Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 2 tsamba 86-tsamba 88 ndime 3
  • Kulankhula Momveka Bwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhula Momveka Bwino
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhala ndi Kalankhulidwe Kabwino Tsiku ndi Tsiku
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kuwongolera Kamvekedwe ka Mawu ndi Kugwiritsa Ntchito Cholankhulira
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 2 tsamba 86-tsamba 88 ndime 3

PHUNZIRO 2

Kulankhula Momveka Bwino

Kodi muyenera kuchita motani?

Lankhulani m’njira yosavuta kumva kwa omvera. Zimenezi zimaphatikizapo (1) kugwiritsa ntchito bwino ziwalo zolankhulira ndipo (2) kumvetsa kapangidwe ka mawu.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Pamene mulankhula bwino, ena amamva zimene mukunena. Ngati mulankhula momveka bwino, anthu amalabadira mosavuta mawuwo.

KUTI munene zogwira mtima, muyenera kulankhula momveka bwino. Zimene mukufuna kunena zingakhale zosangalatsa, kapena zofunika kwambiri, koma zambiri zingatayike ngati mawu anu sakumveka bwinobwino.

Anthu sakopeka ndi nkhani imene sakuimva bwinobwino. Ngakhale munthu atakhala ndi liwu lamphamvu ndi lomveka kwambiri, ngati mawu ake akumveka ngati obulumunyira, salimbikitsa aliyense kuchitapo kanthu. Zimakhala ngati akulankhula m’chinenero chachilendo, chosadziŵika kwa omvera. (Yer. 5:15) Baibulo limatikumbutsa kuti: “Ngati lipenga lipereka mawu osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo? Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mawu omveka bwino, kudzazindikirika bwanji chimene chilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.”—1 Akor. 14:8, 9.

N’chiyani Chimachititsa Mawu Kusamveka Bwino? Kungakhale kusatsegula pakamwa mokwanira. Ngati nyama za m’nsagwada zikhala zokungika, ndiponso ngati milomo siiyenda momasuka, mawu amamveka ngati mwavumata chinthu m’kamwa.

Kumakhalanso kovuta kumvetsa mawu a munthu wolankhula mofulumira kwambiri. Kumakhala ngati kuchunira pothamanga kwambiri kaseti imene anajambulamo nkhani. Mawu amakhalamo, koma matanthauzo ake amatayika.

Nthaŵi zina, chimachititsa kusalankhula bwino ndi vuto la m’ziwalo zolankhulira. Koma ngakhale amene ali ndi vuto lotero, akhoza kuwongokerapo mwa kuyesetsa kugwiritsa ntchito maganizo operekedwa m’phunziro lino.

Koma kaŵirikaŵiri, chimachititsa kulankhula zosamveka bwino ndi kulankhula molumikiza mawu ambiri—kulankhula mosalekanitsa bwino mawu moti kumakhala kovuta kuwamvetsa. Vutolo lingaphatikizepo kulumphira masilabo (maphatikizo amalembo), kapena malembo ofunika, kapenanso kutchula mawu mosamalizitsa. Munthu akamalankhula molumikiza mawu ambiri mosasamala, omvera ake angatolere malingaliro ena ndi mawu ena, koma zinazo amangoyerekeza zimene akutanthauza. Iwo angatolere malingaliro ndi mawu ena ndi ena, komano adzafunikiranso kuyesa kulumikiza ichi ndi ichi kuti apeze ganizo lake. Choncho, kusalankhula momveka bwino kumafooketsa mphamvu ya zimene munthuyo akuphunzitsa.

Mmene Mungalankhulire Momveka Bwino. Chimodzi cha zinsinsi za kulankhula momveka bwino ndicho kumvetsa kapangidwe ka mawu m’chinenero chanu. M’zinenero zambiri, mawu amapangidwa ndi masilabo. M’Chicheŵa, silabo ndiyo vawelo kapena phatikizo limodzi la malembo, m’liwu limodzi, imene imatchulidwa nthaŵi imodzi. M’zinenero zinanso, silabo iliyonse imamveka polankhula, koma ndi kutsindika kosiyanasiyana. Ngati mukufuna kumamveka bwino polankhula, lankhulani modekha ndipo yesetsani kutchula silabo iliyonse. Poyamba mungamveke ngati mukukokomeza, koma popitiriza kuyeseza, mudzafika polankhula mosadodoma. Pofuna kulankhula mosadodoma, nthaŵi zina mungalankhule molumikiza mawu ambiri, koma peŵani zimenezo ngati muona kuti lingaliro la mawu likutayika.

Chenjezo: Kuti mukulitse luso la kulankhula komveka bwino, muziyeseza kulankhula ndi kuŵerenga bwino mokokomeza (mopambanitsa). Koma chisakhale chizoloŵezi cha kalankhulidwe kanu ka tsiku ndi tsiku. Kumamveka koyerekeza osati kwachibadwa.

Ngati polankhula mawu anu amamveka ngati ovumatira, phunzirani kutukula mutu, ndi kukankhira chibwano patali ndi chifuwa. Poŵerenga m’Baibulo, kwezerani Baibulo m’mwamba kotero kuti musamakweze ndi kutsitsa kwambiri maso poyang’ana omvera ndi m’Baibulo. Izi zidzathandiza kuti mawu anu azituluka momasuka.

Kudziŵa kumasula thupi kungakuthandizeninso kulankhula momveka bwino. N’kwachidziŵikire kuti nyama za pankhope zikakungika, kapena za m’ziwalo zopumira, mawu satuluka bwino. Kumangika thupi koteroko kumadodometsa mgwirizano wa pakati pa maganizo anu, ziwalo zolankhulira, ndi ziwalo zopumira—dongosolo limene liyenera kuyenda bwinobwino mwachibadwa.

Kuti nyama za m’nsagwada zilabadire msanga uthenga wochokera ku ubongo, ziyenera kukhala zomasuka. Milomonso izikhala yomasuka. Iyenera kukhala yomasuka kotero kuti izitha kuumba mawu mofulumira ochokera kukholingo ndi m’kamwa. Ngati nsagwada ndi milomo zili zomangika, kamwa silitseguka bwino, ndipo mawu amatulukira m’mano. Zimenezi zimachititsa mawu kumveka ngati ovumatira, osamveka bwino. Komabe, kumasula nsagwada ndi milomo sikutanthauza kulankhula ndi kutchula mawu mwaulesi. Kuyenera kuchitidwa molinganiza mphamvu kotero kuti mawu atuluke omveka bwino.

Pofuna kuona mamvekedwe a mawu anu, ŵerengani mawu mokweza. Onetsetsani mmene mukugwiritsira ntchito ziwalo zanu zolankhulira. Kodi mumatsegula pakamwa panu mokwanira kotero kuti mawu azituluka momasuka? Kumbukirani, ngakhale kuti lilime ndilo limagwira ntchito kwambiri, sindilo chiwalo chokha cholankhulira. Khosi, chibwano, milomo, nyama za pankhope, ndi kholingo, chilichonse chimachita mbali yake. Kodi mumalankhula popanda kugwedeza nkhope? Ngati mumatero, n’zokayikitsa ngati mawu anu amamveka bwino.

Ngati muli ndi wailesi yojambulira mawu, dzijambuleni mukulankhula mwachibadwa, mmene mumachitira polankhula ndi munthu mu ulaliki. Jambulani kukambiranako kwa mphindi zingapo. Kumvetsera mawu ojambulidwawo kungakuthandizeni kuzindikira vuto lililonse limene mungakhale nalo potchula mawu ena. Onani mmene mumalumikiza mawu ambiri osapumira, mmene mumavumata mawu, kapena mmene mumadulira mawu, ndipo yesani kuzindikira chochititsa. Vutoli lingathe mwa kulimbikira mfundo zimene tafotokozazo.

Kodi muli ndi vuto lachibadwa la kusalankhula bwino? Yesezani kutsegula pakamwa moposerapo mmene munali kuchitira m’mbuyomu ndipo yesani kulankhula mosamala kwambiri. Popuma, dzazani mpweya m’chifuwa, ndiyeno lankhulani pang’onopang’ono. Kuchita zimenezi kwathandiza ambiri okhala ndi vuto polankhula kuti azitha kulankhula momvekerapo bwino. Ngati mumalankhulira palilime, kokerani lilime m’kati pang’ono kuti lichoke pamano apatsogolo potchula s ndi z m’mawu. Ngakhale kuti vuto lanu silingatheretu, musataye mtima. Kumbukirani kuti Yehova anasankha Mose, amene panthaŵiyo kukhala ngati anali ndi vuto losatha kulankhula bwino, kuti akapereke mauthenga ofunika kwambiri kwa Aisrayeli ndi Farao wa ku Igupto. (Eks. 4:10-12) Ngati inunso muli wofunitsitsa, adzakugwiritsani ntchito, ndipo adzakuthandizani kupambana pa utumiki wanu.

MMENE MUNGACHITIRE ZIMENEZO

  • Lankhulani ndi kuŵerenga mawu limodzi ndi limodzi momveka bwino—kuwatchula bwino, mphamvu ya mawu yabwino, ndi liŵiro labwino.

  • Musalumikize mawu ambiri mosapumira moti omvera anu n’kulephera kumvetsa tanthauzo lenileni.

  • Polankhula, kwezani mutu ndipo tsegulani pakamwa mokwanira.

  • Yesezani kumasula minofu ya pammero, nsagwada, milomo, ndi pankhope.

ZOCHITA: Lankhulani mwachibadwa. Kodi mumatsegula pakamwa motani? Kodi muyenera kupatsegula mowonjezerako pang’ono ndi kumasula bwino minofu yapankhope panu? Yesezani zimenezo poŵerenga mokweza pa Mateyu 8:23-27. Onetsetsani kuti mukukweza mutu wanu ndi kumasula nsagwada zanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena