Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rq phunziro 3 tsamba 6-7
  • Kodi Yesu Kristu Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yesu Kristu Ndani?
  • Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Kristu—Kodi Anatumidwa ndi Mulungu?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Yesu Khristu Ndani?
    Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Kodi Yesu Khristu Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Yesu Kristu, kupyolera mwa Amene Mulungu Adzawadalitsa Anthu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Onani Zambiri
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
rq phunziro 3 tsamba 6-7

Phunziro 3

Kodi Yesu Kristu Ndani?

Kodi n’chifukwa ninji Yesu amatchedwa Mwana “wobadwa woyamba” wa Mulungu? (1)

N’chifukwa ninji amatchedwa “Mawu”? (1)

N’chifukwa ninji Yesu anabwera padziko lapansi monga munthu? (2-4)

Kodi anachitiranji zozizwitsa? (5)

Kodi Yesu adzachitanji patsogolopa? (6)

1. Yesu anali kumwamba monga munthu wauzimu asanabwere padziko lapansi. Iye anali cholengedwa choyamba cha Mulungu, choncho amatchedwa Mwana “wobadwa woyamba” wa Mulungu. (Akolose 1:15; Chivumbulutso 3:14) Yesu ndiye Mwana yekha amene Mulungu mwini analenga mwachindunji. Yehova anagwiritsira ntchito Yesu wauzimu monga “mmisiri” wake polenga zinthu zina zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi. (Miyambo 8:22-31; Akolose 1:16, 17) Mulungu anamgwiritsiranso ntchito monga womlankhulira Wake wamkulu. N’chifukwa chake Yesu amatchedwa “Mawu.”—Yohane 1:1-3; Chivumbulutso 19:13.

2. Mulungu anatuma Mwana Wake kudziko lapansi mwa kusamutsira moyo wake m’mimba mwa Mariya. Chotero Yesu analibe atate waumunthu. N’chifukwa chake sanalandire choloŵa cha uchimo kapena kupanda ungwiro. Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi kaamba ka zifukwa zitatu: (1) Kudzaphunzitsa choonadi ponena za Mulungu (Yohane 18:37), (2) kusunga umphumphu wangwiro, akumapereka chitsanzo chakuti ife titsatire (1 Petro 2:21), ndipo (3) kupereka moyo wake nsembe yotimasulira ku uchimo ndi imfa. Kodi n’chifukwa ninji zimenezi zinali zofunikira?—Mateyu 20:28.

3. Mwa kuswa lamulo la Mulungu, munthu woyamba, Adamu, anachita chimene Baibulo limatcha “uchimo.” Chotero Mulungu anamweruzira ku imfa. (Genesis 3:17-19) Sanalinso pamlingo wa miyezo ya Mulungu, chotero sanalinso wangwiro. Pang’ono ndi pang’ono iye anakalamba namwalira. Adamu anapatsira uchimo kwa ana ake. N’chifukwa chake nafenso timakalamba, kudwala, ndi kufa. Kodi anthu akanapulumutsidwa motani?—Aroma 3:23; 5:12.

4. Yesu anali munthu wangwiro monga analili Adamu. Komabe, mosiyana ndi Adamu, Yesu anamvera Mulungu mwangwiro ngakhale pansi pa chiyeso chachikulu koposa. Chotero anali wokhoza kupereka moyo wake nsembe kulipirira uchimo wa Adamu. Izi n’zimene Baibulo limatcha “chiwombolo.” Motero zinali zotheka kwa ana a Adamu kumasulidwa ku chiweruzo cha imfa. Onse amene asonyeza chikhulupiriro mwa Yesu machimo awo angakhululukidwe ndipo akhoza kulandira moyo wosatha.—1 Timoteo 2:5, 6; Yohane 3:16; Aroma 5:18, 19.

5. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anachiritsa odwala, anadyetsa anjala, natontholetsa namondwe. Anaukitsa ndi akufa. Kodi anachitiranji zozizwitsa? (1) Anachitira chifundo anthu ovutikawo, ndipo anafuna kuwathandiza. (2) Zozizwitsa zake zinatsimikizira kuti analidi Mwana wa Mulungu. (3) Zinasonyeza zimene adzachitira anthu omvera pamene adzalamulira dziko lapansi monga Mfumu.—Mateyu 14:14; Marko 2:10-12; Yohane 5:28, 29.

6. Yesu anamwalira ndipo anaukitsidwa ndi Mulungu monga cholengedwa chauzimu, ndipo anabwerera kumwamba. (1 Petro 3:18) Chiyambire nthaŵiyo, Mulungu wamuika kukhala Mfumu. Posachedwapa Yesu adzachotsa kuipa konse ndi mavuto padziko lino lapansi.—Salmo 37:9-11; Miyambo 2:21, 22.

[Zithunzi patsamba 7]

Utumiki wa Yesu unaphatikizapo kuphunzitsa, kuchita zozizwitsa, ngakhale ndi kupereka moyo wake kaamba ka ife

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena