Phunziro 13
Kuwongolera Kamvekedwe ka Mawu ndi Kugwiritsa Ntchito Cholankhulira
1-3. Kodi zofooka zina za mawu n’zotani, ndipo n’chiyani chingathandize munthu kudziŵa vuto lake?
1 ‘Anam’pangira munthu kamwa ndani?’ linali funso kwa Mose, lochokera kwa Mlengi, Yehova Mulungu. (Eks. 4:10, 11) Ndipo tingawonjezerepo kuti, Kodi ndani anapanga ziwalo zodabwitsa zonsezo zotulutsira mawu a munthu? Potsirizira pake Mose anaphunzira kuti, ngakhale kuti iye anali “wa m’kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera,” Mulungu anafuna kum’thandiza ndipo anam’thandizadi kuwongolera kamvekedwe ka mawu ake polankhula, moti mneneriyo anakhoza kulankhula bwino lomwe kwa mtundu wa Israyeli.
2 Lerolino alipo atumiki a Mulungu ambiri amene amazindikira vuto lawo polankhula. Ena ali ndi mawu apansi kwambiri, ena ali ndi mawu aang’ono koma apamwamba kwambiri, komanso ena ali ndi mawu aakulu kapena osasa. Mawu aang’ono koma apamwamba, mawu olankhulira m’mphuno, kapena mawu osasa samveka bwino. Mawu ozizira, opanda umoyo sakopa aliyense. Ngati mawu anu amaonetsa chimodzi mwa zofooka zimenezi, musataye mtima. Musangozilekerera mukumati inu basi ndi choncho, ngati kuti palibe njira yothetsera vutolo.
3 Komabe, kuti pakhale kusintha munthuyo ayenera kudziŵa vuto limene ali nalo lofunikira kuliwongolera. Apa m’pamene Sukulu ya Utumiki Wateokalase, limodzi ndi uphungu wothandiza wa woyang’anira sukulu, zingakuthandizeni kupenda zofooka za mawu zilizonse. Ndiponso, n’kothandiza kujambula mawu anu patepi ndi kuwamvetsera. Ngati simunachitepo zimenezo, mudzadabwa ndi zimene mudzamva. Chimene chimachitika n’chakuti pamene mulankhula, mumamvanso phokoso la kunjenjemera kwa mafupa m’mutu mwanu ndipo phokoso limenelo limasakanikirana bwinobwino ndi kamvekedwe ka mawu anu. Koma tepi imamveketsa kamvekedwe kenikeni ka mawu anu mmene amamvekera kwa ena. Kuti tikhale ndi maziko abwino oyambirapo kuwongolera mawu, tiyeni tipende kaye zipangizo za mawu anu, zimene mumazigwiritsa ntchito nthaŵi zonse popanda kuganizira za izo.
4-6. Kodi mawu amapangika motani?
4 Mmene mawu amatulukira. Chimene chimapanga mawu kwenikweni ndicho mpweya umene umachokera m’mapapu, amene amachita ngati mvukuto. Mpweyawo utakwera kudzera m’kolingo umaloŵa pammero m’malo otchedwanso bokosi la mawu, chapakati pammero wanu. M’malowo a pammerowo muli timinofu tiŵiri topyapyala kwambiri totchedwa vocal cords [zingwe za mawu]. Timinofu timeneti ndito zipangizo zazikulu zotulutsa mawu. Zingwe za mawu zimenezi, zili ngati mashelefu osunthika m’makoma a mmero wanu. Ntchito yake yaikulu ndiyo kutsegula ndi kutseka kuti mpweya uziloŵa ndi kutuluka, limodzinso ndi kuletsa zinthu zosafunika kuloŵa m’mapapu. Mpweya wochokera m’mapapu anu ndiwo umayendetsa zingwe zimenezi. Choncho, pamene izo zinjenjemera mpweya ukamazidutsa mwamphamvu, zimatulutsa mawu. Tipereke chitsanzo motere: Ngati muuzira mpweya m’baluni niikhuta, kenako muipanira pakhosi ndi zala zanu ndi kulola mpweya kutulukira pakhosipo, baluniyo imanjenjemera ndi kupanga phokoso. Choncho pamene mulankhula, timinofu tija kapena zingwe zija pammero panu zimapanikizana pamodzi mwamphamvu. Mpata wonga V pakati pawo umatsekeka. Pamene timinofu timeneti tikungika kwambiri, m’pamene timanjenjemera mofulumirirapo kwambiri ndipo m’pamenenso timatulutsa mawu apamwamba. Koma pamene tili tothebwa kwambiri, mawu ake amamveka otsika kwambiri.
