PHUNZIRO 12
Manja ndi Nkhope Polankhula
M’MAYIKO ena, anthu amalankhula ndi manja momasuka kuposa kumayiko ena. Komabe, munthu aliyense polankhula amagwiritsa ntchito nkhope ndi manja. Kaya pokambirana kapena polankhula pamaso pa gulu.
Yesu ndi ophunzira ake oyambirira anali kugwiritsa ntchito manja mwachibadwa polankhula. Panthaŵi ina, munthu wina anafika kwa Yesu ndi kumuuza kuti mayi wake ndi abale ake anafuna kulankhulana naye. Poyankha Yesu anati: “Amayi wanga ndani? Ndi abale anga ndani?” Kenako Baibulo limapitiriza kuti: ‘Anatambasula dzanja lake pa ophunzira ake, nati, Penyani amayi wanga ndi abale anga!’ (Mat. 12:48, 49) Mwa malemba ena, Baibulo limasonyezanso pa Machitidwe 12:17 ndi 13:16 kuti atumwiwonso, Petro ndi Paulo, anagwiritsa ntchito manja mwachibadwa polankhula.
Si mawu okha amene timasonyezera maganizo athu ndi mmene tikumvera, komanso manja ndi nkhope. Wolankhula akapanda kugwiritsa ntchito bwino manja ndi nkhope, amaonetsa kuti alibe chidwi ndi nkhani imene akunena. Koma ngati tizigwiritsa ntchito mwaluso, timalankhula mogwira mtima kwambiri. Ngakhale polankhula pafoni, ngati mugwiritsa ntchito bwino manja ndi nkhope, kamvekedwe ka mawu anu kadzasonyeza kufunika kwa uthenga wanu ndi mmene mukumvera pa zimene mukunenazo. Choncho, kaya mukulankhula kuchokera mumtima kapena mukuŵerenga, kaya omvera anu akukuyang’anani kapena akuyang’ana m’mabaibulo awo, kugwiritsa ntchito manja ndi nkhope n’kofunika kwambiri.
Kachitidwe ka manja ndi nkhope kakhale kachibadwa, osati kotengera wina. Simunachite kuphunzira kuseka kapena kukwiya. Manja ayenera kusonyezanso mmene mukumvera m’mtima mwanu. Manja akakhala achibadwa, mumalankhula bwino.
Manja ali m’magulu aŵiri: ofotokoza ndi otsindika. Manja ofotokoza amaonetsa mmene chinthu chinachitikira, ukulu, kapena kulozera malo. M’sukuluyi, ngati munauzidwa kukonzekera kugwiritsa ntchito manja, musakhutire ndi kulankhula ndi manja kamodzi kapena kaŵiri kokha. Yesani kugwiritsa ntchito manja mwachibadwa m’nkhani yonseyo. Ngati zikukuvutani, yesani kupeza mawu osonyeza malo, mtunda, ukulu, kapena malo oyerekezedwa ndi anzake. Komabe, nthaŵi zambiri zimangofuna kuika maganizo onse pankhaniyo, osada nkhaŵa kuti anthu akuganiza chiyani za inu, koma lankhulani ndi kuchita zinthu monga mwa tsiku ndi tsiku. Munthu akamalankhula momasuka, manja amangochitika mwachibadwa.
Manja otsindika amasonyeza mmene munthu akumvera ndi kutsimikiza mtima kwake. Amapereka mphamvu ya malingaliro, ndi chithunzi cha m’maganizo. Manja otsindika ndi ofunika kwambiri. Koma samalani! Manja otsindika akhoza kukhala chizoloŵezi choipa. Ngati mupanga manja ofanana mobwerezabwereza, anthu angayambe kudabwa manjawo m’malo mwakuti awathandize kumvera nkhani. Ngati woyang’anira sukulu anena kuti muli ndi vuto limeneli, yesani kumapanga manja ofotokoza okha pakali pano. M’kupita kwa nthaŵi, dzayeseninso kupanga manja otsindika.
Pofuna kudziŵa mmene mungapangire manja moyenerera, ganizirani kalingaliridwe ka anthu amene mukulankhula nawo. Kuloza chala omvera kungawakhumudwitse. Kumadera ena, amuna sagwira pakamwa posonyeza kudabwa. Akazi ndiwo amachita zimenezo. Kumbali zina za dziko, ndi kupanda ulemu ngati mkazi alankhula ndi manja momasuka kwambiri. M’madera amenewo, ndi bwino kuti alongo azigwiritsa ntchito kwambiri nkhope polankhula. Ndiponso, kulikonse padziko lapansi, kuponya manja kwambiri polankhula kwa anthu ochepa amakuona ngati chinthu choseketsa.
Pamene mukuzoloŵera kulankhula, manja otsindika alionse amene mungapange adzaonetsa mwachibadwa mmene mukumvera m’mtima, kutsimikiza mtima ndi kuona mtima kwanu. Adzawonjezera tanthauzo la mawu anu.
Maonekedwe a Nkhope Yanu. Kuposa mbali iliyonse ya thupi lanu, nkhope yanu kaŵirikaŵiri ndiyo imasonyeza kwambiri mmene mukumvera m’mtima. Maso anu, mmene pakamwa panu pachitira, kaimidwe ka mutu wanu, zonsezi zimachita mbali yofunika. Popanda mawu alionse, nkhope yanu imatha kuonetsa mphwayi, kunyansidwa, kuthedwa nzeru, kudabwa, kapena kukondwa. Machitidwe a nkhope ameneŵa akatsagana ndi mawu, amapereka zithunzi za m’maganizo ndi kukhudza mtima. Mlengi anaika nkhosi zambiri za mnofu pankhope panu—zopitirira 30. Pafupifupi theka la zimenezi zimagwira ntchito pamene mumwetulira.
Kaya muli papulatifomu kapena mu utumiki wa kumunda, cholinga chanu ndi kuuza anthu uthenga wosangalatsa, umene ungatsitsimule mitima yawo. Kumwetulira mwaubwenzi kumasonyeza zimenezo. Koma ngati nkhope yanu siisonyeza chilichonse, anthu angayambe kukukayikirani.
Ndiponso, kumwetulira kumasonyeza anthu ena kuti mukuwafunira zabwino. Izi n’zofunika kwambiri makamaka masiku ano pamene anthu nthaŵi zambiri amaopa anthu osawadziŵa. Kumwetulira kwanu kungapangitse anthu kumasuka ndi kumvetsera zimene mukunena.