakumwamba kwenikweni sali Aisrayeli. Mateyu 22:1-14; Eksodo 19:1-6; Chivumbulutso 14:1-3.

▪ Kodi ndani amene ali oyambilira kuitanidwa kuphwando laukwati, ndipo kodi ndiliti pamene anaitanidwa?

▪ Kodi ndiliti pamene chiitano choyamba chikuperekedwa kwa oitanidwawo, ndipo ndani amene ali akapolo ochipereka?

▪ Kodi ndiliti pamene chiitano chachiŵiri chikuperekedwa, ndipo kodi pambuyo pake ndayani amene akuitanidwa?

▪ Kodi ndani amene akuphiphiritsiridwa ndi munthu wopanda chovala chaukwati?

▪ Kodi ndani amene ali anthu ambiri oitanidwa, ndi oŵerengeka osankhidwa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena