Msonkhano Wautumiki Umatikonzekeretsa Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino
1 Chifuno cha Msonkhano Wautumiki ncha kusonkhezera ndi kutikonzekeretsa kukhala ndi phande mokwanira m’ntchito ya kulalikira ndi kupanga ophunzira. (2 Tim. 3:17) Komabe, ngati sitikonzekera moyenerera misonkhanoyo kapena ngati tilephera kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira, mapindu ake adzakhala ochepa kwambiri.
2 Kukonzekera pasadakhale kudzakuthandizani kuloŵetsa malangizo ake bwino kwambiri. Pendani zofalitsidwa zimene zidzagwiritsiridwa ntchito, ndi kuzitenga kotero kuti mukakhoze kutsatira ndi kukhala wokhoza kutengamo mbali. Khalani womvetsera watcheru, ndipo lembani manotsi kuti muwagwiritsire ntchito mtsogolo.
3 Woyang’anira wotsogoza amapenda mosamalitsa nkhani zolinganizidwa za msonkhanowo. Akulu ndi atumiki otumikira okhoza bwino ndi oyenerera amapatsidwa nkhanizo kuti akonzekere. (om-CN tsa. 70) Mipingo imene ili ndi akulu ndi atumiki otumikira oŵerengeka ingagaŵire nkhanizo kwa abale ena okhoza bwino kuti awathandize. (km-CN 12/76, Mbali ya Mafunso) Wokamba nkhani aliyense ayenera kukonzekera mosamalitsa, kumamatira kwambiri pamalangizo operekedwa, ndi kutsimikizira kuti sakudya nthaŵi.
4 Kaŵirikaŵiri msonkhanowo umayamba ndi zilengezo. Mbale wogaŵiridwa mbali imeneyi ayenera kuonana ndi woyang’anira wotsogoza pasadakhale kuti adziŵe kuti nzinthu ziti zimene ziyenera kulengezedwa. Zimenezi zingaphatikizepo makalata ochokera ku Sosaite kapena zikumbutso zonena za makonzedwe a utumiki kapena malipoti amwezi ndi mwezi. Tikhoza kudziŵa kuti pali odwala amene afunikira kukaonedwa kapena kumva tsatanetsatane wa zochitika za mpingo zimene zalinganizidwa kaamba ka mtsogolo. Mvetserani mosamalitsa kotero kuti mudziŵe ndi kukhala wokonzekera kuchita mbali yanu.
5 Pamene nkhani ina ifunikira kutengamo mbali kwa omvetsera, konzekerani mwa kuŵerenga nkhani yonseyo ndi kuona malemba ake. Ganizirani za mmene mungalinganizire kugwiritsira ntchito malingalirowo ndi kuti ndimtundu wotani wa ndemanga zimene munganene kulimbikitsa ena. Inu mungaperekere chitsanzo cha phindu lothandiza la malangizowo mwa kusimba chokumana nacho chachidule.
6 Pamene pali chitsanzo, yesayesani kudziika inu eni m’chithunzithunzicho m’mikhalidwe imodzimodziyo, ndipo ganizirani za zimene mukanena. Onani zifukwa zake zogwiritsiridwa ntchito ndi njira yogomekera nayo. Yesani kukumbukira zimene munanena papitapo pamene munali mumkhalidwe wa mtundu umenewu, ndipo lingalirani mmene mfundo zosonyezedwazo zingakuthandizireni kupeza zotulukapo zabwino kwambiri mtsogolo.
7 Otenga mbali m’zitsanzozo ndi m’kufunsana ayenera kuyeseza bwino kwambiri pasadakhale. Aliyense ayenera kudziŵa zimene ati akanene ndi zimene ati akachite pa pulatifomu. Zitsanzo zosayesezedwa kaŵirikaŵiri sizimasonkhezera kapena kulimbikitsa omvetsera. Otenga mbali ena amadza ali okonzekera kudzayeseza chitsanzo chawo pamapeto a Phunziro la Nsanja ya Olonda kotero kuti ayeseze pa pulatifomu ndi kulola abale osamalira mamaikolofoni kudziŵa zimene zidzafunika.
8 Nthaŵi zina programuyo idzaphatikizapo nkhani yonena za chosoŵa china chapadera cha mpingo kapena nkhani ya panthaŵi yake ya mu Nsanja ya Olonda. Mvetserani mosamalitsa, landirani uphunguwo, ndipo yesetsani kuugwiritsira ntchito.
9 Tikufuna kukhala ‘okonzekera ntchito yonse yabwino.’ (2 Tim. 2:21) Msonkhano Wautumiki uli amodzi a makonzedwe amene Yehova amapanga kutithandiza kuchita zimenezo. Kufikapo mokhazikika ndi kuyesayesa kowona mtima kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira kudzatithandizadi kotero kuti ‘tikwaniritse utumiki [wathu]’ mokwanira.—2 Tim. 4:5.