Chiitano Chathu kwa Inu
Tasangalala kulankhula nanu kudzera m’kabuku kano. Tikhulupirira kuti inunso mwasangalala kudziŵa zambiri zokhudza Mboni za Yehova. Chonde, bwerani mudzacheze nafe ku Nyumba ya Ufumu ya kwathu kuno. Dzaoneni mmene misonkhano yathu imachitikira. Dzaoneni mmene timauzira ena za uthenga wabwino wonena za dziko laparadaiso mu Ufumu wa Kristu.
Limenelo ndi lonjezo la Mulungu. “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Papita zaka mazanamazana. Nthaŵi yodikira ikutha tsopano. Mikhalidwe ya m’dziko imasonyeza zimenezo.
“Monga momwe muona tsiku lilikuyandikira,” anatero mtumwi Paulo, “tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi.” (Ahebri 10:24, 25) Tikukulimbikitsani kumvera uphungu wa Paulo mwa kumasonkhana nafe.