Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tingatani kuti tizisunga nthaŵi pamisonkhano ya mpingo?
Nthaŵi imathamanga kwambiri tikamakambirana zinthu zosangalatsa ndi mabwenzi athu. Pachifukwa chimenechi, kungakhale kovuta kukamba nkhani malinga ndi nthaŵi yake. Kodi chingathandize n’chiyani?
Yambani panthaŵi yake. Mpingo wonse ukasonkhana, zimathandiza kupempha omvera kuti akhale pansi kudakali mphindi imodzi kapena ziŵiri pulogalamu isanayambe. Zikatere, msonkhano umayamba panthaŵi yake komanso mwadongosolo. (Mlal. 3:1) Misonkhano ya timagulu tochepa, monga misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda, isamayambe mochedwa pofuna kuyembekeza obwera mochedwa.
Konzekerani bwinobwino. Chinsinsi chosungira nthaŵi ndi kukonzekera pasadakhale. Khalani ndi cholinga cha nkhani yanuyo m’maganizo. Dziŵani mfundo zazikulu, ndipo gogomezerani zimenezo kuti zionekere. Peŵani kutengeka ndi mfundo zing’onozing’ono zosafunikira kwenikweni. Feŵetsani nkhani yanu poikamba. Ngati nkhani yanu ili ndi zitsanzo kapena kufunsa, yesezani zimenezo pasadakhale. Ngati kutheka, onani kuti nkhani yanu ikutenga nthaŵi yaitali bwanji pamene mukuyeseza kuikamba mokweza.
Gaŵani nkhani yanuyo. Kaya nkhani yanuyo ndi yokamba inu nokha kapena yokambirana ndi omvera, zidzakuthandizani kuigaŵa zigawozigawo. Sankhani mphindi zimene mudzathera pa chigawo chilichonse, ndipo lembani zimenezi m’mphepete mwa notsi zanu. Ndiye pamene mukukamba, yang’anani nthaŵiyo kuti muone ngati mukuisunga. Pankhani yokambirana ndi omvera, peŵani msampha wofuna ndemanga zambiri m’chigawo choyambirira chifukwa, kupanda kutero, mudzafulumira pokambirana mfundo zikuluzikulu zofunika kwambiri zimene zili kutsogolo. Ochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda ayenera kuonetsetsa kuti ali ndi nthaŵi yokwanira yokambirana bokosi la mafunso obwereza la kumapeto kwa phunzirolo. Afunikanso kusamala kuti asadye nthaŵi ya nyimbo ndi pemphero lomaliza.
Malizani panthaŵi yake. Msonkhano ukakhala ndi mbali zingapo, mwachitsanzo Msonkhano wa Utumiki, wokamba nkhani aliyense ayenera kudziŵa nthaŵi imene nkhani yake iyambe ndi kutha. Kodi angachite chiyani akaona kuti msonkhano ukhoza kupitirira nthaŵi imene ukufunika kutha? Mbale mmodzi kapena oposerapo angafupikitse nkhani yake kuti msonkhanowo uthebe panthaŵi yake mwa kukamba mfundo zikuluzikulu zokha ndi kusiya mfundo zosafunikira kwenikweni. Mphunzitsi waluso amatha kuchita zimenezi.
Ifeyo monga omvera, tingam’thandize kwambiri mbale amene akuchititsa msonkhanowo ngati tipereka ndemanga zachidule komanso mfundo zofunikira zokha. Chotero, tonsefe tingalimbikitse kuti misonkhano izichitika “koyenera ndi kolongosoka.”—1 Akor. 14:40.