Malangizo Okhudza Abale Amene Amakamba Nkhani pa Msonkhano wa Utumiki
Kuyambira Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi uno, ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki taisintha mawu ake kuti ikhale yosavuta kutsatira. Chotero malangizo otsatirawa akulowa m’malo ndiponso kumveketsa bwino zimene zili mu nkhani ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2009 ya mutu wakuti: “Kodi Tingakonzekere Bwanji Msonkhano wa Utumiki?”
◼ Nkhani: Imeneyi ndi nkhani yokambidwa kuchokera pa mfundo zimene zaperekedwa ndipo omvera satenga nawo mbali. Wokamba nkhani ayenera kufotokoza mfundo zimene akuona kuti zidzathandiza kwambiri ofalitsa mumpingo.
◼ Mafunso ndi Mayankho: Nkhani imeneyi imachitika mofanana ndi phunziro la Nsanja ya Olonda. Imakhala ndi mawu oyamba komanso omaliza achidule ndipo mafunso a ndime iliyonse amafunsidwa. Amene akuchititsa nkhaniyi sayenera kulankhulapo kwambiri. Ngati nthawi ilipo, mungawerenge malemba amene mukuona kuti akugwirizana kwambiri ndi nkhaniyo. Simuyenera kuwerenga ndime, pokhapokha ngati mwauzidwa kuti muchite zimenezi.
◼ Nkhani Yokambirana: Imeneyi ndi nkhani imene omvera amatenga nawo mbali mwa apo ndi apo. Si nkhani imene wokamba amafotokoza mfundo zonse yekha mpaka kumapeto. Komanso nkhani yonseyo siyenera kukhala ya mafunso ndi mayankho.
◼ Zitsanzo ndi Kufunsa Mafunso: Malangizo oti “muchite chitsanzo” akutanthauza kuti ndi udindo wa m’bale yemwe akukamba nkhani kusankha ndi kukonzekeretsa anthu oti achite chitsanzo. Wokamba nkhaniyo sayenera kuchita nawo chitsanzocho. Anthu amene angawasenkhewo ayenera kukhala oyenerera ndiponso achitsanzo chabwino. Ngati n’kotheka mwini wake wa nkhaniyo ayenera kukonzekeretsa ochita chitsanzowo nthawi idakalipo. Zingakhale bwino ngati mungapewe kugwiritsira ntchito ofalitsa atsopano kuti achite chitsanzo chosonyeza mmene ntchito yolalikira imachitikira pongofuna kuwapatsa mwayi woonekera papulatifomu, ngakhale kuti ofalitsa atsopano ena angagwiritsidwe ntchito kukhala eni nyumba. Ofalitsa amene akuchita chitsanzo ayenera kuonetsetsa kuti ayang’ana omvera. Anthu amene ati “akafunsidwe mafunso” ayenera kukafotokoza zimene akuwafunsazo ali ku pulatifomu m’malo mokazifotokoza atakhala pa malo awo m’gulu la omvetsera. Mwini nkhani ayenera kuonetsetsa kuti zitsanzo ndi kufunsa mafunso aziyeserera kaye anthuwo asanakazichite ku pulatifomu. Ngati m’bale amene akukamba nkhaniyo akuona kuti nthawi yake ikutha moti ayenera kuchotsa mbali zina za m’nkhani yake, iye sayenera kuchotsa mbali ya chitsanzo kapena ya kufunsa mafunso ofalitsa kupulatifomu. Atumiki othandiza ayenera kufunsa kaye wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu kapena mkulu wina asanasankhe anthu oti akachite chitsanzo kapena kukawafunsa kupulatifomu.
Ngati mbali ina ya nkhani ili ndi malangizo apadera, muyenera kuwatsatira mosamala. Kutsatira zimene tafotokoza pamwambapazi pochita Msonkhano Wautumiki, kudzathandiza abale kupindula kwambiri ndi Misonkhano ya Utumiki yomwe imachitika “moyenera ndi mwadongosolo.”—1 Akor. 14:40.