Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 11 tsamba 118-tsamba 120 ndime 5
  • Mzimu Waubwenzi ndi Mmene Mukumvera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mzimu Waubwenzi ndi Mmene Mukumvera
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuonetsa Kutengeka Mtima ndi Mzimu Waubwenzi
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kupsinjika Mtima Kodi Mungakulake?
    Galamukani!—1992
  • Lolani Kudziletsa Kwanu Kukhalepo Nikusefukire
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 11 tsamba 118-tsamba 120 ndime 5

PHUNZIRO 11

Mzimu Waubwenzi ndi Mmene Mukumvera

Kodi muyenera kuchita motani?

Lankhulani mwa njira yoonetsa mmene mukumvera mu mtima mwanu ndi mogwirizana ndi zimene mukunena.

N’chifukwa chiyani zili zofunikira?

Zimathandiza kuwafika pamtima omvera anu.

KUKHUDZIKA mtima ndi mbali yaikulu ya moyo wa munthu. Pamene munthu aonetsa mmene wakhudzidwira mumtima, amavumbula zimene zili mumtima mwake, umunthu wake wam’kati, mmene akuonera makhalidwe akutiakuti ndi anthu. Anthu ambiri amabisa mmene amamvera m’mtima mwawo chifukwa chozoloŵera kukumana ndi zovuta pamoyo wawo—nthaŵi zina chifukwa cha chikhalidwe cha kumene anakulira. Koma Yehova amatilimbikitsa kusonyeza makhalidwe abwino a munthu wam’kati ndi kuwaonetsa m’njira yoyenera.—Aroma 12:10; 1 Ates. 2:7, 8.

Pamene tilankhula, mawu athu amasonyeza mmene tikumvera mumtima. Ngati mawu athu sasonyeza mmene tikumvera, otimvera angayambe kutikayikira. Koma ngati mawu athu tiwatchula mosonyeza mmene tikumvera, nkhani yathu imakhala yokoma ndi yopindulitsa ndipo imakhudza mitima ya omvera athu.

Kusonyeza Mzimu Waubwenzi. Mzimu waubwenzi kaŵirikaŵiri umasonyezedwa polingalira za anthu ena. Choncho, polankhula za makhalidwe a chikondi cha Yehova ndi polankhula zoyamikira Yehova chifukwa cha ubwino wake, mawu athu ayenera kusonyeza mzimu waubwenzi. (Yes. 63:7-9) Polankhula ndi anthu anzathu, malankhulidwe athu azisonyezanso mzimu waubwenzi.

Tayerekezani kuti munalipo pachochitikacho. Mukumuona wakhateyo akubwera kwa Yesu ndipo akupempha kuti am’chiritse. Tamverani mmene mawu a Yesu akumvekera pamene akunena kuti: “Ndikufuna; khala wokonzedwa.” (Marko 1:40, 41) Yerekezaninso kuti munalipo pamene mkazi yemwe ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12 anafikira Yesu mwakachetechete mom’dzera kumbuyo, nagwira mphonje ya chovala chake. Mkaziyo ataona kuti Yesu wazindikira zimene iye wachita, akubwera kumaso kwake akunjenjemera, nagwa pamapazi pa Yesu, ndi kuulula pamaso pa anthu onse chimene wagwirira chovala cha Yesu ndi kuti tsopano wachira. Tamverani mawu a Yesu pamene akunena kuti: “Mwana wanga, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.” (Luka 8:42b-48) Mzimu waubwenzi umene Yesu anasonyeza pazochitikazo wakhudza mitima ya anthufe mpaka lero.

Mofanana ndi Yesu, pamene timvera chifundo anthu ena ndi pofunitsitsa kuwathandiza, kalankhulidwe kathu kasonyeze zimenezo. Kusonyeza mzimu waubwenzi koteroko kumakhala kochokera pansi pa mtima, osati kwachiphamaso. Mzimu wathu waubwenzi ukhoza kuthandiza anthu kulabadira. Zambiri zimene timanena mu utumiki wa kumunda zimafuna kusonyeza mzimu waubwenzi, makamaka pamene tikukambirana ndi anthu, powalimbikitsa, powalangiza ndi powapepesa.

Ngati muli ndi mzimu waubwenzi kwa ena, uonetseni pankhope panu. Mukasonyeza mzimu waubwenzi, omvera anu amakopeka nanu, muja timakopekera ndi moto kukazizira madzulo. Ngati mzimu waubwenzi suonekera pankhope panu, omvera anu sangakhutire kuti mukuwaderadi nkhaŵa. N’zosatheka kungouvala pankhope mzimu waubwenzi—uyenera kukhala weniweni.

