PHUNZIRO 4
Kulankhula Mosadodoma
KODI mukamaŵerenga mokweza mumapunthwa pa mawu ena? Kapena mukaimirira pamaso pa gulu kuti mulankhule, kodi mumakhala ndi vuto posankha mawu oyenerera? Ngati mumatero, mungakhale ndi vuto la kudodoma. Munthu wosadodoma amaŵerenga ndi kulankhula m’njira yoti mawu ndi malingaliro ake amveke bwinobwino, komanso mosavuta kuwatsatira. Zimenezi sizitanthauza kuti iye amangolankhula mosapumira, kapena kuti amalankhula mothamanga kwambiri, kapena kulankhula mosalingalira ayi. Mawu ake amamveka osangalatsa ndi okoma. Kulankhula mosadodoma kwafotokozedwa bwino kwambiri mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Pali zinthu zosiyanasiyana zimene zingapangitse munthu kumadodoma polankhula. Kodi inuyo mungafunikire kuwongolera pa mbali zotsatirazi? (1) Poŵerengera ena, mungadodome chifukwa cha mawu amene simunawazoloŵere. (2) Kuimaima paliponse kumajejemetsa kaŵerengedwe. (3) Kusakonzekera kungapangitsenso vuto limenelo. (4) Polankhula pamaso pa gulu, chimene chimachititsa kudodoma kaŵirikaŵiri ndi kusayala mfundo m’ndondomeko yabwino. (5) Kusadziŵa kwambiri chinenero kungachititse munthu kudodomadodoma pofunafuna mawu oyenerera. (6) Ngati mutsindika mawu ambiri, mumayamba kulankhula mododoma. (7) Kusadziŵa bwino galamala kungapangitsenso vutolo.
Ngakhale kuti mukulankhula mododoma anthu sangatulukemo mu Nyumba ya Ufumu ayi koma maganizo awo angayambe kuyendayenda. Pachifukwa chimenechi, zambiri zimene munganene zingatayike.
Komanso, m’pofunika kusamala kotero kuti kalankhulidwe kamene kakanakhala kamphamvu ndi kosadodoma kasakhale kolamula, osatinso konyazitsa omvera ayi. Kalankhulidwe kooneka kukhala kamwano kwa anthu ena, kapena komveka kosadalirika chifukwa cha kusiyana kwa zikhalidwe, kamawononga cholinga chanu. Ngakhale kuti mtumwi Paulo anali katswiri wokamba nkhani, onani kuti anafikira Akorinto “mofooka ndi m’mantha, ndi monthunthumira” pokana kudzikweza.—1 Akor. 2:3.
Zizoloŵezi Zoyenera Kupeŵa. Anthu ambiri polankhula amakonda kunena pafupipafupi mawu akuti “ndipo-ee.” Ena amakonda kuyamba chilichonse chimene afuna kunena ndi mawu akuti “choncho,” “mudziŵa,” “mungaone kuti,” ndi ena otero. Mwina simukudziŵa kuti mumatchula mawuŵa kaŵirikaŵiri. Yesani kuti wina azikumvetserani ndipo azibwereza nthaŵi iliyonse pamene muwanena mawuwo. Mukhoza kudabwa.
Anthu ena amakonda kubwerezabwereza poŵerenga. Amayamba sentensi, kenako n’kudzidula okha ndi kuyambiranso zimene anena kale.
Pali ena amene amalankhula bwino, koma vuto lawo n’lakuti amayamba ndi lingaliro ili, kenako chapakati pa sentensi, amasinthira ku lingaliro lina. Ngakhale kuti mawu amatuluka bwinobwino, kusinthasintha malingaliro kumawononga kalankhulidwe kabwino.
Mmene Mungathetsere Vutolo. Ngati vuto lanu ndi kupeza mawu oyenerera, muyenera kuchita khama kuti muphunzire mawu ambiri a chinenerocho. Samalani kwambiri mawu osazoloŵereka mu Nsanja ya Olonda, Galamukani!, ndi mabuku ena amene mumaŵerenga. Yang’anani mawuwo mu mtanthauzira mawu, ndipo awonjezereni pa mawu amene mukuwadziŵa kale. Ngati mulibe mtanthauzira mawu, funsani kwa munthu wina amene amalankhula bwino chinenerocho.