5 Mpweyawo ukachoka pamalowo apakati pammero umadzaloŵa m’gawo la kumwamba kwa mmero lotchedwa pharynx pa Chingelezi. Ndiyeno umapitirira mpaka m’kamwa ndi m’mphuno. Munomo muli zipangizo zina zimene zimasintha kamvekedwe koyamba kaja ka mawu. Zimenezi zimasalaza mawu, kuwakulitsa ndi kuwonjezera mphamvu yake. Kumwamba kwa kamwa, lilime, mano, nkhama, nsagwada ndi milomo zimagwirizana kufafaniza kamvekedwe konjenjemera ka mawuwo ndi kuwaumba kukhala mavawelo ndi makonsonanti kuti mawuwo amveke bwinobwino.
6 Kunena zoona, mawu a munthu ndi chozizwitsa chapadera kwabasi, chopanda chiŵiya china chilichonse chopangidwa ndi munthu chofanana nacho, makamaka pakusinthasintha kamvekedwe kake. Mawu a munthu akhoza kuonetsa mikhalidwe yosiyanasiyana, monga chifundo, chikondi, ngakhalenso mkwiyo ndi chidani chachiwawa. Ngakhale m’kupanda ungwiro kwawo, mawu a munthu akhoza kutulutsa kamvekedwe kokoma ka nyimbo, ngakhalenso malankhulidwe otonthoza mtima pamene wina aphunzitsidwa kusankha mawu oyenera ndi kuwaumba bwino. Kuwongolera mawu, monga mmene tidzaonera, kuli ndi mbali zofunika ziŵiri.
7-10. Kodi mpweya wa munthu uyenera kulamuliridwa motani, ndipo chifukwa chiyani?
7 Kulamulira katulutsidwe ka mpweya. Kuti munthu akambe nkhani yogwira mtima, afunikira mpweya wokwanira limodzinso ndi kupuma kwabwino. Anthu ambiri sakudziŵa kapumidwe koyenera polankhula. Amangogwiritsa ntchito mbali yapamwamba ya mapapu, n’chifukwa chake akamalankhula mofulumira amachita befu. Kusiyana ndi zimene ambiri amadziŵa, mbali yaikulu ya mapapu siili kumwamba kwa chifuŵa; mbali imeneyi imangooneka yokulirapo chifukwa cha mafupa athu a mapewa. M’malo mwake, mapapu anakulira kwambiri pamwamba pang’ono pa diaphragm, yolekanitsa mimba ndi chifuŵa. Chimenechi ndi chifunga cha nyama yolimba yotundumuka imene imagwira ntchito ngati pompi, pothandiza mapapu kukokera m’kati mpweya watsopano ndi kutulutsa wotha ntchito. Chifunga chotundumuka chimenechi n’chimene chimagwira ntchito kwambiri popuma. Pamene chitundumukira kumwamba, chimakankha mpweya kuutulutsa m’mapapu. Pamene chipita pansi, mpweya umaloŵa m’mapapu.
8 Pofuna kuphunzira kuwongolera kamvekedwe ka mawu anu, chofunika choyamba ndicho kulamulira kapumidwe kanu. Yesetsani kupeŵa kutulutsa mbali yakumwamba ya chifuŵa chanu pamene mukoka mpweya polankhula. Futukulani mapapu anu m’munsi. Ndiyeno tulutsani mpweya pang’onopang’ono mwa kugwiritsa ntchito mphamvu yakumwamba kwa mimba. Zimenezi zidzaletsa mpweya kutha msanga. Koma ngati saulamulira, wolankhulayo amatha mpweya mwamsanga ndipo mawu ake amamveka okokera ndi abefu.
9 Ambiri amayesa kulamulira mpweya mwa kukunga kapena kulimbitsa nyama zapammero, komatu zimenezo zimangopangitsa mawu kusatuluka mwachibadwa ndipo zimatopetsa. Kuti mupeŵe zimenezo, yesani kumasula nyama zanu zapammero.
10 Monga momwe wothamanga amapangira pulakatisi pokonzekera mpikisano wothamanga, wolankhula nkhaninso ayenera kuchita pulakatisi yolamulira kapumidwe kake. Iye angamapange izi: Aime chilili, akoke mpweya wambiri kenako autulutse pang’onopang’ono, akumatchula zilembo za alifabeti pang’onopang’ono komanso bwinobwino, kapena kuŵerenga manambala mpaka pamene angafike pakupuma kulikonse. Angachitenso pulakatisi mwa kuŵerenga mawu mofuula.
11-15. Kodi kuumitsa thupi kumachititsa motani mawu kumvekera aang’ono komanso osokosera, omvekera m’mphuno kapena omveka monga munthu wavumata chinthu china?
11 Kumasula nyama zokungika. China chofunika pofuna kuthetsa mavuto a mawu ndicho kungomasula mawu basi! M’povuta kwambiri kuphunzitsa aliyense kuwongolera mawu ake ngati saphunzira mmene angakhalire womasuka thupi. Koma mungadabwe kuwongokera kumene kungakhalepo mutaphunzira kukhala womasuka. Maganizo ndi thupi ziyenera kukhala zomasuka, pakuti kumangika kwa maganizo kumaumitsanso thupi. Masulani maganizo anu mwa kukhala ndi malingaliro abwino ponena za omvetsera anu, amene, kaŵirikaŵiri, adzakhala anthu a Yehova. Kodi mabwenzi anuwo, tsopano akhala adani anu kokha chifukwa chakuti akhala m’mizera pamaso panu? Iyayi. Palibe anthu alionse padziko lapansi amene amaimirira pamaso pa omvetsera aubwenzi ndi achikondi monga momwe timachitira ife nthaŵi zonse.
12 Choyamba mudzafunikira kupuma kaye kuti mumasuke ndi kukhazikitsa mtima pansi. Mungapeze kuti, musanayambe kulankhula, kupuma kumakhala kopereŵeza komanso kosakhazikika kwenikweni chifukwa cha mantha. Mungathetse zimenezi mwa kuyesa kupuma pang’onopang’ono, poyesa kumasula nyama za pammero panu.
13 Monga tanena kale, kulimbitsa pammero kumachepetsa mawu ndi kuwapangitsa kumvekera pamwamba. Choncho mukakunga kwambiri nyama zapakhosi panu, mawu anu amamveka okwererapo kwambiri. Zimenezi zimapangitsa mawu kumveka aphokoso. Munthu akamalankhula momangika amachititsanso omvetsera kukhala omangika. Kodi munthu angachitenji kuti athetse vuto limeneli? Eya, kumbukirani kuti zingwe zanu za mawu zija zimayamba kunjenjemera mpweya pomazidutsa. Kamvekedwe kake kamasintha pamene minofuyo imakungika kapena pomasuka, monga momwe zimachitira zingwe za gitala akazikoka kapena kuzimasulako. Pamene mumasula zingwe za mawu, mawu anu amatsika. Choncho chofunika kumachita ndicho kumasula nyama zapakhosi. Kuumitsa thupi kungachititsenso minofu yomezera kupinga ija yolamulira zingwe zotulutsa mawu, kupangitsa mawu kutuluka opanikizika. Koma mutha kuwongolera vutolo pamene mumasula maganizo ndi thupi.
14 Nthaŵi zina pamene munthu akunga minofu ya pakhosi ndi kukamwa amatseka njira ya m’mphuno kotero kuti mpweya sungathe kudzeramo bwino. Zimenezi zimachititsa mawu kumvekera m’mphuno. Kuti munthu apeŵe zimenezi afunikiranso kumasula thupi. Komabe, nthaŵi zina chimene chimachititsa vuto limenelo ndi kutsekeka m’mphuno.
15 Nsagwada zimafunikiranso kuzimasula. Ngati zikhala zomangika, kamwa silitseguka bwino moti mawu amatulukira m’mano. Zimenezi zimapangitsa mawu kumveka ngati mwavumata chinthu m’kamwa. Komabe, kumasula nsagwada sikutanthauza kuzithebwetsa moti n’kukhala ndi chizoloŵezi cholankhula mwaulesi ayi. N’kofunika kulinganizidwa bwino ndi mchitidwe woumba mawu kotero kuti pakhale kutchula mawu kwabwino.
16, 17. N’chiyani chingathandize munthu kuwongolera kamvekedwe ka namaloŵe wa mawu ake, ndipo n’chifukwa chiyani kuteroko kuli kofunika kwambiri?
16 Kumasula nyama za m’thupi kumathandiza kwambiri kutulutsa namaloŵe wa mawu. Pamene mawu omvekera bwino atuluka pammero pomasuka bwino, namaloŵe wake amapatsa mawuwo mphamvu ya kumveka kopitiriza. Namaloŵeyo amatuluka mwa kugwiritsa ntchito thupi lonse monga ng’oma, koma kulimbitsa thupi kumalepheretsa kumvekera bwino kwake. Mawu otuluka pammero amapanga namaloŵe osati m’mphuno mokha, komanso amagunda kumafupa a m’chifuŵa, kumano, kumwamba kwa kamwa ndi m’mutu. Zonsezi zimapanga namaloŵe womvekera bwino kwambiri. Ngati munthu akhazika chinthu cholemera pa ng’oma, simvekanso; kuti imveke iyenera kukhala yomasuka. N’chimodzimodzi ndi thupi lathu, limene lakoŵanitsidwa ndi minofu. Pothandizidwa ndi namaloŵe mukhoza kumveka mosavuta kwa anthu ambiri, popanda kupanikiza mawu anu. Popanda namaloŵe n’kovuta kuti mawu anu amveke mopitirira, kuti muwasinthesinthe mofunikira kapena kuti mumveketse mzimu wake.
17 Mungawongolere kumvekera bwino kwa mawu a namaloŵe mwa kuyesa kung’ung’udza, kwinaku mukumasula thupi lanu. Milomo iyenera kukhudzana pang’ono chabe, osati kuipanira mwamphamvu. Mwa njira imeneyo, nyama sizidzakungika ndi kulepheretsa mawu kumvekera bwino ndipo mawuwo sadzatulukira m’mphuno. Kubwerezabwereza mawu ena ndi kumakokera mawu omvekera kuti ng, m, n ndi l kungakhale kothandiza. Njira ina yowongolera kamvekedwe ka mawu ndiyo yotchula mavawelo, mwa kuwatalikitsa potsegula pammero, kumasula nsagwada ndi mphamvu ya mawu pang’ono.
18-22. Kodi ndi langizo lotani limene tiyenera kulikumbukira ponena za kagwiritsidwe kabwino ka cholankhulira?
18 Kugwiritsa ntchito bwino cholankhulira. M’malo aakulu osonkhanira kumakhala kofunika kukulitsa mawu a munthu ndi ziwiya zamagetsi, ponse paŵiri kuti wolankhulayo asavutike ndi kufuula komanso kuti omvetsera amve bwino. Choncho wolankhulayo samafunikira kukweza mawu kwambiri, ndipo omverawo safunikira kuvutika kuchinjikira makutu awo kuti amve zimene zikunenedwa. Zolankhulira amazigwiritsa ntchito m’mipingo yambiri, osati papulatifomu pokha, komanso ndi oyankha m’kati mwa gulu, kotero kuti mayankho onse amveke bwino. Ngakhale ngati m’Nyumba ya Ufumu ya kwanu mulibe zolankhulira, izo zimagwira ntchito kaŵirikaŵiri pamisonkhano yaikulu. Choncho m’pofunika kuti tidziŵe njira yake yozigwiritsa ntchito.
19 Kodi mlomo wanu uyenera kukhala pafupi motani ndi cholankhulira? Uyenera kukhala pa masentimita 9 mpaka 15. Vuto limene limakhalapo kaŵirikaŵiri pogwiritsa ntchito cholankhulira n’lakuti wolankhulayo amakhala patali kwambiri ndi cholankhuliracho. Choncho samalani mtundawo. Ndiponso lunjikitsani mawu anu pa cholankhuliracho kapena chapafupi pamene chingathe kugwira mawu. Mukapanda kutero, m’povuta kuti wosamalira makina okuzira mawu awasinthe moyenera kuti amveke bwino kwa omvetsera. Komano kukhosomola, kuyetsemula kapena kuchotsa makhololo pammero pafupi ndi cholankhulira n’kosaloleka.
20 Pogwiritsa ntchito cholankhulira, mvetserani mmene mawu anu akumvekera mu mkuza mawu (laudisipika). Pamenepo mukhoza kupima ukulu wa mawu ndi kusintha poima panu, ngati n’kofunika. Mwina mungafunikire kuyandikira pafupi ndi cholankhuliracho kapena kuchitalikira ndi masentimita atatu kapena anayi. Olankhula nkhani ena amafunikira kupeŵa kulankhula mokweza mawu kwambiri, chifukwa kuteroko kumawononga mawu awo, ndipo kumasokosera omvetsera. Kumbukiraninso kuti, ngati mufuna kutsitsa mawu anu apo ndi apo pofuna kugogomeza mfundo, omvetsera anu angamvebe ngakhale mutanong’ona, chifukwa cha makina okuzira mawu amakono.
21 Palinso mbali zina zofuna kusamala pogwiritsa ntchito cholankhulira. Kodi mwaona kuti nthaŵi zina “p” amapanga phokoso? Zimenezi zimachitika pamene munthu alankhulira mwachindunji m’cholankhulira komanso atachiika pafupi kwambiri ndi mlomo. Ndiponso “s” mutamt’chula mwamphamvu amapanganso phokoso. Zilembozi n’zofunika kuzitchula mofeŵerapo, chifukwa chokuzira mawu chimawonjezera kamvekedwe kake. Mutadziŵa kapeŵedwe ka vuto limenelo, m’posavuta kuzitchula bwinobwino.
22 Kapangidwe ka mawu ndi mphatso yodabwitsa yochokera kwa Mlengi wathu. Magetsinso limodzi ndi maganizo otumba zinthuzo alinso mphatso zochokera kwa iyeyo, ndipo zimenezo zatheketsa cholankhulira kukhalapo. Nthaŵi zonse pamene tigwiritsa ntchito mawu athu, kaya kudzera m’chipangizo chokuzira mawu kapena popanda chipangizocho, tiyeni titero mwa njira yolemekeza Myambitsi wa chinenero.