Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndani ayenera kuuza mpingo kuti uimirire ndi kuimba nyimbo yotsegulira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, Msonkhano wa Utumiki, Msonkhano wa Onse, ndiponso Msonkhano wa Phunziro la Nsanja ya Olonda? Nanga ayenera kuchita zimenezi motani?
Pa Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu amalembapo nyimbo zotsegulira msonkhano mlungu uliwonse. Ndandandayi imakhala mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa October. Nyimbo zotsegulira ndi kutsekera Msonkhano wa Utumiki uliwonse zimalembedwa pa tsamba 2 la Utumiki Wathu wa Ufumu. Nazonso nyimbo za Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu uliwonse zimapezeka pa tsamba 2 la magazini iliyonse ya Nsanja ya Olonda. Nyimbo iliyonse imene yasankhidwa pa msonkhano uliwonse ndi mbali ya msonkhanowo, motero m’bale amene akutsogolera msonkhanowo ndiye ayenera kuuza anthu kuti aimirire ndi kuimba nyimboyo, osati tcheyamani wa msonkhano umene wangotha kumene.
Mwachitsanzo, woyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu azilonjera anthu, kuwauza kuti aimirire ndi kuimba nyimbo yotsegulira. Ndiyeno azichititsa sukuluyo, ndipo akatsiriza aziitana m’bale amene ali ndi mbali yoyamba mu Msonkhano wa Utumiki. M’bale ameneyu ndiye ayenera kuuza anthu kuti aimirire ndi kuimba nyimbo yotsegulira Msonkhano wa Utumiki.
Msonkhano wa Onse uyeneranso kuyambitsidwa ndi tcheyamani. Iyeyu azilonjera anthu onse obwera pa msonkhanowu mwansangala, n’kuwapempha kuti aimirire ndi kuimba nyimbo yotsegulira imene wokamba nkhaniyo wasankha. Tcheyamaniyo (kapena m’bale wina woyenerera amene wapatsidwa mbali imeneyi pasadakhale) azitsegula msonkhanowo ndi pemphero. Iyeyu aziitana wokamba nkhani n’kutchula mutu wa nkhani ya onseyo. Nkhani ikatha, tcheyamaniyo asachulutse gaga mdiwa mwa kubwereza mfundo za m’nkhaniyo mwachidule. Koma angoyamikira nkhaniyo mwachidule basi. Akatero azilengeza mutu wa nkhani ya onse ya mlungu wotsatira, ndipo aziuza omvetsera kuti tsopano ndi nthawi ya Phunziro la Nsanja ya Olonda. Ngati wokamba nkhaniyo wachokera ku mpingo wina, tcheyamaniyo asafunse omvetsera kuti iye awatengere moni wawo kupita ku mpingo umene wachokera. Kenaka tcheyamaniyo aziitana wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda.
Wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olondayo aziuza anthu kuti aimirire ndi kuimba nyimbo yotsegulira phunziroli. Iye azichititsa msonkhanowu mogwirizana ndi malangizo amene gulu la Yehova linapereka ndipo akamaliza azilengeza nyimbo yothera. Iyeyu amayenera kuitana m’bale amene wakamba nkhaniyo kuti apereke pemphero lomaliza.
Kutsatira mfundo zotsatirazi kungathandize kuti misonkhano yathu izikhala yofanana m’mipingo yonse.