Phunziro 12
Kulemekeza Moyo ndi Mwazi
Kodi ndi motani mmene tiyenera kuonera moyo? (1) kuchotsa mimba? (1)
Kodi Akristu amasonyeza motani kuti amasamala kupeŵa ngozi? (2)
Kodi kupha nyama nkulakwa? (3)
Kodi ndi machitachita ena ati amene samalemekeza moyo? (4)
Kodi lamulo la Mulungu pa mwazi n’lotani? (5)
Kodi ilo limaphatikizapo kuika mwazi? (6)
1. Yehova ndiye Magwero a moyo. Zamoyo zonse zinalandira moyo kwa Mulungu. (Salmo 36:9) Moyo ngwopatulika kwa Mulungu. Ngakhale moyo wa mwana wosabadwa ali m’mimba mwa amake ngwamtengo wapatali kwa Yehova. Kupha dala khanda lomakula limenelo nkulakwa pamaso pa Mulungu.—Eksodo 21:22, 23; Salmo 127:3.
2. Akristu oona amasamala kupeŵa ngozi. Amatsimikiza kuti galimoto ndi nyumba zawo sizili zangozi. (Deuteronomo 22:8) Atumiki a Mulungu samaikira dala moyo wawo pangozi kuti asanguluke kapena kukondwera. Chotero samachitako maseŵero achiwawa amene amavulaza dala anthu ena. Amapeŵa zosangulutsa zimene zimasonkhezera chiwawa.—Salmo 11:5; Yohane 13:35.
3. Moyo wa nyama ulinso wopatulika kwa Mlengi. Mkristu angaphe nyama kuti apeze chakudya ndi chovala kapena kuti apeŵe matenda ndi ngozi. (Genesis 3:21; 9:3; Eksodo 21:28) Koma nkulakwa kuchitira nkhanza nyama kapena kuzipha monga kuseŵera kapena kusanguluka.—Miyambo 12:10.
4. Akristu sayenera kusuta fodya, kutafuna betel nut, ndi kumwa anamgoneka kuti asanguluke. Machitachita ameneŵa ngolakwa chifukwa (1) timakhala akapolo ake, (2) amavulaza matupi athu, ndipo (3) ngodetsa. (Aroma 6:19; 12:1; 2 Akorinto 7:1) Kumakhala kovuta kwambiri kusiya zizoloŵezi zimenezi. Koma tiyenera kutero kuti tikondweretse Yehova.
5. Mwazi ulinso wopatulika pamaso pa Mulungu. Mulungu amati moyo uli m’mwazi. Chotero nkulakwa kudya mwazi. Ndiponso nkulakwa kudya nyama imene sinakhetsedwe bwino. Ngati nyama yapotoledwa kapena ngati yafera mumsampha, siyenera kudyedwa. Ngati yabayidwa kapena kuwomberedwa mfuti, iyenera kukhetsedwa mwamsanga ngati ndi yakudya.—Genesis 9:3, 4; Levitiko 17:13, 14; Machitidwe 15:28, 29.
6. Kodi nkulakwa kuvomereza kuikidwa mwazi? Kumbukirani, Yehova amafuna kuti tisale mwazi. Zimenezi zikutanthauza kuti sitiyenera kuika m’thupi mwathu mwanjira iliyonse mwazi wa anthu ena ngakhale mwazi wathu umene wasungidwa. (Machitidwe 21:25) Chotero Akristu oona samavomereza kuikidwa mwazi. Iwo amavomereza mitundu ina ya kuchiritsa, monga ngati kuikidwa zinthu zopanda mwazi. Iwo amafuna kukhala ndi moyo, koma samayesa kupulumutsa moyo wawo mwa kuswa malamulo a Mulungu.—Mateyu 16:25.
[Zithunzi patsamba 25]
Kuti tikondweretse Mulungu, tiyenera kupeŵa kuikidwa mwazi, zizoloŵezi zodetsa, ndi ngozi zosafunikira