Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 17 tsamba 139-tsamba 142 ndime 1
  • Kugwiritsa Ntchito Maikolofoni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwiritsa Ntchito Maikolofoni
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwongolera Kamvekedwe ka Mawu ndi Kugwiritsa Ntchito Cholankhulira
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Mphamvu ya Mawu Yoyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Ntchito Yomasulira Msonkhano Wachigawo wa 2020 Wakuti ‘Kondwerani Nthawi Zonse.’
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
  • Msonkhano Wautumiki Umatikonzekeretsa Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 17 tsamba 139-tsamba 142 ndime 1

PHUNZIRO 17

Kugwiritsa Ntchito Maikolofoni

Kodi muyenera kuchita motani?

Ngati mugwiritsa ntchito maikolofoni kuti mawu anu amveke bwino pamsonkhano, igwiritseni ntchito moyenerera.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Mawu olankhulidwa amapindulitsa ena pokhapokha akamamveka bwino.

ABALE ndi alongo athu achikristu amawononga nthaŵi ndi nyonga yochuluka kuti apezeke kumisonkhano yachikristu. Kuti apindule kwathunthu ndi zolankhulidwa kumeneko, ziyenera kumamveka bwino lomwe.

M’nthaŵi za Israyeli wakale, analibe zipangizo zamagetsi zokwezera mawu. Pamene Mose analankhula kwa mtundu wa Israyeli m’Chidikha cha Moabu asanakaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, kodi anatha bwanji kulankhula ku khwimbi la anthu ofika m’mamiliyoni, moti onsewo n’kumamva zimene anali kunena? Mwachionekere, Mose anagwiritsa ntchito njira yolandirana mawu kudzera kwa amuna oikidwa m’malo oyenerera mumsasa wonsewo. (Deut. 1:1; 31:1) Aisrayeliwo atayamba kugonjetsa dziko lakumadzulo kwa Yordano, Yoswa anasonkhanitsa mtunduwo kumbali kwa phiri la Gerizimu ndi kumbali kwa phiri la Ebala, mwachionekere Alevi anawaika m’chigwa cha pakati pa mapiriwo. Pamalopo, anthu onse anatha kumva ndi kuyankha za madalitso ndi matemberero a Mulungu omwe anafotokozedwa kwa iwo. (Yos. 8:33-35) N’zotheka kuti pachochitika ichinso, anagwiritsa ntchito njira yolandirana mawu. Ndipo n’zosakayikitsa kuti namaloŵe wabwino kwambiri wa malowo anathandizanso kumveketsa mawu patali.

Patapita zaka pafupifupi 1,500 pamene “khamu lalikulukulu” linasonkhana ku nyanja ya Galileya kuti akamvetsere kwa Yesu, iye anakwera bwato nalikankhira pataliko m’madzi, kenako anakhala pansi kuti ayambe kulankhula kwa khamulo. (Marko 4:1, 2) N’chifukwa chiyani Yesu analankhulira m’bwato? Mwachionekere, n’chifukwa chakuti pamadzi okhazikika ndi abata, mawu a munthu amapita patali ndipo amamveka bwino kwambiri.

Kumbuyo konseko mpaka kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, kuti omvera amve bwino zimene wokamba nkhani akunena, zinali kudalira mphamvu ya mawu ake. Komabe, kuyambira m’ma 1920, atumiki a Yehova anayamba kugwiritsa ntchito zipangizo zamagetsi zokwezera mawu pamisonkhano ikuluikulu.

Zipangizo Zolankhulira. Zipangizozo zimatha kukweza moŵirikiza mawu a wolankhula koma iye n’kumvekabe bwino kwambiri. Wolankhulayo safunikiranso kuvutika ndi kukunga minofu yapakhosi yotulutsa mawu. Omveranso safunika kuchita kuvutikira ndi kutchera khutu kwambiri kuti amve akunena chiyani. M’malo mwake amaika maganizo pa uthenga wake.

Pakhala kuyesetsa kupeza zipangizo zolankhulira zabwino zogwiritsa ntchito pamisonkhano ikuluikulu ya Mboni za Yehova. Ndiponso, mu Nyumba za Ufumu zambiri amagwiritsa ntchito zipangizo zolankhulira kuti mawu a okamba nkhani, ochititsa misonkhano, kapena oŵerenga papulatifomu azimveka bwino. Ndipo mipingo ina ili ndi maikolofoni amene omvera amagwiritsa ntchito poyankha pamisonkhano. Ngati mpingo wanu uli ndi zolankhulira zoterozo, phunzirani kuzigwiritsa ntchito moyenerera.

Malangizo Osavuta. Kuti mugwiritse ntchito chipangizocho moyenerera, kumbukirani mfundo izi: (1) Maikolofoni iyenera kukhala pa masentimita pafupifupi 10 mpaka 15 kuchokera pakamwa panu. Ikafupikira kwambiri, mawu anu samveka bwino. Ikatalikiranso, mawu anu samveka. (2) Maikolofoniyo ilunjikane nanu, isaloze kumbali ayi. Ngati musunthira mutu wanu kumanja kapena kumanzere, lankhulani kokha mutayang’anizana ndi maikolofoni. (3) Lankhulani ndi mawu okwererako pang’ono kusiyana ndi masiku onse; koma musafuule. Zolankhulirazo zidzafikitsa mawu anu ngakhale kwa omvera omwe akhala kutali. (4) Ngati mukufuna kukhosomola kapena kuyetsemula, cheukirani kumbali.

Pokamba Nkhani. Pamene muima pasitandi yolankhulira, mbale wina adzakukonzerani maikolofoni. Mmene akukukonzerani maikolofoniyo, imani bwino ndipo yang’anani omvera. Ikani autilaini yanu pasitandipo, ndipo onetsetsani kuti maikolofoniyo siikutchinga autilaini yanu.

