Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • la mutu 6 tsamba 20-21
  • Kodi Yehova Anatilengeranji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yehova Anatilengeranji?
  • Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Sayansi Ingabweretse Moyo Wosatha?
    Galamukani!—2000
  • Kodi Moyo Wosatha Ndi Wothekadi?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Mulungu Wachita Zinthu Ziti?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Kodi Tingapambane Motani Pamene Tikufunafuna Moyo Wautali?
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
la mutu 6 tsamba 20-21

Mutu 6

Kodi Yehova Anatilengeranji?

1. Kodi maganizo a Solomo anali otani pa cholinga cha moyo?

KODI mudzafunikira kuchitanji kuti mum’dziŵe Yehova? Mwa zina, mudzafunikira kupeza yankho pa funso limene limasokoneza anthu ambiri: ‘Kodi n’chifukwa chiyani ndilipo?’ Mwina nthaŵi zina mwaganizirapo zimenezo. Mfumu ina yanzeru imene “inaposa mafumu onse a padziko lapansi,” pa za chuma m’nthaŵi yake, inaganizira za tanthauzo la moyo. (2 Mbiri 9:22; Mlaliki 2:1-13) Mfumu imeneyo, Solomo, inali ndi mphamvu zochuluka, chuma chambiri, ndi nzeru zosayerekezeka. Kodi chimene inaphulapo pa kupambana konseko chinali chiyani? “Mawu atha, zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.” (Mlaliki 12:13) Popeza Solomo anaona ndi kudziŵa zambiri koposa anthu ochuluka, maganizo akewo ndi oyenera kuti tiwalingalire.—Mlaliki 2:12.

2. Kodi kuopa Mulungu kumatanthauza chiyani?

2 Kuopa Mulungu kumene Solomo anatchula si ndiko mantha oopa kuvulazidwa ndi mphamvu inayake yosadziŵika ya mzimu ayi. M’malo mwake, ndi mantha abwino oopa kukhumudwitsa munthu amene mumam’konda kwambiri. Ngati munthu wina mumam’konda kwambiri, ndithudi mudzafuna kumam’kondweretsa nthaŵi zonse ndi kupeŵa kuchita china chilichonse chimene chingam’khumudwitse. Pamene muyamba kum’konda Yehova, mudzaonanso chimodzimodzi ponena za iye.

3. Kodi cholinga cha Yehova polenga anthu chinali chiyani?

3 Mwa kuŵerenga Baibulo, mutha kuphunzira zimene Mlengi wathu amakonda ndi zimene sakonda, limodzinso ndi cholinga chake popanga dziko lapansi. Ponena za Yehova monga “amene anaumba dziko lapansi, nalipanga,” Baibulo limatinso “Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Yehova anakonza dziko lapansi kuti akhalemo anthu, amene anayenera kuyang’anira dziko lapansili ndi zolengedwa zonse zili mmenemo. (Genesis 1:28) Koma kodi cholinga cha Yehova chinali chokhacho polenga anthu—kukhala oyang’anira basi?

4. Kodi n’chiyani chimene chikanapangitsa moyo wa anthu kukhala wokhutiritsa?

4 Ayi, chinalipo cholinga china chokulirapo. Munthu woyambayo, Adamu, anali paubale watanthauzo ndi Yehova. Adamu amatha kulankhula ndi Mlengiyo mwachindunji. Iye amatha kumvetsera zimene Mulungu ankamuuza komanso amatha kumuuza Yehova maganizo ake. (Genesis 1:28-30; 3:8-13, 16-19; Machitidwe 17:26-28) Chotero, Adamu ndi mkazi wake, Hava, anali ndi mwayi waukulu kwambiri wom’dziŵa Yehova bwino lomwe ndi kupalana naye ubale wozama kwambiri. Kum’dziŵa Yehova ndi kum’tsanzira kunapangitsa miyoyo yawo kukhala yokhutiritsa, pakuti iye ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Monga Mulungu “amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo,” Yehova anaika munthu woyamba m’paradaiso, wotchedwa munda wa Edene, ndi kum’patsa chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha.—1 Timoteo 6:17; Genesis 2:8, 9, 16, 17.

5, 6. Kodi malingaliro anu ndi otani ponena za moyo wosatha? Chifukwa chiyani?

5 Moyo wosatha? Mwina zokhala ndi moyo wosatha mungazione kukhala zosatheka, koma kodi n’zosathekadi? Asayansi amakhulupirira kuti tsopano akudziŵa chimene chimachititsa maselo kukalamba. Tinthu tina ta m’majini totchedwa ma telomere, timene timatseka kumapeto kwa ma chromosome, timafupikirapo nthaŵi zonse pamene selo ligaŵika. Selo litagaŵika ka 50 mpaka ka 100, ma telomere amenewo amatha ndipo maselo ambiri amasiya kugaŵikana. Komabe, zimene asayansi atulukira posachedwapa zimasonyeza kuti mothandizidwa ndi puloteni ina yotchedwa telomerase, maselo a anthu akhoza kupitiriza kumagaŵikana mosalekeza. Ngakhale kuti zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amatheketsa moyo wosatha kudzera mwa puloteni yapadera imeneyi, zimasonyezabe chinthu chimodzi: Kuti kukhala ndi moyo wosatha ndi chinthu chotheka ndithu.

6 Inde, nkhani ya m’Baibulo yonena kuti anthu aŵiri oyambirira analengedwa kuti akhale ndi moyo wosatha ndi yoona. Anthu anafunikira kuti akhale ndi ubale wozama ndi Yehova mpaka ku nthaŵi zosatha. Anafunikira kukhala ndi mgwirizano wamphamvu ndi Atate wawo wakumwamba, podziŵa bwino lomwe za cholinga chake kwa anthu padziko lapansi ndi kuchikwaniritsa. Miyoyo yawo siikanakhala yotopetsa. Adamu ndi Hava anali ndi chiyembekezo chodabwitsa chodzaza dziko lapansi ndi ana achimwemwe ndi angwiro. Iwo akanakhala ndi ntchito zokhutiritsa ndi zatanthauzo kosatha. Ha, kukhutiritsa kwake mmene moyo umenewo ukanakhalira!—Genesis 1:28.

[Chithunzi patsamba 21]

(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)

Kodi zimene zadziŵika posachedwapa ponena za maselo a munthu zikusonyezanji?

Chromosome

Telomere

Telomere

[Chithunzi patsamba 20]

Mfumu Solomo inasinkhasinkha za cholinga cha moyo

[Chithunzi patsamba 20]

Adamu ndi Hava anali paubale wabwino ndi Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena