Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 29 tsamba 181-tsamba 185 ndime 2
  • Kamvekedwe Kabwino ka Mawu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kamvekedwe Kabwino ka Mawu
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwongolera Kamvekedwe ka Mawu ndi Kugwiritsa Ntchito Cholankhulira
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kulankhula Momveka Bwino
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Chenjerani ndi “Mawu a Alendo”
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Phunzirani Kuimba Mwaluso
    Galamukani!—2008
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 29 tsamba 181-tsamba 185 ndime 2

PHUNZIRO 29

Kamvekedwe Kabwino ka Mawu

Kodi muyenera kuchita motani?

Konzani kamvekedwe ka mawu anu, osati mwa kutengera munthu wina ayi, koma mwa kupuma bwino ndi kumasula minofu yomangika ya m’thupi.

N’chifukwa chiyani kali kofunikira?

Kamvekedwe kabwino ka mawu kamathandiza ena kukhala omasuka ndipo amamvetsera kwa inu mosangalala. Mawu osamveka bwino amadodometsa kulankhulana, ndipo angagwetse mphwayi wolankhulayo ndi omvera ake.

CHIMENE makamaka chimalimbikitsa anthu, si mawu okha amene timanena, komanso mmene timawanenera. Ngati munthu alankhula nanu ndi mawu omveka okoma, achikondi, aubwenzi, ndi okoma mtima, kodi si zoona kuti mumamvetsera mokondwa, kusiyana ndi mmene mungachitire mawu ake akakhala opola kapena aukali?

Kukhala ndi mawu omveka bwino si nkhani yofuna kungodziŵa kutulutsa bwino mawu kokha, ayi. Kungaphatikizepo mtima wa munthuyo. Pamene munthu akupita patsogolo m’kudziŵa choonadi cha Baibulo ndi kuchigwiritsa ntchito, kusintha kumaonekera m’kalankhulidwe kake. Makhalidwe aumulungu ngati chikondi, chimwemwe, ndi chifundo amamveka m’mawu ake. (Agal. 5:22, 23) Pamene adera nkhaŵa anthu ena, nkhaŵayo imamveka m’mawu ake. Pamene munthu asiya kukhala wodandaula nthaŵi zonse nayamba kukhala woyamikira, mawu ake ndi kamvekedwe kake zimasonyeza kusintha kumeneko. (Maliro 3:39-42; 1 Tim. 1:12; Yuda 16) Ngakhale pamene simukumva chinenerocho, ngati munthu wina akumveka wamwano, wosalolera, wosuliza, ndi waukali, ndipo wina akumveka wodzichepetsa, woleza, wokoma mtima, ndi wachikondi, n’zosavuta kuti muwasiyanitse anthuwo.

Nthaŵi zina munthu amakhala ndi mawu osamveka bwino chifukwa matenda anawononga mphako ya m’kholingo yotulutsa mawu kapena chifukwa cha chilema china. Zovuta zimenezo zingakhale zazikulu moti sizingatheretu m’dziko lino lakale. Komabe, kuphunzira kugwiritsa ntchito bwino ziwalo zolankhulira kumawongolerako zinthu.

Choyamba, m’pofunika kudziŵa kuti anthufe timasiyana mamvekedwe a mawu. Cholinga chanu chisakhale kutengera mawu a munthu wina. M’malo mwake, yesetsani kukhala ndi mawu anuanu, okhala ndi kamvekedwe kanukanu. Kodi chingakuthandizeni n’chiyani kuchita zimenezo? Pali mbali ziŵiri zofunika kwambiri.

Kapumidwe Koyenera. Kuti mawu anu azimveka bwino, muyenera kudziŵa kapumidwe koyenera. Popanda kutero, mawu anu angamamveke ofooka, ndipo kalankhulidwe kanu kangakhale kodukaduka.

Mbali yaikulu ya mapapu anu siili kumwamba kwa chifuŵa chanu ayi; kumwamba kwa chifuŵa kumangooneka kwakukulu chifukwa cha mafupa a mapewa. M’malo mwake, mapapu anakulira kwambiri pamwamba pa chifundamtima. Chifundamtimachi n’cholumikizika ku nthiti za m’munsi, ndipo chimalekanitsa chifuŵa ndi mimba.

Ngati popuma mudzaza mbali yakumwamba yokha ya mapapu anu, mumatha mpweya msanga. Mawu anu amatha mphamvu, ndipo mumatopa msanga. Kuti mupume moyenerera, mufunikira kukhala tsonga kapena kuimirira mowongoka ndi kukankhira mapeŵa anu kumbuyo. Musatundumutse mbali yakumwamba yokha ya chifuŵa chanu pokoka mpweya kuti mulankhule. Yambani mwadzaza mpweya m’mbali ya m’munsi ya mapapu anu. Mbali imeneyi ikadzaza, mphako ya m’munsi ya nthiti zanu imatundumukira m’mbali mwake. Panthaŵi imodzimodzi, chifundamtima chimatsikira m’munsi, ndipo pang’onopang’ono chimakankhira pansi mimba ndi matumbo, moti mumatha kumva mimba ikukanikiza lamba wanu kapena chovala chanu pamimbapa. Koma mapapu anu saali m’mimba ayi; iwo ali m’mphako ya nthiti zanu. Kuti mumve zimenezo, gwirani uku ndi uku m’munsi mwa nthiti zanu. Tsopano kokani mpweya wambiri. Ngati mukupuma moyenerera, simuziloŵetsa mimba m’kati ndi kukweza mapeŵa anu ayi. M’malo mwake, mumva nthiti zikumakwera ndi kutsika pang’onopang’ono.

Chotsatira, phunzirani kutulutsa bwino mpweya. Musauwononge mwa kuutulutsa mofulumira nthaŵi imodzi. Utulutseni pang’onopang’ono. Musaulamulire mwa kumanga pakhosi panu. Mukatero, mawu anu adzamveka osamasuka kapena otsinira. Minofu ya m’mimba ndi ya m’nthiti imakankha mpweya kuti utuluke, pamene chifundamtima chimalamulira liŵiro la katulukidwe ka mpweyawo.

Monga mmene wothamanga amakonzekerera mpikisano, wokamba nkhaninso akhoza kukonzekera mapumidwe oyenera. Imani mowongoka ndi kukankhira mapeŵa anu kumbuyo, kokani mpweya ndi kudzaza m’mbali ya m’munsi ya mapapu anu, ndiyeno pang’onopang’ono tulutsani mpweyawo mwa kuŵerenga bwinobwino kuyambira pa wani kufikira pamene mungathere popanda kupuma. Ndiyeno yesezani kuŵerenga mawu mokweza kwinaku mukupuma m’njira yofananayo.

Masulani Minofu Yokungika. China chofunika kuti mawu amveke bwino ndicho kumasuka. Mukadziŵa kumasuka polankhula, mawu anu akhoza kumamveka bwino kwambiri. Maganizo anu limodzi ndi thupi ziyenera kukhala zomasuka, chifukwa kumangika kwa maganizo kumachititsanso minofu kukungika.

Masulani maganizo anu mwa kuwaona moyenerera omvera anu. Ngati ndi anthu amene mumakumana nawo mu utumiki wa kumunda, kumbukirani kuti ngakhale mwaphunzira nawo Baibulo kwa miyezi yochepa chabe, inuyo mukudziŵa zinthu zabwino zokhudza cholinga cha Yehova zimene mungawafotokozere. Ndipo mwawafikira chifukwa akufunikira thandizo, zilibe kanthu kaya iwo akuzindikira zimenezo kapena sakutero. Koma ngati mukulankhulira mu Nyumba ya Ufumu, ochuluka mwa omvera anu amakhala anthu a Yehova. Iwo ndi mabwenzi anu, ndipo akufuna kuti muchite bwino. Palibe anthu enanso padziko lapansi amene amalankhula kwa omvera aubwenzi ndi achikondi ngati mmene timachitira ife nthaŵi zambiri.

Masulani nyama zapakhosi panu mwa kuganizira za minofuyo ndi kuifeŵetsa dala. Kumbukirani kuti mpweya ukamadutsa pa timinofu tapakhosi totulutsa mawu timanjenjemera ngati nembanemba. Kamvekedwe ka mawu kamasinthasintha pamene nyama zapakhosi zikungika ndi kumasuka, ngati mmene gitala imasinthira kamvekedwe pamene mawaya ake akungika kapena kulera. Mukamasula timinofu totulutsa mawu ta m’kholingo, mawu anu amamveka apansi. Kumasulanso nyama zapakhosi kumathandiza kutsegula njira za m’mphuno, ndipo zimenezi zimathandiza kuti mawu anu atuluke akumveka bwino.

Masulani thupi lanu lonse—mawondo, manja, mapeŵa, ndi khosi lanu. Zimenezi zidzachititsa namalowe kapena kuti kayowozi wothandiza kuti mawu anu amveke bwino. Namaloweyo amamveka pamene mawu agunda m’mbali zosiyanasiyana za thupi lanu; koma ngati lamangika zimenezi sizitheka. Kamvekedwe ka mawu, kamene kamapangikira m’mphako ya mawu m’kholingo, kamatulutsa namalowe m’njira za m’mphuno komanso pogunda mafupa a chifuŵa, mano, ndi kumwamba kwa kamwa, komanso m’njira za m’mphuno. Zonsezo zimathandiza mawu kumveka bwino. Ngati mukanikiza chinthu pa chibokosi kapena chitini cha gitala, maimbidwe ake samveka kwenikweni; chiyenera kukhala chomasuka kuti chitulutse maimbidwe abwino. Chimodzimodzinso ndi mafupa a m’thupi lathu, amene amalimbitsidwa pamodzi ndi minofu. Mawu anu pogunda mafupa ndi kutulutsa namalowe, mumatha kusinthasintha mawu anu moyenerera kuti agwirizane ndi lingaliro la zimene mukunena. Mumatha kulankhula kwa anthu ochuluka mosachita kukuŵa kwambiri.

MMENE MAWU AMAPANGIKIRA

Chimene chimatheketsa mawu onse kumveka ndi mpweya umene mumatulutsa kuchokera m’mapapu anu. Mapapu amachita ngati mivukuto imene imapemerera mpweya kudzera m’kholingo ndi kuloŵa m’mphako ya mawu, imene ili pakati pa mmero wanu. M’kati mwa mphako yanu ya mawu, mbali ya uku ndi uku, muli timinofu tiŵiri timene timachita ngati nembanemba. Timeneti n’timene timatulutsa mawu. Timinofuti timatseka ndi kutsegula njira ya mpweya yoloŵera ku mphako ya mawuyo polola mpweya kuloŵa ndi kutuluka; timatchinganso zinthu zosafunikira kuti zisaloŵe m’mapapu. Tikamapuma mwa nthaŵi zonse, mpweya supanga mawu ukamadutsa pamwamba pa timinofu timeneto. Koma munthu akafuna kulankhula, timinofuto timakungika ndipo mpweya wochokera ku mapapu ukamadutsa pamenepo timayamba kunjenjemera ngati nembanemba. Basi mawu amanzenene n’kumatuluka pamenepo.

Timinofuto tikakungika kwambiri, timanjenjemeranso mofulumira, ndipo manzenenewo amamveka kwambiri. Koma tikakhala tolera, manzenenenso amamveka pang’ono. Manzenenewo akatuluka m’mphako ya mawuyo, amakaloŵa m’mphako inanso ya kumtunda kwa mmero. Kenako amadzatulukira m’kamwa ndi m’mphuno. Namalowe kapena kuti kayowozi wa mmenemo amasintha manzenenewo ndi kuwapangitsa kuti amveke mawu abwinobwino. Kumwamba kwa kamwa limodzi ndi lilime, mano, milomo, ndi nsagwada zimagwirizana pothetsa manzenenewo kuti amveke mawu atanthauzo.

Mawu a munthu ndi chozizwitsa chapadera; kunena za kusinthasintha mamvekedwe, palibe chipangizo choimbira chopangidwa ndi munthu chimene chingafanane nawo. Amatha kusonyeza makhalidwe osiyanasiyana, kuyambira pa chikondi chaubwenzi mpaka pa chidani, ukali ndi chiwawa. Mwa kuyeseza mwakhama, mawu a munthu akhoza kuimba mwanthetemya ndi mochititsa kaso, komanso kulankhula mawu okopa, olimbikitsa ndi ogwira mtima.

KUTHANA NDI MAVUTO ENA

Mawu ofooka. Tikati mawu ofooka sitikutanthauza kwenikweni mawu ofeŵa. Ngati mawu ofeŵa akumveka olemerera bwino ndi okoma, ena angasangalale kuwamvera. Koma kuti mawu akhale ogwira mtima, ayenera kukhala ndi mphamvu yokwanira.

Kuti mawu anu azimveka bwino, muyenera kuwongolera kamvekedwe kake. Zimenezo zimafuna kuphunzira kumasula thupi lanu lonse, m’njira imene tafotokoza m’mphunziro lino. N’kothandizanso kumayeseza kumasula thupi lanu lonse ndi kumalankhula mong’ung’udzira. Milomo izikhudzana pang’ono chabe, osati mwamphamvu ayi. Pamene mukung’ung’udzira, kunjenjemerako kuyenera kuti kuzimveka m’mutu mwanu ndi m’chifuŵa.

Nthaŵi zina mawu amamveka ofooka kapena omangika chifukwa munthuyo sakupeza bwino kapena sanagone mokwanira. Zikatero, mawu ake amadzamvekanso bwino iye akakhala bwino.

Mawu okwera kwambiri. Timinofu ta mawu tikakungika kwambiri mawunso amakwera kwambiri. Mawu omveka omangika amachititsanso omvera kumangika. Mukhoza kutsitsako mawuwo mwa kumasula nyama zapakhosi kuti timinofu ta mawu timasukeko. Chitani zimenezo mozindikira, ndipo yesezani kutero pokambirana ndi anthu tsiku ndi tsiku. Kukoka mpweya wambiri kumathandizanso.

Mawu omvekera m’mphuno. Nthaŵi zina vuto limeneli limakhalapo chifukwa cha kutsekeka kwa mphuno, koma si chimene chimachititsa nthaŵi zambiri. Nthaŵi zina munthu amatha kutseka njira za m’mphuno mwa kulimbitsa nyama zapakhosi ndi m’kamwa; akatero mpweya umalephera kudutsa momasuka. Zimenezi zimachititsa mawu kumvekera m’mphuno. Mungapeŵe vuto limeneli mwa kumasula thupi lanu.

Mawu omveka ngati aukali. Mawu oterowo salimbikitsa ena kuti aperekepo maganizo awo pokambirana. Angapangitse ena kuona ngati mukuwaukira.

Nthaŵi zina, chimene chimafunika ndicho kuyesetsa kusintha mtima wanu. (Akol. 3:8, 12) Mukachita zimenezo, limbikirani tsopano kugwiritsa ntchito malangizo okonzera mawu kuti azimveka bwino. Masulani pakhosi ndi nsagwada zomwe. Zimenezi zidzachititsa mawu anu kumveka okoma ndipo sazitulukira m’mano, chifukwa ndi chinanso chimene chimawononga mamvekedwe abwino a mawu.

CHIMENE CHINGAKUTHANDIZENI

  • Khalani ndi mtima wa Mkristu.

  • Phunzirani kupuma moyenerera mwa kudzaza mpweya m’mbali ya m’munsi ya mapapu anu.

  • Polankhula, masulani minofu yanu—kholingo, pakhosi, mapeŵa, ndi thupi lonse.

ZOCHITA: (1) Kwa mphindi zingapo tsiku lililonse kwa mlungu wathunthu, yesezani kupuma m’njira yodzaza mpweya m’mbali ya m’munsi ya mapapu anu. (2) Kamodzi pa tsiku kwa mlungu wathunthu, masulani nyama zapakhosi panu pamene mukulankhula.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena