Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/08 tsamba 1
  • Ndandanda Yatsopano ya Misonkhano ya Mpingo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda Yatsopano ya Misonkhano ya Mpingo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Mungatani Kuti Msonkhano Wokonzekera Utumiki Uzikhala Wothandiza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Muli Olandiridwa
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Misonkhano Imene Imatilimbikitsa “pa Chikondi Ndi Ntchito Zabwino”
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 10/08 tsamba 1

Ndandanda Yatsopano ya Misonkhano ya Mpingo

1, 2. Kodi misonkhano yathu isintha bwanji kuyambira mu January 2009?

1 Mlungu woyambira April 21 mpaka 27, 2008, abale padziko lonse tinamva chilengezo chosangalatsa kwambiri. Chilengezo chake chinali chakuti: “Kuyambira pa January 1, 2009, Phunziro la Buku la Mpingo lizichitikira limodzi ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Msonkhano wa Utumiki. Dzina la Phunziro la Buku la Mpingo lidzasintha kukhala Phunziro la Baibulo la Mpingo.”

2 Ndandanda ya Misonkhanoyi Mlungu Uliwonse: Misonkhano yonseyi, kuphatikizapo nyimbo ndi mapemphero, izichitika kwa ola limodzi ndi mphindi 45. Misonkhanoyi iziyamba ndi nyimbo ndi pemphero (mph. 5), kenako tizichita Phunziro la Baibulo la Mpingo (mph. 25). Pambuyo pake tizichita Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (mph. 30), kenaka tiziimba nyimbo (mph. 5) yotsegulira Msonkhano wa Utumiki (mph. 35). Ndiyeno tizimaliza ndi nyimbo ndi pemphero (mph. 5). Pofuna kukuthandizani kuti muzikonzekera misonkhanoyi, mwezi uliwonse mu Utumiki Wathu wa Ufumu tiziikamo ndandanda ya Phunziro la Baibulo la Mpingo, Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ndiponso ya Msonkhano wa Utumiki.

3. Kodi Phunziro la Baibulo la Mpingo lizichitika motani?

3 Phunziro la Baibulo la Mpingo: Msonkhano umenewu uzichitika mofanana ndi mmene timachitira Phunziro la Nsanja ya Olonda. Poyamba phunziroli musabwereze mfundo za mlungu watha. Koma muziyamba ndi mawu achidule basi. Tikufuna kuti pazikhala nthawi yokwanira yoti aliyense aziyankhapo koma mwachidule. Woyang’anira wotsogolera ndiye aziyang’anira ntchito yosankha akulu oti azichititsa msonkhanowu mosinthanasinthana, mlungu uliwonse. Mlungu uliwonse azichititsa mkulu wina.

4. Kodi ndi zinthu zotani zimene zisinthe pa Msonkhano wa Utumiki?

4 Msonkhano wa Utumiki: Msonkhano wa Utumiki sunasinthe, kungoti nkhani zake zizikhala zifupizifupi. Nthawi zambiri zilengezo zizikhala mphindi zisanu basi. Iyi ndi nthawi yokwanira kulengeza zinthu zofunika panthawiyo komanso kuwerenga makalata ena ochokera kunthambi. Zilengezo zonse monga zokhudza kulowa mu utumiki wa kumunda, kuyeretsa, malipoti a maakaunti, ndiponso makalata amene timalandira nthawi zonse kuchokera ku ofesi ya nthambi, zisamawerengedwe pa pulatifomu, koma zizikhomedwa pabolodi kuti aliyense azidziwerengera yekha. Anthu amene apatsidwa nkhani azikonzekera kwambiri, asamadye nthawi ngakhale pang’ono, komanso azitsatira ndendende malangizo a nkhani yawo.

5. Kodi misonkhano izichitika motani pamlungu umene woyang’anira dera akuchezera mpingo?

5 Kuyendera kwa Woyang’anira Dera: Ndandanda ya mlungu umene woyang’anira dera amachezera mpingo sinasinthe ayi. Lachiwiri tizichita Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Msonkhano wa Utumiki ndiyeno n’kuimba nyimbo. Kenaka woyang’anira dera azikamba nkhani ya mphindi 30. Monga mmene tikuchitira panopa, m’kati mwa mlungu umenewu pazikhalanso tsiku limodzi limene tizichita Phunziro la Baibulo la Mpingo kenaka n’kuimba nyimbo. Ndiyeno woyang’anira dera azitikambira nkhani ya utumiki ndipo pamapeto pa msonkhanowu tiziimba nyimbo n’kumaliza ndi pemphero.

6. Kodi udindo wa woyang’anira kagulu ndi wotani?

6 Misonkhano Yokonzekera Utumiki wa Kumunda: Oyang’anira timagulu azisankhidwa ndi bungwe la akulu kuti azitsogolera timagulu ta utumiki wa kumunda komanso kuti azipanga maulendo a ubusa kwa anthu a m’kaguluko. Ngati m’baleyo ali mtumiki wothandiza, azitchedwa kuti “mtumiki wakagulu.”

7. Kodi tiyembekezere kuti misonkhano yathu yatsopano itithandiza motani?

7 Mungathe kuona m’nkhani ino kuti pamisonkhano yathuyi tizilandira malangizo otilimbikitsa kwambiri mwauzimu. Motero tikhala alaliki komanso aphunzitsi ogwira mtima, odziwadi kuchita utumiki mobala zipatso.—Aef. 4:13, 14; 2 Tim. 3:17.

8. Kodi kukonzekera kungatithandize motani ifeyo komanso anthu ena?

8 Tiyenera kukonzekera misonkhano imeneyi kuti tidziwe mfundo zazikulu zimene zizifotokozedwa pa misonkhano imeneyi. Pazikhala mwayi woyankhapo ndipo zimenezi zizithandiza kuti tizilimbikitsana. (Aroma 1:11, 12; Aheb. 10:24) Cholinga chathu chikhale choti ‘kupita kwathu patsogolo kuonekere kwa anthu onse.’ Izi zingaonekere ngati ‘tikuwalondoloza bwino mawu a choonadi.’—1 Tim. 4:15; 2 Tim. 2:15.

9. Kodi tonsefe tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani ndipo n’chifukwa chifukwa chiyani tiyenera kutero?

9 Ndife osangalala kwambiri ndi kusintha kwa misonkhano kumeneku. Tonsefe tiyenera kuyesetsa kupitiriza kugwiritsira ntchito malangizo amene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akutipatsa. Tiyeneranso kuyesetsa kuyandikira kwambiri kwa Mbusa wathu Wamkulu, amene akutithandiza kukonzekera “chisautso chachikulu” chimene chili pafupi.—Mat. 24:21, 45; Aheb. 13:20, 21; Chiv. 7:14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena