Ndandanda ya Mlungu wa September 20
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 20
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 19-22
Na. 1: 2 Mafumu 20:1-11
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Ofatsa? (Mat. 5:5)
Na. 3: Kodi Zingatheke Bwanji Kuti Munthu Aziopa Yehova Ndiponso Kumukonda? (rs-CN tsa. 422 ndime 4 ndi 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Bwanji Chaka Chathachi? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani zimene mpingo wanu unachita mu utumiki chaka chautumiki chathachi, makamaka zinthu zabwino zimene unakwanitsa kuchita, ndipo uyamikireni mpingowo. Konzani zakuti wofalitsa mmodzi kapena awiri adzafotokoze zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo. Tchulani mfundo imodzi kapena ziwiri zimene mpingo wanu uyenera kugwirirapo ntchito chaka talowachi, ndipo fotokozani zimene zingathandize mpingo wanu kuwongolere m’chaka chimenechi.
Mph. 10: “Malangizo Okhudza Abale Amene Amakamba Nkhani pa Msonkhano wa Utumiki.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu.
Mph. 10: Thandizani Mwana Wanu Kukhala Wofalitsa. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Gulu, tsamba 81 ndi 82, ndime 1. Funsani kholo lachitsanzo chabwino limene lili ndi mwana wamng’ono yemwe ndi wofalitsa wosabatizidwa. Kodi linathandiza bwanji mwanayo kuti apite patsogolo ndi kuyenerere kukhala wofalitsa?