Mzimu waubwenzi uyenera kumvekanso m’mawu anu. Ngati muli ndi mawu amphamvu ndi okakala, kungakhale kovuta kuti musonyeze mzimu waubwenzi m’mawu anu. Koma m’kupita kwanthaŵi ndi poyesayesa mwakhama, mukhoza kutero. Kumbukirani kuti, kulankhula modukizadukiza komanso mofulumira, kumachititsa mawu kumveka opanda mzimu waubwenzi. Phunzirani kutchula mawu modekha ndi mowatalikitsako. Mukatero mawu anu azimveka aubwenzi.

Komabe, chofunika kwambiri ndicho kumene mumaika chidwi chanu. Ngati maganizo anu amakhala pa anthu amene mukulankhula nawo ndipo mukufunitsitsa kupereka uthenga umene ungawapindulitse, chikhumbo chimenecho chidzaonekera m’kalankhulidwe kanu.

Kulankhula kwaumoyo kumalimbikitsa, koma mzimu waubwenzi ndi wofunikiranso. Sitiyenera kungokhutiritsa maganizo nthaŵi zonse; tiyeneranso kukopa mtima.

Kusonyeza Makhalidwe Ena Okhudza Mtima. Makhalidwe okhudza mtima monga nkhaŵa, mantha, ndi kuvutika maganizo angaonekere kwa munthu wokhala pavuto linalake. Chimwemwe ndi mkhalidwe wokhudza mtima, tiyenera kuukulitsa m’mitima yathu ndi kuusonyeza momasuka polankhula ndi ena. Komabe, pali makhalidwe ena okhudza mtima amene tiyenera kuwalamulira. Amenewo sagwirizana ndi khalidwe lachikristu. (Aef. 4:31, 32; Afil. 4:4) Makhalidwe okhudza mtima osiyanasiyana tingawasonyeze ndi mawu amene timagwiritsa ntchito, kamvekedwe ka mawu, mphamvu ya mawu, nkhope, ndi manja.

Baibulo limafotokoza za mitundu yosiyanasiyana ya makhalidwe okhudza mtima. Nthaŵi zina limangotchula kuti mtima. Nthaŵi zina limasimba zochitika kapena limagwira mawu omwe amasonyeza makhalidwe okhudza mtima. Pamene muŵerenga momveka nkhani zoterozo, zidzakhomerezeka kwambiri kwa inuyo ndi okumverani, ngati mawu anu asonyeza makhalidwe okhudza mtimawo. Kuti muchite zimenezo muyenera kudziyerekeza kukhala munthu amene mukuŵerenga za iye. Komabe, nkhani siiyenera kukhala ngati seŵero kapena chisudzo. Choncho samalani kuti musachite monyanyira. Ŵerengani zigawozo mwaumoyo kuti zikhomerezeke m’maganizo mwa omvera.

Kusonyeza Kukhudzika Mtima Koyenerana ndi Nkhaniyo. Mofanana ndi kulankhula mwaumoyo, mzimu waubwenzi ndi mitundu ina ya makhalidwe okhudza mtima imene mumasonyeza m’mawu anu, imadalira kwambiri zimene mukunena.

Tsegulani pa Mateyu 11:28-30 ndi kuona zimene akunena. Ndiyeno ŵerengani mawu a Yesu odzudzula alembi ndi Afarisi, olembedwa pa Mateyu chaputala 23. N’zosatheka kuyerekeza kuti Yesu anali kupereka chidzudzulo choŵaŵa chimenechi ndi mawu opola ndi amphwayi.

Muganiza ndi mzimu wotani wofunika kuŵerenga nawo nkhani yopezeka pa Genesis chaputala 44 yonena za kuchonderera kwa Yuda m’malo mwa mbale wake Benjamini? Onani kukhudzika mtima kosonyezedwa pavesi 13, kapena mmene Yuda anamvera chifukwa cha tsokalo pa vesi 16, ndi mmenenso Yosefe mwiniwakeyo analankhulira, pa Genesis 45:1.

Choncho, kaya tikuŵerenga kapena kulankhula, kuti titero mogwira mtima, tisalingalire za mawu ndi maganizo okha, komanso mzimu wake wa mawuwo.

MMENE TINGASONYEZERE MMENE TIKUMVERA

  • M’malo modera nkhaŵa kwambiri za mawu amene mukugwiritsa ntchito, khalani ndi chidwi chofuna kuthandiza omvera anu.

  • Mawu anu ndi nkhope ziyenera kusonyeza makhalidwe okhudza mtima oyenerera nkhaniyo.

  • Phunzirani mwa kuonetsetsa mmene ena amalankhulira mogwira mtima.

ZOCHITA: Ŵerengani mokweza Malemba otsatiraŵa, ndi kusonyeza mzimu woyenerera zochitikazo: Mateyu 20:29-34; Luka 15:11-32.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena