Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 10/15 tsamba 4-7
  • Kodi Tingapambane Motani Pamene Tikufunafuna Moyo Wautali?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingapambane Motani Pamene Tikufunafuna Moyo Wautali?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Kugwiritsa Ntchito Mahomoni ndi Majini Kumapereka Zifukwa Zokhalira ndi Chiyembekezo?
  • Kodi Sayansi ya Nanotechnology ndi Cryonics Ndiyo Idzatheketsa Zimenezo?
  • Kodi Tiyenera Kukhulupirira Ndani?
  • Chomwe Chimachititsa Ukalamba ndi Imfa
  • Chiyembekezo Chenicheni
  • Moyo Wosatha M’Dziko Lapansi la Paradaiso
  • N’chifukwa Chiyani Timakalamba?
    Galamukani!—2006
  • Kufufuza Moyo Wautali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Nchifukwa Ninji Timakalamba ndi Kufa?
    Galamukani!—1995
  • Anthu Akhala Akufunafuna Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 10/15 tsamba 4-7

Kodi Tingapambane Motani Pamene Tikufunafuna Moyo Wautali?

ENA amakhulupirira kuti tikadzalowa m’zaka za 2000, zoyesayesa za munthu zofuna kutalikitsa moyo zidzapambana. Mmodzi wa iwo ndi Dr. Ronald Klatz. Iye ndi mkulu wa bungwe la American Academy of Anti-Aging Medicine. Bungweli ndi la madokotala ndi asayansi amene akulingalira kuti angathe kutalikitsa zaka zimene munthu angakhale ndi moyo. Iyeyu ndi anzake ena akufuna kuti akhale ndi moyo kwa nthaŵi yaitali kwambiri. “Ndikuyembekezera kukhala ndi moyo kwa zaka 130 kapena kupitirirapo,” anatero Dr. Klatz. “Tikukhulupirira kuti kukalamba kungapeŵeke. Pali njira zamakono zimene zingachedwetse, kuletseratu, ngakhalenso kulepheretsa kunyonyotsoka kwa mphamvu za m’thupi ndi matenda zomwe tsopano zikutchedwa ukalamba wachibadwidwe.” Dr. Klatz mwiniyo amamwa mapilisi 60 tsiku lililonse poyesetsa kuti akhale ndi moyo wautali.

Kodi Kugwiritsa Ntchito Mahomoni ndi Majini Kumapereka Zifukwa Zokhalira ndi Chiyembekezo?

Kugwiritsa ntchito mahomoni ngati mankhwala kwapangitsa ena kukhala ndi chiyembekezo. Kuyesera homoni yotchedwa DHEA pa nyama, kunaonetsa kuti kungachedwetse ukalamba wa nyama za m’nyumba zopangira kafukufuku wa za sayansi.

Ponena za homoni ya zomera, yotchedwa kinetin, nyuzipepala ina yotchedwa Aftonbladet ya ku Sweden inagwira mawu a Dr. Suresh Rattan, pulofesa wa pa yunivesite ya Aarhus, ku Denmark akuti: “Kuyesa komwe tinapanga m’nyumba zathu zopangira kafukufuku wa sayansi, kunasonyeza kuti maselo a khungu la munthu oikidwa mu kinetin sanasinthe monga mmene ena ofanana nawo zaka anachitira. Sanakalambe m’moyo wawo onse.” Tizilombo tomwe taikidwa mahomoni amenewo, moyo wawo umatalika ndi 30 kapena 45 peresenti ya utali wa moyo wawo wanthaŵi zonse.

Kuthira homoni ya Melatonin akuti kunatalikitsa moyo wa mbeŵa ndi 25 peresenti. Komanso, mbeŵazo zimaoneka kuti n’zosakalamba, ndi zathanzi, ndiponso zamphamvu zedi.

Olimbikitsa kugwiritsa ntchito homoni yomwe imathandiza kukula kwa munthu akuti imapangitsa munthu kukhala wonyezimira khungu, wonenepa, chilakolako cha kugonana chimawonjezeka, amakhala wosangalala, wanzeru zochuluka, ndiponso thupi lake limayamba kugwira ntchito ngati la wachinyamata.

Enanso amakhulupirira majini. Asayansi akuti angathe kuchepetsa kapena kuchulukitsa masiku amoyo wa nyongolotsi mwa kusintha kagwiridwe ntchito ka majini. Ndithudi, iwo atha kusunga zina kuŵirikiza kasanu ndi kamodzi nthaŵi yomwe zimayenera kukhala ndi moyo. Zimenezi zawapatsa chiyembekezo chakuti adzapeza ndi kusintha kagwiridwe ka ntchito ka majini onga amenewo mwa anthu. Times magazine inagwira mawu Dr. Siegfried Hekimi wa pa yunivesite ya McGill ku Montreal, akuti: “Tikatulukira majini amene amakalambitsa munthu, mwina tingaŵapange kuti adzitha kuchedwetsa ntchito yawo yokalambitsa munthuyo, ndipo potero munthu adzatha kukhala ndi moyo wautali.”

Akatswiri a zamoyo akhala akudziŵa kwanthaŵi yaitali kuti kumapeto kwa ma chromosome komwe kumatchedwanso telomere, kumafupika nthaŵi zonse pamene seloyo yabala maselo ena. Pamene telomere yafupika ndi 20 peresenti, maselo ake samakhalanso ndi mphamvu yakuti angaswane ndipo nthaŵi yomweyo imafa. Enzyme ina yotchedwa telomerase imabwezeretsa telomere yonse, zomwe zimathandiza kuti maselo azichulukanabe. M’maselo ena enzyme imeneyi yachotsedwamo ndipo imakhala yofooka, koma telomerase yamphamvu yabwezeretsedwa m’maselo ena, zomwe zatheketsa kuti akule ndi kuswana mowirikiza.

Opanga kafukufuku akunena kuti zimenezi zitheketsa thupi kulimbana ndi matenda amene amadza munthu akamakula. Kodi n’kotheka kubwezeretsa maselo ena, omwe amachulukitsa maselo a mtundu umodzi (maselo amene amathandiza kuti mnofu wa m’thupi ubwezeretsedwe) ndi maselo enanso a mtundu omwewo, koma amene apatsidwa mphamvu ya “kusafa” poŵathira telomerase? Dr. William A. Haseltine anati: “Zimenezi n’zachionekere kuti pang’ono ndi pang’ono moyo udzayamba kukhala wosafa mwa njira imeneyi m’zaka zina 50 zikubwerazi.”​—The New York Times.

Kodi Sayansi ya Nanotechnology ndi Cryonics Ndiyo Idzatheketsa Zimenezo?

Nanotechnology, Sayansi yogwira ntchito mwaluso, pa mlingo waung’ono zedi wa mita (chigawo chimodzi mwa zigawo biliyoni za mita) imaperekanso chiyembekezo. Akatswiri amene amatha kuoneratu zam’tsogolo pa nkhani imeneyi, amafotokoza kuti timakompyuta tating’onoting’ono kwambiri kuposa maselo, tidzagwiritsidwa ntchito mwaluso ngati mamolekyu kuti tizikonza ndi kupatsanso nyonga yatsopano maselo okalamba, minofu ndi ziwalo zina. Pamsonkhano wina wokambirana zothetsa ukalamba, wofufuza wina ananena kuti m’zaka za zana la 21, madokotala azidzagwiritsa ntchito njira ya nanotechnology, potheketsa thupi la munthu kukhala losafa.

Cryonics ndi sayansi youmitsa matupi a anthu akufa mwa kuwaziziritsa ndi chiyembekezo chakuti sayansi idzabwezera moyo ku maselo akufawo, ndipo munthuyo n’kukhalanso ndi moyo. Amaziziritsa thupi lonse kapena ubongo wokha. Munthu wina anaziziritsa shitibedi. N’chifukwa chiyani anaziziritsa nsalu? Inali ya bwenzi lake lomwe linamwalira, ndipo munatsalira maselo a khungu ndi tsitsi loŵerengeka. Anaziziritsa zimenezi ndi cholinga chakuti sayansi ikadzafika pobwezeretsa moyo wa anthu, pogwiritsa ntchito ngakhale selo imodzi yokha, mnzakeyo adzakhalenso ndi moyo.

Kodi Tiyenera Kukhulupirira Ndani?

Munthu mwachibadwa amafuna kukhala ndi moyo, osati kumafanso. Choncho, kupita patsogolo kwa sayansi pambali imeneyi, kwatamandidwa zedi ndiponso kwapereka chiyembekezo chachikulu. Koma pakalipano palibe umboni wogwira mtima wakuti DHEA, kinetin, melatonin, hGH, kapena mankhwala ena alionse angaletse anthu kukalamba. Okayikira malingaliro asayansiŵa amanena kuti mwina kuika telomerase m’maselo kungayambitse maselo a kansa. Ndiponso nanotechnology ndi cryonics ndi nthanthi chabe za asayansi osati zenizeni.

Sayansi yathandiza ndipo ipitirizabe kuthandiza ena kukhala ndi moyo wotalikirapo ndi wathanzi, koma siidzapatsa moyo wamuyaya kwa aliyense. Chifukwa chiyani? Kunena mwachidule, chifukwa chake n’chakuti chimene chimachititsa ukalamba ndi imfa asayansiwo sakuchidziŵa.

Chomwe Chimachititsa Ukalamba ndi Imfa

Asayansi ambiri amavomereza kuti ukalamba ndi imfa n’zachibadwa m’majini. Funso n’lakuti: Kodi ukalamba ndi imfa zinaloŵa liti ndipo zinaloŵa motani m’dongosolo la majini athu? Nanga n’chifukwa chiyani zinaloŵa m’majini anthuwo?

Baibulo likupereka yankho losavuta​—ngakhale kuti sililongosola za majini kapena DNA. Aroma 5:12 amati: “Chifukwa chake, monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”

Munthu woyambayo, Adamu, anafunikira kukhala ndi moyo wosatha. Thupi lake linapangidwa ndi zonse zofunikira kuti athe kukhala ndi kusangalala ndi moyo wamuyaya. Komabe, moyo wosathawo unadalira kanthu kena. Adamu anayenera kugwirizana kotheratu ndi kukhala womvera Mwini moyo, Mlengi wake, kuti akhalebe ndi moyo kunthaŵi zosatha.​—Genesis 1:31; 2:15-17.

Adamu anasankha kusamvera Mlengiyo. Potero, Adamu anaonetsa maganizo akuti munthu angakhale ndi moyo wabwino kwambiri mwa kudziimira payekha osadalira Mulungu. Choncho anachimwa. Kuyambira pamenepo, zinakhala ngati kuti dongosolo la majini ake linasokonezeka. M’malo mopatsira moyo wosatha kwa mbadwa zake, Adamu anapatsira uchimo ndi imfa.​—Genesis 3:6, 19; Aroma 6:23.

Chiyembekezo Chenicheni

Komabe zinthu sizinali kudzakhala choncho nthaŵi zonse. Aroma 8:20 amati: “Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha iye amene anachigonjetsa.” Mlengi wa munthu, Yehova Mulungu, anagonjetsera anthu ku imfa chifukwa chakuti anam’chimwira, komabe pamene anali kuchita izi, anaikanso maziko a chiyembekezo.

Maziko amenewa anaonekeratu pamene Yesu Kristu anabwera padziko lapansi. Yohane 3:16 amati: “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Komabe, kukhala wokhulupirira mwa Yesu Kristu kungatipulumutse motani ku imfa?

Ngati tchimo ndilo linadzetsa imfa, ndiyeno tchimolo liyenera kuchotsedwa choyamba, kuti imfa ithetsedwe. Kuchiyambiyambi kwa utumiki wa Yesu monga Kristu, Yohane Mbatizi anati: “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!” (Yohane 1:29) Yesu Kristu analibiretu tchimo. Choncho, sanagonjetsedwe ku imfa, yomwe ndi chilango cha uchimo. Komabe, analola kuphedwa. Chifukwa chiyani? Chifukwa mwa kuchita zimenezo anapereka dipo la machimo athu.​—Mateyu 20:28; 1 Petro 3:18.

Dipo limenelo, linatsegula njira ya kumoyo wosatha kwa onse okhulupirira mwa Yesu. Sayansi ingathandize pang’ono chabe kutalikitsa masiku a moyo wathu, koma kukhulupirira mwa Yesu, ndiyo njira yokhayo yakumuka nayo ku moyo wosatha. Yesu anapeza moyo umenewo kumwamba, ndiponso atumwi ake okhulupirika ndi enanso adzatero. Koma ochulukafe amene tikhulupirira mwa Yesu, tidzasangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi, pamene Yehova Mulungu adzabwezeretsa Paradaiso pa dziko lonse lapansi.​—Yesaya 25:8; 1 Akorinto 15:48, 49; 2 Akorinto 5:1.

Moyo Wosatha M’Dziko Lapansi la Paradaiso

Mwamuna wina anafunsa kuti: “Ndi anthu angati amene angakonde kudzakhala ndi moyo wopanda imfa?” Kodi moyo wopanda imfa udzakhala wotopetsa? Baibulo limatitsimikizira kuti sudzakhala wotopetsa. “Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.” (Mlaliki 3:11). Chilengedwe cha Yehova Mulungu n’chosaneneka kuchuluka kwake, ndipo n’chocholowana mwakuti chidzapitirizabe kutichititsa chidwi, kutisonkhezera, ndi kutisangalatsa pamene tikukhala ndi moyo​—ngakhale wosatha.

Munthu wina amene anafufuza za mbalame ina yodziŵika ndi dzina lakuti Siberian Jay anaitcha kuti “n’njodabwitsa, bwenzi lokondweretsa.” Ndipo ananenanso kuti kuonerera mbalame chinali chimodzi mwa zinthu zosangalatsa zedi zomwe wachita m’moyo wake. Chidwi chake chinakula zedi pamene anawonjeza ntchito yake yofuna kudziŵa zambiri za mbalameyo. Iye ananenanso kuti atapanga kafukufuku ameneyo kwa zaka 18, anaona kuti ntchito yakeyo inali yambiri zedi kwakuti sakanaitsiriza m’nthaŵi yochepa. Ngati mtundu umodzi wa mbalame ungachititse chidwi, kusonkhezera, ndi kupangitsa munthu wanzeru kusangalala m’nyengo ya zaka 18 ya kafukufuku wamphamvu, tangolingalirani za chimwemwe ndi chikhutiro zomwe zidzakhalapo pamene tizidzafufuza chilengedwe chonse cha dziko lapansi.

Talingalirani za mbali zosiyanasiyana zosangalatsa zedi za sayansi zomwe anthu adzafufuze popanda kuda nkhawa za kuchepa kwa nthaŵi. Talingalirani za malo osangalatsa zedi omwe tizidzayendera ndi anthu ochititsa chidwi amene tizidzakumana nawo kumeneko. N’zambiri zomwe zidzachitika polingalira, kupanga, ndi kumanga zinthu. Sipadzakhala malire popititsa patsogolo ndi kugwiritsa ntchito maluso athu opanga zinthu. Tikalingalira za kuchuluka kwa chilengedwe, sitikayika kuti moyo wosatha ndi umene udzatipatsa nthaŵi yokwanira yochita chilichonse chomwe moyo ungathe kuchita.

Baibulo limasonyeza kuti chiukiriro chidzatheketsa awo amene ali m’manda kudzalandiranso moyo wosatha. (Yohane 5:28, 29) Zinsinsi za m’mbiri yakale tidzazimvetsetsa bwino lomwe pamene omwe anazionawo adzatilongosolere zambiri ndi kuyankha mafunso athu. Ganizirani za nkhani zonse za m’nthaŵi zosiyanasiyana za m’mbiri zomwe oukitsidwa adzafotokoza.​—Machitidwe 24:15.

Polingalira za nthaŵiyo, mungazindikire kuti Yobu akadzaukitsidwa angadzafune kusintha mawu ake opezeka pa Yobu 14:1. Mwinamwake m’malo mwa mawu amenewo, adzanena kuti: ‘Munthu wobadwa ndi mkazi, tsopano n’ngwa moyo wosatha nakhutira nawo.’

Kwa awo amene aika chikhulupiriro chawo mwa Yehova, ndi kukhulupirira Yesu, moyo wosatha siloto chabe. Posachedwa udzakhala weniweni. Kukalamba ndi imfa zidzatheratu. Zimene zikugwirizana kotheratu ndi Salmo 68:20, lomwe limati: ‘Ndipo Yehova, Ambuye Mfumu ali nazo zopulumutsira kuimfa.’​—Chivumbulutso 21:3, 4.

[Zithunzi patsamba 4, 5]

Kupita patsogolo kwa sayansi kwadzutsa chiyembekezo ponena za kuthekera kokhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali

[Chithunzi patsamba 7]

Moyo wosatha ndi umene udzatipatse nthaŵi yokwanira yochitira chilichonse chimene moyo ungathe kuchita

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena