Mutu 4
Wolemba Wamkulu wa Buku Lapaderalo
1, 2. Kodi mukuganiza kuti chilengedwe chinayamba motani?
NGAKHALE kuti 96 peresenti ya anthu a ku America amati amakhulupirira Mulungu, ku Ulaya ndi Asia chiŵerengero n’chochepa kwambiri. Ngakhale m’mayiko kumene anthu ambiri amati sakhulupirira Mulungu, aliko ochuluka ndithu amene amavomereza kuti pali mphamvu inayake yosadziŵika imene inachititsa kuti chilengedwe choonekachi chikhalepo. Mphunzitsi wina wodziŵika kwambiri wachijapani, Yukichi Fukuzawa, amene nkhope yake ili pa ndalama yapepala ya 10,000 yen, analemba kuti: “Amati kumwamba sikulenga munthu wina kukhala woposa mnzake.” Potchula mawu akuti “kumwamba,” Fukuzawa anali kunena za mphamvu ya chilengedwe imene ankaganiza kuti ndiyo inapanga anthu. Ambiri amavomereza kuti mphamvu yotchedwa “kumwamba” imeneyo ilikodi, mofanana ndi wopata mphoto ya Nobel, Kenichi Fukui. Iye ananena za kukhulupirira kwake dongosolo lalikulu limene lili m’chilengedwe, lofanana ndi “Mulungu” m’chipembedzo, koma analitcha kuti ndi “mbali yapadera ya chilengedwe.”
2 Anthu ophunzira oterowo amakhulupirira kuti pali chinachake kapena winawake wamuyaya amene anayambitsa chilichonse chimene chili m’chilengedwe. Chifukwa chiyani? Chabwino, talingalirani izi: Dzuŵa ndi nyenyezi yaikulu kwambiri moti likhoza kuloŵetsa m’kati mwake mayiko apansi okwanira wani miliyoni, komabe ilo n’laling’onong’ono mu mlalang’amba wotchedwa Milky Way. Komanso mlalang’amba umenewunso wa Milky Way, ndi umodzi chabe wa mabiliyoni a milalang’amba kuthambo. Umboni wa sayansi ukuonetsa kuti milalang’amba imeneyo ikuyenda mofutukana paliŵiro lalikulu kwambiri. Poyambitsa chilengedwecho kuyenda, payenera kuti panali mphamvu yaikulu koopsa. Kodi ndani kapena n’chiyani chinayambitsa mphamvu imeneyo? “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo,” limatero Baibulo. “Amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse mayina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.” (Yesaya 40:25, 26) Mawu ameneŵa amasonyeza kuti analipo winawake amene anayambitsa chilengedwe kuyenda—Gwero la ‘mphamvu zazikulu.’
3. Kodi mukuona kukhala zotheka kuti moyo unangoyamba wokha?
3 Taganiziraninso za moyo padziko lapansi. Kodi n’kutheka kuti moyo unangoyamba wokha, mmene amanenera okhulupirira ivolushoni kapena kuti kusinthika? Katswiri wa zinthu zamoyo Michael Behe anati: “Asayansi apita patsogolo kwambiri pa kuzindikira mmene moyo wa zinthu umagwirira ntchito, komabe madongosolo a m’mamolekyu awagometsa moti alephereratu kufotokoza magwero ake. . . . Asayansi ambiri mwaliuma ayesa kunena kuti mafotokozedwe ake akuyamba kudziŵika tsopano, kapena kuti adzadziŵika posachedwa, koma zimenezo zilibe umboni uliwonse m’mabuku a akatswiri a sayansi. Chofunika koposa, pali zifukwa zosakanika—malinga ndi mpangidwe wa madongosolo [a mamolekyu] enieniwo—oonetsa kuti mafotokozedwe a Darwin onena za mmene moyo unayambira adzakhalabe opanda umboni wodalirika mpaka kalekale.”
4. Kodi mphamvu ya ubongo wa munthu imakuuzani chiyani ponena za mmene ubongo unakhalirako?
4 Kodi mulidi okhutira ndi maganizo amenewo akuti moyo wa munthu unakhalapo wokha popanda winawake wanzeru wouyambitsa? Tiyeni titenge chinthu china chimene ena achiona kukhala “chinthu chodabwitsa koposa m’chilengedwe,” ubongo wa munthu, ndi kuona zimene tingaganize. Dr. Richard M. Restak anati: “Luso la kompyuta yotsogola kwambiri yotsanzira mmene ubongo wa munthu umagwirira ntchito, yotchedwa neural-network computer, ili chabe 1 kwa 10,000. . . poiyerekeza ndi luso la ntchentche.” Koma ubongo wa ntchentche suli kanthu pouyerekeza ndi ubongo wa munthu. Pobadwa, ubongo wa munthu umakhala utalembedwa kale luso lophunzira zinenero m’kati mwake. Umadzikonza wokha, umalemba mapulogalamu, ndipo umawonjezera luso lake. Ndithudi, inunso mukuvomereza kuti ngakhale kompyuta yamphamvu kwambiriyo, yokhala ndi luso la “1 kwa 10,000 poiyerekeza ndi luso la ntchentche,” ili ndi winawake wanzeru amene anaipanga. Bwanji nanga za ubongo wa munthu?a
5, 6. Kodi maganizo anu tsopano ndi otani ponena za Gwero la moyo?
5 Zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, anthu asanafike pozindikira mokwanira zodabwitsa za matupi awo, wolemba Baibulo wina anasinkhasinkha za mpangidwe wa thupi la munthu ndipo anati: ‘Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu n’zodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.’ Asakudziŵa chilichonse za mamolekyu a DNA, iye analemba kuti: “Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziŵalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu.” (Salmo 139:14, 16) Kodi anali kunena za ndani? Kodi ndani amene ndi ‘mphamvu zazikulu’ anapanga zonse zimene zili m’chilengedwe?
6 Vesi loyambirira lenilenilo la m’Baibulo limati: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Ameneyu ndi amenenso ali Mlembi Wamkulu wa Baibulo, amenenso anauzira nkhani zomwe zili mmenemo. Iyeyo akudzidziŵikitsa yekha kukhala Mulungu amene tingakhale naye paubwenzi wopindulitsa.
[Mawu a M’munsi]
a Mudzasangalala poŵerenga mfundo zina pamitu 2 mpaka 4 m’buku lachingelezi lakuti Is There a Creator Who Cares About You?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 16]
“Dongosolo la puloteni imodzi . . . lingayerekezedwe ndi samu yovuta kwambiri kuipeza kwake,” anatero Michael Behe. Komabe, thupi la munthu lili ndi masauzande ambirimbiri a masamu oterowo. Asayansi akuyesetsa kupeza masamu amenewo, koma kodi anawalemba ndani?
[Chithunzi]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Ma amino acid
Ma protein subunit
Ma complex protein
[Chithunzi patsamba 15]
Yukichi Fukuzawa
[Chithunzi patsamba 15]
Kenichi Fukui
[Zithunzi patsamba 17]
Kodi chopambana paluso ndi chiti, kompyuta yotsogola kwambiri yotchedwa neural-network computer, kapena ntchentche wamba?