“Lemekeza Yehova ndi Chuma Chako”—Gawo 1
1. (a) Kodi njira imodzi imene tingalemekezere Yehova ndi yotani? (b) Kodi mabokosi onse a zopereka ndi ofanana?
1 Werengani Miyambo 3:9. Malinga ndi lembali, mipingo yonse iyenera kukhala ndi mabokosi a zopereka. Dongosolo limeneli limatipatsa mwayi wothandiza nawo mwa kufuna kwathu mbali zosiyanasiyana za kulambira koyera. Komabe, kodi cholinga cha mabokosi osiyanasiyana a zopereka amenewa n’chiyani? Kodi tiyenera kuwagwiritsa ntchito bwanji? Kwa miyezi ingapo , tikambirana mafunso amenewa m’nkhani imeneyi ya zigawo zitatu. Chigawo choyamba chifotokoza mmene tizigwiritsira ntchito bokosi kapena kachigawo kolembedwa kuti, “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse—Mateyu 24:14.”
2. (a) Kodi cholinga cha bokosi lolembedwa kuti, “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse—Mateyu 24:14” n’chiyani?
2 Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse—Mateyu 24:14: Timagwiritsa ntchito bokosi limeneli pothandiza pa ntchito yolalikira ya padziko lonse. Tikafuna kusonyeza kuyamikira chifukwa cha zofalitsa zathu ndiponso kuchirikiza ntchito yolalikira, timaika zopereka zathu m’bokosi limeneli. Komanso, ndalama zilizonse zimene tingalandire kwa anthu achidwi mu utumiki wakumunda tiyenera kuziika m’bokosi limeneli. Kenako mpingo uyenera kutumiza ndalamazi kapena kuziika mu akaunti ya ofesi ya nthambi ku banki mwezi uliwonse. Ndalama zimene zimaikidwa m’bokosi limeneli siziyenera kugwiritsidwa ntchito pampingo kapena kudera. Cholinga choikira ndalama m’bokosi limeneli ndicho kuthandiza pa ntchito yolalikira ya padziko lonse.
(b) Kodi ndalama zoiikidwa m’bokosi limeneli muyenera kutani nazo mwezi uliwonse?
(c) Kodi simuyenera kuchita nazo chiyani ndalama zimenezi?