Kukhala ndi chizoloŵezi choŵerenga mokweza nthaŵi zonse kungathandize kuthetsa vutolo. Samalirani mawu ovuta, ndipo muziwatchula mobwerezabwereza.
Kuti muziŵerenga mosadodoma, m’pofunika kudziŵa mmene mawu amagwirira nchito pamodzi m’sentensi. Kaŵirikaŵiri, mawu ayenera kuŵerengedwa m’magulu kuti apereke lingaliro la wolemba. Samalani magulu a mawu oterowo. Ngati kungakuthandizeni, aikeni chizindikiro. Cholinga chanu si kungoŵerenga mawu molondola, koma kuperekanso malingaliro momvekera bwino. Mutapenda sentensi imodzi, pitani pasentensi ina mpaka mutaŵerenga ndime yonse. Dziŵani bwino mgwirizano wa malingalirowo. Kenako yesezani kuŵerenga mokweza. Ŵerengani ndime imodzi mobwerezabwereza kufikira mutakhoza kuŵerenga mosapunthwa ndi mosapumira m’malo olakwika. Ndiyeno pitani pa ndime zina.
Kenako, wonjezerani liŵiro lanu. Ngati mwadziŵa mmene mawu amagwirira ntchito pamodzi m’sentensi, mudzatha kumaona mawu angapo nthaŵi imodzi ndi kudziŵiratu mawu otsatira. Zimenezi zidzathandiza kwambiri kuti muziŵerenga mwaluso.
Kukhala ndi chizoloŵezi choŵerenga mokweza mosakonzekera kungakhale kothandiza. Mwachitsanzo, ŵerengani mokweza lemba la tsiku ndi ndemanga yake popanda kukonzekera; chitani zimenezi nthaŵi zonse. Zoloŵezani maso anu kuona magulu a mawu opereka malingaliro m’malo moona liwu limodzi nthaŵi imodzi.
Kuti mulankhule mosadodoma pokambirana, muyenera kulingalira musanalankhule. Khalani ndi chizoloŵezi chimenecho pamoyo wanu wa tsiku ndi tsiku. Sankhani malingaliro amene mukufuna kunena ndi dongosolo lowanenera; mukatero yambani kulankhula. Musadye mfulumira. Yesetsani kunena ganizo lonse popanda kuima kapena kusintha malingaliro musanamalize ganizolo. N’kothandiza kunena masentensi aafupi ndi osavuta.
Ngati mukudziŵa zimene mukufuna kunena, mawu amatuluka mwachibadwa. Kwenikweni, m’pofunika kusankha mawu amene mukufuna kunena. Pofuna kuzoloŵera, ndi bwino kutsimikiza choyamba m’maganizo mwanu za malingaliro, kenako n’kuganiza za mawu pamene mukulankhula. Ngati mutero, komanso ngati muika maganizo anu pa malingaliro m’malo mwa mawu amene mukulankhula, mawu ake adzabwera mwachibadwa, ndipo mudzawalankhula mochokeradi mumtima. Koma mukangoyamba kuganiza za mawu m’malo mwa malingaliro, kalankhulidwe kanu kadzakhala kododoma. Mwa kuyeseza, mukhoza kupambana pakulankhula mosadodoma, kumene ndiko mbali yofunika kwambiri ya kulankhula ndi kuŵerenga mogwira mtima.
Pamene Mose anatumidwa kukaimira Yehova ku mtundu wa Israyeli ndi pamaso pa Farao wa ku Igupto, anaona kuti sakanatha. Chifukwa chiyani? Sanali kutha kulankhula bwinobwino; mwina anali ndi vuto lachibadwa. (Eks. 4:10; 6:12) Mose anapereka zifukwa zodzikhululukira, koma Mulungu sanavomereze n’chimodzi chomwe. Yehova anatumiza Aroni kukhala wolankhulira Mose, koma anathandizanso Mose kulankhula. Mobwerezabwereza komanso mogwira mtima, Mose analankhula osati chabe kwa mmodzi ndi mmodzi wa anthu, komanso ku timagulu ta anthu, ndi ku mtundu wonse. (Deut. 1:1-3; 5:1; 29:2; 31:1, 2, 30; 33:1) Inunso ngati mulimbikira mbali yanu ndi mtima wonse podalira Yehova, mukhoza kugwiritsa ntchito luso lanu la kulankhula kulemekezera Mulungu.