Pamene muyamba kulankhula, mvetserani mmene mawu anu akutulukira m’laudisipika. Kodi akukwera kwambiri, kapena kodi mawu ena akumveka ngati kuphulika kwa mbuluuli? Ngati zikutero, futukani pang’ono. Pamene mukuyang’ana autilaini yanu, kumbukirani kuti muyenera kulankhula ndi kuŵerenga kokha pamene nkhope yanu yalunjika maikolofoni kapena pamwamba pake pang’ono, osati m’munsi mwake.

Poŵerenga ku Pulatifomu. Ndi bwino kukweza Baibulo kapena buku m’dzanja kotero kuti nkhope yanu izipenya omvera. Popeza kuti mudzalunjikana ndi maikolofoni, mungachite bwino Baibulolo kuliikira pambali pang’ono. Kutanthauza kuti mutu wanu ukhale pambali pang’ono pa maikolofoni. Ndiyeno poŵerenga, mawu anu aziloŵa molunjika m’maikolofoni.

Abale ambiri omwe amaŵerenga paphunziro la Nsanja ya Olonda amaima ndi kulankhulira pamaikolofoni yoimikidwa. Zimenezi zimawalola kupuma bwino ndi kuŵerenga momasuka. Dziŵani kuti kuŵerenga ndime ndi mbali yaikulu ya msonkhano. Phindu limene omvera amapeza limadalira kwambiri kumva mawu omwe akuŵerengedwawo.

Popereka Ndemanga Pamsonkhano. Ngati mpingo wanu umagwiritsa ntchito maikolofoni yoyankhira, kumbukirani kuti muyenerabe kulankhula bwinobwino ndi mawu omveka. Poyankha, yesani kugwira chofalitsacho kapena Baibulo m’dzanja lanu. Mukatero mungathe kuona bwino pankhaniyo pamene mukulankhula pamaikolofoni.

M’mipingo ina abale amasankhidwa kukhala opatsira maikolofoni kwa ofuna kuyankhapo. Ngati zilinso choncho mumpingo wanu, pamene mwatchulidwa kuti muyankhe, dzanja lanu likhalebe m’mwamba kuti mbale woperekera maikolofoniyo aone pamene mwakhala kuti afike msanga. Ngati maikolofoniyo ndi yochita kupatsirana m’manja, konzekerani kuilandira. Musayambe kulankhula musanaigwire bwino. Mukamaliza kulankhula, ibwezereni msanga maikolofoniyo.

Pamene Muli Pachitsanzo. Kugwiritsa ntchito maikolofoni pachitsanzo kumafuna kulingalira bwino. Ngati maikolofoni yaikidwa ku sitandi yake, ndiye kuti manja anu adzakhala omasuka kugwira Baibulo ndi autilaini yanu. Polankhula pa maikolofoni yogwira m’manja mungakhale womasuka kwambiri, koma mungachite bwino kupempha wina kuti akugwirireni. Mukatero, manja anu adzakhala omasuka kugwiritsa ntchito Baibulo. Pamodzi ndi mwininyumba muyenera kuyeseza zimenezi kuti mnzanuyo adziŵe kuigwira moyenerera. Kumbukiraninso kuti pamene muli papulatifomu, musawafulatire omvera, makamaka pamene mukulankhula.

Zitsanzo za pa Msonkhano wa Utumiki zingakhale ndi anthu angapo, ndipo angafunikire kuyendayenda papulatifomu. Choncho pangafunikire maikolofoni angapo. Ameneŵa ayenera kuwaikiratu m’malo kapena kuwapereka msanga achitsanzo akapita kupulatifomu. Kuti mamaikolofoni akhale m’malo oyenera panthaŵi yake kumafuna kukonzekereratu. Kuyeseratu zitsanzo kumapereka mpata wolangiza otenga mbaliwo mmene angagwiritsire ntchito bwino maikolofoni. Ngati n’kosatheka kuyesera chitsanzo papulatifomu, ndi bwino kuti otenga mbaliwo agwire kanthu kena m’manja koyerekeza maikolofoni kuti azoloŵere kuiika pamalo oyenerera. Atatha chitsanzocho, otenga mbaliwo aike m’malo ake maikolofoniyo bwinobwino ndi kusamala kuti asakole nthambo za maikolofoni ena pamene akuchoka papulatifomu.

Kusamala pogwiritsa ntchito maikolofoni ndi mbali ina ya cholinga chachikulu cha misonkhano yathu, chimene ndi kupindulitsana wina ndi mnzake mwa kukambirana Mawu a Mulungu. (Aheb. 10:24, 25) Tikadziŵa kugwiritsa ntchito mwaluso maikolofoni, tidzathandiza kukwaniritsa cholinga chofunika kwambiri chimenecho.

MMENE MUNGACHITIRE ZIMENEZO

  • Maikolofoni ikhale pa masentimita 10 mpaka 15 kuchokera pakamwa panu.

  • Lankhulani kokha pamene maikolofoni yalunjikana ndi pakamwa panu.

  • Lankhulani ndi mawu okwererako pang’ono kusiyana ndi masiku onse.

  • Pofuna kukhosomola, cheukirani kumbali kwa maikolofoni.

ZOCHITA: Ngati mumagwiritsa ntchito maikolofoni m’Nyumba yanu ya Ufumu, penyetsetsani mmene okamba nkhani ozoloŵera amagwiritsira ntchito maikolofoni yoimikidwa ndi yogwira kumanja. Onani njira zimene mukufuna kutengera ndi zimene mukufuna kupeŵa ndi zifukwa zake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena